Judges 1 (BOGWICC)

1 Atamwalira Yoswa Aisraeli anafunsa Yehova kuti, “Ndani mwa ife ayambe nkhondo yomenyana ndi Akanaani?” 2 Yehova anayankha kuti, “Fuko la Yuda ndilo liyambe kupita. Ndawapatsa dzikolo mʼmanja mwawo.” 3 Choncho Ayuda anawuza abale awo a fuko la Simeoni kuti, “Bwerani tipitire limodzi mʼdziko limene tapatsidwa kuti tikamenyane ndi Akanaani. Ifenso tidzapita nanu mʼdziko limene anakugawirani.” Ndipo Asimeoni anapita nawo. 4 Choncho Ayuda ananyamuka, ndipo Yehova anapereka Akanaani ndi Aperezi mʼmanja mwawo. Ndipo anapha anthu 10,000 ku Bezeki. 5 Ku Bezekiko anakumana ndi ankhondo a mfumu Adoni-Bezeki ndipo anamenyana nawo, ndipo Ayudawo anagonjetsa Akanaani ndi Aperezi. 6 Adoni-Bezekiyo anathawa, koma anamuthamangira ndi kumupeza, namugwira. Atamugwira anamudula zala zake zazikulu za ku manja ndi miyendo. 7 Tsono Adoni-Bezeki anati, “Mafumu 70 omwe anadulidwa zala zazikulu za ku manja ndi miyendo yawo ankatola nyenyeswa pansi pa tebulo langa. Mulungu tsopano wandibwezera zomwe ndinawachita.” Kenaka anapita naye ku Yerusalemu ndipo anafera komweko. 8 Pambuyo pake Ayuda anakathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu ndipo anawulanda. Anapha anthu ambiri ndi kutentha mzinda wonse. 9 Kenaka Ayuda anapita kukamenyana ndi Akanaani omwe amakhala ku dziko la ku mapiri, dziko la Negevi kummwera ndiponso mu zigwa. 10 Anakalimbananso ndi Akanaani amene ankakhala ku Hebroni (mzinda womwe kale unkatchedwa Kiriyati-Araba). Kumeneko anagonjetsa Sesai, Ahimani ndi Talimai. 11 Kuchokera kumeneko, iwo anakathira nkhondo anthu amene ankakhala ku Debri (mzindawu poyamba unkatchedwa Kiriati Seferi). 12 Tsono Kalebe anati, “Munthu amene angathire nkhondo mzinda wa Kiriati Seferi ndi kuwulanda, ndidzamupatsa mwana wanga Akisa kuti akhale mkazi wake.” 13 Otanieli mwana wa Kenazi, mngʼono wake wa Kalebe, ndiye anawulanda. Choncho Kalebe anamupatsa mwana wake Akisa kuti akhale mkazi wake. 14 Tsiku lina atafika Akisayo, Otanieli anamuwumiriza mkazi wakeyo kuti apemphe munda kwa Kalebe abambo ake. Pamene Akisa anatsika pa bulu wake, Kalebe anamufunsa kuti, “Kodi ukufuna ndikuchitire chiyani?” 15 Iye anayankha kuti, “Mundikomere mtima. Popeza mwandipatsa ku Negevi, kumalo kumene kulibe madzi, mundipatsenso akasupe amadzi.” Choncho Kalebe anamupatsa akasupe a kumtunda ndi a kumunsi. 16 Tsono zidzukulu za Hobabu, Mkeni uja, mpongozi wa Mose, zinachoka ku Yeriko mzinda wa migwalangwa pamodzi ndi anthu a fuko la Yuda mpaka ku chipululu chimene chili kummwera kwa Aradi ndi kukakhala ndi Aamaleki. 17 Kenaka anthu a fuko la Yuda anapita pamodzi ndi abale awo a fuko la Simeoni ndi kukagonjetsa Akanaani amene amakhala ku Zefati, ndipo mzindawo anawuwononga kwambiri. Choncho mzindawo anawutcha Horima. 18 Anthu a fuko la Yuda analandanso mzinda wa Gaza ndi dziko lonse lozungulira, mzinda wa Asikeloni pamodzi ndi dziko lake lonse lozungulira, ndi mzinda wa Ekroni pamodzi ndi dziko lonse lozungulira. 19 Yehova anathandiza anthu a fuko la Yuda. Iwo analanda dziko la kumapiri, koma sanathe kuwachotsa anthu ku zigwa, chifukwa anali ndi magaleta azitsulo. 20 Monga analonjezera Mose, Kalebe anapatsidwa Hebroni. Kalebe anapirikitsa mafuko atatu a Anaki mu mzindamo. 21 Koma fuko la Benjamini linalephera kuwachotsa Ayebusi, amene amakhala mu Yerusalemu. Choncho Ayebusiwo akukhalabe ndi fuko la Benjamini mu Yerusalemu mpaka lero. 22 A banja la Yosefe nawonso anathira nkhondo mzinda wa Beteli, ndipo Yehova anali nawo. 23 Anatumiza anthu kuti akazonde Beteli. Mzindawo kale unkatchedwa Luzi. 24 Anthu okazondawo anaona munthu akutuluka mu mzindamo ndipo anamuwuza kuti, “Tisonyeze njira yolowera mu mzindamu, ndipo ife tidzakuchitira chifundo.” 25 Choncho iye anawaonetsa njirayo, ndipo iwo anapha anthu onse mu mzindamo ndi lupanga koma munthu uja pamodzi ndi banja lake sanawaphe. 26 Ndipo iye anapita ku dziko la Ahiti, kumene anamangako mzinda nawutcha dzina lake Luzi. Mpaka lero lino mzindawo dzina lake ndi lomwelo. 27 Koma a fuko la Manase sanachotse nzika za mzinda wa Beti-Seani pamodzi ndi mʼmidzi yake yozungulira, kapena nzika za mzinda wa Taanaki ndi mʼmidzi yake yozungulira, kapenanso nzika za mzinda wa Dori ndi mʼmidzi yake yozungulira. Iwo sanapirikitse nzika za mzinda wa Ibuleamu ndi mʼmidzi yake yozungulira, kapena mzinda wa Megido ndi mʼmidzi yake yozungulira. Choncho Akanaani anapitirirabe kukhala mʼdzikomo. 28 Aisraeli atakhala amphamvu, anawagwiritsa Akanaaniwo ntchito yakalavulagaga, koma sanawapirikitse. 29 Nawonso Aefereimu sanathamangitse Akanaani amene amakhala mu Gezeri, choncho Akanaaniwo ankakhalabe pakati pawo ku Gezeriko. 30 Azebuloni sanathamangitse Akanaani amene amakhala mu Kitironi kapena a ku Nahaloli. Iwo ankakhala pakati pawo ndipo ankawagwiritsa ntchito yakalavulagaga. 31 A fuko la Aseri nawo sanathamangitse amene amakhala mu Ako, Sidoni, Ahilabu, Akizibu, Heliba, Afiki, ndi Rehobu. 32 Choncho anthu a fuko la Aseri anakhala pakati pa Akanaani amene ankakhala mʼdzikomo popeza sanawapirikitse. 33 Nalonso fuko la Nafutali silinathamangitse anthu amene ankakhala ku Beti Semesi kapena ku Beti Anati. Koma Anafutaliwo ankakhala pakati pa Akanaaniwo mʼdzikomo. Koma anthu amene ankakhala ku Beti Semesi ndi ku Beti Anati anawasandutsa kukhala ogwira ntchito yathangata. 34 Aamori anapirikitsira anthu a fuko la Dani ku dziko la ku mapiri popeza sanawalole kuti atsikire ku chigwa. 35 Aamori anatsimikiza mtima zokhalabe ku phiri la Hara-Heresi, ku Ayaloni, ndiponso ku Saalibimu. Koma a fuko la Yosefe anakula mphamvu ndipo anagwiritsa Aamoriwo ntchito yakalavulagaga. 36 Malire a Aamori anayambira ku chikweza cha Akirabimu nʼkulowera ku Sela napitirira kumapita chakumapiri ndithu.

In Other Versions

Judges 1 in the ANGEFD

Judges 1 in the ANTPNG2D

Judges 1 in the AS21

Judges 1 in the BAGH

Judges 1 in the BBPNG

Judges 1 in the BBT1E

Judges 1 in the BDS

Judges 1 in the BEV

Judges 1 in the BHAD

Judges 1 in the BIB

Judges 1 in the BLPT

Judges 1 in the BNT

Judges 1 in the BNTABOOT

Judges 1 in the BNTLV

Judges 1 in the BOATCB

Judges 1 in the BOATCB2

Judges 1 in the BOBCV

Judges 1 in the BOCNT

Judges 1 in the BOECS

Judges 1 in the BOHCB

Judges 1 in the BOHCV

Judges 1 in the BOHLNT

Judges 1 in the BOHNTLTAL

Judges 1 in the BOICB

Judges 1 in the BOILNTAP

Judges 1 in the BOITCV

Judges 1 in the BOKCV

Judges 1 in the BOKCV2

Judges 1 in the BOKHWOG

Judges 1 in the BOKSSV

Judges 1 in the BOLCB

Judges 1 in the BOLCB2

Judges 1 in the BOMCV

Judges 1 in the BONAV

Judges 1 in the BONCB

Judges 1 in the BONLT

Judges 1 in the BONUT2

Judges 1 in the BOPLNT

Judges 1 in the BOSCB

Judges 1 in the BOSNC

Judges 1 in the BOTLNT

Judges 1 in the BOVCB

Judges 1 in the BOYCB

Judges 1 in the BPBB

Judges 1 in the BPH

Judges 1 in the BSB

Judges 1 in the CCB

Judges 1 in the CUV

Judges 1 in the CUVS

Judges 1 in the DBT

Judges 1 in the DGDNT

Judges 1 in the DHNT

Judges 1 in the DNT

Judges 1 in the ELBE

Judges 1 in the EMTV

Judges 1 in the ESV

Judges 1 in the FBV

Judges 1 in the FEB

Judges 1 in the GGMNT

Judges 1 in the GNT

Judges 1 in the HARY

Judges 1 in the HNT

Judges 1 in the IRVA

Judges 1 in the IRVB

Judges 1 in the IRVG

Judges 1 in the IRVH

Judges 1 in the IRVK

Judges 1 in the IRVM

Judges 1 in the IRVM2

Judges 1 in the IRVO

Judges 1 in the IRVP

Judges 1 in the IRVT

Judges 1 in the IRVT2

Judges 1 in the IRVU

Judges 1 in the ISVN

Judges 1 in the JSNT

Judges 1 in the KAPI

Judges 1 in the KBT1ETNIK

Judges 1 in the KBV

Judges 1 in the KJV

Judges 1 in the KNFD

Judges 1 in the LBA

Judges 1 in the LBLA

Judges 1 in the LNT

Judges 1 in the LSV

Judges 1 in the MAAL

Judges 1 in the MBV

Judges 1 in the MBV2

Judges 1 in the MHNT

Judges 1 in the MKNFD

Judges 1 in the MNG

Judges 1 in the MNT

Judges 1 in the MNT2

Judges 1 in the MRS1T

Judges 1 in the NAA

Judges 1 in the NASB

Judges 1 in the NBLA

Judges 1 in the NBS

Judges 1 in the NBVTP

Judges 1 in the NET2

Judges 1 in the NIV11

Judges 1 in the NNT

Judges 1 in the NNT2

Judges 1 in the NNT3

Judges 1 in the PDDPT

Judges 1 in the PFNT

Judges 1 in the RMNT

Judges 1 in the SBIAS

Judges 1 in the SBIBS

Judges 1 in the SBIBS2

Judges 1 in the SBICS

Judges 1 in the SBIDS

Judges 1 in the SBIGS

Judges 1 in the SBIHS

Judges 1 in the SBIIS

Judges 1 in the SBIIS2

Judges 1 in the SBIIS3

Judges 1 in the SBIKS

Judges 1 in the SBIKS2

Judges 1 in the SBIMS

Judges 1 in the SBIOS

Judges 1 in the SBIPS

Judges 1 in the SBISS

Judges 1 in the SBITS

Judges 1 in the SBITS2

Judges 1 in the SBITS3

Judges 1 in the SBITS4

Judges 1 in the SBIUS

Judges 1 in the SBIVS

Judges 1 in the SBT

Judges 1 in the SBT1E

Judges 1 in the SCHL

Judges 1 in the SNT

Judges 1 in the SUSU

Judges 1 in the SUSU2

Judges 1 in the SYNO

Judges 1 in the TBIAOTANT

Judges 1 in the TBT1E

Judges 1 in the TBT1E2

Judges 1 in the TFTIP

Judges 1 in the TFTU

Judges 1 in the TGNTATF3T

Judges 1 in the THAI

Judges 1 in the TNFD

Judges 1 in the TNT

Judges 1 in the TNTIK

Judges 1 in the TNTIL

Judges 1 in the TNTIN

Judges 1 in the TNTIP

Judges 1 in the TNTIZ

Judges 1 in the TOMA

Judges 1 in the TTENT

Judges 1 in the UBG

Judges 1 in the UGV

Judges 1 in the UGV2

Judges 1 in the UGV3

Judges 1 in the VBL

Judges 1 in the VDCC

Judges 1 in the YALU

Judges 1 in the YAPE

Judges 1 in the YBVTP

Judges 1 in the ZBP