Genesis 12 (BOGWICC)

1 Tsiku lina Yehova anamuwuza Abramu kuti, “Tuluka mʼdziko lako. Siya abale ako ndi banja la abambo ako ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza. 2 “Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu wa anthundipo ndidzakudalitsa;ndi kukusandutsa wotchuka kotero kutiudzakhala dalitso kwa anthu ambiri. 3 Ndidzadalitsa amene adzadalitsa iwe,ndi kutemberera amene adzatemberera iwe;ndipo mafuko onse a pa dziko lapansiadzadalitsika kudzera mwa iwe.” 4 Choncho Abramu ananyamuka monga momwe Yehova anamuwuzira, napita pamodzi ndi Loti. Pamene Abramu amachoka ku Harani nʼkuti ali ndi zaka 75. 5 Abramu anatenga mkazi wake Sarai, Loti, mwana wamngʼono wake, pamodzi ndi chuma chawo chimene anapeza ndi antchito amene anali nawo ku Harani. Iwo ananyamuka ulendo mpaka kukafika ku dziko la Kanaani. 6 Abramu anadutsa mʼdzikomo mpaka kukafika ku Sekemu pa mtengo wa thundu wa ku More. Nthawi imeneyo Akanaani analipobe mʼdzikomo. 7 Yehova anadza kwa Abramu nati, “Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko limeneli.” Choncho Abramu anamangira Yehova amene anadza kwa iye, guwa lansembe. 8 Atachoka pamenepo analowera cha ku mapiri a kummawa kwa Beteli namangako tenti yake pakati pa Beteli chakumadzulo ndi Ai chakummawa. Kumeneko anamangira Yehova guwa lansembe napemphera mʼdzina la Yehovayo. 9 Kenaka Abramu ananyamuka kumalowera cha ku Negevi. 10 Kunagwa njala yayikulu mʼdzikomo, ndipo Abramu anapita ku Igupto kukakhala ngati mlendo kwa kanthawi kochepa popeza njalayo inakula kwambiri. 11 Atatsala pangʼono kulowa mu Igupto, Abramu anamuwuza mkazi wake Sarai kuti, “Ndimadziwa kuti ndiwe mkazi wokongola kwambiri. 12 Tsono Aigupto akakuona adzanena kuti ‘Ameneyu ndi mkazi wake.’ Tsono adzandipha ine nakusiya iwe ndi moyo. 13 Tsono udzikawawuza kuti iwe ndiwe mlongo wanga. Ukatero zidzandiyendera bwino ndipo ndidzapulumuka chifukwa cha iwe.” 14 Pamene Abramu anafika ku Igupto, Aigupto aja anaona kuti Sarai anali mkazi wokongoladi. 15 Pamene akuluakulu a ku nyumba ya Farao anamuona, anakamuyamikira pamaso pa Farao ndipo ananka naye ku nyumba ya Farao. 16 Abramu naye zinthu zinkamuyendera bwino chifukwa cha Sarai. Farao anamupatsa nkhosa, ngʼombe, abulu aamuna ndi abulu aakazi, antchito aakazi pamodzi ndi ngamira. 17 Koma Yehova anabweretsa matenda owopsa pa Farao pamodzi ndi banja lake lonse chifukwa cha Sarai mkazi wa Abramu. 18 Choncho Farao anayitanitsa Abramu namufunsa kuti, “Nʼchiyani wandichitirachi? Nʼchifukwa chiyani sunandiwuze kuti ameneyu ndi mkazi wako? 19 Nʼchifukwa chiyani unati ndi mlongo wako, mpaka ine ndinamutenga kukhala mkazi wanga? Eko mkazi wako. Mutenge uzipita!” 20 Farao analamula asilikali ake ndipo iwo anamutulutsa Abramu pamodzi ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo.

In Other Versions

Genesis 12 in the ANGEFD

Genesis 12 in the ANTPNG2D

Genesis 12 in the AS21

Genesis 12 in the BAGH

Genesis 12 in the BBPNG

Genesis 12 in the BBT1E

Genesis 12 in the BDS

Genesis 12 in the BEV

Genesis 12 in the BHAD

Genesis 12 in the BIB

Genesis 12 in the BLPT

Genesis 12 in the BNT

Genesis 12 in the BNTABOOT

Genesis 12 in the BNTLV

Genesis 12 in the BOATCB

Genesis 12 in the BOATCB2

Genesis 12 in the BOBCV

Genesis 12 in the BOCNT

Genesis 12 in the BOECS

Genesis 12 in the BOHCB

Genesis 12 in the BOHCV

Genesis 12 in the BOHLNT

Genesis 12 in the BOHNTLTAL

Genesis 12 in the BOICB

Genesis 12 in the BOILNTAP

Genesis 12 in the BOITCV

Genesis 12 in the BOKCV

Genesis 12 in the BOKCV2

Genesis 12 in the BOKHWOG

Genesis 12 in the BOKSSV

Genesis 12 in the BOLCB

Genesis 12 in the BOLCB2

Genesis 12 in the BOMCV

Genesis 12 in the BONAV

Genesis 12 in the BONCB

Genesis 12 in the BONLT

Genesis 12 in the BONUT2

Genesis 12 in the BOPLNT

Genesis 12 in the BOSCB

Genesis 12 in the BOSNC

Genesis 12 in the BOTLNT

Genesis 12 in the BOVCB

Genesis 12 in the BOYCB

Genesis 12 in the BPBB

Genesis 12 in the BPH

Genesis 12 in the BSB

Genesis 12 in the CCB

Genesis 12 in the CUV

Genesis 12 in the CUVS

Genesis 12 in the DBT

Genesis 12 in the DGDNT

Genesis 12 in the DHNT

Genesis 12 in the DNT

Genesis 12 in the ELBE

Genesis 12 in the EMTV

Genesis 12 in the ESV

Genesis 12 in the FBV

Genesis 12 in the FEB

Genesis 12 in the GGMNT

Genesis 12 in the GNT

Genesis 12 in the HARY

Genesis 12 in the HNT

Genesis 12 in the IRVA

Genesis 12 in the IRVB

Genesis 12 in the IRVG

Genesis 12 in the IRVH

Genesis 12 in the IRVK

Genesis 12 in the IRVM

Genesis 12 in the IRVM2

Genesis 12 in the IRVO

Genesis 12 in the IRVP

Genesis 12 in the IRVT

Genesis 12 in the IRVT2

Genesis 12 in the IRVU

Genesis 12 in the ISVN

Genesis 12 in the JSNT

Genesis 12 in the KAPI

Genesis 12 in the KBT1ETNIK

Genesis 12 in the KBV

Genesis 12 in the KJV

Genesis 12 in the KNFD

Genesis 12 in the LBA

Genesis 12 in the LBLA

Genesis 12 in the LNT

Genesis 12 in the LSV

Genesis 12 in the MAAL

Genesis 12 in the MBV

Genesis 12 in the MBV2

Genesis 12 in the MHNT

Genesis 12 in the MKNFD

Genesis 12 in the MNG

Genesis 12 in the MNT

Genesis 12 in the MNT2

Genesis 12 in the MRS1T

Genesis 12 in the NAA

Genesis 12 in the NASB

Genesis 12 in the NBLA

Genesis 12 in the NBS

Genesis 12 in the NBVTP

Genesis 12 in the NET2

Genesis 12 in the NIV11

Genesis 12 in the NNT

Genesis 12 in the NNT2

Genesis 12 in the NNT3

Genesis 12 in the PDDPT

Genesis 12 in the PFNT

Genesis 12 in the RMNT

Genesis 12 in the SBIAS

Genesis 12 in the SBIBS

Genesis 12 in the SBIBS2

Genesis 12 in the SBICS

Genesis 12 in the SBIDS

Genesis 12 in the SBIGS

Genesis 12 in the SBIHS

Genesis 12 in the SBIIS

Genesis 12 in the SBIIS2

Genesis 12 in the SBIIS3

Genesis 12 in the SBIKS

Genesis 12 in the SBIKS2

Genesis 12 in the SBIMS

Genesis 12 in the SBIOS

Genesis 12 in the SBIPS

Genesis 12 in the SBISS

Genesis 12 in the SBITS

Genesis 12 in the SBITS2

Genesis 12 in the SBITS3

Genesis 12 in the SBITS4

Genesis 12 in the SBIUS

Genesis 12 in the SBIVS

Genesis 12 in the SBT

Genesis 12 in the SBT1E

Genesis 12 in the SCHL

Genesis 12 in the SNT

Genesis 12 in the SUSU

Genesis 12 in the SUSU2

Genesis 12 in the SYNO

Genesis 12 in the TBIAOTANT

Genesis 12 in the TBT1E

Genesis 12 in the TBT1E2

Genesis 12 in the TFTIP

Genesis 12 in the TFTU

Genesis 12 in the TGNTATF3T

Genesis 12 in the THAI

Genesis 12 in the TNFD

Genesis 12 in the TNT

Genesis 12 in the TNTIK

Genesis 12 in the TNTIL

Genesis 12 in the TNTIN

Genesis 12 in the TNTIP

Genesis 12 in the TNTIZ

Genesis 12 in the TOMA

Genesis 12 in the TTENT

Genesis 12 in the UBG

Genesis 12 in the UGV

Genesis 12 in the UGV2

Genesis 12 in the UGV3

Genesis 12 in the VBL

Genesis 12 in the VDCC

Genesis 12 in the YALU

Genesis 12 in the YAPE

Genesis 12 in the YBVTP

Genesis 12 in the ZBP