Exodus 34 (BOGWICC)

1 Yehova anati kwa Mose, “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo Ine ndidzalembapo mawu amene anali pa miyala yoyamba ija, imene unayiphwanya. 2 Ukonzeke mmamawa, ndipo ubwere ku Phiri la Sinai. Udzaonekera pamaso panga pamwamba pa phiri. 3 Palibe amene abwere nawe kapena kuoneka pena paliponse pafupi ndi phiri. Ndipo ngakhale nkhosa kapena ngʼombe zisadye mʼmbali mwa phirilo.” 4 Choncho Mose anasema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija ndipo anapita ku Phiri la Sinai mmawa atanyamula miyala iwiri mʼmanja mwake monga momwe Yehova anamulamulira. 5 Ndipo Yehova anatsika mu mtambo ndi kuyima pamodzi ndi Mose ndi kulengeza dzina lake lakuti Yehova. 6 Ndipo Iye anadutsa kutsogolo kwa Mose akulengeza kuti, “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosapsa mtima msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika, 7 waonetsa chikondi chosasinthika kwa anthu miyandamiyanda, wokhululukira zoyipa, kuwukira, ndiponso tchimo, komatu salekerera ochimwa kuti asalangidwe. Iye amalanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha machimo a makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi.” 8 Pamenepo Mose anawerama pansi napembedza. 9 Iye anati, “Chonde Ambuye, ngati ndapeza chisomo pamaso panu, lolani Ambuye kuti mupite nafe pamodzi. Ngakhale kuti anthuwa ndi nkhutukumve, khululukirani zoyipa ndi machimo athu, ndipo mutenge ife kukhala anthu anu.” 10 Choncho Yehova anati: “Ine ndikuchita nanu pangano. Ndidzachita zodabwitsa pamaso pa anthu onse zimene sizinachitikenso ndi mtundu wina uliwonse wa anthu pa dziko lonse lapansi. Anthu amene mudzakhala pakati pawo adzaona kuopsa kwa ntchito imene Ine Yehova ndidzakuchitireni. 11 Mverani zimene ndikukulamulirani lero. Ine ndidzathamangitsa pamaso panu Aamori, Akanaani, Ahiti, Aperezi, Ahivi, ndi Ayebusi. 12 Musamale kuti musakachite mgwirizano ndi anthu amene akukhala mʼdziko limene mukupitalo, chifukwa mukadzatero iwo adzakhala ngati msampha pakati panu. 13 Mukagumule maguwa awo ansembe, mukaswe miyala yawo yachipembedzo, ndipo mukadule mitengo yawo ya Asera. 14 Musapembedze mulungu wina, pakuti Yehova amene dzina lake ndi Nsanje, ndi Mulungu wa nsanje. 15 “Musamale kuti musakachite mgwirizano ndi anthu amene akukhala mʼdziko limene mukupitalo, chifukwa iwo akamakachita zadama ndi milungu yawo ndi kupereka nsembe, adzakuyitanani ndipo inu mudzadya nsembe zawo. 16 Ndipo inu mukasankha ena mwa ana awo aakazi kukhala akazi a ana anu, akaziwo akakachita zadama ndi milungu yawo, akatsogolera ana anu aamuna kuchita chimodzimodzi. 17 “Musadzipangire milungu yosungunula. 18 “Muzichita chikondwerero cha buledi wopanda yisiti. Kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti monga momwe ndinakulamulirani. Muzichita zimenezi pa nthawi yoyikika mwezi wa Abibu, pakuti mwezi umenewu inu munatuluka mʼdziko la Igupto. 19 “Mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga, pamodzi ndi ziweto zoyamba kubadwa zazimuna kuchokera ku ngʼombe kapena nkhosa. 20 Muziwombola mwana woyamba kubadwa wa bulu popereka mwana wankhosa. Mukapanda kumuwombola mupheni. Muziwombola ana anu onse aamuna.“Palibe ndi mmodzi yemwe adzaonekere pamaso panga wopanda kanthu mʼdzanja lake. 21 “Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri, musagwire ntchito ina iliyonse, Ngakhale nthawi yolima ndi yokolola muyenera kupuma. 22 “Muzichita Chikondwerero cha Masabata, chifukwa ndi chikondwerero cha tirigu woyambirira kucha, ndiponso ndi chikondwerero cha kututa zokolola pakutha pa chaka. 23 Amuna onse azionekera pamaso pa Yehova Mulungu wa Israeli, katatu pa chaka. 24 Ine ndidzapirikitsa mitundu inayo pamene inu mukufikako ndi kukulitsa malire anu. Palibe ndi mmodzi yemwe adzafune kulanda dziko lanu ngati inu muzidzapita katatu pa chaka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, chaka chilichonse. 25 “Musapereke magazi anyama ngati nsembe kwa Ine pamodzi ndi chilichonse chimene chili ndi yisiti, ndipo musasunge nsembe ya pa Chikondwerero cha Paska mpaka mmawa. 26 “Muzibwera ndi zipatso zoyambirira kucha zabwino kwambiri ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu.“Musamaphike kamwana kambuzi mu mkaka wa mayi wake.” 27 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Lemba mawu awa pakuti potsatira mawuwa, ine ndipangana pangano ndi iwe ndi Israeli.” 28 Mose anakhala kumeneko pamodzi ndi Yehova masiku 40, usana ndi usiku, wosadya kanthu kapena kumwa madzi. Ndipo iye analemba pa miyala ija mawu a pangano, malamulo khumi. 29 Mose anatsika kuchokera mʼPhiri la Sinai pamodzi ndi miyala iwiri ija ya pangano mʼmanja mwake. Iye sanazindikire kuti nkhope yake imanyezimira pakuti anayankhula ndi Yehova. 30 Aaroni ndi Aisraeli ataona kuti nkhope ya Mose imanyezimira anaopa kumuyandikira. 31 Koma Mose anawayitana. Kotero Aaroni ndi atsogoleri onse a gululo anabwera kwa iye, ndipo anawayankhula. 32 Kenaka Aisraeli onse anamuyandikira, ndipo anawapatsa malamulo onse omwe Yehova anamupatsa pa Phiri la Sinai. 33 Mose atamaliza kuyankhula nawo anaphimba nkhope yake. 34 Koma nthawi zonse popita pamaso pa Yehova kukayankhula naye amachotsa chophimbacho mpaka atatuluka. Ndipo akatuluka kudzawuza Aisraeli zimene walamulidwa, 35 iwo amaona nkhope yake ikunyezimira. Choncho Mose amaphimba nkhope yake ngakhale pamene amapita kukayankhula ndi Yehova.

In Other Versions

Exodus 34 in the ANGEFD

Exodus 34 in the ANTPNG2D

Exodus 34 in the AS21

Exodus 34 in the BAGH

Exodus 34 in the BBPNG

Exodus 34 in the BBT1E

Exodus 34 in the BDS

Exodus 34 in the BEV

Exodus 34 in the BHAD

Exodus 34 in the BIB

Exodus 34 in the BLPT

Exodus 34 in the BNT

Exodus 34 in the BNTABOOT

Exodus 34 in the BNTLV

Exodus 34 in the BOATCB

Exodus 34 in the BOATCB2

Exodus 34 in the BOBCV

Exodus 34 in the BOCNT

Exodus 34 in the BOECS

Exodus 34 in the BOHCB

Exodus 34 in the BOHCV

Exodus 34 in the BOHLNT

Exodus 34 in the BOHNTLTAL

Exodus 34 in the BOICB

Exodus 34 in the BOILNTAP

Exodus 34 in the BOITCV

Exodus 34 in the BOKCV

Exodus 34 in the BOKCV2

Exodus 34 in the BOKHWOG

Exodus 34 in the BOKSSV

Exodus 34 in the BOLCB

Exodus 34 in the BOLCB2

Exodus 34 in the BOMCV

Exodus 34 in the BONAV

Exodus 34 in the BONCB

Exodus 34 in the BONLT

Exodus 34 in the BONUT2

Exodus 34 in the BOPLNT

Exodus 34 in the BOSCB

Exodus 34 in the BOSNC

Exodus 34 in the BOTLNT

Exodus 34 in the BOVCB

Exodus 34 in the BOYCB

Exodus 34 in the BPBB

Exodus 34 in the BPH

Exodus 34 in the BSB

Exodus 34 in the CCB

Exodus 34 in the CUV

Exodus 34 in the CUVS

Exodus 34 in the DBT

Exodus 34 in the DGDNT

Exodus 34 in the DHNT

Exodus 34 in the DNT

Exodus 34 in the ELBE

Exodus 34 in the EMTV

Exodus 34 in the ESV

Exodus 34 in the FBV

Exodus 34 in the FEB

Exodus 34 in the GGMNT

Exodus 34 in the GNT

Exodus 34 in the HARY

Exodus 34 in the HNT

Exodus 34 in the IRVA

Exodus 34 in the IRVB

Exodus 34 in the IRVG

Exodus 34 in the IRVH

Exodus 34 in the IRVK

Exodus 34 in the IRVM

Exodus 34 in the IRVM2

Exodus 34 in the IRVO

Exodus 34 in the IRVP

Exodus 34 in the IRVT

Exodus 34 in the IRVT2

Exodus 34 in the IRVU

Exodus 34 in the ISVN

Exodus 34 in the JSNT

Exodus 34 in the KAPI

Exodus 34 in the KBT1ETNIK

Exodus 34 in the KBV

Exodus 34 in the KJV

Exodus 34 in the KNFD

Exodus 34 in the LBA

Exodus 34 in the LBLA

Exodus 34 in the LNT

Exodus 34 in the LSV

Exodus 34 in the MAAL

Exodus 34 in the MBV

Exodus 34 in the MBV2

Exodus 34 in the MHNT

Exodus 34 in the MKNFD

Exodus 34 in the MNG

Exodus 34 in the MNT

Exodus 34 in the MNT2

Exodus 34 in the MRS1T

Exodus 34 in the NAA

Exodus 34 in the NASB

Exodus 34 in the NBLA

Exodus 34 in the NBS

Exodus 34 in the NBVTP

Exodus 34 in the NET2

Exodus 34 in the NIV11

Exodus 34 in the NNT

Exodus 34 in the NNT2

Exodus 34 in the NNT3

Exodus 34 in the PDDPT

Exodus 34 in the PFNT

Exodus 34 in the RMNT

Exodus 34 in the SBIAS

Exodus 34 in the SBIBS

Exodus 34 in the SBIBS2

Exodus 34 in the SBICS

Exodus 34 in the SBIDS

Exodus 34 in the SBIGS

Exodus 34 in the SBIHS

Exodus 34 in the SBIIS

Exodus 34 in the SBIIS2

Exodus 34 in the SBIIS3

Exodus 34 in the SBIKS

Exodus 34 in the SBIKS2

Exodus 34 in the SBIMS

Exodus 34 in the SBIOS

Exodus 34 in the SBIPS

Exodus 34 in the SBISS

Exodus 34 in the SBITS

Exodus 34 in the SBITS2

Exodus 34 in the SBITS3

Exodus 34 in the SBITS4

Exodus 34 in the SBIUS

Exodus 34 in the SBIVS

Exodus 34 in the SBT

Exodus 34 in the SBT1E

Exodus 34 in the SCHL

Exodus 34 in the SNT

Exodus 34 in the SUSU

Exodus 34 in the SUSU2

Exodus 34 in the SYNO

Exodus 34 in the TBIAOTANT

Exodus 34 in the TBT1E

Exodus 34 in the TBT1E2

Exodus 34 in the TFTIP

Exodus 34 in the TFTU

Exodus 34 in the TGNTATF3T

Exodus 34 in the THAI

Exodus 34 in the TNFD

Exodus 34 in the TNT

Exodus 34 in the TNTIK

Exodus 34 in the TNTIL

Exodus 34 in the TNTIN

Exodus 34 in the TNTIP

Exodus 34 in the TNTIZ

Exodus 34 in the TOMA

Exodus 34 in the TTENT

Exodus 34 in the UBG

Exodus 34 in the UGV

Exodus 34 in the UGV2

Exodus 34 in the UGV3

Exodus 34 in the VBL

Exodus 34 in the VDCC

Exodus 34 in the YALU

Exodus 34 in the YAPE

Exodus 34 in the YBVTP

Exodus 34 in the ZBP