Ezra 6 (BOGWICC)

1 Atalandira mawuwo mfumu Dariyo anapereka lamulo ndipo kafukufuku anachitikadi ku Babuloni mʼnyumba yosungira chuma ndi mabuku ambiri yakale. 2 Ndipo ku Ekibatana, likulu la dera la Mediya, kunapezeka mpukutu mmene munalembedwa kuti,Chikumbutso: 3 Mʼchaka choyamba cha ufumu wa Koresi, mfumuyo inapereka lamulo lokhudza Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu. Analamula kuti Nyumba ya Mulungu imangidwenso kukhala malo woperekerako nsembe. Maziko ake amangidwe kolimba pa malo pomwe paja pali maziko ake akale ndipo mulitali mwake mukhale mamita 27, mulifupi mwake mukhale mamita 27. 4 Mumange mizere itatu ya miyala yayikulu ndi mzere umodzi wa matabwa, ndalama zake zolipirira ntchitoyo zichokere mʼthumba la ufumu. 5 Ndipo ziwiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara anatenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu kupita nazo ku Babuloni, zonsezi zibwezedwe ndipo zipite ku Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Chilichonse chikabwezedwe pamalo pake mʼNyumbayo. 6 Tsopano Tatenai, bwanamkubwa wa dera la Patsidya pa Yufurate ndiponso Setari-Bozenai pamodzi ndi anzanu muchokeko kumeneko. 7 Ntchito yomanga Nyumba ya Mulunguyi muyileke. Mulekeni bwanamkubwa wa Ayuda ndiponso akuluakulu a Ayuda kuti amangenso Nyumba ya Mulunguyo pamalo pake. 8 Kuwonjezera pamenepo, ndikukhazikitsa lamulo lonena za mmene mudzachitire ndi akuluakulu a Ayuda powathandiza kumanganso Nyumba ya Mulunguyo:Anthuwa muwalipire msanga kuchokera mʼthumba la ufumu, kuchotsa pa msonkho wa dera la Patsidya pa Yufurate. 9 Ndipo zonse zofunikira monga, ana angʼombe, nkhosa zazimuna, ana ankhosa aamuna zoperekera nsembe yopsereza kwa Mulungu wakumwamba, ndi tirigu, mchere, vinyo ndi mafuta monga mmene ansembe a ku Yerusalemu angafunire, muziwapatsa zimenezo tsiku ndi tsiku ndipo musamalephere kutero. 10 Zikatero ndiye kuti azipereka nsembe za fungo lokomera Mulungu wakumwamba ndi kupempherera moyo wa mfumu ndi ana ake. 11 Ndikulamulanso kuti ngati wina asintha zimene ndalamulazi, mtanda umodzi wa nyumba yake udzasololedwa ndi kumunkhomera pamenepo ndipo nyumba yake adzayisandutse dzala. 12 Mulungu amene anasankha kuti anthu azimupembedza pa malo amenewa, achotse mfumu iliyonse kapena munthu aliyense amene adzasinthe zimenezi kapena kuwononga Nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemuko.Ine Dariyo ndikuyika lamuloli, aliyense alitsate mosamala kwambiri. 13 Tsono potsata zomwe analamula mfumu Dariyo, Tatenai bwanamkubwa wa dera la Patsidya pa Yufurate, Setari-Bozenai ndi anzawo anatsatira mosamala kwambiri zimene mfumu Dariyo analamula. 14 Ndipo akuluakulu a Ayuda anapitiriza ntchito yomanga ija molimbikitsidwa ndi aneneri Hagai ndi Zekariya mwana wa Ido. Anamaliza ntchito yomanga Nyumbayo, monga momwe Mulungu wa Israeli analamulira ndiponso potsata lamulo la Koresi, Dariyo ndi Aritasasita, mafumu a ku Perisiya. 15 Anatsiriza kumanga Nyumbayo pa tsiku lachitatu la mwezi wa Adara mʼchaka chachisanu ndi chimodzi cha ulamuliro wa mfumu Dariyo. 16 Choncho Aisraeli, ansembe, Alevi ndi anthu ena onse amene anali atabwerako ku ukapolo, anachita chikondwerero chopereka Nyumba ya Mulungu mwachimwemwe. 17 Poporeka Nyumba ya Mulunguyi, anthu anapereka nsembe za ngʼombe zazimuna 100, nkhosa zazimuna 200, ana ankhosa aamuna 400. Anaperekanso mbuzi zazimuna 12 ngati nsembe yopepesera machimo a anthu onse, potsata chiwerengero cha mafuko a Israeli. 18 Ndipo anakhazikitsa ansembe ndi Alevi pa ntchito zawo zotumikira Mulungu mu Yerusalemu monga zinalembedwera mʼbuku la Mose. 19 Pa tsiku la khumi ndi chinayi la mwezi woyamba, obwera ku ukapolo aja anachita chikondwerero cha Paska. 20 Ansembe ndi Alevi anali atadziyeretsa ndipo onsewo anali oyeretsedwa. Alevi anapha mwana wankhosa wa Paska kuphera onse amene anatuluka ku ukapolo, ansembe anzawo ndi iwo eni. 21 Nkhosa ya Paskayo anayidya ndi Aisraeli onse amene anatuluka ku ukapolo, wina aliyense amene anaphatikana nawo atadziyeretsa ku zonyansa za mitundu ina ya anthu akunja a mʼdzikomo kuti apembedze Yehova Mulungu wa Israeli. 22 Choncho pa masiku asanu ndi awiri anasangalala pa chikondwerero cha buledi wopanda yisiti, chifukwa Yehova anawadzaza ndi chimwemwe. Iye anatembenuza mtima wa mfumu ya ku Asiriya motero kuti iyo inakomera mtima Aisraeli ndi kuwathandiza ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israeli.

In Other Versions

Ezra 6 in the ANGEFD

Ezra 6 in the ANTPNG2D

Ezra 6 in the AS21

Ezra 6 in the BAGH

Ezra 6 in the BBPNG

Ezra 6 in the BBT1E

Ezra 6 in the BDS

Ezra 6 in the BEV

Ezra 6 in the BHAD

Ezra 6 in the BIB

Ezra 6 in the BLPT

Ezra 6 in the BNT

Ezra 6 in the BNTABOOT

Ezra 6 in the BNTLV

Ezra 6 in the BOATCB

Ezra 6 in the BOATCB2

Ezra 6 in the BOBCV

Ezra 6 in the BOCNT

Ezra 6 in the BOECS

Ezra 6 in the BOHCB

Ezra 6 in the BOHCV

Ezra 6 in the BOHLNT

Ezra 6 in the BOHNTLTAL

Ezra 6 in the BOICB

Ezra 6 in the BOILNTAP

Ezra 6 in the BOITCV

Ezra 6 in the BOKCV

Ezra 6 in the BOKCV2

Ezra 6 in the BOKHWOG

Ezra 6 in the BOKSSV

Ezra 6 in the BOLCB

Ezra 6 in the BOLCB2

Ezra 6 in the BOMCV

Ezra 6 in the BONAV

Ezra 6 in the BONCB

Ezra 6 in the BONLT

Ezra 6 in the BONUT2

Ezra 6 in the BOPLNT

Ezra 6 in the BOSCB

Ezra 6 in the BOSNC

Ezra 6 in the BOTLNT

Ezra 6 in the BOVCB

Ezra 6 in the BOYCB

Ezra 6 in the BPBB

Ezra 6 in the BPH

Ezra 6 in the BSB

Ezra 6 in the CCB

Ezra 6 in the CUV

Ezra 6 in the CUVS

Ezra 6 in the DBT

Ezra 6 in the DGDNT

Ezra 6 in the DHNT

Ezra 6 in the DNT

Ezra 6 in the ELBE

Ezra 6 in the EMTV

Ezra 6 in the ESV

Ezra 6 in the FBV

Ezra 6 in the FEB

Ezra 6 in the GGMNT

Ezra 6 in the GNT

Ezra 6 in the HARY

Ezra 6 in the HNT

Ezra 6 in the IRVA

Ezra 6 in the IRVB

Ezra 6 in the IRVG

Ezra 6 in the IRVH

Ezra 6 in the IRVK

Ezra 6 in the IRVM

Ezra 6 in the IRVM2

Ezra 6 in the IRVO

Ezra 6 in the IRVP

Ezra 6 in the IRVT

Ezra 6 in the IRVT2

Ezra 6 in the IRVU

Ezra 6 in the ISVN

Ezra 6 in the JSNT

Ezra 6 in the KAPI

Ezra 6 in the KBT1ETNIK

Ezra 6 in the KBV

Ezra 6 in the KJV

Ezra 6 in the KNFD

Ezra 6 in the LBA

Ezra 6 in the LBLA

Ezra 6 in the LNT

Ezra 6 in the LSV

Ezra 6 in the MAAL

Ezra 6 in the MBV

Ezra 6 in the MBV2

Ezra 6 in the MHNT

Ezra 6 in the MKNFD

Ezra 6 in the MNG

Ezra 6 in the MNT

Ezra 6 in the MNT2

Ezra 6 in the MRS1T

Ezra 6 in the NAA

Ezra 6 in the NASB

Ezra 6 in the NBLA

Ezra 6 in the NBS

Ezra 6 in the NBVTP

Ezra 6 in the NET2

Ezra 6 in the NIV11

Ezra 6 in the NNT

Ezra 6 in the NNT2

Ezra 6 in the NNT3

Ezra 6 in the PDDPT

Ezra 6 in the PFNT

Ezra 6 in the RMNT

Ezra 6 in the SBIAS

Ezra 6 in the SBIBS

Ezra 6 in the SBIBS2

Ezra 6 in the SBICS

Ezra 6 in the SBIDS

Ezra 6 in the SBIGS

Ezra 6 in the SBIHS

Ezra 6 in the SBIIS

Ezra 6 in the SBIIS2

Ezra 6 in the SBIIS3

Ezra 6 in the SBIKS

Ezra 6 in the SBIKS2

Ezra 6 in the SBIMS

Ezra 6 in the SBIOS

Ezra 6 in the SBIPS

Ezra 6 in the SBISS

Ezra 6 in the SBITS

Ezra 6 in the SBITS2

Ezra 6 in the SBITS3

Ezra 6 in the SBITS4

Ezra 6 in the SBIUS

Ezra 6 in the SBIVS

Ezra 6 in the SBT

Ezra 6 in the SBT1E

Ezra 6 in the SCHL

Ezra 6 in the SNT

Ezra 6 in the SUSU

Ezra 6 in the SUSU2

Ezra 6 in the SYNO

Ezra 6 in the TBIAOTANT

Ezra 6 in the TBT1E

Ezra 6 in the TBT1E2

Ezra 6 in the TFTIP

Ezra 6 in the TFTU

Ezra 6 in the TGNTATF3T

Ezra 6 in the THAI

Ezra 6 in the TNFD

Ezra 6 in the TNT

Ezra 6 in the TNTIK

Ezra 6 in the TNTIL

Ezra 6 in the TNTIN

Ezra 6 in the TNTIP

Ezra 6 in the TNTIZ

Ezra 6 in the TOMA

Ezra 6 in the TTENT

Ezra 6 in the UBG

Ezra 6 in the UGV

Ezra 6 in the UGV2

Ezra 6 in the UGV3

Ezra 6 in the VBL

Ezra 6 in the VDCC

Ezra 6 in the YALU

Ezra 6 in the YAPE

Ezra 6 in the YBVTP

Ezra 6 in the ZBP