Ezra 9 (BOGWICC)

1 Zitachitika izi, atsogoleri anabwera kwa ine nati, “Aisraeli, kuphatikizanso ansembe ndi Alevi, sanadzipatule ku makhalidwe onyansa a anthu a mitundu ina amene ayandikana nafe: Akanaani, Ahiti, Aperezi, Ayebusi, Aamoni, Amowabu, Aigupto ndi Aamori. 2 Zomwe zikuchitika ndi izi. Aisraeli ena ndi ana awo aamuna anayamba kukwatira ana aakazi a anthuwa. Choncho mtundu wopatulika wadzisokoneza ndi mitundu ya anthu a mʼderali. Ndipo atsogoleri ndi akuluakulu ndiwo akupambana pa makhalidwe osakhulupirikawa.” 3 Nditamva zimenezi, ndinangʼamba chovala changa ndi mwinjiro wanga ndipo ndinamwetula tsitsi la kumutu kwanga ndi ndevu zanga nʼkukhala pansi ndili wokhumudwa. 4 Ndinakhala pansi chomwecho wokhumudwa mpaka nthawi ya nsembe ya madzulo. Ndipo onse amene ankaopa mawu a Mulungu wa Israeli chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu obwerako ku ukapolo anayamba kubwera kwa ine kudzasonkhana. 5 Ndipo pa nthawi ya nsembe ya madzulo, ndinadzidzimuka mu mtima wanga wokhumudwa nʼkuyimirira, zovala zanga ndi mwinjiro wanga zikanali zongʼambika ndipo ndinagwada ndi kukweza manja anga kwa Yehova Mulungu wanga 6 ndipo ndinapemphera kuti,“Inu Mulungu wanga, ndine wamanyazi ndi wachisoni moti sindingathe kukweza nkhope yanga kwa Inu Mulungu wanga, chifukwa machimo athu akwera kupambana mitu yathu, ndipo kulakwa kwathu kwafika ku thambo. 7 Ndipo chifukwa cha machimo athu, ifeyo, mafumu athu, ndi ansembe athu takhala akutipereka mʼmanja mwa mafumu a mitundu ina ya anthu kuti atiphe pa nkhondo, atitenge ku ukapolo, atilande zinthu zathu ndi kutichititsa manyazi monga zilili leromu. 8 “Koma tsopano, pa kanthawi kochepa, Inu Yehova Mulungu wathu mwaonetsa kukoma mtima. Inu mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke ku ukapolo ndi kutipatsa cholowa mʼmalo anu oyera. Mwatipulumutsa ku ukapolo ndi kutipatsa mpumulo pangʼono mu ukapolo wathu. 9 Ndifedi akapolo. Koma Inu Yehova simunatileke mu ukapolo wathu. Mwationetsa chikondi chanu chosasinthika pamaso pa mafumu a ku Perisiya. Mwatitsitsimutsa kuti timange Nyumba yanu pokonzanso mabwinja ake. Mwatitchinjiriza mʼdziko la Yuda ndi Yerusalemu. 10 “Koma tsopano, Inu Mulungu wathu, kodi tinganene chiyani titachita zoyipa zonsezi? Ife taphwanya malamulo anu 11 amene munawapereka kudzera mwa atumiki anu aneneri. Inu munati, ‘Dziko limene mukulowamolo kuti likhale cholowa chanu, ndi dziko lodetsedwa ndi zonyansa za mitundu ya mʼmayikomo. Ndipo adzaza dzikolo ndi zochita zawo zonyansa. 12 Nʼchifukwa chake, musapereke ana anu aakazi kuti akwatiwe ndi ana awo aamuna kapena kulola kuti ana awo aakazi akwatiwe ndi ana anu aamuna. Musagwirizane nawo, kapena kuchita nawo malonda kuti mukhale amphamvu ndi kudya zokoma za mʼdzikomo ndi kusiyira ana anu dzikoli ngati cholowa chawo mpaka kalekale.’ 13 “Tsono pambuyo pa zonse zimene zatigwera chifukwa cha ntchito zathu zoyipa ndi uchimo wathu waukulu, komanso pambuyo poona kuti Inu Mulungu wathu simunangotilanga kokha pangʼono kuyerekeza ndi kuchimwa kwathu komanso mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke, 14 kodi ife nʼkuphwanyanso malamulo anu ndi kukwatirana ndi anthu amitundu ina amene amachita zonyansa zimenezi? Kodi simudzatikwiyira ndi kutiwononga kwathunthu popanda wina wotsala kapena wopulumuka? 15 Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, ndinu wachifundo, pakuti ndife otsala amene tapulumuka monga mmene zilili lero lino. Ife tayima pamaso panu ngakhale tikudziwa kuchimwa kwathu pakuti palibe munthu amene angathe kuyima pamaso panu chifukwa cha machimo ake.”

In Other Versions

Ezra 9 in the ANGEFD

Ezra 9 in the ANTPNG2D

Ezra 9 in the AS21

Ezra 9 in the BAGH

Ezra 9 in the BBPNG

Ezra 9 in the BBT1E

Ezra 9 in the BDS

Ezra 9 in the BEV

Ezra 9 in the BHAD

Ezra 9 in the BIB

Ezra 9 in the BLPT

Ezra 9 in the BNT

Ezra 9 in the BNTABOOT

Ezra 9 in the BNTLV

Ezra 9 in the BOATCB

Ezra 9 in the BOATCB2

Ezra 9 in the BOBCV

Ezra 9 in the BOCNT

Ezra 9 in the BOECS

Ezra 9 in the BOHCB

Ezra 9 in the BOHCV

Ezra 9 in the BOHLNT

Ezra 9 in the BOHNTLTAL

Ezra 9 in the BOICB

Ezra 9 in the BOILNTAP

Ezra 9 in the BOITCV

Ezra 9 in the BOKCV

Ezra 9 in the BOKCV2

Ezra 9 in the BOKHWOG

Ezra 9 in the BOKSSV

Ezra 9 in the BOLCB

Ezra 9 in the BOLCB2

Ezra 9 in the BOMCV

Ezra 9 in the BONAV

Ezra 9 in the BONCB

Ezra 9 in the BONLT

Ezra 9 in the BONUT2

Ezra 9 in the BOPLNT

Ezra 9 in the BOSCB

Ezra 9 in the BOSNC

Ezra 9 in the BOTLNT

Ezra 9 in the BOVCB

Ezra 9 in the BOYCB

Ezra 9 in the BPBB

Ezra 9 in the BPH

Ezra 9 in the BSB

Ezra 9 in the CCB

Ezra 9 in the CUV

Ezra 9 in the CUVS

Ezra 9 in the DBT

Ezra 9 in the DGDNT

Ezra 9 in the DHNT

Ezra 9 in the DNT

Ezra 9 in the ELBE

Ezra 9 in the EMTV

Ezra 9 in the ESV

Ezra 9 in the FBV

Ezra 9 in the FEB

Ezra 9 in the GGMNT

Ezra 9 in the GNT

Ezra 9 in the HARY

Ezra 9 in the HNT

Ezra 9 in the IRVA

Ezra 9 in the IRVB

Ezra 9 in the IRVG

Ezra 9 in the IRVH

Ezra 9 in the IRVK

Ezra 9 in the IRVM

Ezra 9 in the IRVM2

Ezra 9 in the IRVO

Ezra 9 in the IRVP

Ezra 9 in the IRVT

Ezra 9 in the IRVT2

Ezra 9 in the IRVU

Ezra 9 in the ISVN

Ezra 9 in the JSNT

Ezra 9 in the KAPI

Ezra 9 in the KBT1ETNIK

Ezra 9 in the KBV

Ezra 9 in the KJV

Ezra 9 in the KNFD

Ezra 9 in the LBA

Ezra 9 in the LBLA

Ezra 9 in the LNT

Ezra 9 in the LSV

Ezra 9 in the MAAL

Ezra 9 in the MBV

Ezra 9 in the MBV2

Ezra 9 in the MHNT

Ezra 9 in the MKNFD

Ezra 9 in the MNG

Ezra 9 in the MNT

Ezra 9 in the MNT2

Ezra 9 in the MRS1T

Ezra 9 in the NAA

Ezra 9 in the NASB

Ezra 9 in the NBLA

Ezra 9 in the NBS

Ezra 9 in the NBVTP

Ezra 9 in the NET2

Ezra 9 in the NIV11

Ezra 9 in the NNT

Ezra 9 in the NNT2

Ezra 9 in the NNT3

Ezra 9 in the PDDPT

Ezra 9 in the PFNT

Ezra 9 in the RMNT

Ezra 9 in the SBIAS

Ezra 9 in the SBIBS

Ezra 9 in the SBIBS2

Ezra 9 in the SBICS

Ezra 9 in the SBIDS

Ezra 9 in the SBIGS

Ezra 9 in the SBIHS

Ezra 9 in the SBIIS

Ezra 9 in the SBIIS2

Ezra 9 in the SBIIS3

Ezra 9 in the SBIKS

Ezra 9 in the SBIKS2

Ezra 9 in the SBIMS

Ezra 9 in the SBIOS

Ezra 9 in the SBIPS

Ezra 9 in the SBISS

Ezra 9 in the SBITS

Ezra 9 in the SBITS2

Ezra 9 in the SBITS3

Ezra 9 in the SBITS4

Ezra 9 in the SBIUS

Ezra 9 in the SBIVS

Ezra 9 in the SBT

Ezra 9 in the SBT1E

Ezra 9 in the SCHL

Ezra 9 in the SNT

Ezra 9 in the SUSU

Ezra 9 in the SUSU2

Ezra 9 in the SYNO

Ezra 9 in the TBIAOTANT

Ezra 9 in the TBT1E

Ezra 9 in the TBT1E2

Ezra 9 in the TFTIP

Ezra 9 in the TFTU

Ezra 9 in the TGNTATF3T

Ezra 9 in the THAI

Ezra 9 in the TNFD

Ezra 9 in the TNT

Ezra 9 in the TNTIK

Ezra 9 in the TNTIL

Ezra 9 in the TNTIN

Ezra 9 in the TNTIP

Ezra 9 in the TNTIZ

Ezra 9 in the TOMA

Ezra 9 in the TTENT

Ezra 9 in the UBG

Ezra 9 in the UGV

Ezra 9 in the UGV2

Ezra 9 in the UGV3

Ezra 9 in the VBL

Ezra 9 in the VDCC

Ezra 9 in the YALU

Ezra 9 in the YAPE

Ezra 9 in the YBVTP

Ezra 9 in the ZBP