1 Samuel 1 (BOGWICC)

1 Panali munthu wina wochokera ku Ramataimu, Mzofimu wa ku dziko la mapiri la Efereimu. Iyeyu dzina lake anali Elikana ndipo anali mwana wa Yerohamu, mwana wa Elihu, mwana wa Tohu, mwana wa Zufu wa fuko la Efereimu. 2 Iye anali ndi akazi awiri, Hana ndi Penina. Penina anali ndi ana, koma Hana analibe. 3 Chaka ndi chaka Elikana ankachoka ku mudzi kwawo kupita ku Silo kukapembedza ndi kukapereka nsembe kwa Yehova Wamphamvuzonse. Ku Siloko kunali ana awiri a Eli, Hofini ndi Finehasi amene anali ansembe a Yehova. 4 Tsiku lopereka nsembe likafika Elikana amapereka magawo a nsembeyo kwa mkazi wake Penina ndi kwa ana ake onse aamuna ndi aakazi. 5 Ngakhale ankamukonda Hana, koma ankamupatsa gawo limodzi popeza Yehova sanamupatse ana. 6 Tsono popeza Yehova sanamupatse Hana ana, mkazi mnzakeyo ankamuyamba dala ndi cholinga chomukwiyitsa. 7 Izi zimachitika chaka ndi chaka. Hana ankati akamapita ku Nyumba ya Yehova mkazi mnzakeyo ankamunyogodola. Choncho Hana ankangokhalira kulira osafuna ndi kudya komwe. 8 Tsono mwamuna wake Elikana ankamufunsa kuti, “Hana ukulira chifukwa chiyani? Wakhumudwa ndi chiyani kuti sukufuna ndi kudya komwe? Kodi ine kwa iwe sindili woposa ana aamuna khumi?” 9 Tsiku lina atatha kudya ndi kumwa ku Silo kuja, Hana anayimirira kukapemphera. Nthawiyi nʼkuti wansembe Eli atakhala pa mpando pa khomo la Nyumba ya Yehova. 10 Hana anavutika mʼmoyo mwake, ndipo anapemphera kwa Yehova akulira kwambiri. 11 Ndipo iye analumbira kuti, “Inu Yehova Wamphamvuzonse, ngati muyangʼana kusauka kwa mtumiki wanune, ndi kuyankha pemphero langa osandiyiwala ine mtumiki wanu pondipatsa mwana wamwamuna, ine ndidzamupereka mwanayo kwa inu Yehova masiku onse a moyo wake. Lumo silidzapita pa mutu pake.” 12 Akupemphera choncho kwa Yehova, Eli ankamuyangʼana pakamwa. 13 Hana ankapemphera chamumtima ndipo milomo yake inkangogwedera koma mawu ake samamveka. Choncho Eli anaganiza kuti anali ataledzera. 14 Ndipo anamufunsa Hana kuti, “Kodi mukhala chiledzerere mpaka liti? Pitani, ayambe wakuchokani vinyo mwamwayo.” 15 Koma Hana anayankha kuti, “Sichoncho mbuye wanga. Ndakhala ndikumukhuthulira Yehova chisoni changa. Sindinamwe vinyo kapena chakumwa choledzeretsa chilichonse, popeza nthawi yonseyi ndakhala ndikupereka kwa Yehova nkhawa yayikulu ndi mavuto anga. 16 Musaganize kuti mtumiki wanu ndi kukhala mkazi wachabechabe. Ine ndakhala ndi kupereka nkhawa yanga yayikulu ndi zowawa zanga.” 17 Eli anayankha, “Pitani mu mtendere, ndipo Mulungu wa Israeli akupatseni zimene mwamupemphazo.” 18 Hana anati, “Mundikomerebe mtima mtumiki wanune.” Kenaka anachoka nakadya, ndipo sanaonekenso wachisoni. 19 Elikana ndi banja lake anadzuka mmawa mwake nakapemphera pamaso pa Yehova. Pambuyo pake anabwerera kwawo ku Rama. Elikana anakhala pamodzi ndi mkazi wake, ndipo Yehova anamukumbuka Hanayo. 20 Motero Hana anakhala ndi pakati ndipo anabereka mwana wamwamuna. Anamutcha dzina lake Samueli, popeza anati, “Ndinachita kumupempha kwa Yehova.” 21 Elikana ndi banja lake lonse anapita kukapereka nsembe ya pa chaka kwa Yehova ndi kukakwaniritsa malonjezo ake. 22 Koma Hana sanapite nawo popeza anawuza mwamuna wake kuti, “Mwanayu akadzaleka kuyamwa, ndidzapita naye ndi kukamupereka pamaso pa Yehova ndipo adzakhala kumeneko moyo wake wonse.” 23 Elikana mwamuna wake anamuwuza kuti, “Chita chimene chakukomera. Tsala kuno mpaka utamusiyitsa kuyamwa, Yehova yekha akwaniritse mawu ake.” Choncho mkaziyo anatsala ku nyumba ndi kusamalira mwana wake mpaka atamuletsa kuyamwa. 24 Atamuletsa kuyamwa, Hana anatenga mwanayo ali wachichepere, ndikupita naye ku nyumba ya Yehova ku Silo. Anatenga ngʼombe yamphongo ya zaka zitatu, ufa wa makilogalamu khumi, ndi thumba lachikopa la vinyo. 25 Tsono anapha ngʼombe yamphongo ija ndi kupereka mwana uja kwa Eli. 26 Ndipo Hana anati kwa Eli, “Mbuye wanga, ine ndikunenetsadi pamaso panu kuti ndine mkazi uja amene anayima pamaso panu ndi kumapemphera kwa Yehova. 27 Ndinapempha mwana uyu, ndipo Yehova wandipatsa chimene ndinamupempha. 28 Ndiye tsopano ine ndikumupereka kwa Yehova. Pa moyo wake wonse adzakhala wa Yehova.” Ndipo onse anapembedza Yehova kumeneko.

In Other Versions

1 Samuel 1 in the ANGEFD

1 Samuel 1 in the ANTPNG2D

1 Samuel 1 in the AS21

1 Samuel 1 in the BAGH

1 Samuel 1 in the BBPNG

1 Samuel 1 in the BBT1E

1 Samuel 1 in the BDS

1 Samuel 1 in the BEV

1 Samuel 1 in the BHAD

1 Samuel 1 in the BIB

1 Samuel 1 in the BLPT

1 Samuel 1 in the BNT

1 Samuel 1 in the BNTABOOT

1 Samuel 1 in the BNTLV

1 Samuel 1 in the BOATCB

1 Samuel 1 in the BOATCB2

1 Samuel 1 in the BOBCV

1 Samuel 1 in the BOCNT

1 Samuel 1 in the BOECS

1 Samuel 1 in the BOHCB

1 Samuel 1 in the BOHCV

1 Samuel 1 in the BOHLNT

1 Samuel 1 in the BOHNTLTAL

1 Samuel 1 in the BOICB

1 Samuel 1 in the BOILNTAP

1 Samuel 1 in the BOITCV

1 Samuel 1 in the BOKCV

1 Samuel 1 in the BOKCV2

1 Samuel 1 in the BOKHWOG

1 Samuel 1 in the BOKSSV

1 Samuel 1 in the BOLCB

1 Samuel 1 in the BOLCB2

1 Samuel 1 in the BOMCV

1 Samuel 1 in the BONAV

1 Samuel 1 in the BONCB

1 Samuel 1 in the BONLT

1 Samuel 1 in the BONUT2

1 Samuel 1 in the BOPLNT

1 Samuel 1 in the BOSCB

1 Samuel 1 in the BOSNC

1 Samuel 1 in the BOTLNT

1 Samuel 1 in the BOVCB

1 Samuel 1 in the BOYCB

1 Samuel 1 in the BPBB

1 Samuel 1 in the BPH

1 Samuel 1 in the BSB

1 Samuel 1 in the CCB

1 Samuel 1 in the CUV

1 Samuel 1 in the CUVS

1 Samuel 1 in the DBT

1 Samuel 1 in the DGDNT

1 Samuel 1 in the DHNT

1 Samuel 1 in the DNT

1 Samuel 1 in the ELBE

1 Samuel 1 in the EMTV

1 Samuel 1 in the ESV

1 Samuel 1 in the FBV

1 Samuel 1 in the FEB

1 Samuel 1 in the GGMNT

1 Samuel 1 in the GNT

1 Samuel 1 in the HARY

1 Samuel 1 in the HNT

1 Samuel 1 in the IRVA

1 Samuel 1 in the IRVB

1 Samuel 1 in the IRVG

1 Samuel 1 in the IRVH

1 Samuel 1 in the IRVK

1 Samuel 1 in the IRVM

1 Samuel 1 in the IRVM2

1 Samuel 1 in the IRVO

1 Samuel 1 in the IRVP

1 Samuel 1 in the IRVT

1 Samuel 1 in the IRVT2

1 Samuel 1 in the IRVU

1 Samuel 1 in the ISVN

1 Samuel 1 in the JSNT

1 Samuel 1 in the KAPI

1 Samuel 1 in the KBT1ETNIK

1 Samuel 1 in the KBV

1 Samuel 1 in the KJV

1 Samuel 1 in the KNFD

1 Samuel 1 in the LBA

1 Samuel 1 in the LBLA

1 Samuel 1 in the LNT

1 Samuel 1 in the LSV

1 Samuel 1 in the MAAL

1 Samuel 1 in the MBV

1 Samuel 1 in the MBV2

1 Samuel 1 in the MHNT

1 Samuel 1 in the MKNFD

1 Samuel 1 in the MNG

1 Samuel 1 in the MNT

1 Samuel 1 in the MNT2

1 Samuel 1 in the MRS1T

1 Samuel 1 in the NAA

1 Samuel 1 in the NASB

1 Samuel 1 in the NBLA

1 Samuel 1 in the NBS

1 Samuel 1 in the NBVTP

1 Samuel 1 in the NET2

1 Samuel 1 in the NIV11

1 Samuel 1 in the NNT

1 Samuel 1 in the NNT2

1 Samuel 1 in the NNT3

1 Samuel 1 in the PDDPT

1 Samuel 1 in the PFNT

1 Samuel 1 in the RMNT

1 Samuel 1 in the SBIAS

1 Samuel 1 in the SBIBS

1 Samuel 1 in the SBIBS2

1 Samuel 1 in the SBICS

1 Samuel 1 in the SBIDS

1 Samuel 1 in the SBIGS

1 Samuel 1 in the SBIHS

1 Samuel 1 in the SBIIS

1 Samuel 1 in the SBIIS2

1 Samuel 1 in the SBIIS3

1 Samuel 1 in the SBIKS

1 Samuel 1 in the SBIKS2

1 Samuel 1 in the SBIMS

1 Samuel 1 in the SBIOS

1 Samuel 1 in the SBIPS

1 Samuel 1 in the SBISS

1 Samuel 1 in the SBITS

1 Samuel 1 in the SBITS2

1 Samuel 1 in the SBITS3

1 Samuel 1 in the SBITS4

1 Samuel 1 in the SBIUS

1 Samuel 1 in the SBIVS

1 Samuel 1 in the SBT

1 Samuel 1 in the SBT1E

1 Samuel 1 in the SCHL

1 Samuel 1 in the SNT

1 Samuel 1 in the SUSU

1 Samuel 1 in the SUSU2

1 Samuel 1 in the SYNO

1 Samuel 1 in the TBIAOTANT

1 Samuel 1 in the TBT1E

1 Samuel 1 in the TBT1E2

1 Samuel 1 in the TFTIP

1 Samuel 1 in the TFTU

1 Samuel 1 in the TGNTATF3T

1 Samuel 1 in the THAI

1 Samuel 1 in the TNFD

1 Samuel 1 in the TNT

1 Samuel 1 in the TNTIK

1 Samuel 1 in the TNTIL

1 Samuel 1 in the TNTIN

1 Samuel 1 in the TNTIP

1 Samuel 1 in the TNTIZ

1 Samuel 1 in the TOMA

1 Samuel 1 in the TTENT

1 Samuel 1 in the UBG

1 Samuel 1 in the UGV

1 Samuel 1 in the UGV2

1 Samuel 1 in the UGV3

1 Samuel 1 in the VBL

1 Samuel 1 in the VDCC

1 Samuel 1 in the YALU

1 Samuel 1 in the YAPE

1 Samuel 1 in the YBVTP

1 Samuel 1 in the ZBP