Exodus 4 (BOGWICC)

1 Mose anayankha, “Aisraeliwo sakandikhulupirira ndipo sakandimvera. Iwowo adzati, ‘Yehova sanakuonekere iwe.’ ” 2 Ndipo Yehova anamufunsa nati, “Nʼchiyani chili mʼdzanja lakolo?”Mose anayankha kuti, “Ndodo.” 3 Yehova anati, “Tayiponya pansi.”Mose anayiponya pansi ndipo inasanduka njoka ndipo anayithawa. 4 Kenaka Yehova anati kwa iye, “Igwire mtchira.” Ndipo Mose anayigwira mchira njokayo ndipo inasandukanso ndodo mʼdzanja lake. 5 Yehova anati, “Ukachite zimenezi ndipo akakukhulupirira kuti Yehova, Mulungu wa makolo awo, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo, wakuonekera iwe.” 6 Yehova anatinso, “Pisa dzanja lako mʼmalaya akowo.” Choncho Mose anapisa dzanja lake mʼmalaya ake ndipo pamene analitulutsa, linali la khate kuchita kuti mbuu ngati ufa. 7 Yehova anati, “Tsopano pisanso dzanja lako mʼmalaya.” Mose anapisanso dzanja lakelo mʼmalaya ake ndipo atalitulutsa, linali labwinobwino, ngati thupi lake lonse. 8 Tsono Yehova anati “Akakapanda kukukhulupirira, osalabadira chozizwitsa choyambacho, akakhulupirira ndithu chifukwa cha chozizwitsa chachiwiricho. 9 Koma ngati sakakhulupirira zizindikiro ziwiri izi kapena kukumvera, ukatunge madzi a mu mtsinje wa Nailo ndi kuwathira pa mtunda powuma ndipo madziwo adzasanduka magazi.” 10 Mose anati kwa Yehova, “Chonde Ambuye, chikhalire ine ndakhala munthu wosatha kuyankhula bwino. Ngakhale tsopano pamene mukundiyankhula, lilime langa ndi lolemera. Ndine wachibwibwi.” 11 Yehova anati kwa iye, “Kodi anapatsa munthu pakamwa ndani? Ndani amasandutsa munthu kuti akhale wosayankhula kapena wosamva? Ndani amapanga munthu kukhala wopenya kapena wosaona? Kodi si Ine Yehova? 12 Tsopano pita, Ine ndidzakuthandiza kuyankhula ndipo ndidzakulangiza zoti ukanene.” 13 Koma Mose anati, “Chonde Ambuye, pepani, tumani wina kuti akachite zimenezi.” 14 Kenaka Yehova anamupsera mtima Mose ndipo anati, “Kodi suli ndi mʼbale wako Aaroni wa fuko la Levi? Ine ndikudziwa kuti iye amayankhula bwino. Iye wanyamuka kale kudzakumana nawe ndipo adzasangalala akadzakuona. 15 Iwe udzayankhula naye ndi kumuwuza mawu oti akanene. Ine ndidzakuthandizani kuyankhula nonse awirinu ndi kukulangizani zoti mukachite. 16 Iye akayankhula kwa anthu mʼmalo mwako. Iye adzakhala wokuyankhulira ndipo iweyo udzakhala ngati Mulungu kwa iye. 17 Koma utenge ndodo imene ili mʼdzanja lakoyo kuti ukachite nayo zizindikiro zozizwitsa.” 18 Tsono Mose anabwerera kwa Yetero, mpongozi wake ndipo anati kwa Iye, “Chonde ndiloleni kuti ndibwerere ku Igupto kwa anthu anga kuti ndikaone ngati ali moyo.”Yeteri anati, “Pitani mu mtendere.” 19 Nthawiyi Yehova anali atamuwuza kale Mose ku Midiyani kuti, “Bwerera ku Igupto, pakuti anthu onse amene amafuna kukupha aja anamwalira.” 20 Kotero Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, ndipo anawakweza pa bulu nayamba ulendo wobwerera ku Igupto. Ndipo anatenga ndodo ya Mulungu ija mʼdzanja lake. 21 Yehova anati kwa Mose, “Ukaonetsetse kuti wachita pamaso pa Farao zodabwitsa zonse zimene ndayika mphamvu mwa iwe kuti ukachite. Koma Ine ndidzawumitsa mtima wake kotero kuti sadzalola anthuwo kuti apite. 22 Ndipo iwe ukati kwa Farao, ‘Yehova akuti, Israeli ali ngati mwana wanga wachisamba.’ 23 Choncho ndikuti, ‘Mulole mwana wanga apite kuti akandipembedze. Koma ngati ukana, Ine ndidzapha mwana wako wachisamba.’ ” 24 Pambuyo pake Mose ali mʼnjira, pamalo wogona, Yehova anakumana naye, ndipo anafuna kumupha. 25 Koma Zipora anatenga mwala wakuthwa nachita mdulidwe mwana wake ndipo khungulo analikhudzitsa pa mapazi a Mose. Iye anati “Zoonadi, kwa ine ndiwe mkwati wamagazi.” 26 Choncho Yehova anamuleka Mose wosamupha. Pa nthawiyo, Zipora anati, “Mkwati wa magazi,” ponena za mdulidwe. 27 Yehova anati kwa Aaroni, “Pita ku chipululu ukakumane ndi Mose.” Iye anapitadi nakakumana ndi Mose pa phiri la Mulungu namupsompsona. 28 Kenaka Mose anamufotokozera Aaroni chilichonse chimene Yehova anamutuma kuti akanene. Anamufotokozera za zizindikiro zozizwitsa zimene anamulamulira kuti akazichite. 29 Mose ndi Aaroni anapita kukasonkhanitsa pamodzi akuluakulu onse a Aisraeli. 30 Ndipo Aaroni anawafotokozera zonse zimene Yehova ananena kwa Mose. Anachita zizindikirozo pamaso pa anthu onse, 31 ndipo anakhulupirira. Iwo atamva kuti Yehova anadzawayendera ndi kuti waona mmene akuzunzikira, anaweramitsa mitu pansi napembedza.

In Other Versions

Exodus 4 in the ANGEFD

Exodus 4 in the ANTPNG2D

Exodus 4 in the AS21

Exodus 4 in the BAGH

Exodus 4 in the BBPNG

Exodus 4 in the BBT1E

Exodus 4 in the BDS

Exodus 4 in the BEV

Exodus 4 in the BHAD

Exodus 4 in the BIB

Exodus 4 in the BLPT

Exodus 4 in the BNT

Exodus 4 in the BNTABOOT

Exodus 4 in the BNTLV

Exodus 4 in the BOATCB

Exodus 4 in the BOATCB2

Exodus 4 in the BOBCV

Exodus 4 in the BOCNT

Exodus 4 in the BOECS

Exodus 4 in the BOHCB

Exodus 4 in the BOHCV

Exodus 4 in the BOHLNT

Exodus 4 in the BOHNTLTAL

Exodus 4 in the BOICB

Exodus 4 in the BOILNTAP

Exodus 4 in the BOITCV

Exodus 4 in the BOKCV

Exodus 4 in the BOKCV2

Exodus 4 in the BOKHWOG

Exodus 4 in the BOKSSV

Exodus 4 in the BOLCB

Exodus 4 in the BOLCB2

Exodus 4 in the BOMCV

Exodus 4 in the BONAV

Exodus 4 in the BONCB

Exodus 4 in the BONLT

Exodus 4 in the BONUT2

Exodus 4 in the BOPLNT

Exodus 4 in the BOSCB

Exodus 4 in the BOSNC

Exodus 4 in the BOTLNT

Exodus 4 in the BOVCB

Exodus 4 in the BOYCB

Exodus 4 in the BPBB

Exodus 4 in the BPH

Exodus 4 in the BSB

Exodus 4 in the CCB

Exodus 4 in the CUV

Exodus 4 in the CUVS

Exodus 4 in the DBT

Exodus 4 in the DGDNT

Exodus 4 in the DHNT

Exodus 4 in the DNT

Exodus 4 in the ELBE

Exodus 4 in the EMTV

Exodus 4 in the ESV

Exodus 4 in the FBV

Exodus 4 in the FEB

Exodus 4 in the GGMNT

Exodus 4 in the GNT

Exodus 4 in the HARY

Exodus 4 in the HNT

Exodus 4 in the IRVA

Exodus 4 in the IRVB

Exodus 4 in the IRVG

Exodus 4 in the IRVH

Exodus 4 in the IRVK

Exodus 4 in the IRVM

Exodus 4 in the IRVM2

Exodus 4 in the IRVO

Exodus 4 in the IRVP

Exodus 4 in the IRVT

Exodus 4 in the IRVT2

Exodus 4 in the IRVU

Exodus 4 in the ISVN

Exodus 4 in the JSNT

Exodus 4 in the KAPI

Exodus 4 in the KBT1ETNIK

Exodus 4 in the KBV

Exodus 4 in the KJV

Exodus 4 in the KNFD

Exodus 4 in the LBA

Exodus 4 in the LBLA

Exodus 4 in the LNT

Exodus 4 in the LSV

Exodus 4 in the MAAL

Exodus 4 in the MBV

Exodus 4 in the MBV2

Exodus 4 in the MHNT

Exodus 4 in the MKNFD

Exodus 4 in the MNG

Exodus 4 in the MNT

Exodus 4 in the MNT2

Exodus 4 in the MRS1T

Exodus 4 in the NAA

Exodus 4 in the NASB

Exodus 4 in the NBLA

Exodus 4 in the NBS

Exodus 4 in the NBVTP

Exodus 4 in the NET2

Exodus 4 in the NIV11

Exodus 4 in the NNT

Exodus 4 in the NNT2

Exodus 4 in the NNT3

Exodus 4 in the PDDPT

Exodus 4 in the PFNT

Exodus 4 in the RMNT

Exodus 4 in the SBIAS

Exodus 4 in the SBIBS

Exodus 4 in the SBIBS2

Exodus 4 in the SBICS

Exodus 4 in the SBIDS

Exodus 4 in the SBIGS

Exodus 4 in the SBIHS

Exodus 4 in the SBIIS

Exodus 4 in the SBIIS2

Exodus 4 in the SBIIS3

Exodus 4 in the SBIKS

Exodus 4 in the SBIKS2

Exodus 4 in the SBIMS

Exodus 4 in the SBIOS

Exodus 4 in the SBIPS

Exodus 4 in the SBISS

Exodus 4 in the SBITS

Exodus 4 in the SBITS2

Exodus 4 in the SBITS3

Exodus 4 in the SBITS4

Exodus 4 in the SBIUS

Exodus 4 in the SBIVS

Exodus 4 in the SBT

Exodus 4 in the SBT1E

Exodus 4 in the SCHL

Exodus 4 in the SNT

Exodus 4 in the SUSU

Exodus 4 in the SUSU2

Exodus 4 in the SYNO

Exodus 4 in the TBIAOTANT

Exodus 4 in the TBT1E

Exodus 4 in the TBT1E2

Exodus 4 in the TFTIP

Exodus 4 in the TFTU

Exodus 4 in the TGNTATF3T

Exodus 4 in the THAI

Exodus 4 in the TNFD

Exodus 4 in the TNT

Exodus 4 in the TNTIK

Exodus 4 in the TNTIL

Exodus 4 in the TNTIN

Exodus 4 in the TNTIP

Exodus 4 in the TNTIZ

Exodus 4 in the TOMA

Exodus 4 in the TTENT

Exodus 4 in the UBG

Exodus 4 in the UGV

Exodus 4 in the UGV2

Exodus 4 in the UGV3

Exodus 4 in the VBL

Exodus 4 in the VDCC

Exodus 4 in the YALU

Exodus 4 in the YAPE

Exodus 4 in the YBVTP

Exodus 4 in the ZBP