1 Kings 20 (BOGWICC)
1 Tsono Beni-Hadadi mfumu ya ku Aramu inasonkhanitsa magulu ake onse a ankhondo. Iye pamodzi ndi mafumu 32, akavalo awo ndi magaleta awo, anapita kukawuzungulira mzinda wa Samariya ndi kuwuthira nkhondo. 2 Iye anatuma amithenga ake mu mzindamo kwa Ahabu mfumu ya Israeli, kukanena kuti, 3 “Beni-Hadadi akuti, ‘Siliva wako ndi golide wako ndi wanga, ndipo akazi ako okongola ndi ana ako ndi anganso.’ ” 4 Mfumu ya Israeli inayankha kuti, “Monga mmene mwanenera, mbuye wanga mfumu, ine pamodzi ndi zonse zomwe ndili nazo ndi zanu.” 5 Amithenga aja anabwereranso kwa Ahabu ndipo anamuwuza kuti, “Beni-Hadadi akuti, ‘Ine ndinakulamula kuti undipatse siliva wako ndi golide wako, akazi ako ndi ana ako. 6 Koma mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzatuma atumiki anga kudzafufuza mʼnyumba yako yaufumu ndi nyumba za akuluakulu ako. Iwo adzatenga chilichonse chimene umachidalira ndi kupita nacho.’ ” 7 Pamenepo mfumu ya Israeli inayitanitsa akuluakulu a mʼdzikomo niwawuza kuti, “Taonani momwe munthuyu akufunira kutibweretsera mavuto! Atatumiza mawu oti ndimupatse akazi anga ndi ana anga, siliva wanga ndi golide wanga, ine sindinamukanize.” 8 Akuluakulu onse ndi anthu onse anayankha kuti, “Musamumvere kapena kuvomereza zofuna zake.” 9 Tsono Ahabu anayankha amithenga a Beni-Hadadi kuti, “Kamuwuzeni mbuye wanga mfumu kuti, ‘Mtumiki wanu adzachita zonse zimene munazifuna nthawi yoyamba ija, koma izi mwazifunazi sindingazikwanitse.’ ” Iwo anachoka nakapereka yankho kwa Beni-Hadadi. 10 Pamenepo Beni-Hadadi anatumizanso uthenga wina kwa Ahabu kuti, “Milungu indilange koopsa, ngati mu Samariya mudzakhale fumbi loti nʼkudzaza dzanja la aliyense wa anthu anga.” 11 Mfumu ya Israeli inayankha kuti, “Kamuwuzeni kuti, ‘Mwamuna mnzako nʼpachulu, nʼkulinga utakwerapo.’ ” 12 Beni-Hadadi anamva uthenga umenewu pamene iye ankamwa ndi mafumu anzake mʼmatenti awo, ndipo analamula anthu ake kuti, “Konzekerani kukathira nkhondo.” Choncho anakonzekera kukathira nkhondo mzindawo. 13 Ndipo taonani, mneneri wina anabwera kwa Ahabu mfumu ya Israeli nadzalengeza kuti, “Yehova akuti, ‘Kodi ukuchiona chigulu chachikulu cha ankhondochi? Taona, ndikuchipereka chimenechi lero mʼdzanja lako, ndipo pamenepo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ” 14 Ahabu anafunsa kuti, “Koma ndani adzachita zimenezi?”Mneneri anayankha kuti, “Yehova akuti, ‘Adzachita zimenezi ndi asilikali a nduna za mʼzigawo.’ ”Ndipo iye anafunsa kuti, “Kodi ndani adzayambe nkhondoyi?”Mneneriyo anayankha kuti, “Ndinu.” 15 Choncho Ahabu anawerenga asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo ndipo onse analipo 232. Ndipo anawerenganso ankhondo a ku Israeli ndipo onse analipo 7,000. 16 Iwo ananyamuka nthawi yamasana pamene Beni-Hadadi ndi mafumu 32 othandizana naye ankamwa mpaka kuledzera mʼmatenti awo. 17 Asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo ndiwo amene anayamba kupita ku nkhondo.Nthawi imeneyi Beni-Hadadi nʼkuti atatumiza anthu oti akazonde, amene anadzafotokoza kuti, “Anthu ankhondo akubwera kuchokera ku Samariya.” 18 Iye anati, “Kaya akubwera mwamtendere kapena mwankhondo, muwagwire amoyo.” 19 Choncho asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo anatuluka mu mzinda, gulu lankhondo lili pambuyo pawo. 20 Ndipo aliyense wa iwo anapha munthu wake. Ataona izi, Aaramu anathawa Aisraeli ali pambuyo pawo kuwapirikitsa. Koma Beni-Hadadi mfumu ya ku Aaramu anathawa atakwera pa kavalo pamodzi ndi ankhondo ena okweranso pa akavalo. 21 Mfumu ya Israeli inapita chitsogolo ndi kugwira akavalo ndi magaleta ndipo Aaramu ambiri anaphedwa. 22 Zitachitika izi, mneneri wina anabwera kwa mfumu ya Israeli ndipo anati, “Mulimbike ndipo muganize bwino zoti mudzachite, chifukwa chaka chikudzachi mfumu ya Aramu idzakuthiraninso nkhondo.” 23 Nthawi imeneyi, akuluakulu a mfumu ya Aramu anamulangiza kuti, “Milungu ya anthu a ku Israeli ndi milungu ya mʼmapiri. Nʼchifukwa chake anali ndi mphamvu zotipambana ife. Koma ngati tidzamenyana nawo ku chigwa, ndithudi ife tidzakhala ndi mphamvu kuposa iwo. 24 Inu chitani izi: chotsani mafumu onse pa maudindo awo ndipo mʼmalo mwawo muyikemo atsogoleri a ankhondo. 25 Musonkhanitsenso gulu lankhondo lofanana ndi lomwe linaphedwa lija, akavalo monga omwe anaphedwa aja, ndi magaleta monga omwe anawonongedwa aja, kuti tikamenyane ndi Israeli ku chigwa. Pamenepo, ife tidzapambana iwowo.” Beni-Hadadi anagwirizana nawo ndipo anachita momwemo. 26 Chaka chinacho Beni-Hadadi anasonkhanitsa Aaramu, napita ku Afeki kukamenyana ndi Israeli. 27 Aisraeli atasonkhananso, napatsidwa zakudya zawo anapita kukakumana nawo. Aisraeli anamanga misasa yawo moyangʼanana ndi Aaramu ndipo ankaoneka ngati timagulu tiwiri ta mbuzi, pomwe Aaramu anali atakuta dera lonselo. 28 Munthu wa Mulungu anabwera, nawuza mfumu ya Israeli kuti, “Yehova akuti, ‘Popeza Aaramu akuganiza kuti Yehova ndi mulungu wa ku mapiri, osati wa ku zigwa, Ine ndidzapereka chigulu chonsechi kwa iwe, ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ” 29 Kwa masiku asanu ndi awiri anakhala moyangʼanana mʼmisasa yawo, ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri nkhondo inayambika. Aisraeli anapha Aaramu okwana 100,000 tsiku limodzi lokha. 30 Ena onse otsala anathawira ku Afeki, kumene khoma linagwera anthu 27,000. Ndipo Beni-Hadadi anathawira mu mzinda, nakabisala mʼchipinda chamʼkati. 31 Atumiki ake anamuwuza kuti, “Taonani, ife tamva kuti mafumu a fuko la Israeli ndi achifundo. Tiyeni tipite kwa mfumu ya ku Israeli titavala ziguduli mʼchiwuno mwathu ndi kumanga zingwe mʼmakosi mwathu. Mwina iye sakakuphani.” 32 Atavala ziguduli mʼchiwuno mwawo ndi kumanga zingwe mʼmakosi mwawo, anapita kwa mfumu ya ku Israeli ndipo anayiwuza kuti, “Mtumiki wanu Beni-Hadadi akunena kuti, ‘Chonde loleni kuti ndikhale moyo.’ ”Mfumu inayankha kuti, “Kodi iye akanali ndi moyo? Iye ujatu ndi mʼbale wanga.” 33 Anthuwo ankaganiza kuti mawuwo anali abwino ndipo anavomereza mawuwa mofulumira. Iwo anati, “Inde, Beni-Hadadi ndi mʼbale wanu!”Mfumu inati, “Pitani kamutengeni.” Beni-Hadadi atatuluka, Ahabu anamukweza mʼgaleta lake. 34 Beni-Hadadi anawuza Ahabu kuti, “Ndidzabweza mizinda imene abambo anga analanda abambo anu. Ndipo mutha kumanga nyumba zanu zamalonda mu Damasiko, monga anachitira abambo anga ku Samariya.”Ahabu anati, “Chifukwa cha mgwirizano umenewu, ine ndidzakumasula.” Choncho anachita naye mgwirizano, ndipo anamulola kuti apite. 35 Molamulidwa ndi Yehova, mmodzi mwa ana a aneneri anawuza mnzake kuti, “Chonde, menye ndi chida chako,” koma mnzakeyo anakana. 36 Choncho mneneriyo anati, “Chifukwa sunamvere Yehova, ukangochoka pano, mkango ukupha.” Ndipo munthuyo atangochoka pamenepo, mkango unamupeza ndi kumupha. 37 Mneneriyo anapeza munthu wina ndipo anamuwuza kuti, “Chonde, menye.” Choncho munthuyo anamumenya ndi kumuvulaza. 38 Pamenepo mneneriyo anapita nakayima pa msewu kudikirira mfumu. Iye anadzibisa nakulunga nsalu nkhope yake. 39 Mmene mfumu inkadutsa pamenepo, mneneriyo anafuwula kwa mfumuyo kuti, “Ine mtumiki wanu ndinalowa pakati pa nkhondo, ndipo munthu wina anabwera kwa ine atatenga mmodzi mwa anthu ogwidwa pa nkhondo, nandiwuza kuti, ‘Sunga munthu uyu. Ngati asowa, ndiye kuti ndidzakupha, kapena udzalipira ndalama 3,000 za siliva.’ 40 Pamene ine mtumiki wanu ndinali wotanganidwa apa ndi apa, munthuyo anasowa.”Mfumu ya Israeli inati, “Chimenechi ndiye chilango chako. Iwe wadziweruza wekha.” 41 Pamenepo mneneriyo anachotsa msangamsanga nsalu yomwe anakulunga pa nkhope yake, ndipo mfumu ya Israeli inamuzindikira kuti ndi mmodzi mwa aneneri. 42 Iye anawuza mfumu kuti, “Yehova akuti, ‘Chifukwa chakuti mwamasula munthu amene Ine ndinati ndi woyenera kuphedwa, inuyo ndi amene mudzaphedwe mʼmalo mwa iyeyo, anthu anu mʼmalo mwa anthu ake.’ ” 43 Mwachisoni ndi mokwiya, mfumu ya Israeli inapita ku nyumba yake yaufumu ku Samariya.