Esther 1 (BOGWICC)

1 Izi ndi zimene zinachitika pa nthawi ya ufumu wa Ahasiwero, amene analamulira zigawo 127 kuyambira ku India mpaka ku Kusi. 2 Pa nthawi imeneyi nʼkuti mfumu Ahasiwero atakhazikika pa mpando wake wa ufumu mu mzinda wa Susa, 3 ndipo mʼchaka chachitatu cha ufumu wake anakonza phwando la olemekezeka ndi nduna zake. Atsogoleri a nkhondo a ku Peresiya ndi Mediya, anthu olemekezeka pamodzi ndi nduna za mʼzigawo zonse anasonkhana kwa iye. 4 Pa nthawi yomweyi kwa masiku 180 a phwando mfumu inkaonetsa kulemera kwa ulemerero wa ufumu wake ndiponso kukongola ndi kukula kwa ufumu wake. 5 Atatha masiku amenewa, kwa masiku ena asanu ndi awiri mfumu inakonzanso phwando la anthu onse okhala mu mzinda wa Susa kuyambira anthu olemekezeka mpaka anthu wamba ku bwalo la munda la nyumba yake yaufumu. 6 Bwalo la mundali analikongoletsa ndi makatani a nsalu zoyera ndi za mtundu wamtambo zimene anazimangirira ndi zingwe za nsalu zoyera ndi zapepo ku mphete za siliva zimene anazikoloweka pa nsanamira za maburo. Anayika mipando yopumirapo yagolide ndi siliva pabwalo la miyala yoyala yamtengowapatali yofiira, ya marabulo, ndi yonyezimira. 7 Anapereka zakumwa mʼchikho zagolide zamitundumitundu, ndipo vinyo waufumu anali wochuluka kwambiri monga mwa kukoma mtima kwa mfumu. 8 Monga mwa lamulo la mfumu aliyense anamwa mʼmene anafunira, pakuti mfumu inawuza otumikira ake kuti apatse aliyense monga mwa kukonda kwake. 9 Mkazi wa mfumu Vasiti nayenso anakonzera phwando amayi ku nyumba ya ufumu ya mfumu Ahasiwero. 10 Pa tsiku la chisanu ndi chiwiri, pamene mfumu Ahasiwero inaledzera ndi vinyo, inalamula adindo ofulidwa asanu ndi awiri amene ankamutumikira: Mehumani, Bizita, Haribona, Bigita, Abagita, Zetara, ndi Karikasi 11 kuti abwere naye mfumukazi Vasiti pamaso pa mfumu atavala chipewa chaufumu. Cholinga cha mfumu chinali choti adzamuonetse kwa anthu onse ndi olemekezeka, chifukwa anali wokongola kwambiri. 12 Koma antchito atapereka uthenga wa mfumu kwa mfumukazi, Vasiti anakana kubwera. Tsono mfumu inakwiya ndi kupsa mtima. 13 Mfumu inayankhula ndi anthu anzeru ndi ozindikira choyenera kuchita popeza chinali chikhalidwe chake kufunsa uphungu kwa akatswiri pa nkhani za malamulo ndi kuweruza kolungama. 14 Anthu amene ankakhala pafupi ndi mfumu anali awa: Karisena, Setara, Adimata, Tarisisi, Meresi, Marisena ndi Memukani, olemekezeka asanu ndi awiri a ku Peresiya ndi Medina amene ankaloledwa mwapadera kuonana ndi mfumu ndipo anali pamwamba kwambiri mu ufumuwo. 15 Mfumu inafunsa kuti, “Kodi titani naye mfumukazi Vasiti mwa lamulo, popeza sanamvere lamulo la ine mfumu Ahasiwero limene adindo ofulidwa anakamuwuza?” 16 Ndipo Memukani anayankha pa maso pa mfumu ndi olemekezeka anzake kuti, “Mfumukazi Vasiti sanalakwire mfumu yokha, koma walakwiranso olemekezeka onse ndi anthu onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero. 17 Pakuti amayi onse adzadziwa zimene wachita mfumukazi ndipo kotero adzapeputsa amuna awo ndi kunena kuti, ‘Mfumu Ahasiwero analamulira kuti abwere naye mfumukazi Vasiti kwa iye koma sanapite.’ 18 Lero lomwe lino amayi olemekezeka a ku Peresiya ndi Mediya amene amva zimene wachita mfumukazi adzaganiza zochita chimodzimodzi kwa nduna zonse za mfumu. Ndipo kupeputsana ndi kukongola zidzapitirira.” 19 “Choncho, ngati chikukomerani mfumu, lamulirani kuti Vasiti asadzaonekerenso pamaso pa mfumu Ahasiwero. Lamuloli lilembedwe mʼmabuku a malamulo a Aperezi ndi Amedi kuti lisadzasinthike. Pamalo pa Vasiti ngati mfumukazi payikidwepo mkazi wina amene ali bwino kuposa iye. 20 Ndipo lamulo la mfumuli lilengezedwa mʼdziko lake lonse ngakhale lili lalikulu, amayi onse adzapereka ulemu kwa amuna awo, amuna olemekezeka mpaka amuna wamba.” 21 Mfumu ndi nduna zake anakondwera ndi uphungu uwu, kotero mfumu inachita monga momwe ananenera Memukani. 22 Mfumu inatumiza makalata ku madera onse a ufumu wake, chigawo chilichonse mʼzilembo zawo ndi ku mtundu uliwonse mʼchiyankhulo chawochawo kulengeza kuti mwamuna ayankhule chilichonse chimene chikumukomera.

In Other Versions

Esther 1 in the ANGEFD

Esther 1 in the ANTPNG2D

Esther 1 in the AS21

Esther 1 in the BAGH

Esther 1 in the BBPNG

Esther 1 in the BBT1E

Esther 1 in the BDS

Esther 1 in the BEV

Esther 1 in the BHAD

Esther 1 in the BIB

Esther 1 in the BLPT

Esther 1 in the BNT

Esther 1 in the BNTABOOT

Esther 1 in the BNTLV

Esther 1 in the BOATCB

Esther 1 in the BOATCB2

Esther 1 in the BOBCV

Esther 1 in the BOCNT

Esther 1 in the BOECS

Esther 1 in the BOHCB

Esther 1 in the BOHCV

Esther 1 in the BOHLNT

Esther 1 in the BOHNTLTAL

Esther 1 in the BOICB

Esther 1 in the BOILNTAP

Esther 1 in the BOITCV

Esther 1 in the BOKCV

Esther 1 in the BOKCV2

Esther 1 in the BOKHWOG

Esther 1 in the BOKSSV

Esther 1 in the BOLCB

Esther 1 in the BOLCB2

Esther 1 in the BOMCV

Esther 1 in the BONAV

Esther 1 in the BONCB

Esther 1 in the BONLT

Esther 1 in the BONUT2

Esther 1 in the BOPLNT

Esther 1 in the BOSCB

Esther 1 in the BOSNC

Esther 1 in the BOTLNT

Esther 1 in the BOVCB

Esther 1 in the BOYCB

Esther 1 in the BPBB

Esther 1 in the BPH

Esther 1 in the BSB

Esther 1 in the CCB

Esther 1 in the CUV

Esther 1 in the CUVS

Esther 1 in the DBT

Esther 1 in the DGDNT

Esther 1 in the DHNT

Esther 1 in the DNT

Esther 1 in the ELBE

Esther 1 in the EMTV

Esther 1 in the ESV

Esther 1 in the FBV

Esther 1 in the FEB

Esther 1 in the GGMNT

Esther 1 in the GNT

Esther 1 in the HARY

Esther 1 in the HNT

Esther 1 in the IRVA

Esther 1 in the IRVB

Esther 1 in the IRVG

Esther 1 in the IRVH

Esther 1 in the IRVK

Esther 1 in the IRVM

Esther 1 in the IRVM2

Esther 1 in the IRVO

Esther 1 in the IRVP

Esther 1 in the IRVT

Esther 1 in the IRVT2

Esther 1 in the IRVU

Esther 1 in the ISVN

Esther 1 in the JSNT

Esther 1 in the KAPI

Esther 1 in the KBT1ETNIK

Esther 1 in the KBV

Esther 1 in the KJV

Esther 1 in the KNFD

Esther 1 in the LBA

Esther 1 in the LBLA

Esther 1 in the LNT

Esther 1 in the LSV

Esther 1 in the MAAL

Esther 1 in the MBV

Esther 1 in the MBV2

Esther 1 in the MHNT

Esther 1 in the MKNFD

Esther 1 in the MNG

Esther 1 in the MNT

Esther 1 in the MNT2

Esther 1 in the MRS1T

Esther 1 in the NAA

Esther 1 in the NASB

Esther 1 in the NBLA

Esther 1 in the NBS

Esther 1 in the NBVTP

Esther 1 in the NET2

Esther 1 in the NIV11

Esther 1 in the NNT

Esther 1 in the NNT2

Esther 1 in the NNT3

Esther 1 in the PDDPT

Esther 1 in the PFNT

Esther 1 in the RMNT

Esther 1 in the SBIAS

Esther 1 in the SBIBS

Esther 1 in the SBIBS2

Esther 1 in the SBICS

Esther 1 in the SBIDS

Esther 1 in the SBIGS

Esther 1 in the SBIHS

Esther 1 in the SBIIS

Esther 1 in the SBIIS2

Esther 1 in the SBIIS3

Esther 1 in the SBIKS

Esther 1 in the SBIKS2

Esther 1 in the SBIMS

Esther 1 in the SBIOS

Esther 1 in the SBIPS

Esther 1 in the SBISS

Esther 1 in the SBITS

Esther 1 in the SBITS2

Esther 1 in the SBITS3

Esther 1 in the SBITS4

Esther 1 in the SBIUS

Esther 1 in the SBIVS

Esther 1 in the SBT

Esther 1 in the SBT1E

Esther 1 in the SCHL

Esther 1 in the SNT

Esther 1 in the SUSU

Esther 1 in the SUSU2

Esther 1 in the SYNO

Esther 1 in the TBIAOTANT

Esther 1 in the TBT1E

Esther 1 in the TBT1E2

Esther 1 in the TFTIP

Esther 1 in the TFTU

Esther 1 in the TGNTATF3T

Esther 1 in the THAI

Esther 1 in the TNFD

Esther 1 in the TNT

Esther 1 in the TNTIK

Esther 1 in the TNTIL

Esther 1 in the TNTIN

Esther 1 in the TNTIP

Esther 1 in the TNTIZ

Esther 1 in the TOMA

Esther 1 in the TTENT

Esther 1 in the UBG

Esther 1 in the UGV

Esther 1 in the UGV2

Esther 1 in the UGV3

Esther 1 in the VBL

Esther 1 in the VDCC

Esther 1 in the YALU

Esther 1 in the YAPE

Esther 1 in the YBVTP

Esther 1 in the ZBP