2 Kings 14 (BOGWICC)

1 Mʼchaka chachiwiri cha Yehowasi mwana wa Yowahazi mfumu ya Israeli, Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda anayamba kulamulira. 2 Iye anali ndi zaka 25 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 29. Amayi ake anali Yehoyadini wa ku Yerusalemu. 3 Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, koma osafanana ndi zomwe anachita Davide kholo lake. Iye anatsatira zochita zonse za Yowasi abambo ake. 4 Komabe sanachotse malo opembedzerapo mafano. Anthu anapitiriza kupereka nsembe ndi kufukiza lubani kumeneko. 5 Atakhazikika mu ufumu wake, Amaziya anapha atumiki ake amene anapha abambo ake, mfumu ija. 6 Komatu iye sanaphe ana a anthu amene anapha abambo ake potsatira zomwe zinalembedwa mʼbuku la Malamulo a Mose. Mʼmenemo Yehova analamula kuti, “Makolo asaphedwe chifukwa cha ana awo, ndipo ana asaphedwe chifukwa cha makolo awo, koma aliyense ayenera kufa chifukwa cha zolakwa zake.” 7 Iye ndiye amene anapha Aedomu 10,000 mʼchigwa cha Mchere nalanda mzinda wa Sela pa nkhondo ndipo anawutcha Yokiteeli, dzina lake ndi lomwelo mpaka lero lino. 8 Tsono Amaziya anatuma amithenga kwa Yehowasi mwana wa Yehowahazi, mwana wa Yehu mfumu ya Israeli ndi kumuopseza kuti, “Bwera tidzaonane maso ndi maso.” 9 Koma Yehowasi mfumu ya Israeli anabweza mawu kwa Amaziya mfumu ya Yuda kuti, “Mtengo wa minga wa ku Lebanoni unatumiza uthenga kwa mkungudza wa ku Lebanoni. ‘Patse mwana wako wamkazi kuti ndimukwatire.’ Kenaka chirombo cha ku Lebanoni chinabwera ndi kupondaponda mtengo wa mingawo. 10 Inde iwe wagonjetsa Edomu ndipo tsopano wayamba kudzikuza. Dzitamandire chifukwa cha kupambana kwako, koma khala kwanu konko! Nʼchifukwa chiyani ukuyamba dala mavuto amene adzakuwononga pamodzi ndi Yuda?” 11 Koma Amaziya sanamvere zimenezi. Choncho Yehowasi mfumu ya Israeli anakamuthira nkhondo. Yehowasi ndi Amaziya anakumana maso ndi maso ku Beti-Semesi mʼdziko la Yuda. 12 Israeli anagonjetsa Yuda ndipo munthu aliyense anathawira kwawo. 13 Yehowasi mfumu ya Israeli anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi, mwana wa Ahaziya ku Beti-Semesi. Ndipo anapita ku Yerusalemu nakagwetsa khoma la Yerusalemu kuyambira ku Chipata cha Efereimu mpaka ku Chipata Chapangodya, gawo lotalika mamita 180. 14 Iye anatenga golide ndi siliva yense pamodzi ndi ziwiya zonse zimene zinali mʼNyumba ya Yehova ndi zimene zinali mosungira chuma cha nyumba ya mfumu. Iye anagwiranso anthu nabwerera ku Samariya. 15 Ntchito zina za Yehowasi ndi zonse zimene anachita, kuwonjezera za nkhondo yake ndi Amaziya mfumu ya Yuda, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? 16 Yehowasi anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu Samariya pamodzi ndi mafumu a Israeli. Ndipo mwana wake Yeroboamu analowa ufumu mʼmalo mwake. 17 Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda anakhala zaka khumi ndi zisanu atamwalira Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israeli. 18 Ntchito zina za Amaziya, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 19 Anthu anapangana zomuchita chiwembu mu Yerusalemu ndipo Amaziya anathawira ku Lakisi, koma anatumiza anthu ku Lakisiko nakamuphera komweko. 20 Anabwera naye ku pa kavalo ku Yerusalemu ndi kumuyika mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. 21 Ndipo anthu onse a ku Yuda anatenga Azariya, amene anali ndi zaka 16 namulonga ufumu mʼmalo mwa abambo ake Amaziya. 22 Azariya anamanga mzinda wa Elati ndi kuwubwezeretsa ku Yuda, Amaziya atamwalira. 23 Mʼchaka cha khumi ndi chisanu cha Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda, Yeroboamu mwana wa Yehowasi mfumu ya Israeli analowa ufumu ku Samariya ndipo analamulira za 41. 24 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova ndipo sanasiye machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Israeli. 25 Iye ndi amene anabwezeretsanso malire a Israeli kuyambira ku Lebo Hamati mpaka ku Nyanja ya Araba, molingana ndi zimene ananena Yehova Mulungu wa Israeli, kudzera mwa mtumiki wake Yona mwana wa Amitai, mneneri wochokera ku Gati-Heferi. 26 Pakuti Yehova anaona masautso a Israeli amene anali owawa kwambiri, panalibe kapolo kapena mfulu ngakhale wina aliyense amene akanathandiza Israeli. 27 Pakuti Yehova anali asananene zofafaniza ufumu wa Israeli pa dziko lapansi, Iye anawapulumutsa kudzera mʼdzanja la Yeroboamu mwana wa Yowasi. 28 Ntchito zina za Yeroboamu ndi zonse zimene anachita, za kupambana kwake pa nkhondo, za mmene anagonjetsera Damasiko ndi Hamati, imene inali mizinda ya Yuda, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? 29 Yeroboamu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi mafumu a Israeli. Ndipo Zekariya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

In Other Versions

2 Kings 14 in the ANGEFD

2 Kings 14 in the ANTPNG2D

2 Kings 14 in the AS21

2 Kings 14 in the BAGH

2 Kings 14 in the BBPNG

2 Kings 14 in the BBT1E

2 Kings 14 in the BDS

2 Kings 14 in the BEV

2 Kings 14 in the BHAD

2 Kings 14 in the BIB

2 Kings 14 in the BLPT

2 Kings 14 in the BNT

2 Kings 14 in the BNTABOOT

2 Kings 14 in the BNTLV

2 Kings 14 in the BOATCB

2 Kings 14 in the BOATCB2

2 Kings 14 in the BOBCV

2 Kings 14 in the BOCNT

2 Kings 14 in the BOECS

2 Kings 14 in the BOHCB

2 Kings 14 in the BOHCV

2 Kings 14 in the BOHLNT

2 Kings 14 in the BOHNTLTAL

2 Kings 14 in the BOICB

2 Kings 14 in the BOILNTAP

2 Kings 14 in the BOITCV

2 Kings 14 in the BOKCV

2 Kings 14 in the BOKCV2

2 Kings 14 in the BOKHWOG

2 Kings 14 in the BOKSSV

2 Kings 14 in the BOLCB

2 Kings 14 in the BOLCB2

2 Kings 14 in the BOMCV

2 Kings 14 in the BONAV

2 Kings 14 in the BONCB

2 Kings 14 in the BONLT

2 Kings 14 in the BONUT2

2 Kings 14 in the BOPLNT

2 Kings 14 in the BOSCB

2 Kings 14 in the BOSNC

2 Kings 14 in the BOTLNT

2 Kings 14 in the BOVCB

2 Kings 14 in the BOYCB

2 Kings 14 in the BPBB

2 Kings 14 in the BPH

2 Kings 14 in the BSB

2 Kings 14 in the CCB

2 Kings 14 in the CUV

2 Kings 14 in the CUVS

2 Kings 14 in the DBT

2 Kings 14 in the DGDNT

2 Kings 14 in the DHNT

2 Kings 14 in the DNT

2 Kings 14 in the ELBE

2 Kings 14 in the EMTV

2 Kings 14 in the ESV

2 Kings 14 in the FBV

2 Kings 14 in the FEB

2 Kings 14 in the GGMNT

2 Kings 14 in the GNT

2 Kings 14 in the HARY

2 Kings 14 in the HNT

2 Kings 14 in the IRVA

2 Kings 14 in the IRVB

2 Kings 14 in the IRVG

2 Kings 14 in the IRVH

2 Kings 14 in the IRVK

2 Kings 14 in the IRVM

2 Kings 14 in the IRVM2

2 Kings 14 in the IRVO

2 Kings 14 in the IRVP

2 Kings 14 in the IRVT

2 Kings 14 in the IRVT2

2 Kings 14 in the IRVU

2 Kings 14 in the ISVN

2 Kings 14 in the JSNT

2 Kings 14 in the KAPI

2 Kings 14 in the KBT1ETNIK

2 Kings 14 in the KBV

2 Kings 14 in the KJV

2 Kings 14 in the KNFD

2 Kings 14 in the LBA

2 Kings 14 in the LBLA

2 Kings 14 in the LNT

2 Kings 14 in the LSV

2 Kings 14 in the MAAL

2 Kings 14 in the MBV

2 Kings 14 in the MBV2

2 Kings 14 in the MHNT

2 Kings 14 in the MKNFD

2 Kings 14 in the MNG

2 Kings 14 in the MNT

2 Kings 14 in the MNT2

2 Kings 14 in the MRS1T

2 Kings 14 in the NAA

2 Kings 14 in the NASB

2 Kings 14 in the NBLA

2 Kings 14 in the NBS

2 Kings 14 in the NBVTP

2 Kings 14 in the NET2

2 Kings 14 in the NIV11

2 Kings 14 in the NNT

2 Kings 14 in the NNT2

2 Kings 14 in the NNT3

2 Kings 14 in the PDDPT

2 Kings 14 in the PFNT

2 Kings 14 in the RMNT

2 Kings 14 in the SBIAS

2 Kings 14 in the SBIBS

2 Kings 14 in the SBIBS2

2 Kings 14 in the SBICS

2 Kings 14 in the SBIDS

2 Kings 14 in the SBIGS

2 Kings 14 in the SBIHS

2 Kings 14 in the SBIIS

2 Kings 14 in the SBIIS2

2 Kings 14 in the SBIIS3

2 Kings 14 in the SBIKS

2 Kings 14 in the SBIKS2

2 Kings 14 in the SBIMS

2 Kings 14 in the SBIOS

2 Kings 14 in the SBIPS

2 Kings 14 in the SBISS

2 Kings 14 in the SBITS

2 Kings 14 in the SBITS2

2 Kings 14 in the SBITS3

2 Kings 14 in the SBITS4

2 Kings 14 in the SBIUS

2 Kings 14 in the SBIVS

2 Kings 14 in the SBT

2 Kings 14 in the SBT1E

2 Kings 14 in the SCHL

2 Kings 14 in the SNT

2 Kings 14 in the SUSU

2 Kings 14 in the SUSU2

2 Kings 14 in the SYNO

2 Kings 14 in the TBIAOTANT

2 Kings 14 in the TBT1E

2 Kings 14 in the TBT1E2

2 Kings 14 in the TFTIP

2 Kings 14 in the TFTU

2 Kings 14 in the TGNTATF3T

2 Kings 14 in the THAI

2 Kings 14 in the TNFD

2 Kings 14 in the TNT

2 Kings 14 in the TNTIK

2 Kings 14 in the TNTIL

2 Kings 14 in the TNTIN

2 Kings 14 in the TNTIP

2 Kings 14 in the TNTIZ

2 Kings 14 in the TOMA

2 Kings 14 in the TTENT

2 Kings 14 in the UBG

2 Kings 14 in the UGV

2 Kings 14 in the UGV2

2 Kings 14 in the UGV3

2 Kings 14 in the VBL

2 Kings 14 in the VDCC

2 Kings 14 in the YALU

2 Kings 14 in the YAPE

2 Kings 14 in the YBVTP

2 Kings 14 in the ZBP