Judges 3 (BOGWICC)

1 Iyi ndi mitundu ya anthu yomwe Yehova anayisiya kuti ayese nayo Aisraeli amene sanadziwe kumenya nkhondo mu Kanaani 2 (Yehova anachita izi kuti Aisraeli onse aphunzire kumenya nkhondo; makamaka amene nʼkale lonse sanadziwe kumenya nkhondo. 3 Mitundu ya anthuyo ndi: Mafumu asanu a Afilisti, Akanaani onse, Asidoni, ndi Ahivi amene ankakhala ku mapiri a Lebanoni kuyambira ku phiri la Baala-Herimoni mpaka ku Lebo Hamati. 4 Iwowa Yehova anawasiya kuti aziyesa nawo Aisraeli kuti aone ngati angamvere malamulo a Yehova, amene anapatsa makolo awo kudzera mwa Mose. 5 Choncho Aisraeli anakhala pakati pa Akanaani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. 6 Tsono Aisraeli aja amalola ana awo aamuna ndi aakazi kuti azikwatira ndi kukwatiwa ndi anthu amitundu ina. Kenaka anayamba kupembedza milungu yawo. 7 Aisraeli anachita zinthu zoyipira Yehova. Iwowa anayiwala Yehova Mulungu wawo ndi kumatumikira Abaala ndi Asera. 8 Choncho Yehova anawapsera mtima Aisraeliwo ndipo anawagulitsa kwa Kusani-Risataimu mfumu ya ku Mesopotamiya. Choncho Aisraeli anakhala pansi pa ulamuliro wake zaka zisanu ndi zitatu. 9 Koma pamene Aisraeliwo analirira kwa Yehova, Iye anawawutsira mpulumutsi, Otanieli mwana wamwamuna wa Kenazi, mngʼono wake wa Kalebe. Iyeyu ndiye anawapulumutsa. 10 Mzimu wa Yehova unatsika pa iye, choncho anasanduka mtsogoleri wa Israeli. Iye anapita kukamenya nkhondo, ndipo Yehova anapereka Kusani-Risataimu mfumu ya Aaramu mʼmanja mwake. Choncho anayigonjetsa. 11 Ndipo mʼdzikomo munakhala mtendere zaka makumi anayi. Kenaka Otanieli mwana wa Kenazi anamwalira. 12 Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova. Tsono Yehova anapatsa mphamvu Egiloni, mfumu ya Mowabu kuti alimbane ndi Aisraeli aja popeza anachita zinthu zoyipira Yehova. 13 Egiloniyo anamemeza Aamori ndi Aamaleki kupita kukamenyana ndi Israeli, ndipo analanda Yeriko, mzinda wa migwalangwa. 14 Aisraeli anatumikira ngati akapolo Egiloni mfumu ya Mowabu kwa zaka 18. 15 Aisraeli analiranso kwa Yehova, ndipo Iye anawawutsira mpulumutsi, Ehudi. Iyeyu anali mwana wa Gera, munthu wamanzere, wa fuko la Benjamini. Aisraeli ankatumiza msonkho kwa Egiloni, mfumu ya Mowabu, kudzera kwa Ehudi. 16 Ndipo Ehudi anapanga lupanga lakuthwa kuwiri lotalika masentimita makumi asanu, ndipo anamangirira lupangalo pa ntchafu yake ya kumanja mʼkati mwa zovala zake. 17 Iye anakapereka msonkho kwa Egiloni, mfumu ya Mowabu, amene anali munthu wonenepa kwambiri. 18 Ehudi atapereka msonkhowo, anawuza anthu amene ananyamula msonkhowo kuti azipita. 19 Iye mwini anabwerera pamalo a miyala yozokotedwa ku Giligala ndipo anati, “Zikomo mfumu, ine ndili ndi mawu achinsinsi kuti ndikuwuzeni.”Mfumuyo inawuza onse amene amayitumikira kuti akhale chete, ndipo kenaka anawatulutsa. 20 Kenaka Ehudi anayandikira pafupi ndi mfumuyo, ndipo iyo inakhala yokha mʼchipinda chapamwamba, mozizira bwino. Tsono Ehudi anati, “Ndili ndi mawu ochokera kwa Mulungu woti ndikuwuzeni.” Mfumuyo itadzuka pa mpando wake waufumu, 21 Ehudi ndi dzanja lake lamanzere, anasolola lupanga pa ntchafu yake ya kumanja ndi kubaya nalo mfumuyo pa mimba. 22 Lupanga linalowa mʼmimba pamodzi ndi chogwirira chake. Mafuta anaphimba lupangalo popeza silinatulutsidwe mʼmimbamo. Ndiponso matumbo anatuluka. 23 Kenaka Ehudi anatuluka panja pa khonde, atatseka ndi kukhoma zitseko za chipinda chapamwambacho. 24 Ehudi atachoka, atumiki a mfumu aja anabwera, ndipo ataona kuti zitseko za chipinda chapamwamba zinali zokhoma anaganiza kuti mwina mfumu ikudzithandiza mʼkatimo. 25 Iwo anadikira nthawi yayitali koma popanda chochitika. Koma ataona kuti mfumuyo sikutsekulabe zitseko za chipindacho, iwo anatenga makiyi ndi kutsekula zitsekozo, ndipo anangoona mbuye wawo atagwera pansi, ali wakufa. 26 Ehudi anathawa pamene iwo ankadikira. Iye anadzera ku malo a miyala yozokotedwa kuja ndi kuthawa kupita ku Seiri. 27 Atafika kumeneko, anayimba lipenga ku dziko la ku mapiri la Efereimu. Iye akutsogolera, Aisraeli onse anatsika naye pamodzi kuchoka ku mapiriko. 28 Iye anawawuza kuti, “Nditsatireni, chifukwa Yehova wapereka Amowabu, adani anu mʼmanja mwanu.” Choncho anthuwo anamutsatira, nalanda madooko a Yorodani opita ku Mowabu. Iwo sanalole kuti wina aliyense awoloke. 29 Nthawi imeneyo anapha Amowabu pafupifupi 10,000. Ophedwawo anali anthu amphamvu komanso odziwa kumenya nkhondo, ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anathawa. 30 Tsiku limenelo Amowabu anakhala pansi pa ulamuliro wa Israeli, ndipo dzikolo linakhala pa mtendere kwa zaka 80. 31 Ehudi atamwalira, panabwera Samugara mwana wa Anati. Iye anapha Afilisti 600 ndi ndodo yomenyera ngʼombe. Nayenso anapulumutsa Israeli.

In Other Versions

Judges 3 in the ANGEFD

Judges 3 in the ANTPNG2D

Judges 3 in the AS21

Judges 3 in the BAGH

Judges 3 in the BBPNG

Judges 3 in the BBT1E

Judges 3 in the BDS

Judges 3 in the BEV

Judges 3 in the BHAD

Judges 3 in the BIB

Judges 3 in the BLPT

Judges 3 in the BNT

Judges 3 in the BNTABOOT

Judges 3 in the BNTLV

Judges 3 in the BOATCB

Judges 3 in the BOATCB2

Judges 3 in the BOBCV

Judges 3 in the BOCNT

Judges 3 in the BOECS

Judges 3 in the BOHCB

Judges 3 in the BOHCV

Judges 3 in the BOHLNT

Judges 3 in the BOHNTLTAL

Judges 3 in the BOICB

Judges 3 in the BOILNTAP

Judges 3 in the BOITCV

Judges 3 in the BOKCV

Judges 3 in the BOKCV2

Judges 3 in the BOKHWOG

Judges 3 in the BOKSSV

Judges 3 in the BOLCB

Judges 3 in the BOLCB2

Judges 3 in the BOMCV

Judges 3 in the BONAV

Judges 3 in the BONCB

Judges 3 in the BONLT

Judges 3 in the BONUT2

Judges 3 in the BOPLNT

Judges 3 in the BOSCB

Judges 3 in the BOSNC

Judges 3 in the BOTLNT

Judges 3 in the BOVCB

Judges 3 in the BOYCB

Judges 3 in the BPBB

Judges 3 in the BPH

Judges 3 in the BSB

Judges 3 in the CCB

Judges 3 in the CUV

Judges 3 in the CUVS

Judges 3 in the DBT

Judges 3 in the DGDNT

Judges 3 in the DHNT

Judges 3 in the DNT

Judges 3 in the ELBE

Judges 3 in the EMTV

Judges 3 in the ESV

Judges 3 in the FBV

Judges 3 in the FEB

Judges 3 in the GGMNT

Judges 3 in the GNT

Judges 3 in the HARY

Judges 3 in the HNT

Judges 3 in the IRVA

Judges 3 in the IRVB

Judges 3 in the IRVG

Judges 3 in the IRVH

Judges 3 in the IRVK

Judges 3 in the IRVM

Judges 3 in the IRVM2

Judges 3 in the IRVO

Judges 3 in the IRVP

Judges 3 in the IRVT

Judges 3 in the IRVT2

Judges 3 in the IRVU

Judges 3 in the ISVN

Judges 3 in the JSNT

Judges 3 in the KAPI

Judges 3 in the KBT1ETNIK

Judges 3 in the KBV

Judges 3 in the KJV

Judges 3 in the KNFD

Judges 3 in the LBA

Judges 3 in the LBLA

Judges 3 in the LNT

Judges 3 in the LSV

Judges 3 in the MAAL

Judges 3 in the MBV

Judges 3 in the MBV2

Judges 3 in the MHNT

Judges 3 in the MKNFD

Judges 3 in the MNG

Judges 3 in the MNT

Judges 3 in the MNT2

Judges 3 in the MRS1T

Judges 3 in the NAA

Judges 3 in the NASB

Judges 3 in the NBLA

Judges 3 in the NBS

Judges 3 in the NBVTP

Judges 3 in the NET2

Judges 3 in the NIV11

Judges 3 in the NNT

Judges 3 in the NNT2

Judges 3 in the NNT3

Judges 3 in the PDDPT

Judges 3 in the PFNT

Judges 3 in the RMNT

Judges 3 in the SBIAS

Judges 3 in the SBIBS

Judges 3 in the SBIBS2

Judges 3 in the SBICS

Judges 3 in the SBIDS

Judges 3 in the SBIGS

Judges 3 in the SBIHS

Judges 3 in the SBIIS

Judges 3 in the SBIIS2

Judges 3 in the SBIIS3

Judges 3 in the SBIKS

Judges 3 in the SBIKS2

Judges 3 in the SBIMS

Judges 3 in the SBIOS

Judges 3 in the SBIPS

Judges 3 in the SBISS

Judges 3 in the SBITS

Judges 3 in the SBITS2

Judges 3 in the SBITS3

Judges 3 in the SBITS4

Judges 3 in the SBIUS

Judges 3 in the SBIVS

Judges 3 in the SBT

Judges 3 in the SBT1E

Judges 3 in the SCHL

Judges 3 in the SNT

Judges 3 in the SUSU

Judges 3 in the SUSU2

Judges 3 in the SYNO

Judges 3 in the TBIAOTANT

Judges 3 in the TBT1E

Judges 3 in the TBT1E2

Judges 3 in the TFTIP

Judges 3 in the TFTU

Judges 3 in the TGNTATF3T

Judges 3 in the THAI

Judges 3 in the TNFD

Judges 3 in the TNT

Judges 3 in the TNTIK

Judges 3 in the TNTIL

Judges 3 in the TNTIN

Judges 3 in the TNTIP

Judges 3 in the TNTIZ

Judges 3 in the TOMA

Judges 3 in the TTENT

Judges 3 in the UBG

Judges 3 in the UGV

Judges 3 in the UGV2

Judges 3 in the UGV3

Judges 3 in the VBL

Judges 3 in the VDCC

Judges 3 in the YALU

Judges 3 in the YAPE

Judges 3 in the YBVTP

Judges 3 in the ZBP