2 Chronicles 20 (BOGWICC)

1 Zitatha izi, Amowabu ndi Aamoni pamodzi ndi Ameuni ena anabwera kudzachita nkhondo ndi Yehosafati. 2 Anthu ena anabwera kudzamuwuza Yehosafati kuti, “Gulu lalikulu kwambiri lankhondo likubwera kudzachita nanu nkhondo lochokera ku Edomu, ku mbali ina ya Nyanja. Gululi lafika kale ku Hazazoni Tamara” (ndiye kuti Eni-Gedi). 3 Ndi mantha, Yehosafati anaganiza zofunsira kwa Yehova, ndipo analengeza kuti Ayuda onse asale zakudya. 4 Anthu a ku Yuda anabwera pamodzi kudzafuna thandizo kwa Yehova, ndipo anabweradi kuchokera ku mzinda uliwonse wa mu Yuda kudzafunafuna Yehova. 5 Yehosafati anayimirira pakati pa msonkhano wa Yuda ndi Yerusalemu, pa Nyumba ya Yehova patsogolo pa bwalo latsopano 6 ndipo anati:“Inu Yehova, Mulungu wa makolo athu, kodi Inu sindinu Mulungu amene muli kumwamba? Inu mumalamulira maufumu onse a mitundu ya anthu. Mphamvu ndi nyonga zili mʼmanja mwanu, ndipo palibe amene angalimbane nanu. 7 Inu Mulungu wathu, kodi simunathamangitse nzika za dziko lino pamaso pa anthu anu Aisraeli ndipo munalipereka kwa zidzukulu za Abrahamu bwenzi lanu kwamuyaya? 8 Iwo akhala mʼdzikolo ndipo anamangira Dzina lanu malo opatulika, nʼkumati, 9 ‘Ngati tsoka litigwera kaya ndi lupanga lachiweruzo, kapena mliri, kapenanso njala, ife tidzayima pamaso panu patsogolo pa Nyumba ya Mulungu ino imene imatchedwa ndi Dzina lanu ndipo tidzalirira kwa inu mʼmasautso athu, ndipo Inu mudzatimvera ndi kutipulumutsa.’ 10 “Koma tsopano pano pali anthu ochokera ku Amoni, Mowabu ndi Phiri la Seiri amene dziko lawo Inu simunawalole Aisraeli kuti alithire nkhondo pamene amabwera kuchokera ku Igupto. Kotero anatembenuka ndi kuwaleka ndipo sanawawononge. 11 Taonani, mmene akutibwezera ife pobwera kudzatithamangitsa mʼdziko limene inu munatipatsa ngati cholowa chathu. 12 Inu Mulungu wathu, kodi simuwaweruza? Pakuti ife tilibe mphamvu zolimbana ndi gulu lalikulu lankhondo limene likutithira nkhondoli. Ife sitikudziwa choti tichite, koma maso athu ali pa Inu.” 13 Anthu onse a Yuda, pamodzi ndi akazi awo ndi ana ndi makanda, anayima chilili pamaso pa Yehova. 14 Ndipo Mzimu wa Yehova unabwera pa Yahazieli mwana wa Zekariya, mwana wa Benaya, mwana wa Yeiyeli, mwana wa Mataniya Mlevi, chidzukulu cha Asafu, atayimirira mu msonkhano. 15 Iye anati, “Tamverani mfumu Yehosafati ndi onse amene amakhala mu Yuda ndi Yerusalemu! Zimene Yehova akunena kwa inu ndi izi: ‘Musaope kapena kutaya mtima chifukwa cha gulu lalikulu lankhondo ili. Pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu. 16 Mawa mupite mukamenyane nawo. Adzakhala akubwera mokweza kudzera Njira ya Zizi, ndipo mukawapeza kumapeto kwa chigwa cha ku chipululu cha Yeruweli. 17 Sikudzafunika kuti Inu mumenyane nawo pa nkhondo imeneyi. Inu mukhale pa malo anu; imani molimba ndipo onani chipulumutso chimene Yehova adzakupatsani, Inu Yuda ndi Yerusalemu. Musaope, musataye mtima. Pitani kuti mukakumane nawo mawa, ndipo Yehova adzakhala nanu.’ ” 18 Yehosafati anaweramitsa nkhope yake ndi kugunda pansi, ndiponso anthu onse a Yuda ndi Yerusalemu anagwa pansi ndi kulambira Yehova. 19 Kenaka Alevi ena ochokera ku mabanja a Kohati ndi Kora anayimirira ndipo anatamanda Yehova Mulungu wa Israeli ndi mawu ofuwula kwambiri. 20 Mmamawa, ananyamuka kupita ku chipululu cha Tekowa. Akunyamuka, Yehosafati anayimirira ndipo anati, “Tandimverani ine anthu a Yuda ndi Yerusalemu! Khalani ndi chikhulupiriro mwa Yehova Mulungu wanu ndipo mudzatchinjirizidwa, khalani ndi chikhulupiriro mwa aneneri ake ndipo mudzapambana.” 21 Atafunsira kwa anthu, Yehosafati anasankha anthu oti ayimbire Yehova ndi kumutamanda chifukwa cha ulemerero wa chiyero chake pamene amapita ali patsogolo pa gulu la ankhondo, akunena kuti:“Yamikani Yehovapakuti chikondi chake ndi chosatha.” 22 Atangoyamba kuyimba ndi kutamanda, Yehova anapereka mʼmanja mwawo anthu a ku Amoni ndi a ku Mowabu ndiponso a ku Phiri la Seiri amene amalimbana ndi Yuda, ndipo anagonjetsedwa. 23 Anthu a ku Amoni ndi a ku Mowabu anawukira anthu ochokera ku Phiri la Seiri, ndipo anawawononga ndi kuwatheratu. Atatsiriza kuwapha anthu ochokera ku Seiri anamenyana wina ndi mnzake mpaka kuwonongana. 24 Anthu a ku Yuda atafika pa malo oyangʼanana ndi chipululu ndi kuona kumene kunali gulu lalikulu lankhondo, iwo anangoona mitembo yokhayokha itagona pansi ndipo palibe amene anathawa. 25 Choncho Yehosafati ndi anthu ake anapita kukafunkha, ndipo pakati pawo anapeza katundu wambiri ndi zovala ndiponso zinthu zina zamtengowapatali kuposa zomwe akanatha kunyamula. Kunali katundu wambiri kotero kuti zinawatengera masiku atatu kuti amutenge. 26 Tsiku lachinayi anasonkhana ku chigwa cha Beraka kumene anatamanda Yehova. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa chigwa cha Beraka mpaka lero. 27 Tsono motsogozedwa ndi Yehosafati, anthu onse a Yuda ndi Yerusalemu anabwerera ku Yerusalemu mokondwera pakuti Yehova anawagonjetsera adani awo. 28 Iwo analowa mu Yerusalemu ndipo anapita ku Nyumba ya Mulungu akuyimba azeze, apangwe ndi malipenga. 29 Kuopsa kwa Mulungu kunali pa maufumu onse a mayiko amene anamva mmene Yehova anamenyera adani a Aisraeli. 30 Ndipo ufumu wa Yehosafati unali pa mtendere pakuti Mulungu wake anamupatsa mpumulo ku mbali zonse. 31 Choncho Yehosafati analamulira Yuda. Iye anali wa zaka 35 pamene anakhala mfumu ya Yuda ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 25. Dzina la amayi ake linali Azuba mwana wa Sili. 32 Iye ankayenda mʼnjira za Asa abambo ake ndipo sanapatuke pa zimenezi pakuti anachita zolungama pamaso pa Yehova. 33 Komabe malo opembedzerapo mafano sanachotsedwe ndipo anthu sanaperekebe mitima yawo kwa Mulungu wa makolo awo. 34 Zochitika zina zokhudza ufumu wa Yehosafati, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la Yehu mwana wa Hanani, zomwe zikupezeka mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli. 35 Zitapita izi, Yehosafati mfumu ya Yuda inachita mgwirizano ndi Ahaziya mfumu ya Israeli, amene anachita zoyipa kwambiri. 36 Iye anagwirizana ndi Ahaziya kuti apange sitima zapamadzi zochitira malonda. Atazipanga zimenezi ku Ezioni-Geberi, 37 Eliezara mwana wa Dodavahu wa ku Maresa ananenera motsutsana ndi Yehosafati ndipo anati, “Chifukwa chakuti wachita mgwirizano ndi Ahaziya, Yehova adzawononga zimene mwapangazo!” Sitima za pamadzizo zinawonongeka ndipo sizinapite nʼkomwe kumene zimakachita malonda.

In Other Versions

2 Chronicles 20 in the ANGEFD

2 Chronicles 20 in the ANTPNG2D

2 Chronicles 20 in the AS21

2 Chronicles 20 in the BAGH

2 Chronicles 20 in the BBPNG

2 Chronicles 20 in the BBT1E

2 Chronicles 20 in the BDS

2 Chronicles 20 in the BEV

2 Chronicles 20 in the BHAD

2 Chronicles 20 in the BIB

2 Chronicles 20 in the BLPT

2 Chronicles 20 in the BNT

2 Chronicles 20 in the BNTABOOT

2 Chronicles 20 in the BNTLV

2 Chronicles 20 in the BOATCB

2 Chronicles 20 in the BOATCB2

2 Chronicles 20 in the BOBCV

2 Chronicles 20 in the BOCNT

2 Chronicles 20 in the BOECS

2 Chronicles 20 in the BOHCB

2 Chronicles 20 in the BOHCV

2 Chronicles 20 in the BOHLNT

2 Chronicles 20 in the BOHNTLTAL

2 Chronicles 20 in the BOICB

2 Chronicles 20 in the BOILNTAP

2 Chronicles 20 in the BOITCV

2 Chronicles 20 in the BOKCV

2 Chronicles 20 in the BOKCV2

2 Chronicles 20 in the BOKHWOG

2 Chronicles 20 in the BOKSSV

2 Chronicles 20 in the BOLCB

2 Chronicles 20 in the BOLCB2

2 Chronicles 20 in the BOMCV

2 Chronicles 20 in the BONAV

2 Chronicles 20 in the BONCB

2 Chronicles 20 in the BONLT

2 Chronicles 20 in the BONUT2

2 Chronicles 20 in the BOPLNT

2 Chronicles 20 in the BOSCB

2 Chronicles 20 in the BOSNC

2 Chronicles 20 in the BOTLNT

2 Chronicles 20 in the BOVCB

2 Chronicles 20 in the BOYCB

2 Chronicles 20 in the BPBB

2 Chronicles 20 in the BPH

2 Chronicles 20 in the BSB

2 Chronicles 20 in the CCB

2 Chronicles 20 in the CUV

2 Chronicles 20 in the CUVS

2 Chronicles 20 in the DBT

2 Chronicles 20 in the DGDNT

2 Chronicles 20 in the DHNT

2 Chronicles 20 in the DNT

2 Chronicles 20 in the ELBE

2 Chronicles 20 in the EMTV

2 Chronicles 20 in the ESV

2 Chronicles 20 in the FBV

2 Chronicles 20 in the FEB

2 Chronicles 20 in the GGMNT

2 Chronicles 20 in the GNT

2 Chronicles 20 in the HARY

2 Chronicles 20 in the HNT

2 Chronicles 20 in the IRVA

2 Chronicles 20 in the IRVB

2 Chronicles 20 in the IRVG

2 Chronicles 20 in the IRVH

2 Chronicles 20 in the IRVK

2 Chronicles 20 in the IRVM

2 Chronicles 20 in the IRVM2

2 Chronicles 20 in the IRVO

2 Chronicles 20 in the IRVP

2 Chronicles 20 in the IRVT

2 Chronicles 20 in the IRVT2

2 Chronicles 20 in the IRVU

2 Chronicles 20 in the ISVN

2 Chronicles 20 in the JSNT

2 Chronicles 20 in the KAPI

2 Chronicles 20 in the KBT1ETNIK

2 Chronicles 20 in the KBV

2 Chronicles 20 in the KJV

2 Chronicles 20 in the KNFD

2 Chronicles 20 in the LBA

2 Chronicles 20 in the LBLA

2 Chronicles 20 in the LNT

2 Chronicles 20 in the LSV

2 Chronicles 20 in the MAAL

2 Chronicles 20 in the MBV

2 Chronicles 20 in the MBV2

2 Chronicles 20 in the MHNT

2 Chronicles 20 in the MKNFD

2 Chronicles 20 in the MNG

2 Chronicles 20 in the MNT

2 Chronicles 20 in the MNT2

2 Chronicles 20 in the MRS1T

2 Chronicles 20 in the NAA

2 Chronicles 20 in the NASB

2 Chronicles 20 in the NBLA

2 Chronicles 20 in the NBS

2 Chronicles 20 in the NBVTP

2 Chronicles 20 in the NET2

2 Chronicles 20 in the NIV11

2 Chronicles 20 in the NNT

2 Chronicles 20 in the NNT2

2 Chronicles 20 in the NNT3

2 Chronicles 20 in the PDDPT

2 Chronicles 20 in the PFNT

2 Chronicles 20 in the RMNT

2 Chronicles 20 in the SBIAS

2 Chronicles 20 in the SBIBS

2 Chronicles 20 in the SBIBS2

2 Chronicles 20 in the SBICS

2 Chronicles 20 in the SBIDS

2 Chronicles 20 in the SBIGS

2 Chronicles 20 in the SBIHS

2 Chronicles 20 in the SBIIS

2 Chronicles 20 in the SBIIS2

2 Chronicles 20 in the SBIIS3

2 Chronicles 20 in the SBIKS

2 Chronicles 20 in the SBIKS2

2 Chronicles 20 in the SBIMS

2 Chronicles 20 in the SBIOS

2 Chronicles 20 in the SBIPS

2 Chronicles 20 in the SBISS

2 Chronicles 20 in the SBITS

2 Chronicles 20 in the SBITS2

2 Chronicles 20 in the SBITS3

2 Chronicles 20 in the SBITS4

2 Chronicles 20 in the SBIUS

2 Chronicles 20 in the SBIVS

2 Chronicles 20 in the SBT

2 Chronicles 20 in the SBT1E

2 Chronicles 20 in the SCHL

2 Chronicles 20 in the SNT

2 Chronicles 20 in the SUSU

2 Chronicles 20 in the SUSU2

2 Chronicles 20 in the SYNO

2 Chronicles 20 in the TBIAOTANT

2 Chronicles 20 in the TBT1E

2 Chronicles 20 in the TBT1E2

2 Chronicles 20 in the TFTIP

2 Chronicles 20 in the TFTU

2 Chronicles 20 in the TGNTATF3T

2 Chronicles 20 in the THAI

2 Chronicles 20 in the TNFD

2 Chronicles 20 in the TNT

2 Chronicles 20 in the TNTIK

2 Chronicles 20 in the TNTIL

2 Chronicles 20 in the TNTIN

2 Chronicles 20 in the TNTIP

2 Chronicles 20 in the TNTIZ

2 Chronicles 20 in the TOMA

2 Chronicles 20 in the TTENT

2 Chronicles 20 in the UBG

2 Chronicles 20 in the UGV

2 Chronicles 20 in the UGV2

2 Chronicles 20 in the UGV3

2 Chronicles 20 in the VBL

2 Chronicles 20 in the VDCC

2 Chronicles 20 in the YALU

2 Chronicles 20 in the YAPE

2 Chronicles 20 in the YBVTP

2 Chronicles 20 in the ZBP