Exodus 21 (BOGWICC)

1 “Uwawuze Aisraeli malamulo awa: 2 “Mukagula kapolo wa Chihebri, azikugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi. Koma mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri muzimumasula, ndipo asalipire kanthu. 3 Ngati anabwera yekha, amasulidwenso yekha. Koma ngati anali ndi mkazi pamene ankabwera, mkaziyo apite nayenso. 4 Ngati bwana wake amupatsa mkazi ndipo mkaziyo anabereka ana aamuna kapena aakazi, mkazi ndi anawo adzakhala a bwanayo ndipo mwamuna yekhayo ndiye adzamasulidwe. 5 “Koma ngati kapoloyo alengeza kuti, ‘Ine sindikufuna kumasulidwa chifukwa ndimakonda mbuye wanga, mkazi wanga ndi ana,’ 6 mbuye wakeyo abwere naye kwa Yehova. Abwere naye pa chitseko kapena pa mphuthu zachitseko ndipo abowole khutu lake ndi chitsulo. Ndipo iye adzakhala kapolo wake moyo wake wonse. 7 “Ngati munthu agulitsa mwana wake wamkazi kukhala mdzakazi, mwanayo asamasulidwe monga achitira ndi akapolo aamuna. 8 Koma ngati mkaziyo sakukondweretsa bwana wake amene wamusankha kuti amukwatire, amulole kuti awomboledwe. Bwanayo alibe mphamvu zomugulitsa kwa anthu achilendo, chifukwa iyeyo waphwanya pangano lake lomukwatira iye. 9 Ngati anamusankha kuti akhale mkazi wa mwana wake, ayenera kumusunga ngati mwana wake wamkazi. 10 Ngati akwatira mkazi wina, asamumane woyambayo chakudya ngakhale chovala ndipo apiritirize kugona naye ngati mkazi wake. 11 Koma ngati sangathe kumuchitira zonsezi, ndiye amuleke apite popanda kulipira kanthu. 12 “Munthu aliyense amene amenya mnzake namupha, iyenso ayenera kuphedwa. 13 Koma ngati sanachite dala, ndipo Mulungu analola kuti zichitike, iyeyo athawire ku malo kumene ndidzakupatsani. 14 Koma ngati munthu akonza chiwembu ndi kupha mnzake mwadala, ameneyo muchotseni ngakhale ku guwa langa lansembe ndipo aphedwe. 15 “Munthu aliyense amene amenya abambo ake kapena mayi ake ayenera kuphedwa. 16 “Munthu aliyense amene aba munthu mnzake, ndi kukamugulitsa, kapena kumangomusunga, ayenera kuphedwa. 17 “Aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa. 18 “Ngati anthu awiri akangana ndipo wina amenya mnzake ndi mwala kapena nkhonya koma wosamupha, womenyedwayo akadwala nagona pa bedi, 19 kenaka nachira ndi kuyamba kuyenda ndi ndodo kutuluka kunja kwa nyumba yake, ndiye kuti womenya mnzakeyo sadzayimbidwa mlandu. Komabe adzayenera kulipira womenyedwayo chifukwa cha nthawi imene anagona pa bedi ija, ndiponso ayenera kumusala mpaka atachiritsitsa. 20 “Ngati munthu amenya kapolo wake wamwamuna kapena mdzakazi ndi ndodo, kapolo uja ndikufa chifukwa cha kumenyedwako, munthuyo ayenera kulangidwa. 21 Koma ngati kapolo uja akhala ndi moyo tsiku lonse kapena masiku awiri, ndiye kuti mbuye uja asalangidwe chifukwa kapolo ndi chuma chake. 22 “Ngati anthu akumenyana ndi kupweteka mayi woyembekezera, mayiyo napita padera, koma osavulala, wolakwayo ayenera kulipira chilichonse chimene mwamuna wake wa mkaziyo adzalamula ndipo bwalo lamilandu lavomereza. 23 Koma ngati wavulazidwa kwambiri, ndiye malipiro ake adzakhala motere: moyo kulipa moyo, 24 diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, mkono kulipa mkono, phazi kulipa phazi. 25 Kutentha ndi moto kulipa kutentha ndi moto, bala kulipa bala, mkwingwirima kulipa mkwingwirima. 26 “Ngati munthu amenya wantchito wake wa mwamuna kapena mdzakazi wake pa diso ndi kuliwononga, wantchitoyo amasulidwe ngati malipiro a diso lake. 27 Ndipo ngati agulula dzino la wantchito wamwamuna kapena mdzakazi, wantchitoyo amasulidwe ngati malipiro a dzino lake. 28 “Ngati ngʼombe ipha munthu wamwamuna kapena wamkazi ndi nyanga yake, iponyedwe miyala ndipo nyama yake isadyedwe. Ndipo mwini ngʼombeyo asayimbidwe mlandu. 29 Koma ngati ngʼombeyo inali ndi chizolowezi chogunda anthu ndipo mwini wakeyo anachenjezedwa koma iye sanayimange ndipo yapha mwamuna kapena mkazi, ngʼombeyo iponyedwe miyala ndipo mwini wakeyo aphedwenso. 30 Koma ngati wauzidwa kuti alipire, iye apereke zimene wauzidwazo kuti awombole moyo wake. 31 Lamulo ili ligwirenso ntchito ngati ngʼombeyo yagunda mwana wamwamuna kapena wamkazi. 32 Ngati ngʼombeyo yagunda kapolo wamwamuna kapena mdzakazi, mwini ngʼombeyo apereke masekeli makumi atatu a siliva kwa mwini kapoloyo, ndipo ngʼombeyo iponyedwe miyala. 33 “Munthu akasiya dzenje lapululu kapena akakumba dzenje koma wosaphimbapo, ndipo ngʼombe kapena bulu nʼkugweramo, 34 mwini dzenjelo amulipire mwini chiweto chakufacho koma iye atenge chiwetocho. 35 “Ngati ngʼombe ya munthu wina ipha ngʼombe ya mnzake, ngʼombe yamoyo ija igulitsidwe ndipo anthu awiriwo agawane pakati ndalama yake. Achite chimodzimodzi ndi ngʼombe yakufa ija. 36 Koma zikadziwika kuti ngʼombeyo inali ndi khalidwe logunda, ndipo mwini wake samayitsekera mʼkhola, mwini ngʼombeyo alipire ngʼombe ina yamoyo koma atenge yakufayo.”

In Other Versions

Exodus 21 in the ANGEFD

Exodus 21 in the ANTPNG2D

Exodus 21 in the AS21

Exodus 21 in the BAGH

Exodus 21 in the BBPNG

Exodus 21 in the BBT1E

Exodus 21 in the BDS

Exodus 21 in the BEV

Exodus 21 in the BHAD

Exodus 21 in the BIB

Exodus 21 in the BLPT

Exodus 21 in the BNT

Exodus 21 in the BNTABOOT

Exodus 21 in the BNTLV

Exodus 21 in the BOATCB

Exodus 21 in the BOATCB2

Exodus 21 in the BOBCV

Exodus 21 in the BOCNT

Exodus 21 in the BOECS

Exodus 21 in the BOHCB

Exodus 21 in the BOHCV

Exodus 21 in the BOHLNT

Exodus 21 in the BOHNTLTAL

Exodus 21 in the BOICB

Exodus 21 in the BOILNTAP

Exodus 21 in the BOITCV

Exodus 21 in the BOKCV

Exodus 21 in the BOKCV2

Exodus 21 in the BOKHWOG

Exodus 21 in the BOKSSV

Exodus 21 in the BOLCB

Exodus 21 in the BOLCB2

Exodus 21 in the BOMCV

Exodus 21 in the BONAV

Exodus 21 in the BONCB

Exodus 21 in the BONLT

Exodus 21 in the BONUT2

Exodus 21 in the BOPLNT

Exodus 21 in the BOSCB

Exodus 21 in the BOSNC

Exodus 21 in the BOTLNT

Exodus 21 in the BOVCB

Exodus 21 in the BOYCB

Exodus 21 in the BPBB

Exodus 21 in the BPH

Exodus 21 in the BSB

Exodus 21 in the CCB

Exodus 21 in the CUV

Exodus 21 in the CUVS

Exodus 21 in the DBT

Exodus 21 in the DGDNT

Exodus 21 in the DHNT

Exodus 21 in the DNT

Exodus 21 in the ELBE

Exodus 21 in the EMTV

Exodus 21 in the ESV

Exodus 21 in the FBV

Exodus 21 in the FEB

Exodus 21 in the GGMNT

Exodus 21 in the GNT

Exodus 21 in the HARY

Exodus 21 in the HNT

Exodus 21 in the IRVA

Exodus 21 in the IRVB

Exodus 21 in the IRVG

Exodus 21 in the IRVH

Exodus 21 in the IRVK

Exodus 21 in the IRVM

Exodus 21 in the IRVM2

Exodus 21 in the IRVO

Exodus 21 in the IRVP

Exodus 21 in the IRVT

Exodus 21 in the IRVT2

Exodus 21 in the IRVU

Exodus 21 in the ISVN

Exodus 21 in the JSNT

Exodus 21 in the KAPI

Exodus 21 in the KBT1ETNIK

Exodus 21 in the KBV

Exodus 21 in the KJV

Exodus 21 in the KNFD

Exodus 21 in the LBA

Exodus 21 in the LBLA

Exodus 21 in the LNT

Exodus 21 in the LSV

Exodus 21 in the MAAL

Exodus 21 in the MBV

Exodus 21 in the MBV2

Exodus 21 in the MHNT

Exodus 21 in the MKNFD

Exodus 21 in the MNG

Exodus 21 in the MNT

Exodus 21 in the MNT2

Exodus 21 in the MRS1T

Exodus 21 in the NAA

Exodus 21 in the NASB

Exodus 21 in the NBLA

Exodus 21 in the NBS

Exodus 21 in the NBVTP

Exodus 21 in the NET2

Exodus 21 in the NIV11

Exodus 21 in the NNT

Exodus 21 in the NNT2

Exodus 21 in the NNT3

Exodus 21 in the PDDPT

Exodus 21 in the PFNT

Exodus 21 in the RMNT

Exodus 21 in the SBIAS

Exodus 21 in the SBIBS

Exodus 21 in the SBIBS2

Exodus 21 in the SBICS

Exodus 21 in the SBIDS

Exodus 21 in the SBIGS

Exodus 21 in the SBIHS

Exodus 21 in the SBIIS

Exodus 21 in the SBIIS2

Exodus 21 in the SBIIS3

Exodus 21 in the SBIKS

Exodus 21 in the SBIKS2

Exodus 21 in the SBIMS

Exodus 21 in the SBIOS

Exodus 21 in the SBIPS

Exodus 21 in the SBISS

Exodus 21 in the SBITS

Exodus 21 in the SBITS2

Exodus 21 in the SBITS3

Exodus 21 in the SBITS4

Exodus 21 in the SBIUS

Exodus 21 in the SBIVS

Exodus 21 in the SBT

Exodus 21 in the SBT1E

Exodus 21 in the SCHL

Exodus 21 in the SNT

Exodus 21 in the SUSU

Exodus 21 in the SUSU2

Exodus 21 in the SYNO

Exodus 21 in the TBIAOTANT

Exodus 21 in the TBT1E

Exodus 21 in the TBT1E2

Exodus 21 in the TFTIP

Exodus 21 in the TFTU

Exodus 21 in the TGNTATF3T

Exodus 21 in the THAI

Exodus 21 in the TNFD

Exodus 21 in the TNT

Exodus 21 in the TNTIK

Exodus 21 in the TNTIL

Exodus 21 in the TNTIN

Exodus 21 in the TNTIP

Exodus 21 in the TNTIZ

Exodus 21 in the TOMA

Exodus 21 in the TTENT

Exodus 21 in the UBG

Exodus 21 in the UGV

Exodus 21 in the UGV2

Exodus 21 in the UGV3

Exodus 21 in the VBL

Exodus 21 in the VDCC

Exodus 21 in the YALU

Exodus 21 in the YAPE

Exodus 21 in the YBVTP

Exodus 21 in the ZBP