Genesis 38 (BOGWICC)

1 Pa nthawi imeneyi, Yuda anasiyana ndi abale ake napita kukakhala ndi munthu wina wa ku Adulamu wotchedwa Hira. 2 Kumeneko, Yuda anaona mwana wamkazi wa munthu wina wa Chikanaani wotchedwa Suwa. Anamukwatira nagona naye malo amodzi. 3 Iye anatenga pathupi, nabala mwana wamwamuna amene anamutcha Eri. 4 Anatenganso pathupi nabala mwana wa mwamuna ndipo anamutcha Onani. 5 Anaberekanso mwana wina wamwamuna ndipo anamutcha Sela. Ameneyu anabadwa Yuda ali ku Kezibi. 6 Yuda anamupezera mkazi mwana wake woyamba uja Eri, ndipo dzina la mkaziyo linali Tamara. 7 Koma ntchito zoyipa za Eri, mwana wachisamba wa Yuda zinayipira Yehova. Choncho Mulungu anamulanga ndi imfa. 8 Pamenepo Yuda anati kwa Onani, “Kwatira mkazi wamasiye wa mʼbale wako. Ulowe chokolo kuti mʼbale wako akhale ndi mwana.” 9 Koma Onani anadziwa kuti mwanayo sadzakhala wake. Choncho nthawi zonse pamene amagona naye mkaziyo, ankatayira umuna pansi kuti asamuberekere mwana mʼbale wake. 10 Zimene ankachitazi zinayipira Yehova. Choncho anamulanganso ndi imfa. 11 Kenaka Yuda anati kwa mpongozi wake Tamara, “Bwererani ku nyumba ya abambo anu ndi kukhala kumeneko ngati wamasiye mpaka mwana wanga Sela atakula.” Ananena izi chifukwa ankaopa kuti Sela angafenso ngati abale ake aja. Choncho Tamara anapita kukakhala ku nyumba ya abambo ake. 12 Patapita nthawi yayitali, Batishua, mkazi wa Yuda anamwalira. Yuda atatha kulira maliro a mkazi wake, anapita, iyeyu pamodzi ndi bwenzi lake Hira, Mwadulamu uja, ku Timna kumene ankameta nkhosa zawo. 13 Tamara atamva kuti apongozi ake akupita ku Timna kukameta nkhosa, 14 iye anavula zovala zake za umasiye, nadziphimba nkhope ndi nsalu kuti asadziwike, ndipo anakhala pansi pa chipata cha ku Enaimu popita ku Timna. Tamara anachita izi chifukwa anaona kuti ngakhale Selayo anali atakula tsopano, iye sanaperekedwe kuti amulowe chokolo. 15 Yuda atamuona anangomuyesa mkazi wadama chabe, chifukwa anadziphimba nkhope. 16 Tsono anapita kwa mkaziyo pamphepete pa msewu paja nati, “Tabwera ndigone nawe.” Apa Yuda sankadziwa kuti mkazi uja anali mpongozi wake.Ndiye mkazi uja anamufunsa Yuda nati, “Mudzandipatsa chiyani kuti ndigone nanu?” 17 Iye anati, “Ndidzakutumizira kamwana kambuzi ka mʼkhola mwanga.”Mkaziyo anayankha kuti, “Chabwino, ndavomera, koma mungandipatse chikole mpaka mutanditumizira mbuziyo?” 18 Iye anati, “Ndikupatse chikole chanji?”Mkaziyo anayankha, “Mundipatse mphete yanuyo, chingwe chanucho pamodzi ndi ndodo imene ili mʼdzanja lanulo.” Choncho anazipereka kwa iye nagona naye ndipo anatenga pathupi. 19 Kenaka Tamara anachoka, navula nsalu anadziphimba nayo ija, navalanso zovala zake za umasiye zija. 20 Tsono Yuda anatuma bwenzi lake Mwadulamu uja ndi kamwana kambuzi kaja kuti akapereke kwa mkazi wadama uja, ndi kuti akatero amubwezere chikole chake chija. Koma atafika sanamupezepo. 21 Anawafunsa anthu a komweko, “Kodi mkazi wadama uja amene ankakhala pambali pa msewu wa ku Enaimu, ali kuti?”Iwo anayankha, “Sipanakhalepo mkazi wa dama aliyense pano.” 22 Choncho anabwerera kwa Yuda nati, “Sindinamupeze mkazi uja. Kuwonjeza apo, anthu a kumeneko amati, ‘Sipanakhalepo mkazi wadama pano.’ ” 23 Pamenepo Yuda anati, “Mulekeni atenge zinthuzo zikhale zake, kuopa kuti anthu angatiseke. Ine sindinalakwe, ndinamutumizira kamwana kambuzika, koma simunamupeze.” 24 Patapita miyezi itatu, Yuda anawuzidwa kuti, “Mpongozi wanu Tamara anachita zadama, ndipo zotsatira zake nʼzakuti ali ndi pathupi.”Yuda anati, “Kamutulutseni ndipo mukamutenthe kuti afe!” 25 Akumutulutsa, iye anatuma mawu kwa apongozi ake. Anati, “Ndili ndi pathupi pa munthu amene ndi mwini wake wa zinthu izi. Taziyangʼanitsitsani, kodi mwini wa khoza, chingwe ndi ndodo yoyenderayi ndi yani?” 26 Yuda anazizindikira zinthuzo ndipo anati, “Uyu ndi wolungama kuposa ine, chifukwa sindinamupereke kwa mwana wanga Sela.” Ndipo Yuda sanagone nayenso. 27 Pamene Tamara nthawi inamukwanira yoti abeleke, mʼmimbamo munali mapasa. 28 Pamene ankabereka, mmodzi wa iwo anatulutsa dzanja lake. Choncho mzamba anatenga kawulusi kofiira nakamangirira pa mkono pa mwanayo nati, “Uyu ndiye anayamba kubadwa.” 29 Koma pamene anabweza mkonowo, mʼbale wake anabadwa ndipo mzamba anati, “Wachita kudziphotcholera wekha njira chonchi!” Ndipo anamutcha Perezi. 30 Pambuyo pake mʼbale wake amene anali ndi ulusi wofiira pa mkono wake uja anabadwa ndipo anapatsidwa dzina lakuti Zera.

In Other Versions

Genesis 38 in the ANGEFD

Genesis 38 in the ANTPNG2D

Genesis 38 in the AS21

Genesis 38 in the BAGH

Genesis 38 in the BBPNG

Genesis 38 in the BBT1E

Genesis 38 in the BDS

Genesis 38 in the BEV

Genesis 38 in the BHAD

Genesis 38 in the BIB

Genesis 38 in the BLPT

Genesis 38 in the BNT

Genesis 38 in the BNTABOOT

Genesis 38 in the BNTLV

Genesis 38 in the BOATCB

Genesis 38 in the BOATCB2

Genesis 38 in the BOBCV

Genesis 38 in the BOCNT

Genesis 38 in the BOECS

Genesis 38 in the BOHCB

Genesis 38 in the BOHCV

Genesis 38 in the BOHLNT

Genesis 38 in the BOHNTLTAL

Genesis 38 in the BOICB

Genesis 38 in the BOILNTAP

Genesis 38 in the BOITCV

Genesis 38 in the BOKCV

Genesis 38 in the BOKCV2

Genesis 38 in the BOKHWOG

Genesis 38 in the BOKSSV

Genesis 38 in the BOLCB

Genesis 38 in the BOLCB2

Genesis 38 in the BOMCV

Genesis 38 in the BONAV

Genesis 38 in the BONCB

Genesis 38 in the BONLT

Genesis 38 in the BONUT2

Genesis 38 in the BOPLNT

Genesis 38 in the BOSCB

Genesis 38 in the BOSNC

Genesis 38 in the BOTLNT

Genesis 38 in the BOVCB

Genesis 38 in the BOYCB

Genesis 38 in the BPBB

Genesis 38 in the BPH

Genesis 38 in the BSB

Genesis 38 in the CCB

Genesis 38 in the CUV

Genesis 38 in the CUVS

Genesis 38 in the DBT

Genesis 38 in the DGDNT

Genesis 38 in the DHNT

Genesis 38 in the DNT

Genesis 38 in the ELBE

Genesis 38 in the EMTV

Genesis 38 in the ESV

Genesis 38 in the FBV

Genesis 38 in the FEB

Genesis 38 in the GGMNT

Genesis 38 in the GNT

Genesis 38 in the HARY

Genesis 38 in the HNT

Genesis 38 in the IRVA

Genesis 38 in the IRVB

Genesis 38 in the IRVG

Genesis 38 in the IRVH

Genesis 38 in the IRVK

Genesis 38 in the IRVM

Genesis 38 in the IRVM2

Genesis 38 in the IRVO

Genesis 38 in the IRVP

Genesis 38 in the IRVT

Genesis 38 in the IRVT2

Genesis 38 in the IRVU

Genesis 38 in the ISVN

Genesis 38 in the JSNT

Genesis 38 in the KAPI

Genesis 38 in the KBT1ETNIK

Genesis 38 in the KBV

Genesis 38 in the KJV

Genesis 38 in the KNFD

Genesis 38 in the LBA

Genesis 38 in the LBLA

Genesis 38 in the LNT

Genesis 38 in the LSV

Genesis 38 in the MAAL

Genesis 38 in the MBV

Genesis 38 in the MBV2

Genesis 38 in the MHNT

Genesis 38 in the MKNFD

Genesis 38 in the MNG

Genesis 38 in the MNT

Genesis 38 in the MNT2

Genesis 38 in the MRS1T

Genesis 38 in the NAA

Genesis 38 in the NASB

Genesis 38 in the NBLA

Genesis 38 in the NBS

Genesis 38 in the NBVTP

Genesis 38 in the NET2

Genesis 38 in the NIV11

Genesis 38 in the NNT

Genesis 38 in the NNT2

Genesis 38 in the NNT3

Genesis 38 in the PDDPT

Genesis 38 in the PFNT

Genesis 38 in the RMNT

Genesis 38 in the SBIAS

Genesis 38 in the SBIBS

Genesis 38 in the SBIBS2

Genesis 38 in the SBICS

Genesis 38 in the SBIDS

Genesis 38 in the SBIGS

Genesis 38 in the SBIHS

Genesis 38 in the SBIIS

Genesis 38 in the SBIIS2

Genesis 38 in the SBIIS3

Genesis 38 in the SBIKS

Genesis 38 in the SBIKS2

Genesis 38 in the SBIMS

Genesis 38 in the SBIOS

Genesis 38 in the SBIPS

Genesis 38 in the SBISS

Genesis 38 in the SBITS

Genesis 38 in the SBITS2

Genesis 38 in the SBITS3

Genesis 38 in the SBITS4

Genesis 38 in the SBIUS

Genesis 38 in the SBIVS

Genesis 38 in the SBT

Genesis 38 in the SBT1E

Genesis 38 in the SCHL

Genesis 38 in the SNT

Genesis 38 in the SUSU

Genesis 38 in the SUSU2

Genesis 38 in the SYNO

Genesis 38 in the TBIAOTANT

Genesis 38 in the TBT1E

Genesis 38 in the TBT1E2

Genesis 38 in the TFTIP

Genesis 38 in the TFTU

Genesis 38 in the TGNTATF3T

Genesis 38 in the THAI

Genesis 38 in the TNFD

Genesis 38 in the TNT

Genesis 38 in the TNTIK

Genesis 38 in the TNTIL

Genesis 38 in the TNTIN

Genesis 38 in the TNTIP

Genesis 38 in the TNTIZ

Genesis 38 in the TOMA

Genesis 38 in the TTENT

Genesis 38 in the UBG

Genesis 38 in the UGV

Genesis 38 in the UGV2

Genesis 38 in the UGV3

Genesis 38 in the VBL

Genesis 38 in the VDCC

Genesis 38 in the YALU

Genesis 38 in the YAPE

Genesis 38 in the YBVTP

Genesis 38 in the ZBP