Deuteronomy 7 (BOGWICC)

1 Pamene Yehova Mulungu wanu wakufikitsani mʼdziko limene mukukalowa ndi kulilanda ndi kuthamangitsa pamaso panu mitundu ya anthu iyi: Ahiti, Agirigasi, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi; yomwe ndi mitundu isanu ndi iwiri yayikulu ndi yamphamvu kuposa inu; 2 Yehova Mulungu wanu akadzawapereka mʼmanja mwanu, ndipo inu mukadzawagonjetsa, mudzawawononge kwathunthu. Musadzachite mgwirizano ndi anthuwo ndiponso musadzawachitire chifundo. 3 Musadzakwatirane nawo. Musadzapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna kapena kutenga ana anu aamuna ndi kuwapereka kwa ana awo aakazi. 4 Mukadzatero, iwo adzasocheretsa ana anu aamuna kuti asanditsatire ndi kutumikira milungu ina. Motero Yehova adzakukwiyirani ndi kukuwonongani mwachangu. 5 Koma mukachite izi: Mukagumule maguwa awo ansembe, mukaswe miyala yawo yachipembedzo, mukadule mitengo yawo ya Asera, ndi kutentha mafano awo pa moto. 6 Pakuti inu ndinu anthu opatulika kwa Yehova Mulungu wanu. Yehova Mulungu wanu anakusankhani pakati pa anthu onse pa dziko lapansi kuti mukhale ake, chuma chake cha mtengo wapatali. 7 Yehova sanakukondeni chifukwa choti munali ochuluka kuposa ena pakuti inuyo ndiye munali ochepetsetsa mwa anthu onse. 8 Koma chifukwa chakuti Yehova anakukondani nasunga lumbiro lake limene analumbira kwa makolo anu. Ndi chifukwa chake anakutulutsani ndi mphamvu yake yopanda malire ndi kukupulumutsani ku dziko la ukapolo, kuchoka mʼmanja mwa Farao mfumu ya ku Igupto. 9 Choncho dziwani kuti Yehova Mulungu wanu, ndi Mulungu. Iye ndi Mulungu wokhulupirika, wosunga pangano lake la chikondi chosasinthika ku mibadomibado, kwa iwo amene amamukonda nasunga malamulo ake. 10 Komaiwo amene amamuda adzawabwezera powawononga pamaso pawo;sadzachedwa kuwabwezera iwo amene amadana naye. 11 Choncho muziyesetsa kusunga malamulo, malangizo ndi maphunziro amene ndikukulamulani lero lino kuti muchite. 12 Mukamvera malamulo amenewa, ndi kusamala kuwatsata, ndiye kuti Yehova Mulungu wanu adzasunga pangano lake la chikondi chosasinthika ndi inu, monga analumbira kwa makolo anu. 13 Iye adzakukondani nakudalitsani ndi kukuchulukitsani. Adzadalitsa chipatso cha mʼmimba mwanu, zokolola za mʼdziko mwanu, tirigu wanu, vinyo wanu ndi mafuta anu, ana angʼombe zanu ndi ana ankhosa zanu mʼdziko limene analumbirira kwa makolo anu kuti akupatseni inu. 14 Inu mudzadalitsika kuposa mtundu wina uliwonse wa anthu ndipo palibe mwamuna kapena mkazi aliyense pakati panu amene adzakhale wosabereka. Ziweto zanu nazonso, sipadzapezeka zosabereka. 15 Yehova adzakupewetsani ku matenda aliwonse. Sadzakugwetserani matenda owopsa aja munawadziwa ku Igupto, koma adzawagwetsera pa odana nanu. 16 Muwononge anthu onse amene Yehova Mulungu wanu awapereka kwa inu. Musawamvere chisoni ndipo musatumikire milungu yawo pakuti umenewo udzakhala msampha kwa inu. 17 Mukhoza kunena kuti, “Anthu awa ndi amphamvu kuposa ifeyo. Nanga tingawapirikitse bwanji?” 18 Koma musachite nawo mantha, kumbukirani bwino zimene Yehova Mulungu wanu anachita ndi Farao pamodzi ndi Igupto yense. 19 Munadzionera nokha ndi maso anu mayesero aakulu, zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa, mphamvu yake yopanda malire imene Yehova Mulungu wanu anakutulutsirani. Yehova Mulungu adzachita zimenezo ndi anthu onse amene muwaopa tsopano. 20 Kuwonjezera apo, Yehova Mulungu wanu adzatumiza mavu pakati pawo mpaka atamaliza onse amene adzakubisalirani. 21 Musaopsedwe nawo pakuti Yehova Mulungu wanu, amene ali pakati panu, ndi Mulungu wamkulu ndi woopsa. 22 Yehova Mulungu wanu adzapirikitsa anthu a mitundu yonse pamaso panu, pangʼonopangʼono. Sadzakulolani kuti muwathe nthawi imodzi, kuti nyama zakuthengo zingadzaswane mokuzungulirani. 23 Koma Yehova Mulungu wanu adzawapereka kwa inu, adzawasokoneza kufikira atawonongedwa. 24 Iye adzapereka mafumu awo mʼdzanja lanu, ndipo adzafafaniza mayina awo pa dziko lapansi. Palibe amene adzalimbana nanu, inu mudzawawononga. 25 Muwawotche pa moto mafano a milungu yawo. Musasirire siliva ndi golide amene ali pa mafanoyo. Musamutenge kuti akhale wanu chifukwa mukatero mudzakodwa naye ngati msampha, pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa nazo. 26 Musabweretse chinthu chonyansa mʼnyumba mwanu kuopa kuwonongedwa ngati chonyasacho. Muziyipidwa ndi kunyansidwa nacho kwambiri pakuti chidzawonongedwanso.

In Other Versions

Deuteronomy 7 in the ANGEFD

Deuteronomy 7 in the ANTPNG2D

Deuteronomy 7 in the AS21

Deuteronomy 7 in the BAGH

Deuteronomy 7 in the BBPNG

Deuteronomy 7 in the BBT1E

Deuteronomy 7 in the BDS

Deuteronomy 7 in the BEV

Deuteronomy 7 in the BHAD

Deuteronomy 7 in the BIB

Deuteronomy 7 in the BLPT

Deuteronomy 7 in the BNT

Deuteronomy 7 in the BNTABOOT

Deuteronomy 7 in the BNTLV

Deuteronomy 7 in the BOATCB

Deuteronomy 7 in the BOATCB2

Deuteronomy 7 in the BOBCV

Deuteronomy 7 in the BOCNT

Deuteronomy 7 in the BOECS

Deuteronomy 7 in the BOHCB

Deuteronomy 7 in the BOHCV

Deuteronomy 7 in the BOHLNT

Deuteronomy 7 in the BOHNTLTAL

Deuteronomy 7 in the BOICB

Deuteronomy 7 in the BOILNTAP

Deuteronomy 7 in the BOITCV

Deuteronomy 7 in the BOKCV

Deuteronomy 7 in the BOKCV2

Deuteronomy 7 in the BOKHWOG

Deuteronomy 7 in the BOKSSV

Deuteronomy 7 in the BOLCB

Deuteronomy 7 in the BOLCB2

Deuteronomy 7 in the BOMCV

Deuteronomy 7 in the BONAV

Deuteronomy 7 in the BONCB

Deuteronomy 7 in the BONLT

Deuteronomy 7 in the BONUT2

Deuteronomy 7 in the BOPLNT

Deuteronomy 7 in the BOSCB

Deuteronomy 7 in the BOSNC

Deuteronomy 7 in the BOTLNT

Deuteronomy 7 in the BOVCB

Deuteronomy 7 in the BOYCB

Deuteronomy 7 in the BPBB

Deuteronomy 7 in the BPH

Deuteronomy 7 in the BSB

Deuteronomy 7 in the CCB

Deuteronomy 7 in the CUV

Deuteronomy 7 in the CUVS

Deuteronomy 7 in the DBT

Deuteronomy 7 in the DGDNT

Deuteronomy 7 in the DHNT

Deuteronomy 7 in the DNT

Deuteronomy 7 in the ELBE

Deuteronomy 7 in the EMTV

Deuteronomy 7 in the ESV

Deuteronomy 7 in the FBV

Deuteronomy 7 in the FEB

Deuteronomy 7 in the GGMNT

Deuteronomy 7 in the GNT

Deuteronomy 7 in the HARY

Deuteronomy 7 in the HNT

Deuteronomy 7 in the IRVA

Deuteronomy 7 in the IRVB

Deuteronomy 7 in the IRVG

Deuteronomy 7 in the IRVH

Deuteronomy 7 in the IRVK

Deuteronomy 7 in the IRVM

Deuteronomy 7 in the IRVM2

Deuteronomy 7 in the IRVO

Deuteronomy 7 in the IRVP

Deuteronomy 7 in the IRVT

Deuteronomy 7 in the IRVT2

Deuteronomy 7 in the IRVU

Deuteronomy 7 in the ISVN

Deuteronomy 7 in the JSNT

Deuteronomy 7 in the KAPI

Deuteronomy 7 in the KBT1ETNIK

Deuteronomy 7 in the KBV

Deuteronomy 7 in the KJV

Deuteronomy 7 in the KNFD

Deuteronomy 7 in the LBA

Deuteronomy 7 in the LBLA

Deuteronomy 7 in the LNT

Deuteronomy 7 in the LSV

Deuteronomy 7 in the MAAL

Deuteronomy 7 in the MBV

Deuteronomy 7 in the MBV2

Deuteronomy 7 in the MHNT

Deuteronomy 7 in the MKNFD

Deuteronomy 7 in the MNG

Deuteronomy 7 in the MNT

Deuteronomy 7 in the MNT2

Deuteronomy 7 in the MRS1T

Deuteronomy 7 in the NAA

Deuteronomy 7 in the NASB

Deuteronomy 7 in the NBLA

Deuteronomy 7 in the NBS

Deuteronomy 7 in the NBVTP

Deuteronomy 7 in the NET2

Deuteronomy 7 in the NIV11

Deuteronomy 7 in the NNT

Deuteronomy 7 in the NNT2

Deuteronomy 7 in the NNT3

Deuteronomy 7 in the PDDPT

Deuteronomy 7 in the PFNT

Deuteronomy 7 in the RMNT

Deuteronomy 7 in the SBIAS

Deuteronomy 7 in the SBIBS

Deuteronomy 7 in the SBIBS2

Deuteronomy 7 in the SBICS

Deuteronomy 7 in the SBIDS

Deuteronomy 7 in the SBIGS

Deuteronomy 7 in the SBIHS

Deuteronomy 7 in the SBIIS

Deuteronomy 7 in the SBIIS2

Deuteronomy 7 in the SBIIS3

Deuteronomy 7 in the SBIKS

Deuteronomy 7 in the SBIKS2

Deuteronomy 7 in the SBIMS

Deuteronomy 7 in the SBIOS

Deuteronomy 7 in the SBIPS

Deuteronomy 7 in the SBISS

Deuteronomy 7 in the SBITS

Deuteronomy 7 in the SBITS2

Deuteronomy 7 in the SBITS3

Deuteronomy 7 in the SBITS4

Deuteronomy 7 in the SBIUS

Deuteronomy 7 in the SBIVS

Deuteronomy 7 in the SBT

Deuteronomy 7 in the SBT1E

Deuteronomy 7 in the SCHL

Deuteronomy 7 in the SNT

Deuteronomy 7 in the SUSU

Deuteronomy 7 in the SUSU2

Deuteronomy 7 in the SYNO

Deuteronomy 7 in the TBIAOTANT

Deuteronomy 7 in the TBT1E

Deuteronomy 7 in the TBT1E2

Deuteronomy 7 in the TFTIP

Deuteronomy 7 in the TFTU

Deuteronomy 7 in the TGNTATF3T

Deuteronomy 7 in the THAI

Deuteronomy 7 in the TNFD

Deuteronomy 7 in the TNT

Deuteronomy 7 in the TNTIK

Deuteronomy 7 in the TNTIL

Deuteronomy 7 in the TNTIN

Deuteronomy 7 in the TNTIP

Deuteronomy 7 in the TNTIZ

Deuteronomy 7 in the TOMA

Deuteronomy 7 in the TTENT

Deuteronomy 7 in the UBG

Deuteronomy 7 in the UGV

Deuteronomy 7 in the UGV2

Deuteronomy 7 in the UGV3

Deuteronomy 7 in the VBL

Deuteronomy 7 in the VDCC

Deuteronomy 7 in the YALU

Deuteronomy 7 in the YAPE

Deuteronomy 7 in the YBVTP

Deuteronomy 7 in the ZBP