Genesis 37 (BOGWICC)

1 Yakobo ankakhala mʼdziko la Kanaani kumene abambo ake ankakhala. 2 Mbiri ya banja la Yakobo ndi iyi: Yosefe, mnyamata wa zaka 17 ankaweta nkhosa ndi abale ake, pamodzi ndi ana a Biliha ndi Zilipa, akazi a abambo ake. Tsono Yosefe ankabwera kudzawuza abambo ake zoyipa za abale ake. 3 Tsono Israeli ankakonda Yosefe koposa ana ake ena onse, chifukwa anali mwana wobadwa muukalamba wake. Ndipo anamusokera mkanjo wa manja aatali. 4 Pamene abale ake anaona kuti abambo awo ankakonda Yosefe kuposa aliyense wa iwo, anayamba kumuda Yosefe ndipo sankayankhula naye zamtendere. 5 Tsiku lina Yosefe analota maloto ndipo pamene anawuza abale ake za malotowo, iwo anawonjeza kumuda. 6 Iye anawawuza kuti, “Tamvani maloto amene ndinalota: 7 Ife timamanga mitolo ya tirigu ku munda ndipo mwadzidzidzi mtolo wanga unayimirira chilili, pamene mitolo yanu inazungulira mtolo wangawo nʼkumawugwadira.” 8 Abale ake aja anamufunsa nati, “Kodi ukuyesa kuti ungakhale mfumu yathu? Ungadzatilamuliredi iweyo?” Ndipo anamuda kuposa kale chifukwa cha maloto ake ndi zimene ankakonda kunena kwa abambo awo. 9 Tsiku lina analotanso maloto ena, ndipo anafotokozera abale ake za malotowo. Iye anati, “Tamverani, ndinalotanso maloto ena. Ulendo uno dzuwa ndi mwezi pamodzi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zimandigwadira.” 10 Atawuza abambo ake ndi abale ake malotowa, abambo ake anamukalipira nati, “Ndi maloto anji umalotawa? Kodi uganiza kuti ine, amayi ako pamodzi ndi abale ako onsewa tingadzabwere kudzakugwandira iwe?” 11 Abale ake anamuchitira nsanje, koma abambo ake anasunga nkhaniyi mu mtima. 12 Tsono abale ake anapita kukadyetsa ziweto za abambo awo ku Sekemu, 13 ndipo Israeli anati kwa Yosefe, “Tsono, ndikufuna kukutuma kwa abale ako.”Iye anayankha nati, “Chabwino.” 14 Choncho anati kwa iye, “Pita ukaone ngati abale ako ali bwino. Ukaonenso nkhosa ngati zili bwino. Kenaka ubwere udzandiwuze.” Choncho Israeli anatuma Yosefe kuchokera ku chigwa cha Hebroni.Yosefe atafika ku Sekemu, 15 munthu wina anamupeza akungozungulirazungulira mʼmunda ndipo anamufunsa, “Ukufunafuna chiyani?” 16 Iye anayankha, “Ndikufuna abale anga. Mungandiwuze kumene akudyetsa ziweto zawo?” 17 Munthuyo anayankha nati, “Anasamukako kuno. Ndinawamva akuti, ‘Tiyeni tipite ku Dotani.’ ”Choncho Yosefe analondola abale ake ndipo anakawapeza ku Dotani. 18 Abale ake aja anamuonera patali. Ndipo asanafike nʼkomwe kumene kunali iwo kuja, anayamba kale kumupangira chiwembu choti amuphe. 19 Iwo anawuzana nati, “Uyo akubwera apo wamaloto uja. 20 Tsono tiyeni timuphe ndi kuponya thupi lake mu chimodzi mwa zitsime izi ndipo tidzati anadyedwa ndi nyama zakuthengo zolusa. Tsono timuonera zomwe ziti zichitike ndi maloto ake aja.” 21 Koma Rubeni atamva izi, anapulumutsa Yosefe. Iye anati kwa abale ake, “Ayi, tisamuphe, 22 tisakhetse magazi. Tiyeni timuponye mʼchitsime ku chipululu konkuno. Koma tisamuvulaze nʼkomwe. Rubeni ananena zonsezi kuti apulumutse Yosefe ndi kuti pambuyo pake akamupereke kwa abambo awo.” 23 Choncho Yosefe atafika kwa abale ake, iwo anamuvula mkanjo wake wamanja aatali uja umene anavala 24 ndipo anamutenga namuponya mʼchitsime chopanda madzi komanso mopanda chilichonse. 25 Atakhala pansi kuti adye chakudya, anatukula maso naona gulu la Aismaeli akubwera kuchokera ku Giliyadi. Ngamira zawo zinanyamula zonunkhiritsa bwino zakudya zamitundumitundu, ndipo zimenezi ankapita nazo ku Igupto. 26 Yuda anafunsa abale ake nati, “Kodi tidzapindula chiyani tikapha mʼbale wathuyu ndi kuphimbitsa magazi ake? 27 Bwanji timugulitse kwa Aismaeliwa, koma ife tisamuchite kanthu kalikonse. Ameneyu ndi mʼbale wathu thupi limodzi ndi ife.” Abale ake anavomereza zimenezi. 28 Amalonda ena a ku Midiyani ankadutsa pomwepo. Tsono abale ake a Yosefe anamutulutsa Yosefe uja mu chitsime chija ndipo anamugulitsa kwa Aismaeli aja pamtengo wa masekeli makumi awiri. Choncho anapita naye Yosefe ku Igupto. 29 Rubeni atabwerera ku chitsime kuja anapeza kuti Yosefe mulibe mʼchitsimemo. Pamenepo iye anangʼamba zovala zake 30 nabwerera kwa abale ake nati, “Mnyamata uja mulibemo! Nanga ndilowere kuti ine tsopano?” 31 Tsono anapha kamwana ka mbuzi, natenga mkanjo wa Yosefe ndi kuwunyika mʼmagazi ake. 32 Iwo anatenga mkanjo uja nabwerera nawo kwa abambo awo nati, “Ife tapeza mkanjowu. Tawuyangʼanitsitsani muone ngati uli wa mwana wanu.” 33 Iye anawuzindikira ndipo anati, “Ndi mkanjo wa mwana wanga umenewu! Nyama yakuthengo yolusa yamudya. Mosakayika, mwana wanga Yosefe wakhadzulidwa.” 34 Pamenepo Yakobo anangʼamba zovala zake, navala chisaka mʼchiwuno mwake. Iye analira maliro a mwana wake masiku ambiri. 35 Ngakhale kuti ana ake onse aamuna ndi aakazi anasonkhana kudzamutonthoza, iye anakana kutonthozedwa. Iye anati, “Ayi. Ndidzalira mpaka ndidzapite kwa mwana wanga ku manda.” Choncho Israeli anapitirirabe kulira mwana wake. 36 Amidiyani aja anagulitsa Yosefe kwa Potifara, mmodzi mwa nduna za Farao ku Igupto. Potifarayu anali mkulu wa asilikali olonda nyumba ya Farao.

In Other Versions

Genesis 37 in the ANGEFD

Genesis 37 in the ANTPNG2D

Genesis 37 in the AS21

Genesis 37 in the BAGH

Genesis 37 in the BBPNG

Genesis 37 in the BBT1E

Genesis 37 in the BDS

Genesis 37 in the BEV

Genesis 37 in the BHAD

Genesis 37 in the BIB

Genesis 37 in the BLPT

Genesis 37 in the BNT

Genesis 37 in the BNTABOOT

Genesis 37 in the BNTLV

Genesis 37 in the BOATCB

Genesis 37 in the BOATCB2

Genesis 37 in the BOBCV

Genesis 37 in the BOCNT

Genesis 37 in the BOECS

Genesis 37 in the BOHCB

Genesis 37 in the BOHCV

Genesis 37 in the BOHLNT

Genesis 37 in the BOHNTLTAL

Genesis 37 in the BOICB

Genesis 37 in the BOILNTAP

Genesis 37 in the BOITCV

Genesis 37 in the BOKCV

Genesis 37 in the BOKCV2

Genesis 37 in the BOKHWOG

Genesis 37 in the BOKSSV

Genesis 37 in the BOLCB

Genesis 37 in the BOLCB2

Genesis 37 in the BOMCV

Genesis 37 in the BONAV

Genesis 37 in the BONCB

Genesis 37 in the BONLT

Genesis 37 in the BONUT2

Genesis 37 in the BOPLNT

Genesis 37 in the BOSCB

Genesis 37 in the BOSNC

Genesis 37 in the BOTLNT

Genesis 37 in the BOVCB

Genesis 37 in the BOYCB

Genesis 37 in the BPBB

Genesis 37 in the BPH

Genesis 37 in the BSB

Genesis 37 in the CCB

Genesis 37 in the CUV

Genesis 37 in the CUVS

Genesis 37 in the DBT

Genesis 37 in the DGDNT

Genesis 37 in the DHNT

Genesis 37 in the DNT

Genesis 37 in the ELBE

Genesis 37 in the EMTV

Genesis 37 in the ESV

Genesis 37 in the FBV

Genesis 37 in the FEB

Genesis 37 in the GGMNT

Genesis 37 in the GNT

Genesis 37 in the HARY

Genesis 37 in the HNT

Genesis 37 in the IRVA

Genesis 37 in the IRVB

Genesis 37 in the IRVG

Genesis 37 in the IRVH

Genesis 37 in the IRVK

Genesis 37 in the IRVM

Genesis 37 in the IRVM2

Genesis 37 in the IRVO

Genesis 37 in the IRVP

Genesis 37 in the IRVT

Genesis 37 in the IRVT2

Genesis 37 in the IRVU

Genesis 37 in the ISVN

Genesis 37 in the JSNT

Genesis 37 in the KAPI

Genesis 37 in the KBT1ETNIK

Genesis 37 in the KBV

Genesis 37 in the KJV

Genesis 37 in the KNFD

Genesis 37 in the LBA

Genesis 37 in the LBLA

Genesis 37 in the LNT

Genesis 37 in the LSV

Genesis 37 in the MAAL

Genesis 37 in the MBV

Genesis 37 in the MBV2

Genesis 37 in the MHNT

Genesis 37 in the MKNFD

Genesis 37 in the MNG

Genesis 37 in the MNT

Genesis 37 in the MNT2

Genesis 37 in the MRS1T

Genesis 37 in the NAA

Genesis 37 in the NASB

Genesis 37 in the NBLA

Genesis 37 in the NBS

Genesis 37 in the NBVTP

Genesis 37 in the NET2

Genesis 37 in the NIV11

Genesis 37 in the NNT

Genesis 37 in the NNT2

Genesis 37 in the NNT3

Genesis 37 in the PDDPT

Genesis 37 in the PFNT

Genesis 37 in the RMNT

Genesis 37 in the SBIAS

Genesis 37 in the SBIBS

Genesis 37 in the SBIBS2

Genesis 37 in the SBICS

Genesis 37 in the SBIDS

Genesis 37 in the SBIGS

Genesis 37 in the SBIHS

Genesis 37 in the SBIIS

Genesis 37 in the SBIIS2

Genesis 37 in the SBIIS3

Genesis 37 in the SBIKS

Genesis 37 in the SBIKS2

Genesis 37 in the SBIMS

Genesis 37 in the SBIOS

Genesis 37 in the SBIPS

Genesis 37 in the SBISS

Genesis 37 in the SBITS

Genesis 37 in the SBITS2

Genesis 37 in the SBITS3

Genesis 37 in the SBITS4

Genesis 37 in the SBIUS

Genesis 37 in the SBIVS

Genesis 37 in the SBT

Genesis 37 in the SBT1E

Genesis 37 in the SCHL

Genesis 37 in the SNT

Genesis 37 in the SUSU

Genesis 37 in the SUSU2

Genesis 37 in the SYNO

Genesis 37 in the TBIAOTANT

Genesis 37 in the TBT1E

Genesis 37 in the TBT1E2

Genesis 37 in the TFTIP

Genesis 37 in the TFTU

Genesis 37 in the TGNTATF3T

Genesis 37 in the THAI

Genesis 37 in the TNFD

Genesis 37 in the TNT

Genesis 37 in the TNTIK

Genesis 37 in the TNTIL

Genesis 37 in the TNTIN

Genesis 37 in the TNTIP

Genesis 37 in the TNTIZ

Genesis 37 in the TOMA

Genesis 37 in the TTENT

Genesis 37 in the UBG

Genesis 37 in the UGV

Genesis 37 in the UGV2

Genesis 37 in the UGV3

Genesis 37 in the VBL

Genesis 37 in the VDCC

Genesis 37 in the YALU

Genesis 37 in the YAPE

Genesis 37 in the YBVTP

Genesis 37 in the ZBP