2 Samuel 13 (BOGWICC)

1 Patapita nthawi, Amnoni mwana wa Davide anakonda Tamara, mlongo wa Abisalomu, mwana wa Davide, amene anali wokongola. 2 Amnoni sankagona tulo mpaka anadwala chifukwa cha Tamara mlongo wakeyo, pakuti iye anali asanagonepo ndi mwamuna ndipo zimaoneka kuti zinali zosatheka kuti achite chilichonse kwa iye. 3 Koma Amnoni anali ndi mnzake dzina lake Yehonadabu mwana wamwamuna wa Simea, mʼbale wake wa Davide. Yonadabu anali munthu wochenjera kwambiri. 4 Iye anafunsa Amnoni, “Nʼchifukwa chiyani iwe mwana wa mfumu, umaoneka wowonda mmawa uliwonse? Bwanji wosandiwuza?”Amnoni anamuyankha kuti, “Ine ndamukonda Tamara, mlongo wa mʼbale wanga Abisalomu.” 5 Yehonadabu anati, “Pita ukagone ndipo unamizire kudwala. Abambo ako akabwera kudzakuona, udzati kwa iwo, Ine ndikufuna mlongo wanga Tamara abwere kuti adzandikonzere chakudya kuti ndidye. Adzandikonzere chakudyacho ine ndikumuona ndi kudya chili mʼmanja mwake.” 6 Kotero Amnoni anagona nakhala ngati akudwala. Mfumu itabwera kudzamuona, Amnoni anati kwa iyo, “Ine ndikufuna mlongo wanga Tamara kuti abwere adzandipangire buledi wapamwamba ineyo ndikuona, kuti ndidye ali mʼmanja mwake.” 7 Davide anatumiza mawu kwa Tamara ku nyumba yaufumu kuti, “Pita ku nyumba ya mlongo wako Amnoni ndipo ukamukonzere chakudya.” 8 Choncho Tamara anapitadi ku nyumba ya mlongo wake Amnoni kumalo kumene ankagona. Anakanda ufa, nawumba buledi Amunoniyo akuona ndipo anaphika bulediyo. 9 Kenaka iye anatenga chiwaya ndipo anamupatsa bulediyo, koma iyeyo anakana.Amnoni anati “Uza aliyense atuluke muno.” Ndipo aliyense anatuluka. 10 Kenaka Amnoni anati kwa Tamara, “Bweretsa chakudya kuno, ku chipinda changa chogona kuti ndidye chili mʼmanja mwako.” Ndipo Tamara anatenga buledi amene anapanga ndi kubwera naye kwa mlongo wake ku chipinda chake. 11 Koma atabweretsa kwa iye kuti adye, anamugwira ndipo anati, “Bwera ugone nane, iwe mlongo wanga.” 12 Tamara anati kwa iye, “Ayi mlongo wanga! Usandikakamize. Zotere siziyenera kuchitika mu Israeli! Usachite chinthu choyipa chotere. 13 Kodi ukuganiza bwanji za ine? Kodi manyazi anga ndidzawachotsa bwanji? Ndipo nanga iweyo? Udzakhalatu monga mmodzi mwa zitsiru zoyipitsitsa muno mu Israeli. Chonde kapemphe kwa mfumu. Sadzakuletsa kuti undikwatire.” 14 Koma sanamvere zimene amanena Tamara ndipo popeza anali wamphamvu kuposa Tamarayo, iye anamugwirira. 15 Atatero Amnoni anadana naye kwambiri. Iyeyo anamuda kuposa momwe anamukondera. Amnoni anati, “Dzuka ndipo tuluka!” 16 Iye anayankha, “Ayi! Kundithamangitsa kukhala kulakwa kwakukulu kuposa zimene wachita kale kwa ine.”Koma anakana kumumvera. 17 Amnoni anayitana wantchito wake ndipo anati, “Mutulutse mkazi uyu muno ndipo utseke chitseko akatuluka.” 18 Choncho wantchito wakeyo anamutulutsa ndipo anatseka chitseko atatuluka. Tamara anali atavala mkanjo wokongoletsedwa kwambiri, pakuti ichi chinali chovala chimene ana aakazi a mfumu amene sanagonepo ndi mwamuna amavala. 19 Tamara anatsira phulusa pamutu pake ndipo anangʼamba mkanjo wokongoletsedwa umene anavalawo. Iye anagwira manja ake kumutu ndipo anachoka, akulira mokweza pamene amapita. 20 Mlongo wake Abisalomu anati, “Kodi Amnoni uja mlongo wako wagona nawe? Khala chete mlongo wanga. Iye uja ndi mlongo wako ndipo usazilabadire.” Choncho Tamara anakhala mʼnyumba ya Abisalomu mlongo wake ngati woferedwa. 21 Mfumu Davide itamva zimenezi, inakwiya kwambiri. 22 Abisalomu sananene mawu aliwonse kwa Amnoni; abwino kapena oyipa. Iye anamuda Amunoniyo chifukwa anachititsa manyazi mlongo wake Tamara. 23 Patapita zaka ziwiri, pamene wometa nkhosa za Abisalomu anali ku Baala-Hazori pafupi ndi malire a fuko la Efereimu, iye anayitana ana onse aamuna a mfumu kuti apite kumeneko. 24 Abisalomu anapita kwa mfumu ndipo anati, “Ometa nkhosa za mtumiki wanu anabwera. Chonde mfumu ndi akuluakulu anu mubwere kudzakhala nane?” 25 Mfumu inayankha kuti, “Ayi mwana wanga, tisapite tonsefe. Tidzakhala cholemetsa kwa iwe.” Ngakhale Abisalomu anayesetsa kuwumiriza mfumuyo, inakana kupita. Mʼmalo mwake inangomudalitsa Abisalomuyo. 26 Kenaka Abisalomu anati, “Ngati sizitero, chonde mulole mʼbale wanga Amnoni apite nane.”Mfumu inamufunsa kuti, “Apite nawe chifukwa chiyani?” 27 Koma Abisalomu anamuwumiriza, kotero analola kuti Amnoni pamodzi ndi ana onse a mfumu apite naye. 28 Abisalomu analamula antchito ake kuti, “Tamverani! Amnoni akakaledzera ndi vinyo ndipo ine ndikakanena kuti, ‘Mukantheni Amnoni,’ pamenepo mukamuphe. Musakachite mantha. Kodi ine sindinakulamuleni? Mukhale amphamvu ndipo mulimbe mtima.” 29 Kotero antchito a Abisalomu anachita kwa Amnoni zimene Abisalomu anawalamula. Kenaka ana onse a mfumu anayimirira ndipo anakwera pa abulu awo nathawa. 30 Ali mʼnjira, Davide anamva mphekesera yakuti, “Abisalomu wakantha ana onse a mfumu ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene watsala.” 31 Mfumu inayimirira, ningʼamba zovala zake ndi kugona pa dothi. Antchito ake onse anayimirira pomwepo atangʼamba zovala zawo. 32 Koma Yehonadabu mwana wa Simea, mʼbale wake wa Davide anati, “Mbuye wanga mfumu musaganize kuti wapha ana onse a mfumu; wafa ndi Amnoni yekha. Awa ndiwo akhala maganizo a Abisalomu kuyambira tsiku limene Amnoni anagwirira mlongo wake Tamara. 33 Mbuye wanga mfumu musavutike ndi maganizo ndi nkhani yoti ana onse a mfumu afa. Wafa ndi Amnoni yekha.” 34 Nthawi imeneyi nʼkuti Abisalomu atathawa.Tsono munthu amene amalondera anayangʼana ndipo anaona anthu ambiri pa msewu wa kumadzulo kwake, akubwera kutsetsereka phiri. Mlondayo anapita kukawuza mfumu kuti, “Ndikuona anthu pa njira ya Horonaimu, mʼmbali mwa phiri.” 35 Yehonadabu anati kwa mfumu, “Taonani ana a mfumu afika. Zachitika monga momwe mtumiki wanu ananenera.” 36 Pamene amatsiriza kuyankhula, ana a mfumu analowa, akulira mofuwula. Mfumunso ndi antchito ake onse analira mokhudzidwa. 37 Abisalomu anathawa, napita kwa Talimai mwana wa Amihudi, mfumu ya ku Gesuri. Koma mfumu Davide inalira mwana wake tsiku ndi tsiku. 38 Abisalomu atathawa ndi kupita ku Gesuri, anakhala kumeneko zaka zitatu. 39 Ndipo Davide anagwidwa ndi chifundo chofuna kumulondola Abisalomu pakuti anali atatonthozedwa pa imfa ya Amnoni.

In Other Versions

2 Samuel 13 in the ANGEFD

2 Samuel 13 in the ANTPNG2D

2 Samuel 13 in the AS21

2 Samuel 13 in the BAGH

2 Samuel 13 in the BBPNG

2 Samuel 13 in the BBT1E

2 Samuel 13 in the BDS

2 Samuel 13 in the BEV

2 Samuel 13 in the BHAD

2 Samuel 13 in the BIB

2 Samuel 13 in the BLPT

2 Samuel 13 in the BNT

2 Samuel 13 in the BNTABOOT

2 Samuel 13 in the BNTLV

2 Samuel 13 in the BOATCB

2 Samuel 13 in the BOATCB2

2 Samuel 13 in the BOBCV

2 Samuel 13 in the BOCNT

2 Samuel 13 in the BOECS

2 Samuel 13 in the BOHCB

2 Samuel 13 in the BOHCV

2 Samuel 13 in the BOHLNT

2 Samuel 13 in the BOHNTLTAL

2 Samuel 13 in the BOICB

2 Samuel 13 in the BOILNTAP

2 Samuel 13 in the BOITCV

2 Samuel 13 in the BOKCV

2 Samuel 13 in the BOKCV2

2 Samuel 13 in the BOKHWOG

2 Samuel 13 in the BOKSSV

2 Samuel 13 in the BOLCB

2 Samuel 13 in the BOLCB2

2 Samuel 13 in the BOMCV

2 Samuel 13 in the BONAV

2 Samuel 13 in the BONCB

2 Samuel 13 in the BONLT

2 Samuel 13 in the BONUT2

2 Samuel 13 in the BOPLNT

2 Samuel 13 in the BOSCB

2 Samuel 13 in the BOSNC

2 Samuel 13 in the BOTLNT

2 Samuel 13 in the BOVCB

2 Samuel 13 in the BOYCB

2 Samuel 13 in the BPBB

2 Samuel 13 in the BPH

2 Samuel 13 in the BSB

2 Samuel 13 in the CCB

2 Samuel 13 in the CUV

2 Samuel 13 in the CUVS

2 Samuel 13 in the DBT

2 Samuel 13 in the DGDNT

2 Samuel 13 in the DHNT

2 Samuel 13 in the DNT

2 Samuel 13 in the ELBE

2 Samuel 13 in the EMTV

2 Samuel 13 in the ESV

2 Samuel 13 in the FBV

2 Samuel 13 in the FEB

2 Samuel 13 in the GGMNT

2 Samuel 13 in the GNT

2 Samuel 13 in the HARY

2 Samuel 13 in the HNT

2 Samuel 13 in the IRVA

2 Samuel 13 in the IRVB

2 Samuel 13 in the IRVG

2 Samuel 13 in the IRVH

2 Samuel 13 in the IRVK

2 Samuel 13 in the IRVM

2 Samuel 13 in the IRVM2

2 Samuel 13 in the IRVO

2 Samuel 13 in the IRVP

2 Samuel 13 in the IRVT

2 Samuel 13 in the IRVT2

2 Samuel 13 in the IRVU

2 Samuel 13 in the ISVN

2 Samuel 13 in the JSNT

2 Samuel 13 in the KAPI

2 Samuel 13 in the KBT1ETNIK

2 Samuel 13 in the KBV

2 Samuel 13 in the KJV

2 Samuel 13 in the KNFD

2 Samuel 13 in the LBA

2 Samuel 13 in the LBLA

2 Samuel 13 in the LNT

2 Samuel 13 in the LSV

2 Samuel 13 in the MAAL

2 Samuel 13 in the MBV

2 Samuel 13 in the MBV2

2 Samuel 13 in the MHNT

2 Samuel 13 in the MKNFD

2 Samuel 13 in the MNG

2 Samuel 13 in the MNT

2 Samuel 13 in the MNT2

2 Samuel 13 in the MRS1T

2 Samuel 13 in the NAA

2 Samuel 13 in the NASB

2 Samuel 13 in the NBLA

2 Samuel 13 in the NBS

2 Samuel 13 in the NBVTP

2 Samuel 13 in the NET2

2 Samuel 13 in the NIV11

2 Samuel 13 in the NNT

2 Samuel 13 in the NNT2

2 Samuel 13 in the NNT3

2 Samuel 13 in the PDDPT

2 Samuel 13 in the PFNT

2 Samuel 13 in the RMNT

2 Samuel 13 in the SBIAS

2 Samuel 13 in the SBIBS

2 Samuel 13 in the SBIBS2

2 Samuel 13 in the SBICS

2 Samuel 13 in the SBIDS

2 Samuel 13 in the SBIGS

2 Samuel 13 in the SBIHS

2 Samuel 13 in the SBIIS

2 Samuel 13 in the SBIIS2

2 Samuel 13 in the SBIIS3

2 Samuel 13 in the SBIKS

2 Samuel 13 in the SBIKS2

2 Samuel 13 in the SBIMS

2 Samuel 13 in the SBIOS

2 Samuel 13 in the SBIPS

2 Samuel 13 in the SBISS

2 Samuel 13 in the SBITS

2 Samuel 13 in the SBITS2

2 Samuel 13 in the SBITS3

2 Samuel 13 in the SBITS4

2 Samuel 13 in the SBIUS

2 Samuel 13 in the SBIVS

2 Samuel 13 in the SBT

2 Samuel 13 in the SBT1E

2 Samuel 13 in the SCHL

2 Samuel 13 in the SNT

2 Samuel 13 in the SUSU

2 Samuel 13 in the SUSU2

2 Samuel 13 in the SYNO

2 Samuel 13 in the TBIAOTANT

2 Samuel 13 in the TBT1E

2 Samuel 13 in the TBT1E2

2 Samuel 13 in the TFTIP

2 Samuel 13 in the TFTU

2 Samuel 13 in the TGNTATF3T

2 Samuel 13 in the THAI

2 Samuel 13 in the TNFD

2 Samuel 13 in the TNT

2 Samuel 13 in the TNTIK

2 Samuel 13 in the TNTIL

2 Samuel 13 in the TNTIN

2 Samuel 13 in the TNTIP

2 Samuel 13 in the TNTIZ

2 Samuel 13 in the TOMA

2 Samuel 13 in the TTENT

2 Samuel 13 in the UBG

2 Samuel 13 in the UGV

2 Samuel 13 in the UGV2

2 Samuel 13 in the UGV3

2 Samuel 13 in the VBL

2 Samuel 13 in the VDCC

2 Samuel 13 in the YALU

2 Samuel 13 in the YAPE

2 Samuel 13 in the YBVTP

2 Samuel 13 in the ZBP