Judges 4 (BOGWICC)

1 Ehudi atamwalira, Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova. 2 Choncho Yehova anawapereka mʼmanja mwa Yabini, mfumu ya ku Kanaani, imene inkalamulira ku Hazori. Mkulu wa ankhondo ake anali Sisera, amene ankakhala ku Haroseti-Hagoyimu. 3 Aisraeli analira kwa Yehova kuti awathandize, chifukwa Sisera anali ndi magaleta achitsulo 900 ndipo anazunza Aisraeli mwankhanza kwa zaka makumi awiri. 4 Debora, mneneri wamkazi, mkazi wake wa Rapidoti ndiye ankatsogolera Israeli nthawi imeneyo. 5 Iye ankakhala pansi pa mtengo wa mgwalangwa wa Debora, pakati pa Rama ndi Beteli mʼdziko la ku mapiri la Efereimu, ndipo Aisraeli ankapita kwa iye kuti akaweruze milandu yawo. 6 Debora uja anatuma munthu kuti akayitane Baraki mwana wa Abinoamu wa ku Kedesi mʼdziko la Nafutali ndipo anati kwa iye, “Yehova Mulungu wa Israeli akukulamula iwe kuti, ‘Pita kasonkhanitse anthu ku phiri la Tabori. Ubwere nawo anthu 10,000 a fuko la Nafutali ndi a fuko la Zebuloni. 7 Ine ndidzakokera Sisera mkulu wa ankhondo a Yabini pamodzi ndi magaleta ake ndi asilikali ake kwa inu ku mtsinje wa Kisoni ndipo ndidzamupereka mʼmanja mwanu.’ ” 8 Baraki anamuyankha kuti, “Mukapita nane limodzi ine ndipita. Koma ngati sitipitira limodzi, inenso sindipita.” 9 Debora anati, “Chabwino, ine ndipita nawe limodzi. Koma mudziwe kuti inu simudzalandirapo ulemu pa zimene mwachitazi popeza Yehova wapereka Sisera mʼmanja mwa munthu wamkazi.” Choncho Debora ananyamuka kupita ku Kedesi pamodzi ndi Baraki. 10 Baraki anayitana mafuko a Zebuloni ndi Nafutali kuti abwere ku Kedesi. Anthu 10,000 anamutsatira, ndipo Debora anapita naye pamodzi. 11 Nthawi imeneyo nʼkuti Mkeni wina dzina lake Heberi atalekana ndi Akeni anzake, zidzukulu za Hobabu, mlamu wa Mose, nakamanga tenti yake pafupi ndi mtengo wa thundu ku Zananimu pafupi ndi Kedesi. 12 Pamene Sisera anamva kuti Baraki mwana wa Abinoamu wapita ku phiri la Tabori, 13 anasonkhanitsa magaleta ake achitsulo 900 ndi anthu onse amene anali naye ndipo anachoka ku Haroseti-Hagoyimu kupita ku mtsinje wa Kisoni. 14 Debora anawuza Baraki kuti, “Dzukani! Paja ndi lero limene Yehova wapereka Sisera mʼmanja mwako. Kodi Yehova sanakhale akukutsogolerani?” Choncho Baraki anatsika phiri la Tabori, anthu 10,000 akumutsata. 15 Yehova anasokoneza Sisera ndi magaleta ake pamodzi ndi ankhondo ake onse. Baraki ndi anthu ake anawapirikitsa ndipo Sisera anatsika pa galeta yake nayamba kuthawa pansi. 16 Baraki analondola magaletawo pamodzi ndi ankhondo onse mpaka ku Haroseti-Hagoyimu, ndipo ankhondo onse a Sisera anaphedwa ndi lupanga. Palibe munthu ndi mmodzi yemwe anatsala. 17 Komabe Sisera anathawa pansi mpaka anakafika ku tenti ya Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni uja, chifukwa panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori ndi banja la Heberi, Mkeni uja. 18 Yaeli anatuluka kukachingamira Sisera ndipo anati, “Bwerani mbuye wanga, lowani momwemo musaope.” Choncho analowa mʼtenti muja, ndipo anamufunditsa chofunda. 19 Anati, “Ndili ndi ludzu, chonde patseniko madzi pangʼono akumwa, ndili ndi ludzu.” Mkaziyo anatsekula thumba la chikopa mmene munali mkaka, namupatsa kuti amwe, ndipo anamufunditsanso. 20 Kenaka anawuza mkaziyo kuti, “Muyime pa khomo la tentili, ndipo munthu wina akabwera kudzakufunsani kuti, ‘Kodi kwafika munthu wina kuno?’ Inu muyankha kuti, ‘Ayi.’ ” 21 Koma Yaeli mkazi wa Heberi, anatenga chikhomo cha tenti ndi hamara ndi kupita mwakachetechete kwa Sisera uja. Tsono Sisera ali mtulo chifukwa chotopa, mkazi uja anamukhomera chikhomo chija mʼmutu mwake. Chinatulukira kwinaku mpaka kulowa mʼnthaka, ndipo anafa pomwepo. 22 Baraki atafika akulondola Sisera, Yaeli anatuluka kukamuchingamira namuwuza kuti, “Lowani mudzaone munthu amene mukumufunafuna.” Tsono atalowa anangoona Sisera ali thapsa pansi wakufa ndi chikhomo chili mʼmutu mwake. 23 “Choncho pa tsiku limenelo Mulungu anagonjetsa Yabini mfumu ya Akanaani, pamaso pa Aisraeli. 24 Ndipo Aisraeli anapanikizabe Yabini, mfumu ya Akanaani, mpaka kumuwonongeratu.

In Other Versions

Judges 4 in the ANGEFD

Judges 4 in the ANTPNG2D

Judges 4 in the AS21

Judges 4 in the BAGH

Judges 4 in the BBPNG

Judges 4 in the BBT1E

Judges 4 in the BDS

Judges 4 in the BEV

Judges 4 in the BHAD

Judges 4 in the BIB

Judges 4 in the BLPT

Judges 4 in the BNT

Judges 4 in the BNTABOOT

Judges 4 in the BNTLV

Judges 4 in the BOATCB

Judges 4 in the BOATCB2

Judges 4 in the BOBCV

Judges 4 in the BOCNT

Judges 4 in the BOECS

Judges 4 in the BOHCB

Judges 4 in the BOHCV

Judges 4 in the BOHLNT

Judges 4 in the BOHNTLTAL

Judges 4 in the BOICB

Judges 4 in the BOILNTAP

Judges 4 in the BOITCV

Judges 4 in the BOKCV

Judges 4 in the BOKCV2

Judges 4 in the BOKHWOG

Judges 4 in the BOKSSV

Judges 4 in the BOLCB

Judges 4 in the BOLCB2

Judges 4 in the BOMCV

Judges 4 in the BONAV

Judges 4 in the BONCB

Judges 4 in the BONLT

Judges 4 in the BONUT2

Judges 4 in the BOPLNT

Judges 4 in the BOSCB

Judges 4 in the BOSNC

Judges 4 in the BOTLNT

Judges 4 in the BOVCB

Judges 4 in the BOYCB

Judges 4 in the BPBB

Judges 4 in the BPH

Judges 4 in the BSB

Judges 4 in the CCB

Judges 4 in the CUV

Judges 4 in the CUVS

Judges 4 in the DBT

Judges 4 in the DGDNT

Judges 4 in the DHNT

Judges 4 in the DNT

Judges 4 in the ELBE

Judges 4 in the EMTV

Judges 4 in the ESV

Judges 4 in the FBV

Judges 4 in the FEB

Judges 4 in the GGMNT

Judges 4 in the GNT

Judges 4 in the HARY

Judges 4 in the HNT

Judges 4 in the IRVA

Judges 4 in the IRVB

Judges 4 in the IRVG

Judges 4 in the IRVH

Judges 4 in the IRVK

Judges 4 in the IRVM

Judges 4 in the IRVM2

Judges 4 in the IRVO

Judges 4 in the IRVP

Judges 4 in the IRVT

Judges 4 in the IRVT2

Judges 4 in the IRVU

Judges 4 in the ISVN

Judges 4 in the JSNT

Judges 4 in the KAPI

Judges 4 in the KBT1ETNIK

Judges 4 in the KBV

Judges 4 in the KJV

Judges 4 in the KNFD

Judges 4 in the LBA

Judges 4 in the LBLA

Judges 4 in the LNT

Judges 4 in the LSV

Judges 4 in the MAAL

Judges 4 in the MBV

Judges 4 in the MBV2

Judges 4 in the MHNT

Judges 4 in the MKNFD

Judges 4 in the MNG

Judges 4 in the MNT

Judges 4 in the MNT2

Judges 4 in the MRS1T

Judges 4 in the NAA

Judges 4 in the NASB

Judges 4 in the NBLA

Judges 4 in the NBS

Judges 4 in the NBVTP

Judges 4 in the NET2

Judges 4 in the NIV11

Judges 4 in the NNT

Judges 4 in the NNT2

Judges 4 in the NNT3

Judges 4 in the PDDPT

Judges 4 in the PFNT

Judges 4 in the RMNT

Judges 4 in the SBIAS

Judges 4 in the SBIBS

Judges 4 in the SBIBS2

Judges 4 in the SBICS

Judges 4 in the SBIDS

Judges 4 in the SBIGS

Judges 4 in the SBIHS

Judges 4 in the SBIIS

Judges 4 in the SBIIS2

Judges 4 in the SBIIS3

Judges 4 in the SBIKS

Judges 4 in the SBIKS2

Judges 4 in the SBIMS

Judges 4 in the SBIOS

Judges 4 in the SBIPS

Judges 4 in the SBISS

Judges 4 in the SBITS

Judges 4 in the SBITS2

Judges 4 in the SBITS3

Judges 4 in the SBITS4

Judges 4 in the SBIUS

Judges 4 in the SBIVS

Judges 4 in the SBT

Judges 4 in the SBT1E

Judges 4 in the SCHL

Judges 4 in the SNT

Judges 4 in the SUSU

Judges 4 in the SUSU2

Judges 4 in the SYNO

Judges 4 in the TBIAOTANT

Judges 4 in the TBT1E

Judges 4 in the TBT1E2

Judges 4 in the TFTIP

Judges 4 in the TFTU

Judges 4 in the TGNTATF3T

Judges 4 in the THAI

Judges 4 in the TNFD

Judges 4 in the TNT

Judges 4 in the TNTIK

Judges 4 in the TNTIL

Judges 4 in the TNTIN

Judges 4 in the TNTIP

Judges 4 in the TNTIZ

Judges 4 in the TOMA

Judges 4 in the TTENT

Judges 4 in the UBG

Judges 4 in the UGV

Judges 4 in the UGV2

Judges 4 in the UGV3

Judges 4 in the VBL

Judges 4 in the VDCC

Judges 4 in the YALU

Judges 4 in the YAPE

Judges 4 in the YBVTP

Judges 4 in the ZBP