2 Samuel 8 (BOGWICC)

1 Patapita nthawi, Davide anagonjetsa Afilisti ndi kuwapambana ndipo analanda Metegi Ama kuchoka mʼmanja mwa Afilistiwo. 2 Davide anagonjetsanso Amowabu. Iye anawalamula kuti agone pansi mʼmizere itatu pa gulu lililonse ndipo anawayeza ndi chingwe. Pa gulu lililonse ankapha anthu amene anali pa mizere iwiri yoyamba, kusiyapo mzere wachitatu. Kotero Amowabu anakhala pansi pa ulamuliro wa Davide ndipo ankapereka msonkho. 3 Komanso Davide anagonjetsa Hadadezeri mwana wa Rehobu, mfumu ya Zoba, pamene anapita kukakhazikitsa ulamuliro wake mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate. 4 Davide analanda magaleta 1,000, anthu 7,000 okwera magaleta pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha. 5 Aramu wa ku Damasiko atabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya Zoba, Davide anakantha asilikali 22,000. 6 Iye anakhazikitsa maboma mu ufumu wa Aramu wa ku Damasiko, ndipo Aaramu anakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho. Yehova ankamupatsa chipambano Davide kulikonse kumene ankapita. 7 Davide anatenga zishango zagolide za akuluakulu ankhondo a Hadadezeri ndi kubwera nazo ku Yerusalemu. 8 Mfumu Davide inatenga mkuwa wambiri kuchokera ku Beta ndi Berotai, mizinda ya Hadadezeri. 9 Tou, mfumu ya Hamati atamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse lankhondo la Hadadezeri, 10 anatumiza mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide kukamulonjera ndi kukamuyamikira chifukwa cha kupambana kwake pa nkhondo yake ndi Hadadezeriyo, amene analinso pa nkhondo ndi Tou. Yoramu anabweretsa ziwiya zasiliva, zagolide ndi zamkuwa. 11 Mfumu Davide inapereka zinthu zimenezi kwa Yehova, monga anachitira ndi siliva ndi golide zochokera ku mayiko onse amene anawagonjetsa: 12 Edomu ndi Mowabu, Aamoni ndi Afilisti, ndi Aamaleki. Iye anaperekanso zolanda ku nkhondo zochokera kwa Hadadezeri mwana wa Rehobu, mfumu ya Zoba. 13 Ndipo Davide anatchuka atabwera kokakantha Aedomu 18,000 mu Chigwa cha Mchere. 14 Iye anayika maboma mʼdera lonse la Edomu, ndipo Aedomu onse anakhala pansi pa Davide. Yehova ankapambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita. 15 Davide analamulira dziko lonse la Israeli ndipo ankachita zonse mwachilungamo ndi molondola pamaso pa anthu ake onse. 16 Yowabu mwana wa Zeruya anali mkulu wa ankhondo; Yehosafati mwana wa Ahiludi anali mlembi wa zochitika. 17 Zadoki mwana wa Ahitubi ndi Ahimeleki mwana wa Abiatara anali ansembe; Seraya anali mlembi; 18 Benaya mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wa Akereti ndi Apeleti; ndipo ana a Davide anali ansembe.

In Other Versions

2 Samuel 8 in the ANGEFD

2 Samuel 8 in the ANTPNG2D

2 Samuel 8 in the AS21

2 Samuel 8 in the BAGH

2 Samuel 8 in the BBPNG

2 Samuel 8 in the BBT1E

2 Samuel 8 in the BDS

2 Samuel 8 in the BEV

2 Samuel 8 in the BHAD

2 Samuel 8 in the BIB

2 Samuel 8 in the BLPT

2 Samuel 8 in the BNT

2 Samuel 8 in the BNTABOOT

2 Samuel 8 in the BNTLV

2 Samuel 8 in the BOATCB

2 Samuel 8 in the BOATCB2

2 Samuel 8 in the BOBCV

2 Samuel 8 in the BOCNT

2 Samuel 8 in the BOECS

2 Samuel 8 in the BOHCB

2 Samuel 8 in the BOHCV

2 Samuel 8 in the BOHLNT

2 Samuel 8 in the BOHNTLTAL

2 Samuel 8 in the BOICB

2 Samuel 8 in the BOILNTAP

2 Samuel 8 in the BOITCV

2 Samuel 8 in the BOKCV

2 Samuel 8 in the BOKCV2

2 Samuel 8 in the BOKHWOG

2 Samuel 8 in the BOKSSV

2 Samuel 8 in the BOLCB

2 Samuel 8 in the BOLCB2

2 Samuel 8 in the BOMCV

2 Samuel 8 in the BONAV

2 Samuel 8 in the BONCB

2 Samuel 8 in the BONLT

2 Samuel 8 in the BONUT2

2 Samuel 8 in the BOPLNT

2 Samuel 8 in the BOSCB

2 Samuel 8 in the BOSNC

2 Samuel 8 in the BOTLNT

2 Samuel 8 in the BOVCB

2 Samuel 8 in the BOYCB

2 Samuel 8 in the BPBB

2 Samuel 8 in the BPH

2 Samuel 8 in the BSB

2 Samuel 8 in the CCB

2 Samuel 8 in the CUV

2 Samuel 8 in the CUVS

2 Samuel 8 in the DBT

2 Samuel 8 in the DGDNT

2 Samuel 8 in the DHNT

2 Samuel 8 in the DNT

2 Samuel 8 in the ELBE

2 Samuel 8 in the EMTV

2 Samuel 8 in the ESV

2 Samuel 8 in the FBV

2 Samuel 8 in the FEB

2 Samuel 8 in the GGMNT

2 Samuel 8 in the GNT

2 Samuel 8 in the HARY

2 Samuel 8 in the HNT

2 Samuel 8 in the IRVA

2 Samuel 8 in the IRVB

2 Samuel 8 in the IRVG

2 Samuel 8 in the IRVH

2 Samuel 8 in the IRVK

2 Samuel 8 in the IRVM

2 Samuel 8 in the IRVM2

2 Samuel 8 in the IRVO

2 Samuel 8 in the IRVP

2 Samuel 8 in the IRVT

2 Samuel 8 in the IRVT2

2 Samuel 8 in the IRVU

2 Samuel 8 in the ISVN

2 Samuel 8 in the JSNT

2 Samuel 8 in the KAPI

2 Samuel 8 in the KBT1ETNIK

2 Samuel 8 in the KBV

2 Samuel 8 in the KJV

2 Samuel 8 in the KNFD

2 Samuel 8 in the LBA

2 Samuel 8 in the LBLA

2 Samuel 8 in the LNT

2 Samuel 8 in the LSV

2 Samuel 8 in the MAAL

2 Samuel 8 in the MBV

2 Samuel 8 in the MBV2

2 Samuel 8 in the MHNT

2 Samuel 8 in the MKNFD

2 Samuel 8 in the MNG

2 Samuel 8 in the MNT

2 Samuel 8 in the MNT2

2 Samuel 8 in the MRS1T

2 Samuel 8 in the NAA

2 Samuel 8 in the NASB

2 Samuel 8 in the NBLA

2 Samuel 8 in the NBS

2 Samuel 8 in the NBVTP

2 Samuel 8 in the NET2

2 Samuel 8 in the NIV11

2 Samuel 8 in the NNT

2 Samuel 8 in the NNT2

2 Samuel 8 in the NNT3

2 Samuel 8 in the PDDPT

2 Samuel 8 in the PFNT

2 Samuel 8 in the RMNT

2 Samuel 8 in the SBIAS

2 Samuel 8 in the SBIBS

2 Samuel 8 in the SBIBS2

2 Samuel 8 in the SBICS

2 Samuel 8 in the SBIDS

2 Samuel 8 in the SBIGS

2 Samuel 8 in the SBIHS

2 Samuel 8 in the SBIIS

2 Samuel 8 in the SBIIS2

2 Samuel 8 in the SBIIS3

2 Samuel 8 in the SBIKS

2 Samuel 8 in the SBIKS2

2 Samuel 8 in the SBIMS

2 Samuel 8 in the SBIOS

2 Samuel 8 in the SBIPS

2 Samuel 8 in the SBISS

2 Samuel 8 in the SBITS

2 Samuel 8 in the SBITS2

2 Samuel 8 in the SBITS3

2 Samuel 8 in the SBITS4

2 Samuel 8 in the SBIUS

2 Samuel 8 in the SBIVS

2 Samuel 8 in the SBT

2 Samuel 8 in the SBT1E

2 Samuel 8 in the SCHL

2 Samuel 8 in the SNT

2 Samuel 8 in the SUSU

2 Samuel 8 in the SUSU2

2 Samuel 8 in the SYNO

2 Samuel 8 in the TBIAOTANT

2 Samuel 8 in the TBT1E

2 Samuel 8 in the TBT1E2

2 Samuel 8 in the TFTIP

2 Samuel 8 in the TFTU

2 Samuel 8 in the TGNTATF3T

2 Samuel 8 in the THAI

2 Samuel 8 in the TNFD

2 Samuel 8 in the TNT

2 Samuel 8 in the TNTIK

2 Samuel 8 in the TNTIL

2 Samuel 8 in the TNTIN

2 Samuel 8 in the TNTIP

2 Samuel 8 in the TNTIZ

2 Samuel 8 in the TOMA

2 Samuel 8 in the TTENT

2 Samuel 8 in the UBG

2 Samuel 8 in the UGV

2 Samuel 8 in the UGV2

2 Samuel 8 in the UGV3

2 Samuel 8 in the VBL

2 Samuel 8 in the VDCC

2 Samuel 8 in the YALU

2 Samuel 8 in the YAPE

2 Samuel 8 in the YBVTP

2 Samuel 8 in the ZBP