Judges 6 (BOGWICC)

1 Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova, choncho Yehova anawapereka mʼmanja mwa Amidiyani kwa zaka zisanu ndi ziwiri. 2 Amidiyani anapondereza Aisraeli. Tsono chifukwa cha Amidiyaniwa, Aisraeli anakonza malo obisalamo mʼmapiri ndi mʼmapanga. Anamanganso malinga. 3 Aisraeli amati akadzala mbewu, Amidiyani, Aamaleki ndi anthu ena akummawa amabwera ndi kudzawathira nkhondo. 4 Iwo anamanga misasa mʼdzikomo ndi kuwononga zokolola zawo zonse mpaka ku Gaza, ndipo sanawasiyireko chamoyo chilichonse Aisraeliwo, kaya nkhosa kapena ngʼombe ndi bulu yemwe. 5 Iwo ankabwera ndi zoweta zawo ndi matenti awo omwe. Ankabwera ambiri ngati dzombe, motero kuti kunali kovuta kuwawerenga anthuwo ndi ngamira zawo. Tsono iwo ankabwera ndi kuwononga dziko lonse. 6 Aisraeli anasauka chifukwa cha Amidiyani ndipo analirira kwa Yehova kuti awathandize. 7 Pamene Aisraeli analirira kwa Yehova chifukwa cha Amidiyaniwo, 8 Iye anawatumizira mneneri amene anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndine amene ndinakutsogolerani kuchokera ku Igupto. Ndinakutulutsani mʼdziko la ukapolo. 9 Ine ndinakupulumutsani ku ulamuliro wa Igupto komanso mʼmanja mwa amene amakuzunzani. Ndinawathamangitsa adani anu inu mukufika, ndikukupatsani dziko lawo.’ 10 Ndipo ndinakuwuzani kuti, ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu; musapembedze Milungu ya Aamori amene mukukhala mʼdziko lawo.’ Koma inu simunandimvere.” 11 Tsiku lina mngelo wa Yehova anabwera ku Ofura ndi kukhala pansi pa tsinde pa mtengo wa thundu umene unali wa Yowasi Mwabiezeri. Tsono Gideoni, mwana wake nʼkuti pa nthawiyo akupuntha tirigu mʼmalo ofinyira mphesa mowabisalira Amidiyani. 12 Tsono mngelo wa Yehova uja anamuonekera Gideoni nati kwa iye, “Yehova ali nawe, iwe munthu wamphamvu ndi wolimba mtima.” 13 Gideoni anayankha, “Koma mbuye wanga, ngati Yehova ali nafedi, nʼchifukwa chiyani zonsezi zationekera? Nanga ntchito zake zodabwitsa zimene makolo athu anatiwuza pamene anati, ‘Yehova anatitulutsa ku dziko la Igupto,’ zili kuti? Koma tsopano Yehova watitaya ndi kutipereka mʼmanja mwa Amidiyani.” 14 Yehova anamuyangʼana namuwuza kuti, “Pita ndi mphamvu zomwe uli nazo, ukapulumutse Aisraeli mʼmanja mwa Amidiyani. Kodi si ndine amene ndakutuma?” 15 Koma Gideoni anafunsa kuti, “Kodi Ambuye anga ine ndingapulumutse bwanji Israeli? Mbumba yanga ndi yopanda mphamvu mu fuko la Manase, ndiponso ine ndine wamngʼono kwambiri mʼbanja mwa abambo anga.” 16 Yehova anamuyankha kuti, “Ine ndidzakhala nawe, ndipo Amidiyaniwo udzawagonjetsa ngati munthu mmodzi.” 17 Gideoni anati, “Ngati tsopano mwandikomera mtima, ndionetseni chizindikiro kusonyeza kuti ndinudi mukuyankhula ndi ine. 18 Chonde musachoke msanga mpaka nditabwerera kwa inu ndi chopereka changa cha chakudya kudzachipereka kwa inu.”Ndipo Yehova anamuwuza kuti, “Ine ndikudikira mpaka utabweranso.” 19 Gideoni analowa mʼnyumba, ndipo anakakonza mwana wambuzi, nakonzanso makeke wopanda yisiti a ufa wa makilogalamu khumi. Nayika nyamayo mʼdengu ndipo msuzi wake anawuthira mu mʼphika. Anabwera nazo ndi kukazipereka kwa mngelo uja pa tsinde pa mtengo wa thundu paja. 20 Mngelo wa Mulungu anamuwuza iye kuti, “Tenga nyamayi pamodzi ndi makekewa, uziyike pa mwala uwu ndi kuthirapo msuziwu.” Ndipo Gideoni anatero. 21 Mngelo wa Yehova anatenga msonga ya ndodo imene inali mʼmanja mwake nakhudza nayo nyama ndi makeke aja. Nthawi yomweyo moto unabuka pa thanthwepo ndi kupsereza nyama yonse ndi makeke aja. Ndipo mngelo wa Yehova sanaonekenso. 22 Apo Gideoni anazindikira kuti analidi mngelo wa Ambuye, ndipo anati, “Kalanga ine Yehova Wamphamvuzonse! Ine ndaona mngelo wa Yehova ndi maso!” 23 Koma Yehova anamuwuza kuti, “Mtendere ukhale ndi iwe! Usachite mantha, sufa ayi.” 24 Choncho Gideoni anamanga guwa lansembe la Yehova pamenepo ndipo analitcha kuti, Yehova ndiye mtendere. Kufikira lero lino guwali lilipo ku Ofura wa Mwabiezeri. 25 Usiku womwewo Yehova anati kwa Gideoni, “Tenga ngʼombe ya mphongo ya abambo ako, ngʼombe ina yachiwiri ya zaka zisanu ndi ziwiri ndipo ugwetse guwa la Baala limene abambo ako ali nalo, ndi kugwetsanso fano la Asera limene lili pafupi pake. 26 Kenaka umangire Yehova Mulungu wako guwa lansembe ndi miyala yoyala bwino pamwamba pa chiwunda chimenecho. Utenge ngʼombe ya mphongo yachiwiri ija ndipo uyipereke ngati nsembe yopsereza pogwiritsa ntchito mitengo ya fano la Asera imene udule ngati nkhunizo.” 27 Choncho Gideoni anatenga antchito ake khumi nachita monga Yehova anamuwuzira. Ndipo popeza ankaopa anthu a pa banja lake ndiponso anthu a mʼmudzimo sanachite zimenezi masana koma usiku. 28 Anthu a mu mzindamo atadzuka mʼmamawa anangoona guwa la Baala litagwetsedwa ndi fano la Asera limene linali pamwamba pake litadulidwa ndiponso ngʼombe yamphongo yachiwiri ija itaperekedwa ngati nsembe yopsereza pa guwa limene linamangidwa lija. 29 Iwo anafunsana wina ndi mnzake, “Wachita zimenezi ndani?”Atafufuza ndi kufunsafunsa, analingalira kuti, “Gideoni mwana wa Yowasi ndiye wachita zimenezi.” 30 Ndipo anthuwo anawuza Yowasi kuti, “Tulutsa mwana wako, ayenera kufa chifukwa wagumula guwa lansembe la Baala ndipo wadula fano la Asera lomwe linali pamwamba pake.” 31 Koma Yowasi anawuza anthu amene anamuzungulirawo kuti, “Kodi inu mukuti mukhale woyankhulira Baala mlandu? Kodi ndinu amene mukuti mumupulumutse? Amene akufuna kumumenyera nkhondo Baala akhala atafa pofika mmawa! Ngati Baalayo ndi mulungudi, musiyeni adzimenyere yekha nkhondo popeza munthu wina wamugwetsera guwa lansembe lake.” 32 Choncho tsiku limenelo Gideoni anatchedwa, Yeru-Baala, kutanthauza kuti, “Baala alimbana naye, popeza anagwetsa guwa lake la nsembe.” 33 Tsopano Amidiyani, Amaleki ndi anthu ena akummawa anasonkhana ndipo atawoloka Yorodani anakamanga zinthando za nkhondo ku chigwa cha Yezireeli. 34 Ndipo Mzimu wa Yehova unatsikira pa Gideoni, ndipo anayimba lipenga kuyitana Abiezeri kuti amutsatire iye. 35 Iye anatumiza amithenga mʼdziko lonse la Manase kuti akamenye nkhondo ndipo Amanase anayitanidwanso kuti amutsate. Anatumanso amithenga kwa Aseri, Azebuloni ndi Anafutali, ndipo onsewo anapita kukakumana naye. 36 Gideoni anati kwa Mulungu, “Ngati mudzapulumutsa Israeli ndi dzanja langa monga mwalonjezeramu, 37 onani, ine ndiyala ubweya wankhosa pa malo opunthira tirigu. Ngati mame adzagwera pa ubweya wankhosa pokhapa, pa nthaka ponse pakhala powuma, ndiye ndidziwa kuti mudzapulumutsadi Israeli ndi dzanja langa monga mwanenera.” 38 Ndipo zimenezi zinachitikadi. Gideoni atadzuka mʼmamawa ndi kuwufinya ubweya uja, anafinya madzi odzaza mtsuko. 39 Kenaka Gideoni anati kwa Mulungu, “Musandikwiyire. Mundilole ndiyankhule kamodzi kokhaka. Ndiyeseko kamodzi kokha ndi ubweyawu kuti pa ubweya pokhapa pakhale powuma koma pa nthaka ponse pakhale ponyowa ndi mame.” 40 Ndipo Mulungu anachita zomwezo usiku umenewo. Pa ubweya pokha panali powuma, koma pa nthaka ponse panagwa mame.

In Other Versions

Judges 6 in the ANGEFD

Judges 6 in the ANTPNG2D

Judges 6 in the AS21

Judges 6 in the BAGH

Judges 6 in the BBPNG

Judges 6 in the BBT1E

Judges 6 in the BDS

Judges 6 in the BEV

Judges 6 in the BHAD

Judges 6 in the BIB

Judges 6 in the BLPT

Judges 6 in the BNT

Judges 6 in the BNTABOOT

Judges 6 in the BNTLV

Judges 6 in the BOATCB

Judges 6 in the BOATCB2

Judges 6 in the BOBCV

Judges 6 in the BOCNT

Judges 6 in the BOECS

Judges 6 in the BOHCB

Judges 6 in the BOHCV

Judges 6 in the BOHLNT

Judges 6 in the BOHNTLTAL

Judges 6 in the BOICB

Judges 6 in the BOILNTAP

Judges 6 in the BOITCV

Judges 6 in the BOKCV

Judges 6 in the BOKCV2

Judges 6 in the BOKHWOG

Judges 6 in the BOKSSV

Judges 6 in the BOLCB

Judges 6 in the BOLCB2

Judges 6 in the BOMCV

Judges 6 in the BONAV

Judges 6 in the BONCB

Judges 6 in the BONLT

Judges 6 in the BONUT2

Judges 6 in the BOPLNT

Judges 6 in the BOSCB

Judges 6 in the BOSNC

Judges 6 in the BOTLNT

Judges 6 in the BOVCB

Judges 6 in the BOYCB

Judges 6 in the BPBB

Judges 6 in the BPH

Judges 6 in the BSB

Judges 6 in the CCB

Judges 6 in the CUV

Judges 6 in the CUVS

Judges 6 in the DBT

Judges 6 in the DGDNT

Judges 6 in the DHNT

Judges 6 in the DNT

Judges 6 in the ELBE

Judges 6 in the EMTV

Judges 6 in the ESV

Judges 6 in the FBV

Judges 6 in the FEB

Judges 6 in the GGMNT

Judges 6 in the GNT

Judges 6 in the HARY

Judges 6 in the HNT

Judges 6 in the IRVA

Judges 6 in the IRVB

Judges 6 in the IRVG

Judges 6 in the IRVH

Judges 6 in the IRVK

Judges 6 in the IRVM

Judges 6 in the IRVM2

Judges 6 in the IRVO

Judges 6 in the IRVP

Judges 6 in the IRVT

Judges 6 in the IRVT2

Judges 6 in the IRVU

Judges 6 in the ISVN

Judges 6 in the JSNT

Judges 6 in the KAPI

Judges 6 in the KBT1ETNIK

Judges 6 in the KBV

Judges 6 in the KJV

Judges 6 in the KNFD

Judges 6 in the LBA

Judges 6 in the LBLA

Judges 6 in the LNT

Judges 6 in the LSV

Judges 6 in the MAAL

Judges 6 in the MBV

Judges 6 in the MBV2

Judges 6 in the MHNT

Judges 6 in the MKNFD

Judges 6 in the MNG

Judges 6 in the MNT

Judges 6 in the MNT2

Judges 6 in the MRS1T

Judges 6 in the NAA

Judges 6 in the NASB

Judges 6 in the NBLA

Judges 6 in the NBS

Judges 6 in the NBVTP

Judges 6 in the NET2

Judges 6 in the NIV11

Judges 6 in the NNT

Judges 6 in the NNT2

Judges 6 in the NNT3

Judges 6 in the PDDPT

Judges 6 in the PFNT

Judges 6 in the RMNT

Judges 6 in the SBIAS

Judges 6 in the SBIBS

Judges 6 in the SBIBS2

Judges 6 in the SBICS

Judges 6 in the SBIDS

Judges 6 in the SBIGS

Judges 6 in the SBIHS

Judges 6 in the SBIIS

Judges 6 in the SBIIS2

Judges 6 in the SBIIS3

Judges 6 in the SBIKS

Judges 6 in the SBIKS2

Judges 6 in the SBIMS

Judges 6 in the SBIOS

Judges 6 in the SBIPS

Judges 6 in the SBISS

Judges 6 in the SBITS

Judges 6 in the SBITS2

Judges 6 in the SBITS3

Judges 6 in the SBITS4

Judges 6 in the SBIUS

Judges 6 in the SBIVS

Judges 6 in the SBT

Judges 6 in the SBT1E

Judges 6 in the SCHL

Judges 6 in the SNT

Judges 6 in the SUSU

Judges 6 in the SUSU2

Judges 6 in the SYNO

Judges 6 in the TBIAOTANT

Judges 6 in the TBT1E

Judges 6 in the TBT1E2

Judges 6 in the TFTIP

Judges 6 in the TFTU

Judges 6 in the TGNTATF3T

Judges 6 in the THAI

Judges 6 in the TNFD

Judges 6 in the TNT

Judges 6 in the TNTIK

Judges 6 in the TNTIL

Judges 6 in the TNTIN

Judges 6 in the TNTIP

Judges 6 in the TNTIZ

Judges 6 in the TOMA

Judges 6 in the TTENT

Judges 6 in the UBG

Judges 6 in the UGV

Judges 6 in the UGV2

Judges 6 in the UGV3

Judges 6 in the VBL

Judges 6 in the VDCC

Judges 6 in the YALU

Judges 6 in the YAPE

Judges 6 in the YBVTP

Judges 6 in the ZBP