2 Samuel 14 (BOGWICC)

1 Yowabu mwana wa Zeruya anadziwa kuti maganizo a mfumu ali pa Abisalomu. 2 Kotero Yowabu anatuma munthu wina kupita ku Tekowa ndi kukatengako mkazi wanzeru. Yowabu anati kwa mkaziyo, “Ukhale ngati namfedwa. Uvale zovala zaumasiye ndipo usadzole mafuta ena aliwonse. Ukhale ngati mkazi amene wakhala akulira masiku ambiri. 3 Kenaka upite kwa mfumu ndipo ukayankhule mawu awa.” Ndipo Yowabu anamuwuza mawu oti akanene. 4 Mkazi wochokera ku Tekowa uja atapita kwa mfumu anadzigwetsa pansi, napereka ulemu kwa mfumu nati, “Thandizeni mfumu!” 5 Mfumu inamufunsa kuti, “Kodi chikukusautsa iwe nʼchiyani?”Iye anayankha kuti, “Ine ndine mkazi wamasiye, mwamuna wanga anamwalira. 6 Ine wantchito wanu ndinali ndi ana aamuna awiri. Iwo anayamba kumenyana mʼmunda, ndipo panalibe woti awaleretse. Wina anakantha mnzakeyo mpaka kumupha. 7 Tsono banja lonse landiwukira ine, wantchito wanu. Iwo akuti, ‘Utipatse mwana amene anakantha mʼbale wakeyo kuti timuphe chifukwa cha moyo wa mʼbale wake amene anaphedwayo. Ife tidzaphanso mlowamʼmalo.’ Anthuwo adzapha mwana wanga amene wanditsalira, ndipo dzina la mwamuna wanga silidzakumbukika pakuti sipadzakhalanso mwana pa banja lathu.” 8 Mfumu inati kwa mkaziyo, “Pitani ku nyumba kwanu ndipo ine ndidzalamula mʼmalo mwanu.” 9 Koma mkazi wochokera ku Tekowayo anati kwa mfumu, “Mbuye wanga mfumu, kulakwa kukhale pa ine ndi banja la abambo anga ndipo mfumu ndi mpando wanu waufumu mukhale osalakwa.” 10 Mfumu inayankha kuti, “Ngati wina aliyense anene kanthu kwa iwe, umubweretse kwa ine, ndipo sadzakuvutitsanso.” 11 Mkaziyo anati, “Mfumu ipemphe kwa Yehova Mulungu wake kuti aletse wobwezera imfa asaphenso wina kuti mwana wanga asawonongedwe.”Mfumu inati, “Pali Yehova wamoyo ngakhale tsitsi limodzi la pamutu pa mwana wako silidzathotholedwa.” 12 Kenaka mkaziyo anati, “Lolani kuti wantchito wanu ayankhule mawu kwa inu mbuye wanga mfumu.”Iye anayankha kuti, “Yankhula.” 13 Mkaziyo anati, “Nʼchiyani tsono chimene mwaganiza kuchitira zimenezi anthu a Mulungu? Pamene mfumu yanena izi, kodi sikudzitsutsa yokha, pakuti mfumu sinayitanitse mwana amene anamupirikitsa? 14 Koma poti madzi akatayika sawoleka, ndiye tonsefe tiyenera kufa ndithu. Koma Mulungu safuna kuti moyo wa munthu utayike kotero anakonza njira yakuti wopirikitsidwayo asakhale wotayikiratu. 15 “Tsopano ine ndabwera kudzanena izi kwa inu mbuye wanga mfumu chifukwa anthu andichititsa mantha. Mdzakazi wanu anaganiza kuti, ‘Ndikayankhula kwa mfumu, mwina adzachita zimene mdzakazi wake adzamupempha. 16 Mwina mfumu idzavomereza kupulumutsa mdzakazi wake mʼdzanja la munthu amene akufuna kupha ine pamodzi ndi mwana wanga kutichotsa pa cholowa chimene Mulungu anatipatsa.’ 17 “Ndipo tsopano mtumiki wanu akuti, ‘Lolani mawu a mbuye wanga mfumu abweretse mpumulo kwa ine, pakuti mbuye wanga mfumu ali ngati mngelo wa Mulungu pozindikira chabwino ndi choyipa. Yehova Mulungu wanu akhale nanu.’ ” 18 Kenaka mfumu inati kwa mkaziyo, “Usandibisire chilichonse pondiyankha chimene ndidzakufunsa.”Mkaziyo anati, “Mbuye wanga mfumu yankhulani.” 19 Mfumu inafunsa kuti, “Kodi zimenezi sukuchita motsogozedwa ndi Yowabu?”Mkaziyo anayankha kuti, “Pali inu wamoyo, mbuye wanga mfumu, palibe munthu angakhotere kumanja kapena kumanzere pa chilichonse chimene mbuye wanga mfumu mwanena. Inde, ndi mtumiki wanu Yowabu amene wandilangiza ine kuchita zimenezi ndipo ndi amene anandipatsa mawu onsewa woti ine mtumiki wanu ndiyankhule. 20 Mtumiki wanu Yowabu anachita zimenezi kuti asinthe mmene zinthu zilili lero. Mbuye wanga muli ndi nzeru ngati za mngelo wa Mulungu. Mumadziwa zonse zimene zikuchitika mʼdziko.” 21 Mfumu inati kwa Yowabu, “Chabwino, ine ndichita zimenezi. Pita kamutenge Abisalomuyo.” 22 Yowabu anawerama pansi kupereka ulemu kwa mfumu. Yowabuyo anati, “Lero mtumiki wanu wadziwa kuti wapeza chifundo pamaso panu, mbuye wanga mfumu, chifukwa mwavomera pempho lakeli.” 23 Choncho Yowabu anapita ku Gesuri ndipo anamubweretsa Abisalomu ku Yerusalemu. 24 Koma mfumu inati, “Iye apite ku nyumba yake; asaone nkhope yanga.” Kotero Abisalomu anapita ku nyumba yake ndipo sanakumane ndi mfumu. 25 Mʼdziko lonse la Israeli munalibe munthu amene anayamikidwa chifukwa cha maonekedwe ake wokongola ngati Abisalomu. Kuyambira kumutu mpaka ku mapazi ake, analibe chilema. 26 Nthawi ina iliyonse akamameta tsitsi lake, ankameta pamene layamba kumulemera. Akatero amaliyeza, ndipo limalemera makilogalamu awiri pa sikelo yaufumu. 27 Abisalomu anali ndi ana aamuna atatu ndi wamkazi mmodzi. Mwana wamkazi dzina lake linali Tamara, ndipo anali mkazi wokongola kwambiri. 28 Abisalomu anakhala zaka ziwiri mu Yerusalemu osaonekera kwa mfumu. 29 Kenaka Abisalomu anatumiza mawu kwa Yowabu, kumutuma kuti apite kwa mfumu, koma Yowabu anakana kubwera. Kotero anatumizanso mawu kachiwiri, koma Yowabu anakananso. 30 Tsono Abisalomu anati kwa antchito ake, “Taonani, munda wa Yowabu uli pafupi ndi wanga ndipo muli barele mʼmenemo. Pitani mukawutenthe mundawo.” Ndipo antchito a Abisalomu anawutentha mundawo. 31 Ndipo Yowabu anapita ku nyumba ya Abisalomu ndipo anati kwa iye, “Nʼchifukwa chiyani antchito ako atentha munda wanga?” 32 Abisalomu anati kwa Yowabu, “Taona, ine ndinatumiza mawu kwa iwe ndipo ndinati, ‘Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukafunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ine ndinabwera kuchokera ku Gesuri? Zikanakhala bwino ndikanakhala komweko!’ Tsono pano ndikufuna kuonana ndi mfumu, ndipo ngati ndili olakwa mfumuyo indiphe.’ ” 33 Choncho Yowabu anapita kwa mfumu ndipo anayiwuza zimenezi. Ndipo mfumu inamuyitanitsa Abisalomu, ndipo analowa nawerama kugunditsa nkhope yake pansi pamaso pa mfumu. Tsono mfumu inapsompsona Abisalomu.

In Other Versions

2 Samuel 14 in the ANGEFD

2 Samuel 14 in the ANTPNG2D

2 Samuel 14 in the AS21

2 Samuel 14 in the BAGH

2 Samuel 14 in the BBPNG

2 Samuel 14 in the BBT1E

2 Samuel 14 in the BDS

2 Samuel 14 in the BEV

2 Samuel 14 in the BHAD

2 Samuel 14 in the BIB

2 Samuel 14 in the BLPT

2 Samuel 14 in the BNT

2 Samuel 14 in the BNTABOOT

2 Samuel 14 in the BNTLV

2 Samuel 14 in the BOATCB

2 Samuel 14 in the BOATCB2

2 Samuel 14 in the BOBCV

2 Samuel 14 in the BOCNT

2 Samuel 14 in the BOECS

2 Samuel 14 in the BOHCB

2 Samuel 14 in the BOHCV

2 Samuel 14 in the BOHLNT

2 Samuel 14 in the BOHNTLTAL

2 Samuel 14 in the BOICB

2 Samuel 14 in the BOILNTAP

2 Samuel 14 in the BOITCV

2 Samuel 14 in the BOKCV

2 Samuel 14 in the BOKCV2

2 Samuel 14 in the BOKHWOG

2 Samuel 14 in the BOKSSV

2 Samuel 14 in the BOLCB

2 Samuel 14 in the BOLCB2

2 Samuel 14 in the BOMCV

2 Samuel 14 in the BONAV

2 Samuel 14 in the BONCB

2 Samuel 14 in the BONLT

2 Samuel 14 in the BONUT2

2 Samuel 14 in the BOPLNT

2 Samuel 14 in the BOSCB

2 Samuel 14 in the BOSNC

2 Samuel 14 in the BOTLNT

2 Samuel 14 in the BOVCB

2 Samuel 14 in the BOYCB

2 Samuel 14 in the BPBB

2 Samuel 14 in the BPH

2 Samuel 14 in the BSB

2 Samuel 14 in the CCB

2 Samuel 14 in the CUV

2 Samuel 14 in the CUVS

2 Samuel 14 in the DBT

2 Samuel 14 in the DGDNT

2 Samuel 14 in the DHNT

2 Samuel 14 in the DNT

2 Samuel 14 in the ELBE

2 Samuel 14 in the EMTV

2 Samuel 14 in the ESV

2 Samuel 14 in the FBV

2 Samuel 14 in the FEB

2 Samuel 14 in the GGMNT

2 Samuel 14 in the GNT

2 Samuel 14 in the HARY

2 Samuel 14 in the HNT

2 Samuel 14 in the IRVA

2 Samuel 14 in the IRVB

2 Samuel 14 in the IRVG

2 Samuel 14 in the IRVH

2 Samuel 14 in the IRVK

2 Samuel 14 in the IRVM

2 Samuel 14 in the IRVM2

2 Samuel 14 in the IRVO

2 Samuel 14 in the IRVP

2 Samuel 14 in the IRVT

2 Samuel 14 in the IRVT2

2 Samuel 14 in the IRVU

2 Samuel 14 in the ISVN

2 Samuel 14 in the JSNT

2 Samuel 14 in the KAPI

2 Samuel 14 in the KBT1ETNIK

2 Samuel 14 in the KBV

2 Samuel 14 in the KJV

2 Samuel 14 in the KNFD

2 Samuel 14 in the LBA

2 Samuel 14 in the LBLA

2 Samuel 14 in the LNT

2 Samuel 14 in the LSV

2 Samuel 14 in the MAAL

2 Samuel 14 in the MBV

2 Samuel 14 in the MBV2

2 Samuel 14 in the MHNT

2 Samuel 14 in the MKNFD

2 Samuel 14 in the MNG

2 Samuel 14 in the MNT

2 Samuel 14 in the MNT2

2 Samuel 14 in the MRS1T

2 Samuel 14 in the NAA

2 Samuel 14 in the NASB

2 Samuel 14 in the NBLA

2 Samuel 14 in the NBS

2 Samuel 14 in the NBVTP

2 Samuel 14 in the NET2

2 Samuel 14 in the NIV11

2 Samuel 14 in the NNT

2 Samuel 14 in the NNT2

2 Samuel 14 in the NNT3

2 Samuel 14 in the PDDPT

2 Samuel 14 in the PFNT

2 Samuel 14 in the RMNT

2 Samuel 14 in the SBIAS

2 Samuel 14 in the SBIBS

2 Samuel 14 in the SBIBS2

2 Samuel 14 in the SBICS

2 Samuel 14 in the SBIDS

2 Samuel 14 in the SBIGS

2 Samuel 14 in the SBIHS

2 Samuel 14 in the SBIIS

2 Samuel 14 in the SBIIS2

2 Samuel 14 in the SBIIS3

2 Samuel 14 in the SBIKS

2 Samuel 14 in the SBIKS2

2 Samuel 14 in the SBIMS

2 Samuel 14 in the SBIOS

2 Samuel 14 in the SBIPS

2 Samuel 14 in the SBISS

2 Samuel 14 in the SBITS

2 Samuel 14 in the SBITS2

2 Samuel 14 in the SBITS3

2 Samuel 14 in the SBITS4

2 Samuel 14 in the SBIUS

2 Samuel 14 in the SBIVS

2 Samuel 14 in the SBT

2 Samuel 14 in the SBT1E

2 Samuel 14 in the SCHL

2 Samuel 14 in the SNT

2 Samuel 14 in the SUSU

2 Samuel 14 in the SUSU2

2 Samuel 14 in the SYNO

2 Samuel 14 in the TBIAOTANT

2 Samuel 14 in the TBT1E

2 Samuel 14 in the TBT1E2

2 Samuel 14 in the TFTIP

2 Samuel 14 in the TFTU

2 Samuel 14 in the TGNTATF3T

2 Samuel 14 in the THAI

2 Samuel 14 in the TNFD

2 Samuel 14 in the TNT

2 Samuel 14 in the TNTIK

2 Samuel 14 in the TNTIL

2 Samuel 14 in the TNTIN

2 Samuel 14 in the TNTIP

2 Samuel 14 in the TNTIZ

2 Samuel 14 in the TOMA

2 Samuel 14 in the TTENT

2 Samuel 14 in the UBG

2 Samuel 14 in the UGV

2 Samuel 14 in the UGV2

2 Samuel 14 in the UGV3

2 Samuel 14 in the VBL

2 Samuel 14 in the VDCC

2 Samuel 14 in the YALU

2 Samuel 14 in the YAPE

2 Samuel 14 in the YBVTP

2 Samuel 14 in the ZBP