1 Samuel 17 (BOGWICC)

1 Afilisti anasonkhanitsa ankhondo awo ku Soko mʼdziko la Yuda. Iwo anamanga misasa yawo ku Efesi-Damimu, pakati pa Soko ndi Azeka. 2 Sauli ndi Aisraeli anasonkhana namanga misasa mʼchigwa cha Ela ndipo anandandalitsa ankhondo kuti amenyane ndi Afilisti. 3 Afilisti anali phiri lina ndipo Aisraeli analinso phiri lina, ndipo pakati pawo panali chigwa. 4 Tsono munthu wina wamphamvu, dzina lake Goliati wochokera ku Gati anatuluka ku misasa ya Afilisti. Msinkhu wake unali pafupipafupi mamita atatu. 5 Iye ankavala chipewa chamkuwa ndi malaya achitsulo olemera makilogalamu 57. 6 Ankavalanso zokuta miyendo yake zamkuwa, ndipo ankanyamula nthungo ya mkuwa pa phewa pake. 7 Thunthu la mkondo wake linali ngati mkombero wowombera nsalu, ndipo mutu wa mkondowo unkalemera makilogalamu asanu ndi awiri. Patsogolo pake pamakhala munthu wonyamula zida zake za nkhondo. 8 Goliatiyo anayimirira ndi kufuwula kwa ankhondo a Israeli, nati, “Nʼchifukwa chiyani mwakonzekera nkhondo chotere? Kodi sindine Mfilisiti ndipo inu sindinu akapolo a Sauli? Sankhani munthu kuti abwere kwa ine. 9 Ngati angathe kumenyana nane ndi kundipha, ife tidzakhala akapolo anu, koma ngati ine ndimugonjetsa ndi kumupha, inu mudzakhala akapolo athu ndi kumatitumikira.” 10 Ndipo Mfilisitiyo anati, “Bwerani lero timenyane basi! Patseni munthu kuti ndimenyane naye.” 11 Atamva mawu a Mfilisitiyo, Sauli ndi Aisraeli onse anataya mtima nachita mantha kwambiri. 12 Davide anali mwana wa munthu wa fuko la Efurati dzina lake Yese amene amachokera ku Betelehemu mʼdziko la Yuda. Yese anali ndi ana aamuna asanu ndi awiri. Pa nthawi ya Sauli nʼkuti ali wokalamba. 13 Ana atatu oyamba kubadwa a Yese nʼkuti atapita nawo ku nkhondo pamodzi ndi Sauli. Woyamba dzina lake anali Eliabu, wachiwiri anali Abinadabu, ndipo wachitatu anali Sama. 14 Davide ndiye anali mzime. Ana aakulu atatuwo ndiwo anapita ku nkhondo ndi Sauli. 15 Koma Davide ankapita ku misasa ya Sauli ndi kubwerako kuti azikaweta nkhosa za abambo ake ku Betelehemu. 16 Kwa masiku makumi anayi, Mfilisiti uja ankabwera mmawa ndi madzulo kumadzionetsera. 17 Tsiku lina Yese anawuza mwana wake Davide kuti, “Atengere abale ako makilogalamu khumi a tirigu wokazinga ndi malofu a buledi khumi ndipo upite nazo mofulumira ku misasa yawo. 18 Utengerenso wolamulira wa gulu lawo tchizi khumi uyu. Ukaone mmene abale ako akukhalira ndipo ubwere ndi kanthu kosonyeza kuti ali bwino. 19 Sauli, abale akowo ndi asilikali onse a Israeli ali ku chigwa cha Ela, akumenyana ndi Afilisti.” 20 Mʼmamawa mwake Davide anasiya nkhosa mʼmanja mwa munthu wina ndipo anatenga zakudyazo nanyamuka monga momwe Yese abambo ake anamulamulira. Anakafika ku misasa pamene asilikali ankapita kukandanda pa mzere ku nkhondo, nʼkufuwula mfuwu wankhondo. 21 Aisraeli ndi Afilisti anandanda pa mzere wankhondo moyangʼanana. 22 Tsono Davide anasiyira zakudya zija munthu wosunga katundu nathamangira kumene kunali ankhondo kuja ndi kukalonjera abale ake. 23 Pamene iye ankayankhula nawo anangoona Goliati wa ku Gati uja akuchoka pa mzere wa Afilisti akufuwula mawu onyoza monga mwa masiku onse, ndipo Davide ankawamva. 24 Aisraeli ataona munthuyo, anamuthawa ndi mantha aakulu. 25 Ndipo Aisraeli ankanena kuti, “Kodi mwamuona munthu akubwerayo? Iye amangobwera kudzanyoza Israeli. Tsono mfumu inati kuti idzapereka chuma chambiri kwa munthu amene adzamuphe. Idzaperekanso mwana wake wamkazi kuti amukwatire ndiponso banja la abambo ake silidzaperekanso msonkho mu Israeli.” 26 Davide anafunsa anthu amene anayima pafupi naye kuti, “Kodi adzamuchita chiyani munthu amene adzapha Mfilisiti uyu ndi kuchotsa chitonzo pakati pa Israeli? Mfilisiti wosachita mdulidweyu ndi ndani kuti azinyoza gulu lankhondo la Mulungu wamoyo?” 27 Anthu anamuwuzanso zonse zimene mfumu inanena kuti idzachitira munthu amene adzapha Mfilisitiyo. 28 Eliabu, mkulu wake wa Davide, atamumva akuyankhula ndi anthuwo, anamukwiyira ndipo anamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani wabwera kuno? Ndipo wasiyira yani nkhosa zochepazo mʼchipululu? Ndikudziwa kuti ndiwe wodzikuza ndiponso woyipa mtima. Unabwera kuno kuti udzaonere nkhondo.” 29 Davide anati, “Kodi ndachita chiyani ine? Kodi ndisamayankhule?” 30 Ndipo anamuchokera napita kwa munthu wina ndipo anamufunsa nkhani yomweyo, ndipo anthu anamuyankha iye monga poyamba paja. 31 Mawu amene Davide anayankhula atamveka, anthu anakafotokozera Sauli ndipo Sauli anamuyitanitsa. 32 Davide anati kwa Sauli, “Munthu aliyense asataye mtima chifukwa cha Mfilisitiyu. Ine kapolo wanu ndipita kukamenyana naye.” 33 Sauli anayankha Davide kuti, “Iwe sungathe kupita kukamenyana ndi Mfilisitiyu. Iwe ukanali mnyamata, koma iyeyu ndi amene wakhala akumenya nkhondo kuyambira unyamata wake.” 34 Koma Davide anati kwa Sauli, “Kapolo wanune ndinkaweta nkhosa za abambo anga. Ndipo mkango kapena chimbalangondo chikamabwera ndi kugwira mwana wankhosa pakati pa nkhosazo, 35 ine ndinkatsatira ndi kupha chirombocho. Choncho ndinkapulumutsa mwana wankhosa uja mʼkamwa mwake. Ndipo chinkati chikandiwukira, ine ndinkagwira tchowa lake, nʼkuchikantha mpaka kuchipha. 36 Ine kapolo wanu ndinapha mkango ngakhalenso chimbalangondo. Tsono Mfilisiti wosachita mdulidweyu adzaphedwa monga zinazo chifukwa wanyoza ankhondo a Mulungu wamoyo. 37 Yehova amene anandilanditsa mʼkamwa mwa mkango ndi chimbalangondo adzandilanditsa mʼmanja mwa Mfilisiti uyu.”Sauli anati kwa Davide, “Pita, ndipo Yehova akhale nawe.” 38 Ndipo Sauli anamveka Davide mwinjiro wake. Anamuveka zovala zankhondo ndi chipewa cha mkuwa. 39 Davide anamangirira lupanga pa mwinjirowo. Atayesa kuyenda nazo, analephera chifukwa anali asanazizolowere.Iye anati kwa Sauli, “Sindingathe kuyenda nazo chifukwa sindinazizolowere.” Ndipo anazivula. 40 Pambuyo pake anatenga ndodo yake mʼmanja. Kenaka anasankha miyala yosalala bwino mu mtsinje ndi kuyiika mʼthumba lake la ku ubusa. Legeni ili mʼmanja mwake, Davide ananyamuka kukakumana ndi Mfilisiti uja. 41 Tsono Mfilisiti uja anayambapo kupita kumene kunali Davide, mnyamata wonyamula zida zake za nkhondo ali patsogolo pake. 42 Mfilisitiyo atangomuona Davide, anamunyoza popeza kuti Davide anali mnyamata chabe wofiirira ndi wa maonekedwe abwino. 43 Iye anati kwa Davide, “Kodi ndine galu, kuti ubwere kwa ine ndi ndodo?” Ndipo Mfilisitiyo anamutemberera Davide potchula mayina a milungu yake. 44 Iye anatinso, “Bwera kuno ndipo ndidzapereka mnofu wako kwa mbalame zamlengalenga ndi kwa zirombo zakuthengo!” 45 Koma Davide anati kwa Mfilisitiyo, “Iwe wabwera kwa ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo, koma ine ndikubwera kwa iwe mʼdzina la Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa ankhondo Aisraeli amene iwe ukuwanyoza. 46 Anatinso lero lino Yehova adzakupereka mʼmanja mwanga. Ndidzakukantha ndi kudula mutu wako. Ndidzapereka mitembo ya asilikali a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zirombo zakuthengo ndipo dziko lonse lapansi lidzadziwa kuti mu Israeli muli Mulungu. 47 Onse amene asonkhana pano adzadziwa kuti Mulungu sapulumutsa anthu ndi lupanga kapena mkondo, pakuti nkhondo ndi ya Yehova. Iye adzakuperekani mʼmanja mwathu.” 48 Mfilisitiyo akusendera pafupi kuti akumane naye, Davideyo anathamangira mofulumira ku mzere wa nkhondo kukakumana naye. 49 Davideyo anapisa dzanja lake mʼthumba lake natengamo mwala ndipo anawuponya, nalasa pa mphumi pa Mfilisitiyo. Mwalawo unalowa pa chipumi chake, ndipo anagwa chafufumimba. 50 Kotero Davide anamupambana Mfilisitiyo pomugenda ndi mwala wa legeni ndi kumupha. Mʼmanja mwa Davide munalibe lupanga. 51 Davide anathamanga nakayimirira pamwamba pa Mfilisiti uja. Anasolola lupanga lake lomwe moyikamo mwake, namupha pomudula mutu wake.Afilisti ataona kuti ngwazi yawo yafa, anathawa. 52 Ndipo Aisraeli ndi anthu a ku Yuda ananyamuka, ndipo akufuwula anathamangitsa Afilisti aja mpaka ku Gati ndi ku zipata za Ekroni. Anthu akufa awo amagwa njira yonse ya ku Saaraimu mpaka ku Gati ndi ku Ekroni. 53 Aisraeli anabwerako kothamangitsa Afilisti kuja ndipo anadzatenga zonse zimene zinali mʼmisasa ya Afilistiwo. 54 Pambuyo pake Davide anatenga mutu wa Mfilisitiyo napita nawo ku Yerusalemu, koma anayika zida za Mfilisitiyo mu tenti yake. 55 Sauli ataona Davide akupita kukakumana ndi Mfilisitiyo anafunsa Abineri, mkulu wa ankhondo kuti, “Abineri, kodi mnyamatayu ndi mwana wa yani?”Abineri anayankha kuti, “Ndithu mfumu muli apa ine sindikumudziwa.” 56 Mfumu inati, “Pita kafufuze kuti mnyamata ameneyu ndi mwana wa yani.” 57 Davide atangobwerako kokapha Mfilisiti kuja, Abineri anamutenga nabwera naye kwa Sauli, mutu wa Mfilisiti uja uli mʼmanja mwake. 58 Sauli anamufunsa, “Mnyamata iwe, kodi paja ndiwe mwana wayani?”Davide anati, “Ndine mwana wa mtumiki wanu Yese wa ku Betelehemu.”

In Other Versions

1 Samuel 17 in the ANGEFD

1 Samuel 17 in the ANTPNG2D

1 Samuel 17 in the AS21

1 Samuel 17 in the BAGH

1 Samuel 17 in the BBPNG

1 Samuel 17 in the BBT1E

1 Samuel 17 in the BDS

1 Samuel 17 in the BEV

1 Samuel 17 in the BHAD

1 Samuel 17 in the BIB

1 Samuel 17 in the BLPT

1 Samuel 17 in the BNT

1 Samuel 17 in the BNTABOOT

1 Samuel 17 in the BNTLV

1 Samuel 17 in the BOATCB

1 Samuel 17 in the BOATCB2

1 Samuel 17 in the BOBCV

1 Samuel 17 in the BOCNT

1 Samuel 17 in the BOECS

1 Samuel 17 in the BOHCB

1 Samuel 17 in the BOHCV

1 Samuel 17 in the BOHLNT

1 Samuel 17 in the BOHNTLTAL

1 Samuel 17 in the BOICB

1 Samuel 17 in the BOILNTAP

1 Samuel 17 in the BOITCV

1 Samuel 17 in the BOKCV

1 Samuel 17 in the BOKCV2

1 Samuel 17 in the BOKHWOG

1 Samuel 17 in the BOKSSV

1 Samuel 17 in the BOLCB

1 Samuel 17 in the BOLCB2

1 Samuel 17 in the BOMCV

1 Samuel 17 in the BONAV

1 Samuel 17 in the BONCB

1 Samuel 17 in the BONLT

1 Samuel 17 in the BONUT2

1 Samuel 17 in the BOPLNT

1 Samuel 17 in the BOSCB

1 Samuel 17 in the BOSNC

1 Samuel 17 in the BOTLNT

1 Samuel 17 in the BOVCB

1 Samuel 17 in the BOYCB

1 Samuel 17 in the BPBB

1 Samuel 17 in the BPH

1 Samuel 17 in the BSB

1 Samuel 17 in the CCB

1 Samuel 17 in the CUV

1 Samuel 17 in the CUVS

1 Samuel 17 in the DBT

1 Samuel 17 in the DGDNT

1 Samuel 17 in the DHNT

1 Samuel 17 in the DNT

1 Samuel 17 in the ELBE

1 Samuel 17 in the EMTV

1 Samuel 17 in the ESV

1 Samuel 17 in the FBV

1 Samuel 17 in the FEB

1 Samuel 17 in the GGMNT

1 Samuel 17 in the GNT

1 Samuel 17 in the HARY

1 Samuel 17 in the HNT

1 Samuel 17 in the IRVA

1 Samuel 17 in the IRVB

1 Samuel 17 in the IRVG

1 Samuel 17 in the IRVH

1 Samuel 17 in the IRVK

1 Samuel 17 in the IRVM

1 Samuel 17 in the IRVM2

1 Samuel 17 in the IRVO

1 Samuel 17 in the IRVP

1 Samuel 17 in the IRVT

1 Samuel 17 in the IRVT2

1 Samuel 17 in the IRVU

1 Samuel 17 in the ISVN

1 Samuel 17 in the JSNT

1 Samuel 17 in the KAPI

1 Samuel 17 in the KBT1ETNIK

1 Samuel 17 in the KBV

1 Samuel 17 in the KJV

1 Samuel 17 in the KNFD

1 Samuel 17 in the LBA

1 Samuel 17 in the LBLA

1 Samuel 17 in the LNT

1 Samuel 17 in the LSV

1 Samuel 17 in the MAAL

1 Samuel 17 in the MBV

1 Samuel 17 in the MBV2

1 Samuel 17 in the MHNT

1 Samuel 17 in the MKNFD

1 Samuel 17 in the MNG

1 Samuel 17 in the MNT

1 Samuel 17 in the MNT2

1 Samuel 17 in the MRS1T

1 Samuel 17 in the NAA

1 Samuel 17 in the NASB

1 Samuel 17 in the NBLA

1 Samuel 17 in the NBS

1 Samuel 17 in the NBVTP

1 Samuel 17 in the NET2

1 Samuel 17 in the NIV11

1 Samuel 17 in the NNT

1 Samuel 17 in the NNT2

1 Samuel 17 in the NNT3

1 Samuel 17 in the PDDPT

1 Samuel 17 in the PFNT

1 Samuel 17 in the RMNT

1 Samuel 17 in the SBIAS

1 Samuel 17 in the SBIBS

1 Samuel 17 in the SBIBS2

1 Samuel 17 in the SBICS

1 Samuel 17 in the SBIDS

1 Samuel 17 in the SBIGS

1 Samuel 17 in the SBIHS

1 Samuel 17 in the SBIIS

1 Samuel 17 in the SBIIS2

1 Samuel 17 in the SBIIS3

1 Samuel 17 in the SBIKS

1 Samuel 17 in the SBIKS2

1 Samuel 17 in the SBIMS

1 Samuel 17 in the SBIOS

1 Samuel 17 in the SBIPS

1 Samuel 17 in the SBISS

1 Samuel 17 in the SBITS

1 Samuel 17 in the SBITS2

1 Samuel 17 in the SBITS3

1 Samuel 17 in the SBITS4

1 Samuel 17 in the SBIUS

1 Samuel 17 in the SBIVS

1 Samuel 17 in the SBT

1 Samuel 17 in the SBT1E

1 Samuel 17 in the SCHL

1 Samuel 17 in the SNT

1 Samuel 17 in the SUSU

1 Samuel 17 in the SUSU2

1 Samuel 17 in the SYNO

1 Samuel 17 in the TBIAOTANT

1 Samuel 17 in the TBT1E

1 Samuel 17 in the TBT1E2

1 Samuel 17 in the TFTIP

1 Samuel 17 in the TFTU

1 Samuel 17 in the TGNTATF3T

1 Samuel 17 in the THAI

1 Samuel 17 in the TNFD

1 Samuel 17 in the TNT

1 Samuel 17 in the TNTIK

1 Samuel 17 in the TNTIL

1 Samuel 17 in the TNTIN

1 Samuel 17 in the TNTIP

1 Samuel 17 in the TNTIZ

1 Samuel 17 in the TOMA

1 Samuel 17 in the TTENT

1 Samuel 17 in the UBG

1 Samuel 17 in the UGV

1 Samuel 17 in the UGV2

1 Samuel 17 in the UGV3

1 Samuel 17 in the VBL

1 Samuel 17 in the VDCC

1 Samuel 17 in the YALU

1 Samuel 17 in the YAPE

1 Samuel 17 in the YBVTP

1 Samuel 17 in the ZBP