1 Samuel 23 (BOGWICC)

1 Davide atawuzidwa kuti “Onani, Afilisti akuthira nkhondo mzinda wa Keila ndi kulanda zokolola zawo za mʼnkhokwe,” 2 anafunsa Yehova kuti, “Kodi ndipite ndikamenyane nawo Afilistiwa?”Yehova anamuyankha kuti, “Pita, kamenyane nawo Afilisti ndi kupulumutsa mzinda wa Keila.” 3 Koma anthu amene anali ndi Davide anati, “Ngati tikuchita mantha ku Yuda konkuno, nanji kupita ku Keila kukamenyana ndi ankhondo a Afilisti!” 4 Davide anafunsanso Yehova, ndipo Yehova anamuyankha kuti, “Pita ku Keila pakuti ndapereka Afilisti mʼdzanja lako.” 5 Choncho Davide ndi anthu ake anapita ku Keila kukamenyana ndi Afilisti. Anapha Afilisti ambiri ndi kutenga ziweto zawo. Choncho anapulumutsa anthu a ku Keila. 6 (Pamene Abiatara mwana wa Ahimeleki anathawira kwa Davide anabwera ndi efodi mʼmanja mwake). 7 Sauli atamva kuti Davide wapita ku Keila anati, “Mulungu wamupereka kwa ine, pakuti Davide wadzitsekera yekha mʼndende polowa mu mzinda umene uli ndi zipata ndi zotsekera zake.” 8 Choncho Sauli anasonkhanitsa ankhondo ake nawatuma ku Keila kuti akamuzungulire Davide ndi anthu ake. 9 Davide atadziwa kuti Sauli akufuna kumuchita chiwembu, anawuza Abiatara wansembe uja kuti, “Bwera nayo efodiyo.” 10 Tsono Davide anayankhula ndi Yehova kuti, “Inu Yehova Mulungu wa Israeli, ine mtumiki wanu ndamva ndithu kuti Sauli akufuna kubwera ku Keila ndi kudzawononga mzindawu chifukwa cha ine. 11 Kodi anthu a Keila adzandipereka mʼmanja mwa Sauli? Kodi Sauli abweradi monga ndamvera ine mtumiki wanu? Inu Yehova Mulungu wa Israeli, chonde, ndiwuzeni ine mtumiki wanu.”Ndipo Yehova anati, “Sauli abweradi.” 12 Davide anafunsanso, “Kodi anthu a ku Keila adzapereka ine ndi anthu angawa kwa Sauli?”Ndipo Yehova anayankha, “Iwo adzakuperekanidi.” 13 Choncho Davide ndi anthu ake, omwe analipo 600, anachoka ku Keila namayenda mothawathawa. Sauli atamva kuti Davide wathawa ku Keila, sanatumizeko ankhondo ake aja. 14 Davide ankakhala mʼmapanga mʼdziko lamapiri ku chipululu cha Zifi. Sauli ankamufufuza tsiku ndi tsiku, koma Mulungu sanapereke Davide mʼmanja mwake. 15 Davide anaona kuti Sauli akufunafuna kuti amuphe. Nthawiyi nʼkuti Davide ali mʼchipululu cha Zifi ku Horesi. 16 Ndipo Yonatani mwana wa Sauli anapita kwa Davide ku Horesi ndipo anamulimbitsa mtima pomuwuza kuti Yehova ali naye. 17 Iye anamuwuza kuti, “Usaope, abambo anga sadzakupha. Iwe udzakhala mfumu ya Israeli ndipo ine ndidzakhala wachiwiri wako. Ngakhale abambo anga Sauli akudziwa zimenezi.” 18 Awiriwa anachita pangano pamaso pa Yehova. Ndipo Yonatani anabwerera kwawo, koma Davide anakhalabe ku Horesi. 19 Anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ku Gibeya ndipo anamuwuza kuti, “Davide akubisala kwathu, mʼmapanga a ku Horesi, mʼphiri la Hakila, kummwera kwa Yesimoni. 20 Tsopano inu, mubwere nthawi iliyonse imene mukufuna, ndipo ife tidzamupereka kwa mfumu.” 21 Sauli anayankha kuti, “Yehova akudalitseni pakuti mwandichitira chifundo. 22 Pitani mukatsimikizire. Mukaone kumene amakhala ndiponso mupeze munthu amene wamuona. Anthu amandiwuza kuti ndi wochenjera kwambiri. 23 Kafufuzeni ndithu malo onse kumene amabisalako, ndipo mubwerenso kuno mudzandiwuze chenicheni. Pambuyo pake ine ndidzapita nanu. Ngatidi ali mʼderalo ndidzamusaka pakati pa mabanja onse a Yuda.” 24 Kotero iwo ananyamuka ndi kupita ku Zifi, koma Sauli asananyamuke. Nthawi imeneyi Davide ndi anthu ake anali ku chipululu cha Maoni, ku Araba kummwera kwa Yesimoni. 25 Sauli ndi anthu ake anapita kukamufufuza Davide. Koma Davide atamva izi anathawa ndi kukabisala ku thanthwe la chipululu cha Maoni. Sauli atamva kuti Davide anathawira ku Maoni anamutsatira ku chipululu komweko. 26 Sauli amayenda mbali ina ya phirilo, ndipo Davide ndi anthu ake nawonso anali mbali ina ya phirilo. Koma Davide ndi anthu ake anafulumira kumuthawa Sauli pamene Sauliyo ndi anthu ake ali pafupi kuwagwira. 27 Nthawi yomweyo munthu wina wamthenga anabwera kudzamuwuza Sauli kuti, “Bwerani msanga! Afilisti akuthira nkhondo dzikoli.” 28 Choncho Sauli analeka kuthamangitsa Davide ndipo anapita kukamenyana ndi Afilisti. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa Mwala wa Malekano. 29 Ndipo Davide anachoka kumeneko ndi kukakhala ku mapanga a ku Eni Gedi.

In Other Versions

1 Samuel 23 in the ANGEFD

1 Samuel 23 in the ANTPNG2D

1 Samuel 23 in the AS21

1 Samuel 23 in the BAGH

1 Samuel 23 in the BBPNG

1 Samuel 23 in the BBT1E

1 Samuel 23 in the BDS

1 Samuel 23 in the BEV

1 Samuel 23 in the BHAD

1 Samuel 23 in the BIB

1 Samuel 23 in the BLPT

1 Samuel 23 in the BNT

1 Samuel 23 in the BNTABOOT

1 Samuel 23 in the BNTLV

1 Samuel 23 in the BOATCB

1 Samuel 23 in the BOATCB2

1 Samuel 23 in the BOBCV

1 Samuel 23 in the BOCNT

1 Samuel 23 in the BOECS

1 Samuel 23 in the BOHCB

1 Samuel 23 in the BOHCV

1 Samuel 23 in the BOHLNT

1 Samuel 23 in the BOHNTLTAL

1 Samuel 23 in the BOICB

1 Samuel 23 in the BOILNTAP

1 Samuel 23 in the BOITCV

1 Samuel 23 in the BOKCV

1 Samuel 23 in the BOKCV2

1 Samuel 23 in the BOKHWOG

1 Samuel 23 in the BOKSSV

1 Samuel 23 in the BOLCB

1 Samuel 23 in the BOLCB2

1 Samuel 23 in the BOMCV

1 Samuel 23 in the BONAV

1 Samuel 23 in the BONCB

1 Samuel 23 in the BONLT

1 Samuel 23 in the BONUT2

1 Samuel 23 in the BOPLNT

1 Samuel 23 in the BOSCB

1 Samuel 23 in the BOSNC

1 Samuel 23 in the BOTLNT

1 Samuel 23 in the BOVCB

1 Samuel 23 in the BOYCB

1 Samuel 23 in the BPBB

1 Samuel 23 in the BPH

1 Samuel 23 in the BSB

1 Samuel 23 in the CCB

1 Samuel 23 in the CUV

1 Samuel 23 in the CUVS

1 Samuel 23 in the DBT

1 Samuel 23 in the DGDNT

1 Samuel 23 in the DHNT

1 Samuel 23 in the DNT

1 Samuel 23 in the ELBE

1 Samuel 23 in the EMTV

1 Samuel 23 in the ESV

1 Samuel 23 in the FBV

1 Samuel 23 in the FEB

1 Samuel 23 in the GGMNT

1 Samuel 23 in the GNT

1 Samuel 23 in the HARY

1 Samuel 23 in the HNT

1 Samuel 23 in the IRVA

1 Samuel 23 in the IRVB

1 Samuel 23 in the IRVG

1 Samuel 23 in the IRVH

1 Samuel 23 in the IRVK

1 Samuel 23 in the IRVM

1 Samuel 23 in the IRVM2

1 Samuel 23 in the IRVO

1 Samuel 23 in the IRVP

1 Samuel 23 in the IRVT

1 Samuel 23 in the IRVT2

1 Samuel 23 in the IRVU

1 Samuel 23 in the ISVN

1 Samuel 23 in the JSNT

1 Samuel 23 in the KAPI

1 Samuel 23 in the KBT1ETNIK

1 Samuel 23 in the KBV

1 Samuel 23 in the KJV

1 Samuel 23 in the KNFD

1 Samuel 23 in the LBA

1 Samuel 23 in the LBLA

1 Samuel 23 in the LNT

1 Samuel 23 in the LSV

1 Samuel 23 in the MAAL

1 Samuel 23 in the MBV

1 Samuel 23 in the MBV2

1 Samuel 23 in the MHNT

1 Samuel 23 in the MKNFD

1 Samuel 23 in the MNG

1 Samuel 23 in the MNT

1 Samuel 23 in the MNT2

1 Samuel 23 in the MRS1T

1 Samuel 23 in the NAA

1 Samuel 23 in the NASB

1 Samuel 23 in the NBLA

1 Samuel 23 in the NBS

1 Samuel 23 in the NBVTP

1 Samuel 23 in the NET2

1 Samuel 23 in the NIV11

1 Samuel 23 in the NNT

1 Samuel 23 in the NNT2

1 Samuel 23 in the NNT3

1 Samuel 23 in the PDDPT

1 Samuel 23 in the PFNT

1 Samuel 23 in the RMNT

1 Samuel 23 in the SBIAS

1 Samuel 23 in the SBIBS

1 Samuel 23 in the SBIBS2

1 Samuel 23 in the SBICS

1 Samuel 23 in the SBIDS

1 Samuel 23 in the SBIGS

1 Samuel 23 in the SBIHS

1 Samuel 23 in the SBIIS

1 Samuel 23 in the SBIIS2

1 Samuel 23 in the SBIIS3

1 Samuel 23 in the SBIKS

1 Samuel 23 in the SBIKS2

1 Samuel 23 in the SBIMS

1 Samuel 23 in the SBIOS

1 Samuel 23 in the SBIPS

1 Samuel 23 in the SBISS

1 Samuel 23 in the SBITS

1 Samuel 23 in the SBITS2

1 Samuel 23 in the SBITS3

1 Samuel 23 in the SBITS4

1 Samuel 23 in the SBIUS

1 Samuel 23 in the SBIVS

1 Samuel 23 in the SBT

1 Samuel 23 in the SBT1E

1 Samuel 23 in the SCHL

1 Samuel 23 in the SNT

1 Samuel 23 in the SUSU

1 Samuel 23 in the SUSU2

1 Samuel 23 in the SYNO

1 Samuel 23 in the TBIAOTANT

1 Samuel 23 in the TBT1E

1 Samuel 23 in the TBT1E2

1 Samuel 23 in the TFTIP

1 Samuel 23 in the TFTU

1 Samuel 23 in the TGNTATF3T

1 Samuel 23 in the THAI

1 Samuel 23 in the TNFD

1 Samuel 23 in the TNT

1 Samuel 23 in the TNTIK

1 Samuel 23 in the TNTIL

1 Samuel 23 in the TNTIN

1 Samuel 23 in the TNTIP

1 Samuel 23 in the TNTIZ

1 Samuel 23 in the TOMA

1 Samuel 23 in the TTENT

1 Samuel 23 in the UBG

1 Samuel 23 in the UGV

1 Samuel 23 in the UGV2

1 Samuel 23 in the UGV3

1 Samuel 23 in the VBL

1 Samuel 23 in the VDCC

1 Samuel 23 in the YALU

1 Samuel 23 in the YAPE

1 Samuel 23 in the YBVTP

1 Samuel 23 in the ZBP