1 Kings 3 (BOGWICC)

1 Solomoni anachita ubale ndi Farao mfumu ya ku Igupto ndipo anakwatira mwana wake wamkazi. Mkaziyo anabwera naye mu Mzinda wa Davide mpaka anatsiriza kumanga nyumba yaufumu ndi Nyumba ya Yehova ndiponso khoma lozungulira Yerusalemu. 2 Koma anthu ankaperekabe nsembe ku malo achipembedzo osiyanasiyana chifukwa chakuti mpaka pa nthawi imeneyo Dzina la Yehova anali asanalimangire nyumba. 3 Solomoni anaonetsa chikondi chake pa Yehova poyenda motsatira malamulo a abambo ake Davide, kupatula kuti ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani ku malo osiyanasiyana achipembedzo. 4 Mfumu inapita ku Gibiyoni kukapereka nsembe popeza kumeneko ndiye kunali malo oposa malo ofunika kwambiri pachipembedzo. Kumeneko Solomoni anapereka nsembe zopsereza 1,000 pa guwa lansembe. 5 Ku Gibiyoniko Yehova anaonekera kwa Solomoni mʼmaloto usiku, ndipo Mulungu anati, “Pempha chilichonse chimene ukufuna ndipo ndidzakupatsa.” 6 Solomoni anayankha kuti, “Inu munaonetsa kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa kapolo wanu, abambo anga Davide, chifukwa anali wokhulupirika pamaso panu, wolungama mtima ndiponso wa mtima wangwiro. Inu mukupitirizabe kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa iye ndipo mwamupatsa mwana kuti akhale pa mpando wake waufumu lero lino. 7 “Tsopano Inu Yehova Mulungu wanga, mtumiki wanune mwandiyika kukhala mfumu mʼmalo mwa abambo anga Davide. Komatu ndine mwana wamngʼono ndipo sindidziwa kagwiridwe kake ka ntchito yangayi. 8 Mtumiki wanu ali pakati pa anthu amene munawasankha, mtundu waukulu, anthu ochuluka kwambiri osatheka kuwawerenga. 9 Choncho mupatseni mtumiki wanu nzeru zolamulira anthu anu ndi kuti azitha kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choyipa. Pakuti ndani amene angathe kulamulira anthu anu ochulukawa?” 10 Ambuye anakondwera kuti Solomoni anapempha zimenezi. 11 Tsono Mulungu anati kwa Solomoni, “Popeza wapempha zinthu zimenezi osati moyo wautali kapena chuma chako kapena imfa ya adani ako koma nzeru zolamulira anthu mwachilungamo, 12 Ine ndidzakuchitira zimene wapempha. Ndidzakupatsa mtima wanzeru ndi wozindikira zinthu, kotero kuti sipanakhalepo wina wofanana nawe ndipo sipadzapezekanso wina wonga iwe pambuyo pako. 13 Kuwonjeza apo, ndidzakupatsa zimene sunazipemphe: chuma ndi ulemu, kotero kuti pa masiku onse a moyo wako sipadzakhala mfumu yofanana nawe. 14 Ndipo ngati udzayenda mʼnjira zanga ndi kumvera malamulo anga ndiponso malangizo anga monga abambo ako Davide anachitira, ndidzakupatsa moyo wautali.” 15 Kotero Solomoni anadzuka ndipo anazindikira kuti anali maloto.Iye anabwerera ku Yerusalemu nakayimirira patsogolo pa Bokosi la Chipangano la Ambuye ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Kenaka anakonzera phwando atumiki ake onse. 16 Nthawi ina amayi awiri adama anabwera kwa mfumu ndipo anayima pamaso pake. 17 Mmodzi mwa amayiwo anati, “Mbuye wanga, mayi uyu ndi ine timakhala nyumba imodzi. Ine ndinabala mwana tili limodzi ndi mnzangayu. 18 Tsiku lachitatu ine nditabala mwana, mnzangayunso anabereka mwana wake. Tinalipo awiriwiri mʼnyumbamo ndipo munalibe wina aliyense. 19 “Nthawi ya usiku mwana wa mnzangayu anafa chifukwa anamugonera. 20 Tsono iyeyu anadzuka pakati pa usiku, natenga mwana wanga ku mimba kwanga pamene ine mdzakazi wanu ndinali mʼtulo. Anamuyika mwanayo ku mimba kwake ndi kuyika mwana wake wakufayo ku mimba kwanga. 21 Mmawa nditadzuka kuti ndiyamwitse mwana wanga ndinapeza kuti ndi wakufa! Koma kutacha nditamuyangʼanitsitsa ndinaona kuti si mwana amene ine ndinabala.” 22 Koma mayi winayo anati, “Ayi! Mwana wamoyoyu ndi wanga, mwana wakufayu ndi wako.”Koma mayi woyambayo analimbikira kuti. “Ayi! Mwana wakufayu ndi wako; wamoyoyu ndi wanga.” Motero akaziwa anatsutsana pamaso pa mfumu. 23 Pamenepo mfumu inati, “Wina akuti, ‘Mwana wanga ndi wamoyoyu ndipo mwana wako ndi wakufayu,’ pamene winanso akuti, ‘Ayi! Mwana wako ndi wakufayu wanga ndi wamoyoyu.’ ” 24 Pamenepo mfumu inati, “Patseni lupanga.” Ndipo anabwera nalo lupanga kwa mfumu. 25 Tsono mfumu inagamula kuti, “Muduleni pakati mwana wamoyoyu ndipo wina mumupatse gawo limodzi, gawo linalo mumupatse winayo.” 26 Mayi amene mwana wake anali moyo anagwidwa ndi chisoni chifukwa cha mwana wakeyo ndipo anawuza mfumu kuti, “Chonde mbuye wanga, mupatseni mnzangayu mwana wamoyoyu! Musamuphe!”Koma winayo anati, “Ayi, asandipatse ine kapena iwe. Muduleni pakati!” 27 Choncho mfumu inagamula kuti, “Perekani mwana wamoyoyu kwa mayi woyambayu. Musamuphe, iyeyu ndiye mayi wake wa mwanayu.” 28 Pamene Aisraeli onse anamva za chigamulo chimene mfumu inapereka, anaopa mfumuyo kwambiri, chifukwa anaona kuti mfumu inali ndi nzeru zochokera kwa Mulungu zoweruzira mwachilungamo.

In Other Versions

1 Kings 3 in the ANGEFD

1 Kings 3 in the ANTPNG2D

1 Kings 3 in the AS21

1 Kings 3 in the BAGH

1 Kings 3 in the BBPNG

1 Kings 3 in the BBT1E

1 Kings 3 in the BDS

1 Kings 3 in the BEV

1 Kings 3 in the BHAD

1 Kings 3 in the BIB

1 Kings 3 in the BLPT

1 Kings 3 in the BNT

1 Kings 3 in the BNTABOOT

1 Kings 3 in the BNTLV

1 Kings 3 in the BOATCB

1 Kings 3 in the BOATCB2

1 Kings 3 in the BOBCV

1 Kings 3 in the BOCNT

1 Kings 3 in the BOECS

1 Kings 3 in the BOHCB

1 Kings 3 in the BOHCV

1 Kings 3 in the BOHLNT

1 Kings 3 in the BOHNTLTAL

1 Kings 3 in the BOICB

1 Kings 3 in the BOILNTAP

1 Kings 3 in the BOITCV

1 Kings 3 in the BOKCV

1 Kings 3 in the BOKCV2

1 Kings 3 in the BOKHWOG

1 Kings 3 in the BOKSSV

1 Kings 3 in the BOLCB

1 Kings 3 in the BOLCB2

1 Kings 3 in the BOMCV

1 Kings 3 in the BONAV

1 Kings 3 in the BONCB

1 Kings 3 in the BONLT

1 Kings 3 in the BONUT2

1 Kings 3 in the BOPLNT

1 Kings 3 in the BOSCB

1 Kings 3 in the BOSNC

1 Kings 3 in the BOTLNT

1 Kings 3 in the BOVCB

1 Kings 3 in the BOYCB

1 Kings 3 in the BPBB

1 Kings 3 in the BPH

1 Kings 3 in the BSB

1 Kings 3 in the CCB

1 Kings 3 in the CUV

1 Kings 3 in the CUVS

1 Kings 3 in the DBT

1 Kings 3 in the DGDNT

1 Kings 3 in the DHNT

1 Kings 3 in the DNT

1 Kings 3 in the ELBE

1 Kings 3 in the EMTV

1 Kings 3 in the ESV

1 Kings 3 in the FBV

1 Kings 3 in the FEB

1 Kings 3 in the GGMNT

1 Kings 3 in the GNT

1 Kings 3 in the HARY

1 Kings 3 in the HNT

1 Kings 3 in the IRVA

1 Kings 3 in the IRVB

1 Kings 3 in the IRVG

1 Kings 3 in the IRVH

1 Kings 3 in the IRVK

1 Kings 3 in the IRVM

1 Kings 3 in the IRVM2

1 Kings 3 in the IRVO

1 Kings 3 in the IRVP

1 Kings 3 in the IRVT

1 Kings 3 in the IRVT2

1 Kings 3 in the IRVU

1 Kings 3 in the ISVN

1 Kings 3 in the JSNT

1 Kings 3 in the KAPI

1 Kings 3 in the KBT1ETNIK

1 Kings 3 in the KBV

1 Kings 3 in the KJV

1 Kings 3 in the KNFD

1 Kings 3 in the LBA

1 Kings 3 in the LBLA

1 Kings 3 in the LNT

1 Kings 3 in the LSV

1 Kings 3 in the MAAL

1 Kings 3 in the MBV

1 Kings 3 in the MBV2

1 Kings 3 in the MHNT

1 Kings 3 in the MKNFD

1 Kings 3 in the MNG

1 Kings 3 in the MNT

1 Kings 3 in the MNT2

1 Kings 3 in the MRS1T

1 Kings 3 in the NAA

1 Kings 3 in the NASB

1 Kings 3 in the NBLA

1 Kings 3 in the NBS

1 Kings 3 in the NBVTP

1 Kings 3 in the NET2

1 Kings 3 in the NIV11

1 Kings 3 in the NNT

1 Kings 3 in the NNT2

1 Kings 3 in the NNT3

1 Kings 3 in the PDDPT

1 Kings 3 in the PFNT

1 Kings 3 in the RMNT

1 Kings 3 in the SBIAS

1 Kings 3 in the SBIBS

1 Kings 3 in the SBIBS2

1 Kings 3 in the SBICS

1 Kings 3 in the SBIDS

1 Kings 3 in the SBIGS

1 Kings 3 in the SBIHS

1 Kings 3 in the SBIIS

1 Kings 3 in the SBIIS2

1 Kings 3 in the SBIIS3

1 Kings 3 in the SBIKS

1 Kings 3 in the SBIKS2

1 Kings 3 in the SBIMS

1 Kings 3 in the SBIOS

1 Kings 3 in the SBIPS

1 Kings 3 in the SBISS

1 Kings 3 in the SBITS

1 Kings 3 in the SBITS2

1 Kings 3 in the SBITS3

1 Kings 3 in the SBITS4

1 Kings 3 in the SBIUS

1 Kings 3 in the SBIVS

1 Kings 3 in the SBT

1 Kings 3 in the SBT1E

1 Kings 3 in the SCHL

1 Kings 3 in the SNT

1 Kings 3 in the SUSU

1 Kings 3 in the SUSU2

1 Kings 3 in the SYNO

1 Kings 3 in the TBIAOTANT

1 Kings 3 in the TBT1E

1 Kings 3 in the TBT1E2

1 Kings 3 in the TFTIP

1 Kings 3 in the TFTU

1 Kings 3 in the TGNTATF3T

1 Kings 3 in the THAI

1 Kings 3 in the TNFD

1 Kings 3 in the TNT

1 Kings 3 in the TNTIK

1 Kings 3 in the TNTIL

1 Kings 3 in the TNTIN

1 Kings 3 in the TNTIP

1 Kings 3 in the TNTIZ

1 Kings 3 in the TOMA

1 Kings 3 in the TTENT

1 Kings 3 in the UBG

1 Kings 3 in the UGV

1 Kings 3 in the UGV2

1 Kings 3 in the UGV3

1 Kings 3 in the VBL

1 Kings 3 in the VDCC

1 Kings 3 in the YALU

1 Kings 3 in the YAPE

1 Kings 3 in the YBVTP

1 Kings 3 in the ZBP