1 Samuel 24 (BOGWICC)
1 Sauli atabwera kuchokera kumene amathamangitsa Afilisti anamva kuti, “Davide ali mʼchipululu cha Eni Gedi.” 2 Tsono Sauli anatenga asilikali 3,000 odziwa kumenya bwino nkhondo kuchokera pakati pa Aisraeli onse ndipo anapita kukafunafuna Davide ndi anthu ake ku Matanthwe a Mbalale. 3 Iye anafika ku makola a nkhosa amene anali mʼmbali mwa njira. Kumeneko kunali phanga, ndipo Sauli analowa mʼphangamo kuti akadzithandize. Davide ndi anthu ake ankabisala mʼkati mwenimweni mwa phangalo. 4 Tsono anthu a Davide anamuwuza kuti, “Tsiku lija lafika limene Yehova anakuwuzani kuti, ‘Ndidzapereka mdani wanu mʼmanja mwanu, ndi kumuchita chimene chidzakukomereni.’ ” Koma Davide anapita mwakachetechete ndi kukadula msonga ya mkanjo wa Sauli. 5 Atachita izi, Davide anatsutsika mu mtima chifukwa anadula msonga ya mkanjo wa Sauli. 6 Tsono anawuza anthu ake kuti, “Yehova asalole kuti ndimuchite choyipa mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova. Ndisamupweteke pakuti ndi wodzozedwa wa Yehova.” 7 Choncho Davide anabweza mitima ya anthu ake ndi mawu amenewa, ndipo sanawalole kuti aphe Sauli. Pambuyo pake Sauli anatuluka mʼphangamo ndipo anachoka. 8 Kenaka Davide anatuluka mʼphanga muja ndipo anayitana Sauli, “Mbuye wanga!” Sauli atayangʼana mʼmbuyo, Davide anawerama ndi kugunditsa nkhope yake pansi. 9 Anafunsa Sauli kuti, “Nʼchifukwa chiyani mumamvera mawu a anthu kuti, ‘Davide wakukonzerani chiwembu?’ 10 Lero lino inu mwadzionera nokha kuti Yehova anakuperekani mʼmanja mwanga mʼphanga muja. Ena anandiwuza kuti ndikupheni, koma ndakusiyani. Ndinati, ‘Sindidzapha mbuye wanga pakuti ndiye wodzozedwa wa Yehova.’ 11 Tsono abambo anga, onanitu kansalu ka mkanjo wanu kali mʼdzanja langali! Popeza kuti ndinatha kudula msonga ya mkanjo wanu koma osakuphani, pamenepo mudziwe kuti ine ndilibe maganizo woti ndikuchiteni choyipa kapena kukuwukirani. Sindinakulakwireni ngakhale kuti inu mukufuna moyo wanga kuti mundiphe. 12 Yehova aweruze pakati pa inu ndi ine, akulangeni chifukwa cha zoyipa zimene mukundichitazi, koma dzanja langa silidzakukhudzani. 13 Paja anthu akale anati, ‘Munthu woyipa, ntchito zakenso ndi zoyipa.’ Kotero dzanja langa silidzakukhudzani. 14 “Kodi mfumu ya Israeli yadzalondola yani. Inu mukuthamangitsa yani? Galu wakufa kodi? Nsabwe kodi? 15 Nʼchifukwa chake Yehova agamule, inde aweruze pakati pa inu ndi ine ndi kupeza wolakwa. Yehova anditeteze ndi kundipulumutsa mʼdzanja lanu.” 16 Davide atatsiriza kuyankhula mawu awa, Sauli anafunsa kuti, “Kodi mawu amenewa ndi akodi mwana wanga Davide?” Sauli anayamba kulira mokweza. 17 Anawuza Davide kuti, “Ndiwe wolungama kuposa ine. Iwe wandikomera mtima pamene ine ndakuchitira zoyipa. 18 Iweyo lero lino wandifotokozera zabwino zimene wandichitira. Yehova anandipereka mʼdzanja lako koma iwe sunandiphe. 19 Kodi munthu atapeza mdani wake angamulole kuti apite wosamuvulaza? Motero Yehova akuchitire iwe zabwino chifukwa cha zimene wandichitira lerozi. 20 Ona tsono, Ine ndikudziwa kuti udzakhala mfumu ndithu ndipo ufumu wa Israeli udzakhazikika mʼmanja mwako. 21 Tsopano undilonjeze molumbira lero mʼdzina la Yehova kuti sudzapha zidzukulu zanga ine nditamwalira kapena kufuta dzina langa pa banja la makolo anga.” 22 Choncho Davide analumbira pamaso pa Sauli. Pambuyo pake Sauli anabwerera kwawo, koma Davide ndi anthu ake anapitanso ku phanga kuja.
In Other Versions
1 Samuel 24 in the ANGEFD
1 Samuel 24 in the ANTPNG2D
1 Samuel 24 in the AS21
1 Samuel 24 in the BAGH
1 Samuel 24 in the BBPNG
1 Samuel 24 in the BBT1E
1 Samuel 24 in the BDS
1 Samuel 24 in the BEV
1 Samuel 24 in the BHAD
1 Samuel 24 in the BIB
1 Samuel 24 in the BLPT
1 Samuel 24 in the BNT
1 Samuel 24 in the BNTABOOT
1 Samuel 24 in the BNTLV
1 Samuel 24 in the BOATCB
1 Samuel 24 in the BOATCB2
1 Samuel 24 in the BOBCV
1 Samuel 24 in the BOCNT
1 Samuel 24 in the BOECS
1 Samuel 24 in the BOHCB
1 Samuel 24 in the BOHCV
1 Samuel 24 in the BOHLNT
1 Samuel 24 in the BOHNTLTAL
1 Samuel 24 in the BOICB
1 Samuel 24 in the BOILNTAP
1 Samuel 24 in the BOITCV
1 Samuel 24 in the BOKCV
1 Samuel 24 in the BOKCV2
1 Samuel 24 in the BOKHWOG
1 Samuel 24 in the BOKSSV
1 Samuel 24 in the BOLCB
1 Samuel 24 in the BOLCB2
1 Samuel 24 in the BOMCV
1 Samuel 24 in the BONAV
1 Samuel 24 in the BONCB
1 Samuel 24 in the BONLT
1 Samuel 24 in the BONUT2
1 Samuel 24 in the BOPLNT
1 Samuel 24 in the BOSCB
1 Samuel 24 in the BOSNC
1 Samuel 24 in the BOTLNT
1 Samuel 24 in the BOVCB
1 Samuel 24 in the BOYCB
1 Samuel 24 in the BPBB
1 Samuel 24 in the BPH
1 Samuel 24 in the BSB
1 Samuel 24 in the CCB
1 Samuel 24 in the CUV
1 Samuel 24 in the CUVS
1 Samuel 24 in the DBT
1 Samuel 24 in the DGDNT
1 Samuel 24 in the DHNT
1 Samuel 24 in the DNT
1 Samuel 24 in the ELBE
1 Samuel 24 in the EMTV
1 Samuel 24 in the ESV
1 Samuel 24 in the FBV
1 Samuel 24 in the FEB
1 Samuel 24 in the GGMNT
1 Samuel 24 in the GNT
1 Samuel 24 in the HARY
1 Samuel 24 in the HNT
1 Samuel 24 in the IRVA
1 Samuel 24 in the IRVB
1 Samuel 24 in the IRVG
1 Samuel 24 in the IRVH
1 Samuel 24 in the IRVK
1 Samuel 24 in the IRVM
1 Samuel 24 in the IRVM2
1 Samuel 24 in the IRVO
1 Samuel 24 in the IRVP
1 Samuel 24 in the IRVT
1 Samuel 24 in the IRVT2
1 Samuel 24 in the IRVU
1 Samuel 24 in the ISVN
1 Samuel 24 in the JSNT
1 Samuel 24 in the KAPI
1 Samuel 24 in the KBT1ETNIK
1 Samuel 24 in the KBV
1 Samuel 24 in the KJV
1 Samuel 24 in the KNFD
1 Samuel 24 in the LBA
1 Samuel 24 in the LBLA
1 Samuel 24 in the LNT
1 Samuel 24 in the LSV
1 Samuel 24 in the MAAL
1 Samuel 24 in the MBV
1 Samuel 24 in the MBV2
1 Samuel 24 in the MHNT
1 Samuel 24 in the MKNFD
1 Samuel 24 in the MNG
1 Samuel 24 in the MNT
1 Samuel 24 in the MNT2
1 Samuel 24 in the MRS1T
1 Samuel 24 in the NAA
1 Samuel 24 in the NASB
1 Samuel 24 in the NBLA
1 Samuel 24 in the NBS
1 Samuel 24 in the NBVTP
1 Samuel 24 in the NET2
1 Samuel 24 in the NIV11
1 Samuel 24 in the NNT
1 Samuel 24 in the NNT2
1 Samuel 24 in the NNT3
1 Samuel 24 in the PDDPT
1 Samuel 24 in the PFNT
1 Samuel 24 in the RMNT
1 Samuel 24 in the SBIAS
1 Samuel 24 in the SBIBS
1 Samuel 24 in the SBIBS2
1 Samuel 24 in the SBICS
1 Samuel 24 in the SBIDS
1 Samuel 24 in the SBIGS
1 Samuel 24 in the SBIHS
1 Samuel 24 in the SBIIS
1 Samuel 24 in the SBIIS2
1 Samuel 24 in the SBIIS3
1 Samuel 24 in the SBIKS
1 Samuel 24 in the SBIKS2
1 Samuel 24 in the SBIMS
1 Samuel 24 in the SBIOS
1 Samuel 24 in the SBIPS
1 Samuel 24 in the SBISS
1 Samuel 24 in the SBITS
1 Samuel 24 in the SBITS2
1 Samuel 24 in the SBITS3
1 Samuel 24 in the SBITS4
1 Samuel 24 in the SBIUS
1 Samuel 24 in the SBIVS
1 Samuel 24 in the SBT
1 Samuel 24 in the SBT1E
1 Samuel 24 in the SCHL
1 Samuel 24 in the SNT
1 Samuel 24 in the SUSU
1 Samuel 24 in the SUSU2
1 Samuel 24 in the SYNO
1 Samuel 24 in the TBIAOTANT
1 Samuel 24 in the TBT1E
1 Samuel 24 in the TBT1E2
1 Samuel 24 in the TFTIP
1 Samuel 24 in the TFTU
1 Samuel 24 in the TGNTATF3T
1 Samuel 24 in the THAI
1 Samuel 24 in the TNFD
1 Samuel 24 in the TNT
1 Samuel 24 in the TNTIK
1 Samuel 24 in the TNTIL
1 Samuel 24 in the TNTIN
1 Samuel 24 in the TNTIP
1 Samuel 24 in the TNTIZ
1 Samuel 24 in the TOMA
1 Samuel 24 in the TTENT
1 Samuel 24 in the UBG
1 Samuel 24 in the UGV
1 Samuel 24 in the UGV2
1 Samuel 24 in the UGV3
1 Samuel 24 in the VBL
1 Samuel 24 in the VDCC
1 Samuel 24 in the YALU
1 Samuel 24 in the YAPE
1 Samuel 24 in the YBVTP
1 Samuel 24 in the ZBP