Genesis 7 (BOGWICC)
1 Ndipo Yehova anati kwa Nowa, “Lowa mu chombo iwe ndi banja lako lonse, chifukwa ndaona kuti ndiwe wolungama mu mʼbado uwu. 2 Pa mtundu uliwonse wa nyama zoti nʼkudya utengepo zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi zazikazi zisanu ndi ziwirinso. Koma pa mtundu wa nyama iliyonse yosati nʼkudya utengepo zazimuna ziwiri ndi zazikazi ziwirinso. 3 Chimodzimodzinso mbalame, utenge zisanu ndi ziwiri zazimuna ndi zisanu ndi ziwiri zazikazi za mtundu uliwonse kuti mitundu yawo isungike ndi moyo pa dziko lonse lapansi. 4 Pakapita masiku asanu ndi awiri ndidzagwetsa mvula pa dziko lapansi kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku ndipo ndidzawononga cha moyo chilichonse chimene ndinachipanga pa dziko lapansi.” 5 Ndipo Nowa anachita zonse zimene Yehova anamulamulira. 6 Pamene chigumula chinabwera pa dziko lapansi Nowa anali ndi zaka 600. 7 Ndipo Nowa, ana ake aamuna, mkazi wake, pamodzi ndi ana ake aakazi analowa mu chombo chija kuthawa madzi a chigumula. 8 Nyama zoti nʼkudya ndi nyama zosadyedwa, mbalame, pamodzi ndi nyama zokwawa zonse zinadza kwa Nowa ziwiriziwiri ndi kulowa mʼchombomo. 9 Ndipo Nowa anatenga ziwiriziwiri, yayimuna ndi yayikazi monga anamulamulira Mulungu. 10 Patapita masiku asanu ndi awiri chigumula chinabwera pa dziko lapansi. 11 Pa tsiku la 17 la mwezi wachiwiri, Nowa ali ndi zaka 600, akasupe onse akuya kwambiri anasefuka ndiponso zitseko za madzi akumwamba zinatsekuka. 12 Ndipo mvula inagwa pa dziko lapansi masiku makumi anayi usana ndi usiku. 13 Linali tsiku lomwelo pamene Nowa ndi ana ake aamuna, Semu, Hamu ndi Yafeti, pamodzi ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake atatu aja analowa mu chombo. 14 Iwowa analowa mʼchombomo pamodzi ndi nyama iliyonse ya kutchire monga mwa mtundu wake, ziweto zonse monga mwa mitundu yawo, nyama yokwawa iliyonse monga mwa mtundu wake ndi mbalame iliyonse monga mwa mtundu wake. 15 Nowa analowa mu chombo muja pamodzi ndi zamoyo zonse. 16 Iye analowa nazo zazimuna ndi zazikazi monga mmene Mulungu anamulamulira. Kenaka Yehova anatseka pa khomo. 17 Chigumula chinagwa pa dziko la pansi kwa masiku makumi anayi. Madzi anayamba kuchuluka ndipo ananyamula chombo chija ndi kuchiyandamitsa pamwamba pa dziko. 18 Madzi anafika mwamphamvu ndipo anachulukirachulukira pa dziko lapansi moti chombo chinayandama pamwamba pa madziwo. 19 Madzi a chigumula anabwerabe molimbika motero kuti mapiri ataliatali onse a pa dziko anamizidwa. 20 Madzi anakwera namiza mapiri kwa mamita pafupifupi asanu ndi awiri. 21 Chamoyo chilichonse choyenda pa dziko lapansi chinafa: mbalame, ziweto, nyama zakuthengo, miyandamiyanda ya zonse zolengedwa za pa dziko lapansi pamodzi ndi anthu. 22 Chilichonse chamoyo, chokhala pa mtunda chinafa. 23 Chamoyo chilichonse pa dziko lapansi chinawonongedwa, kuyambira munthu, nyama, zokwawa ndi mbalame. Nowa yekha ndiye anatsala pamodzi ndi onse amene anali naye. 24 Madziwo anadzaza dziko lonse lapansi kwa masiku 150.
In Other Versions
Genesis 7 in the ANGEFD
Genesis 7 in the ANTPNG2D
Genesis 7 in the AS21
Genesis 7 in the BAGH
Genesis 7 in the BBPNG
Genesis 7 in the BBT1E
Genesis 7 in the BDS
Genesis 7 in the BEV
Genesis 7 in the BHAD
Genesis 7 in the BIB
Genesis 7 in the BLPT
Genesis 7 in the BNT
Genesis 7 in the BNTABOOT
Genesis 7 in the BNTLV
Genesis 7 in the BOATCB
Genesis 7 in the BOATCB2
Genesis 7 in the BOBCV
Genesis 7 in the BOCNT
Genesis 7 in the BOECS
Genesis 7 in the BOHCB
Genesis 7 in the BOHCV
Genesis 7 in the BOHLNT
Genesis 7 in the BOHNTLTAL
Genesis 7 in the BOICB
Genesis 7 in the BOILNTAP
Genesis 7 in the BOITCV
Genesis 7 in the BOKCV
Genesis 7 in the BOKCV2
Genesis 7 in the BOKHWOG
Genesis 7 in the BOKSSV
Genesis 7 in the BOLCB
Genesis 7 in the BOLCB2
Genesis 7 in the BOMCV
Genesis 7 in the BONAV
Genesis 7 in the BONCB
Genesis 7 in the BONLT
Genesis 7 in the BONUT2
Genesis 7 in the BOPLNT
Genesis 7 in the BOSCB
Genesis 7 in the BOSNC
Genesis 7 in the BOTLNT
Genesis 7 in the BOVCB
Genesis 7 in the BOYCB
Genesis 7 in the BPBB
Genesis 7 in the BPH
Genesis 7 in the BSB
Genesis 7 in the CCB
Genesis 7 in the CUV
Genesis 7 in the CUVS
Genesis 7 in the DBT
Genesis 7 in the DGDNT
Genesis 7 in the DHNT
Genesis 7 in the DNT
Genesis 7 in the ELBE
Genesis 7 in the EMTV
Genesis 7 in the ESV
Genesis 7 in the FBV
Genesis 7 in the FEB
Genesis 7 in the GGMNT
Genesis 7 in the GNT
Genesis 7 in the HARY
Genesis 7 in the HNT
Genesis 7 in the IRVA
Genesis 7 in the IRVB
Genesis 7 in the IRVG
Genesis 7 in the IRVH
Genesis 7 in the IRVK
Genesis 7 in the IRVM
Genesis 7 in the IRVM2
Genesis 7 in the IRVO
Genesis 7 in the IRVP
Genesis 7 in the IRVT
Genesis 7 in the IRVT2
Genesis 7 in the IRVU
Genesis 7 in the ISVN
Genesis 7 in the JSNT
Genesis 7 in the KAPI
Genesis 7 in the KBT1ETNIK
Genesis 7 in the KBV
Genesis 7 in the KJV
Genesis 7 in the KNFD
Genesis 7 in the LBA
Genesis 7 in the LBLA
Genesis 7 in the LNT
Genesis 7 in the LSV
Genesis 7 in the MAAL
Genesis 7 in the MBV
Genesis 7 in the MBV2
Genesis 7 in the MHNT
Genesis 7 in the MKNFD
Genesis 7 in the MNG
Genesis 7 in the MNT
Genesis 7 in the MNT2
Genesis 7 in the MRS1T
Genesis 7 in the NAA
Genesis 7 in the NASB
Genesis 7 in the NBLA
Genesis 7 in the NBS
Genesis 7 in the NBVTP
Genesis 7 in the NET2
Genesis 7 in the NIV11
Genesis 7 in the NNT
Genesis 7 in the NNT2
Genesis 7 in the NNT3
Genesis 7 in the PDDPT
Genesis 7 in the PFNT
Genesis 7 in the RMNT
Genesis 7 in the SBIAS
Genesis 7 in the SBIBS
Genesis 7 in the SBIBS2
Genesis 7 in the SBICS
Genesis 7 in the SBIDS
Genesis 7 in the SBIGS
Genesis 7 in the SBIHS
Genesis 7 in the SBIIS
Genesis 7 in the SBIIS2
Genesis 7 in the SBIIS3
Genesis 7 in the SBIKS
Genesis 7 in the SBIKS2
Genesis 7 in the SBIMS
Genesis 7 in the SBIOS
Genesis 7 in the SBIPS
Genesis 7 in the SBISS
Genesis 7 in the SBITS
Genesis 7 in the SBITS2
Genesis 7 in the SBITS3
Genesis 7 in the SBITS4
Genesis 7 in the SBIUS
Genesis 7 in the SBIVS
Genesis 7 in the SBT
Genesis 7 in the SBT1E
Genesis 7 in the SCHL
Genesis 7 in the SNT
Genesis 7 in the SUSU
Genesis 7 in the SUSU2
Genesis 7 in the SYNO
Genesis 7 in the TBIAOTANT
Genesis 7 in the TBT1E
Genesis 7 in the TBT1E2
Genesis 7 in the TFTIP
Genesis 7 in the TFTU
Genesis 7 in the TGNTATF3T
Genesis 7 in the THAI
Genesis 7 in the TNFD
Genesis 7 in the TNT
Genesis 7 in the TNTIK
Genesis 7 in the TNTIL
Genesis 7 in the TNTIN
Genesis 7 in the TNTIP
Genesis 7 in the TNTIZ
Genesis 7 in the TOMA
Genesis 7 in the TTENT
Genesis 7 in the UBG
Genesis 7 in the UGV
Genesis 7 in the UGV2
Genesis 7 in the UGV3
Genesis 7 in the VBL
Genesis 7 in the VDCC
Genesis 7 in the YALU
Genesis 7 in the YAPE
Genesis 7 in the YBVTP
Genesis 7 in the ZBP