Deuteronomy 34 (BOGWICC)

1 Ndipo Mose anakwera Phiri la Nebo kuchokera ku chigwa cha Mowabu ndi kukafika pamwamba pa Phiri la Pisiga, kummawa kwa Yeriko. Kumeneko Yehova anamuonetsa dziko lonse; kuchokera ku Giliyadi mpaka ku Dani. 2 Dera lonse la Nafutali, dziko lonse la Efereimu ndi Manase, dziko lonse la Yuda mpaka kukafika kumadzulo kwa nyanja, 3 Negevi ndi chigawo chonse kuchokera ku Chigwa cha Yeriko, Mzinda wa mitengo ya migwalangwa, mpaka ku Zowari. 4 Kenaka Yehova anawuza Mose kuti, “Limenelo ndi dziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo pamene ndinanena kuti, ‘Ndidzalipereka kwa zidzukulu zanu.’ Ndakulola kuti ulione, koma sudzawoloka kuti ukalowemo.” 5 Choncho Mose mtumiki wa Yehova anamwalira kumeneko ku Mowabu, monga momwe ananenera Yehova. 6 Yehova anamuyika mʼmanda ku Mowabu, mʼchigwa choyangʼanana ndi Beti-Peori, koma mpaka lero palibe amene amadziwa pamene pali manda ake. 7 Mose anamwalira ali ndi zaka 120, koma maso ake ankaonabe ndipo anali amphamvu. 8 Aisraeli analira maliro a Mose mʼchikhwawa cha Mowabu kwa masiku makumi atatu mpaka nthawi ya kulira maliro ndi kukhuza inatha. 9 Tsono Yoswa, mwana wa Nuni anadzazidwa ndi mzimu wanzeru chifukwa nʼkuti Mose atamusanjika manja. Choncho Aisraeli anamumvera ndipo anachita zomwe Yehova analamula Mose. 10 Kuyambira nthawi imeneyi, mu Israeli simunakhalepo mneneri wina aliyense wofanana ndi Mose, amene Yehova amayankhula naye maso ndi maso. 11 Amene anachita zizindikiro zozizwitsa zonsezi ndi zozizwitsa zimene Yehova anamutuma kuti achite mu Igupto, kwa Farao ndi kwa nduna zake zonse ndiponso mʼdziko lake lonse. 12 Ndithudi palibe mneneri wina aliyense amene anachita zinthu zazikulu ndi zoopsa zofanana ndi zomwe Mose anachita pamaso pa Aisraeli onse.

In Other Versions

Deuteronomy 34 in the ANGEFD

Deuteronomy 34 in the ANTPNG2D

Deuteronomy 34 in the AS21

Deuteronomy 34 in the BAGH

Deuteronomy 34 in the BBPNG

Deuteronomy 34 in the BBT1E

Deuteronomy 34 in the BDS

Deuteronomy 34 in the BEV

Deuteronomy 34 in the BHAD

Deuteronomy 34 in the BIB

Deuteronomy 34 in the BLPT

Deuteronomy 34 in the BNT

Deuteronomy 34 in the BNTABOOT

Deuteronomy 34 in the BNTLV

Deuteronomy 34 in the BOATCB

Deuteronomy 34 in the BOATCB2

Deuteronomy 34 in the BOBCV

Deuteronomy 34 in the BOCNT

Deuteronomy 34 in the BOECS

Deuteronomy 34 in the BOHCB

Deuteronomy 34 in the BOHCV

Deuteronomy 34 in the BOHLNT

Deuteronomy 34 in the BOHNTLTAL

Deuteronomy 34 in the BOICB

Deuteronomy 34 in the BOILNTAP

Deuteronomy 34 in the BOITCV

Deuteronomy 34 in the BOKCV

Deuteronomy 34 in the BOKCV2

Deuteronomy 34 in the BOKHWOG

Deuteronomy 34 in the BOKSSV

Deuteronomy 34 in the BOLCB

Deuteronomy 34 in the BOLCB2

Deuteronomy 34 in the BOMCV

Deuteronomy 34 in the BONAV

Deuteronomy 34 in the BONCB

Deuteronomy 34 in the BONLT

Deuteronomy 34 in the BONUT2

Deuteronomy 34 in the BOPLNT

Deuteronomy 34 in the BOSCB

Deuteronomy 34 in the BOSNC

Deuteronomy 34 in the BOTLNT

Deuteronomy 34 in the BOVCB

Deuteronomy 34 in the BOYCB

Deuteronomy 34 in the BPBB

Deuteronomy 34 in the BPH

Deuteronomy 34 in the BSB

Deuteronomy 34 in the CCB

Deuteronomy 34 in the CUV

Deuteronomy 34 in the CUVS

Deuteronomy 34 in the DBT

Deuteronomy 34 in the DGDNT

Deuteronomy 34 in the DHNT

Deuteronomy 34 in the DNT

Deuteronomy 34 in the ELBE

Deuteronomy 34 in the EMTV

Deuteronomy 34 in the ESV

Deuteronomy 34 in the FBV

Deuteronomy 34 in the FEB

Deuteronomy 34 in the GGMNT

Deuteronomy 34 in the GNT

Deuteronomy 34 in the HARY

Deuteronomy 34 in the HNT

Deuteronomy 34 in the IRVA

Deuteronomy 34 in the IRVB

Deuteronomy 34 in the IRVG

Deuteronomy 34 in the IRVH

Deuteronomy 34 in the IRVK

Deuteronomy 34 in the IRVM

Deuteronomy 34 in the IRVM2

Deuteronomy 34 in the IRVO

Deuteronomy 34 in the IRVP

Deuteronomy 34 in the IRVT

Deuteronomy 34 in the IRVT2

Deuteronomy 34 in the IRVU

Deuteronomy 34 in the ISVN

Deuteronomy 34 in the JSNT

Deuteronomy 34 in the KAPI

Deuteronomy 34 in the KBT1ETNIK

Deuteronomy 34 in the KBV

Deuteronomy 34 in the KJV

Deuteronomy 34 in the KNFD

Deuteronomy 34 in the LBA

Deuteronomy 34 in the LBLA

Deuteronomy 34 in the LNT

Deuteronomy 34 in the LSV

Deuteronomy 34 in the MAAL

Deuteronomy 34 in the MBV

Deuteronomy 34 in the MBV2

Deuteronomy 34 in the MHNT

Deuteronomy 34 in the MKNFD

Deuteronomy 34 in the MNG

Deuteronomy 34 in the MNT

Deuteronomy 34 in the MNT2

Deuteronomy 34 in the MRS1T

Deuteronomy 34 in the NAA

Deuteronomy 34 in the NASB

Deuteronomy 34 in the NBLA

Deuteronomy 34 in the NBS

Deuteronomy 34 in the NBVTP

Deuteronomy 34 in the NET2

Deuteronomy 34 in the NIV11

Deuteronomy 34 in the NNT

Deuteronomy 34 in the NNT2

Deuteronomy 34 in the NNT3

Deuteronomy 34 in the PDDPT

Deuteronomy 34 in the PFNT

Deuteronomy 34 in the RMNT

Deuteronomy 34 in the SBIAS

Deuteronomy 34 in the SBIBS

Deuteronomy 34 in the SBIBS2

Deuteronomy 34 in the SBICS

Deuteronomy 34 in the SBIDS

Deuteronomy 34 in the SBIGS

Deuteronomy 34 in the SBIHS

Deuteronomy 34 in the SBIIS

Deuteronomy 34 in the SBIIS2

Deuteronomy 34 in the SBIIS3

Deuteronomy 34 in the SBIKS

Deuteronomy 34 in the SBIKS2

Deuteronomy 34 in the SBIMS

Deuteronomy 34 in the SBIOS

Deuteronomy 34 in the SBIPS

Deuteronomy 34 in the SBISS

Deuteronomy 34 in the SBITS

Deuteronomy 34 in the SBITS2

Deuteronomy 34 in the SBITS3

Deuteronomy 34 in the SBITS4

Deuteronomy 34 in the SBIUS

Deuteronomy 34 in the SBIVS

Deuteronomy 34 in the SBT

Deuteronomy 34 in the SBT1E

Deuteronomy 34 in the SCHL

Deuteronomy 34 in the SNT

Deuteronomy 34 in the SUSU

Deuteronomy 34 in the SUSU2

Deuteronomy 34 in the SYNO

Deuteronomy 34 in the TBIAOTANT

Deuteronomy 34 in the TBT1E

Deuteronomy 34 in the TBT1E2

Deuteronomy 34 in the TFTIP

Deuteronomy 34 in the TFTU

Deuteronomy 34 in the TGNTATF3T

Deuteronomy 34 in the THAI

Deuteronomy 34 in the TNFD

Deuteronomy 34 in the TNT

Deuteronomy 34 in the TNTIK

Deuteronomy 34 in the TNTIL

Deuteronomy 34 in the TNTIN

Deuteronomy 34 in the TNTIP

Deuteronomy 34 in the TNTIZ

Deuteronomy 34 in the TOMA

Deuteronomy 34 in the TTENT

Deuteronomy 34 in the UBG

Deuteronomy 34 in the UGV

Deuteronomy 34 in the UGV2

Deuteronomy 34 in the UGV3

Deuteronomy 34 in the VBL

Deuteronomy 34 in the VDCC

Deuteronomy 34 in the YALU

Deuteronomy 34 in the YAPE

Deuteronomy 34 in the YBVTP

Deuteronomy 34 in the ZBP