Daniel 7 (BOGWICC)

1 Chaka choyamba cha ufumu wa Belisazara wa ku Babuloni, Danieli akugona pa bedi lake analota maloto ndipo anaona masomphenya. Iye analemba malotowo mwachidule. 2 Danieli anati, “Mʼmasomphenya anga usiku, ndinaona nyanga yayikulu ikuvunduka ndi mphepo zochokera mbali zonse zinayi za mlengalenga. 3 Ndipo mʼnyangayo munatuluka zirombo zazikulu zinayi, chilichonse chosiyana ndi chinzake. 4 “Choyamba chinali ngati mkango, ndipo chinali ndi mapiko ngati a chiwombankhanga. Ndinayangʼanitsitsa, kenaka mapiko ake anakhadzuka ndipo chinanyamulidwa ndi kuyimirira ndi miyendo yake iwiri ngati munthu, ndipo anachipatsa mtima wa munthu. 5 “Ndipo ndinaona chirombo chachiwiri, chimene chimaoneka ngati chimbalangondo. Chinali chonyamuka mbali imodzi, ndipo chinapana nthiti zitatu mʼkamwa mwake pakati pa mano ake. Anachilamula kuti, ‘Nyamuka, idya nyama yambiri!’ 6 “Pambuyo pake, ndinaona chirombo china, chimene chinkaoneka ngati kambuku. Pa msana pake chinali ndi mapiko anayi onga a mbalame. Chirombo ichi chinali ndi mitu inayi, ndipo chinapatsidwa mphamvu kuti chilamulire. 7 “Zitatha izi, mʼmasomphenya anga usiku, ndinaonanso chirombo chachinayi chitayima patsogolo panga. Chinali choopsa, chochititsa mantha ndi champhamvu kwambiri. Chinali ndi mano akuluakulu a chitsulo. Chimati chikatekedza ndi kumeza adani ake kenaka chinapondereza chilichonse chotsala. Ichi chinali chosiyana ndi zirombo zoyambirira zija, ndipo chinali ndi nyanga khumi. 8 “Ndikulingalira za nyangazo, ndinaona nyanga ina, yocheperapo, imene inkatuluka pakati pa zinzake. Zitatu mwa nyanga zoyamba zija zinazulidwa mwa icho. Nyanga iyi inali ndi maso a munthu ndi pakamwa pamene pankayankhula zodzitama. 9 “Ine ndikuyangʼanabe ndinaona“mipando yaufumu ikukhazikitsidwa,ndipo Mkulu Wachikhalire anakhala pa mpando wake.Zovala zake zinali zoyera ngati chisanu chowundana;tsitsi la kumutu kwake linali loyera ngati thonje.Mpando wake waufumu unali wonga malawi a moto,ndipo mikombero yake yonse inkayaka moto. 10 Mtsinje wa moto unkayenda,kuchokera patsogolo pake.Anthu miyandamiyanda ankamutumikira;ndipo anthu osawerengeka anayima pamaso pake.Abwalo anakhala malo awo,ndipo mabuku anatsekulidwa. 11 “Ndinapitiriza kuyangʼanitsitsa chifukwa cha mawu odzitamandira amene nyanga ija inkayankhula. Ndili chiyangʼanire choncho chirombo chachinayi chija chinaphedwa ndipo thupi lake linawonongedwa ndi kuponyedwa mʼngʼanjo ya moto. 12 Zirombo zina zija zinalandidwa ulamuliro wawo, koma zinaloledwa kukhala ndi moyo kwa kanthawi. 13 “Ndikuyangʼanabe zinthu mʼmasomphenya usiku, ndinaona wina ngati mwana wa munthu, akubwera ndi mitambo ya kumwamba. Anayandikira Mkulu Wachikhalire uja. Ena anamuperekeza kwa Iye. 14 Anapatsidwa ulamuliro, ulemerero ndi mphamvu za ufumu kuti anthu a mitundu ina yonse, mayiko ndi anthu aziyankhulo zosiyanasiyana apembedze iye. Mphamvu zake ndi mphamvu zamuyaya zimene sizidzatha, ndipo ufumu wake sudzawonongeka konse. 15 “Ine Danieli ndinavutika mu mzimu, ndipo zimene ndinaziona mʼmasomphenya zinandisautsa mʼmaganizo. 16 Ndinayandikira mmodzi mwa amene anayima pamenepo ndi kumufunsa tanthauzo lenileni la zonsezi.“Kotero anandiwuza ndi kundipatsa tanthauzo la zinthu zonse izi: 17 ‘Zirombo zikuluzikulu zinayi zija ndi maufumu anayi amene adzaoneka pa dziko lapansi. 18 Koma oyera mtima a Wammwambamwamba adzalandira ufumu ndipo udzakhala nawo mpaka muyaya, inde ku nthawi zonse.’ 19 “Kenaka ndinafuna kudziwa tanthauzo lenileni la chirombo chachinayi chija, chimene chinali chosiyana ndi zinzake zonse ndi choopsa kwambiri, cha mano ake achitsulo ndi zikhadabo zamkuwa; chirombo chimene chinapweteka ndi kumeza zinazo ndi kupondaponda chilichonse chimene chinatsala. 20 Ndinafunanso kudziwa za nyanga khumi za pa mutu pake ndiponso ina ija, nyanga imene inaphuka pambuyo pake ndi kugwetsa zitatu zija. Imeneyi ndi nyanga ija yokhala ndi maso ndi pakamwa poyankhula modzitamandira, ndipo inkaoneka yayikulu kupambana zina zonse. 21 Ndikuyangʼanitsitsa, nyanga imeneyi inathira nkhondo anthu oyera mtima ndi kuwagonjetsa, 22 mpaka pamene Mkulu Wachikhalire uja anafika ndi kuweruza mokomera oyera mtima a Wammwambamwamba. Tsono nthawi inafika imene anthu oyera mtimawo analandira ufumu. 23 “Tsono anandifotokozera kuti, ‘Chirombo chachinayi chija ndi ufumu wachinayi umene udzaoneka pa dziko lapansi. Udzakhala wosiyana ndi maufumu anzake onse ndipo udzawononga dziko lonse lapansi. Udzalipondaponda ndi kuliphwasula. 24 Nyanga khumi zija ndiwo mafumu khumi amene adzatuluka mu ufumu umenewu. Pambuyo pake mfumu ina idzadzuka, yosiyana ndi mafumu a mʼmbuyomu; iyo idzagonjetsa mafumu atatu. 25 Idzayankhula motsutsana ndi Wammwambamwamba ndipo adzazunza oyera mtima ndi kusintha masiku azikondwerero ndi malamulo. Oyera mtimawo adzalamulidwa ndi mfumuyi kwa zaka zitatu ndi theka. 26 “ ‘Koma bwalo lidzapereka chiweruzo, ndipo mphamvu zake zidzalandidwa ndi kuwonongedwa kotheratu mpaka muyaya. 27 Kenaka ulamuliro, mphamvu ndi ukulu wa maufumu pa dziko lonse lapansi zidzaperekedwa kwa oyera mtima, a Wammwambamwamba. Ufumu wawo udzakhala ufumu wosatha, ndipo olamulira onse adzawalamulira ndi kuwamvera.’ ” 28 “Apa ndiye pa mapeto pa nkhaniyi. Ine Danieli, ndinasautsidwa kwambiri mʼmaganizo anga, ndipo nkhope yanga inasandulika, koma ndinasunga nkhaniyi mu mtima mwanga.”

In Other Versions

Daniel 7 in the ANGEFD

Daniel 7 in the ANTPNG2D

Daniel 7 in the AS21

Daniel 7 in the BAGH

Daniel 7 in the BBPNG

Daniel 7 in the BBT1E

Daniel 7 in the BDS

Daniel 7 in the BEV

Daniel 7 in the BHAD

Daniel 7 in the BIB

Daniel 7 in the BLPT

Daniel 7 in the BNT

Daniel 7 in the BNTABOOT

Daniel 7 in the BNTLV

Daniel 7 in the BOATCB

Daniel 7 in the BOATCB2

Daniel 7 in the BOBCV

Daniel 7 in the BOCNT

Daniel 7 in the BOECS

Daniel 7 in the BOHCB

Daniel 7 in the BOHCV

Daniel 7 in the BOHLNT

Daniel 7 in the BOHNTLTAL

Daniel 7 in the BOICB

Daniel 7 in the BOILNTAP

Daniel 7 in the BOITCV

Daniel 7 in the BOKCV

Daniel 7 in the BOKCV2

Daniel 7 in the BOKHWOG

Daniel 7 in the BOKSSV

Daniel 7 in the BOLCB

Daniel 7 in the BOLCB2

Daniel 7 in the BOMCV

Daniel 7 in the BONAV

Daniel 7 in the BONCB

Daniel 7 in the BONLT

Daniel 7 in the BONUT2

Daniel 7 in the BOPLNT

Daniel 7 in the BOSCB

Daniel 7 in the BOSNC

Daniel 7 in the BOTLNT

Daniel 7 in the BOVCB

Daniel 7 in the BOYCB

Daniel 7 in the BPBB

Daniel 7 in the BPH

Daniel 7 in the BSB

Daniel 7 in the CCB

Daniel 7 in the CUV

Daniel 7 in the CUVS

Daniel 7 in the DBT

Daniel 7 in the DGDNT

Daniel 7 in the DHNT

Daniel 7 in the DNT

Daniel 7 in the ELBE

Daniel 7 in the EMTV

Daniel 7 in the ESV

Daniel 7 in the FBV

Daniel 7 in the FEB

Daniel 7 in the GGMNT

Daniel 7 in the GNT

Daniel 7 in the HARY

Daniel 7 in the HNT

Daniel 7 in the IRVA

Daniel 7 in the IRVB

Daniel 7 in the IRVG

Daniel 7 in the IRVH

Daniel 7 in the IRVK

Daniel 7 in the IRVM

Daniel 7 in the IRVM2

Daniel 7 in the IRVO

Daniel 7 in the IRVP

Daniel 7 in the IRVT

Daniel 7 in the IRVT2

Daniel 7 in the IRVU

Daniel 7 in the ISVN

Daniel 7 in the JSNT

Daniel 7 in the KAPI

Daniel 7 in the KBT1ETNIK

Daniel 7 in the KBV

Daniel 7 in the KJV

Daniel 7 in the KNFD

Daniel 7 in the LBA

Daniel 7 in the LBLA

Daniel 7 in the LNT

Daniel 7 in the LSV

Daniel 7 in the MAAL

Daniel 7 in the MBV

Daniel 7 in the MBV2

Daniel 7 in the MHNT

Daniel 7 in the MKNFD

Daniel 7 in the MNG

Daniel 7 in the MNT

Daniel 7 in the MNT2

Daniel 7 in the MRS1T

Daniel 7 in the NAA

Daniel 7 in the NASB

Daniel 7 in the NBLA

Daniel 7 in the NBS

Daniel 7 in the NBVTP

Daniel 7 in the NET2

Daniel 7 in the NIV11

Daniel 7 in the NNT

Daniel 7 in the NNT2

Daniel 7 in the NNT3

Daniel 7 in the PDDPT

Daniel 7 in the PFNT

Daniel 7 in the RMNT

Daniel 7 in the SBIAS

Daniel 7 in the SBIBS

Daniel 7 in the SBIBS2

Daniel 7 in the SBICS

Daniel 7 in the SBIDS

Daniel 7 in the SBIGS

Daniel 7 in the SBIHS

Daniel 7 in the SBIIS

Daniel 7 in the SBIIS2

Daniel 7 in the SBIIS3

Daniel 7 in the SBIKS

Daniel 7 in the SBIKS2

Daniel 7 in the SBIMS

Daniel 7 in the SBIOS

Daniel 7 in the SBIPS

Daniel 7 in the SBISS

Daniel 7 in the SBITS

Daniel 7 in the SBITS2

Daniel 7 in the SBITS3

Daniel 7 in the SBITS4

Daniel 7 in the SBIUS

Daniel 7 in the SBIVS

Daniel 7 in the SBT

Daniel 7 in the SBT1E

Daniel 7 in the SCHL

Daniel 7 in the SNT

Daniel 7 in the SUSU

Daniel 7 in the SUSU2

Daniel 7 in the SYNO

Daniel 7 in the TBIAOTANT

Daniel 7 in the TBT1E

Daniel 7 in the TBT1E2

Daniel 7 in the TFTIP

Daniel 7 in the TFTU

Daniel 7 in the TGNTATF3T

Daniel 7 in the THAI

Daniel 7 in the TNFD

Daniel 7 in the TNT

Daniel 7 in the TNTIK

Daniel 7 in the TNTIL

Daniel 7 in the TNTIN

Daniel 7 in the TNTIP

Daniel 7 in the TNTIZ

Daniel 7 in the TOMA

Daniel 7 in the TTENT

Daniel 7 in the UBG

Daniel 7 in the UGV

Daniel 7 in the UGV2

Daniel 7 in the UGV3

Daniel 7 in the VBL

Daniel 7 in the VDCC

Daniel 7 in the YALU

Daniel 7 in the YAPE

Daniel 7 in the YBVTP

Daniel 7 in the ZBP