Jeremiah 11 (BOGWICC)
1 Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, 2 “Imvani mawu a pangano ili, ndipo uwawuze anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. 3 Awuze kuti Yehova, Mulungu wa Israeli akuti ‘adzakhala wotembereredwa munthu amene samvera mawu a pangano ili. 4 Awa anali mawu amene ndinalamulira makolo anu nditawatulutsa mu Igupto, kuchoka mʼngʼanjo yamoto.’ Ine ndinati, ‘Mverani Ine ndi kuchita chilichonse chimene ndakulamulirani. Mukatero mudzakhala anthu anga ndi Ine ndidzakhala Mulungu wanu. 5 Tsono Ine ndidzakwaniritsa lumbiro lomwe ndinalumbira kwa makolo anu kuti ndidzawapatsa dziko loyenda mkaka ndi uchi,’ dziko lomwe inu lero mukukhalamo.”Tsono Ine ndinayankha kuti, “Ameni, Yehova.” 6 Yehova anandiwuza kuti, “Lengeza mawu onsewa mʼmizinda yonse ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu: ‘Mverani mawu a pangano ili ndi kuzitsatira. 7 Kuyambira nthawi imene ndinatulutsa makolo anu ku Igupto mpaka lero, ndakhala ndi kuwachenjeza kawirikawiri kuti, ‘Mverani Ine.’ 8 Koma sanamvere kapena kulabadirako. Aliyense anawumirira kuchita zoyipa za mʼmitima yawo. Ngakhale ndinawalamulira kuti asunge pangano langa koma iwo sanasunge. Choncho ndinawalanga monga ndinaneneramo.’ ” 9 Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu andiwukira. 10 Abwereranso ku machimo a makolo awo, amene anakana kumvera mawu anga. Akutsata milungu ina ndi kumayitumikira. Aisraeli ndi Ayuda aphwanya pangano limene ndinachita ndi makolo awo. 11 Choncho Yehova akuti, ‘Ndidzawagwetsera mavuto amene sadzatha kuwalewa. Ngakhale adzandilirire, sindidzawamvera. 12 Anthu a mʼmizinda ya Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu adzapita ndi kukalirira milungu imene ankayifukizira lubani, koma milunguyo sidzawathandiza ndi pangʼono pomwe mavuto akadzafika. 13 Iwe Yuda, uli ndi milungu yochuluka ngati chiwerengero cha mizinda yako; chiwerengero cha maguwa ansembe amene umafukizirapo lubani kwa Baala chili ngati misewu ya mu Yerusalemu.’ 14 “Tsono iwe Yeremiya usawapempherere anthu amenewa ngakhale kuwadandaulira kapena kuwapepesera, chifukwa sindidzawamvera akadzandiyitana pa nthawi ya mavuto awo. 15 “Kodi anthu anga okondedwa akudzachita chiyani mʼNyumba yanga?Kodi suja iwowa amachita zoyipa zambiri?Kodi mungathe kupulumuka,tsoka osakugweranichifukwa cha nsembe zanuzo?” 16 Kale Yehova ankakutchani mtengo wa olivi wa masamba obiriwira,wokhala ndi zipatso zokongola.Koma tsopano adzawutenthandi mkuntho wamkokomondipo nthambi zake zidzapserera. 17 Yehova Wamphamvuzonse, amene anakudzalani, walamula kuti mavuto akugwereni. Inu a banja la Yuda ndi a banja la Israeli munachitira Yehova zoyipa ndi kumukwiyitsa pamene munkapereka nsembe zanu kwa Baala. 18 Yehova anandiwululira ndipo ndinadziwa. Iye anatsekula maso anga kuti ndione chiwembu chawocho. 19 Ndinali ngati mwana wankhosa wofatsa amene akupita naye kukamupha; sindinkadziwa kuti chiwembu chimene ankakonzekeracho chinkaloza ine. Iwo amati:“Tiyeni timuphemunthu ameneyukuti dzina lake lisadzakumbukiridwenso.” 20 Koma, Inu Yehova Wamphamvuzonse, Inu amene mumaweruza molungamandi kuyesa mitima ndi maganizo,lolani kuti ine ndione kuti mwawalipsira,pakuti mlandu wanga ndawupereka mʼmanja mwanu. 21 “Nʼchifukwa chake Yehova akunena za anthu a ku Anatoti amene akufuna kuwononga moyo wako namanena kuti, ‘Usanenere mʼdzina la Yehova, ukatero ife tidzakupha ndi manja athu,’ 22 koma Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ine ndidzawalanga. Achinyamata awo adzaphedwa ndi lupanga, ana awo aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala. 23 Sipadzakhala otsala ndi mmodzi yemwe, chifukwa ndidzalanga anthu a ku Anatoti chikadzafika chaka chawo cha chilango.’ ”
In Other Versions
Jeremiah 11 in the ANGEFD
Jeremiah 11 in the ANTPNG2D
Jeremiah 11 in the AS21
Jeremiah 11 in the BAGH
Jeremiah 11 in the BBPNG
Jeremiah 11 in the BBT1E
Jeremiah 11 in the BDS
Jeremiah 11 in the BEV
Jeremiah 11 in the BHAD
Jeremiah 11 in the BIB
Jeremiah 11 in the BLPT
Jeremiah 11 in the BNT
Jeremiah 11 in the BNTABOOT
Jeremiah 11 in the BNTLV
Jeremiah 11 in the BOATCB
Jeremiah 11 in the BOATCB2
Jeremiah 11 in the BOBCV
Jeremiah 11 in the BOCNT
Jeremiah 11 in the BOECS
Jeremiah 11 in the BOHCB
Jeremiah 11 in the BOHCV
Jeremiah 11 in the BOHLNT
Jeremiah 11 in the BOHNTLTAL
Jeremiah 11 in the BOICB
Jeremiah 11 in the BOILNTAP
Jeremiah 11 in the BOITCV
Jeremiah 11 in the BOKCV
Jeremiah 11 in the BOKCV2
Jeremiah 11 in the BOKHWOG
Jeremiah 11 in the BOKSSV
Jeremiah 11 in the BOLCB
Jeremiah 11 in the BOLCB2
Jeremiah 11 in the BOMCV
Jeremiah 11 in the BONAV
Jeremiah 11 in the BONCB
Jeremiah 11 in the BONLT
Jeremiah 11 in the BONUT2
Jeremiah 11 in the BOPLNT
Jeremiah 11 in the BOSCB
Jeremiah 11 in the BOSNC
Jeremiah 11 in the BOTLNT
Jeremiah 11 in the BOVCB
Jeremiah 11 in the BOYCB
Jeremiah 11 in the BPBB
Jeremiah 11 in the BPH
Jeremiah 11 in the BSB
Jeremiah 11 in the CCB
Jeremiah 11 in the CUV
Jeremiah 11 in the CUVS
Jeremiah 11 in the DBT
Jeremiah 11 in the DGDNT
Jeremiah 11 in the DHNT
Jeremiah 11 in the DNT
Jeremiah 11 in the ELBE
Jeremiah 11 in the EMTV
Jeremiah 11 in the ESV
Jeremiah 11 in the FBV
Jeremiah 11 in the FEB
Jeremiah 11 in the GGMNT
Jeremiah 11 in the GNT
Jeremiah 11 in the HARY
Jeremiah 11 in the HNT
Jeremiah 11 in the IRVA
Jeremiah 11 in the IRVB
Jeremiah 11 in the IRVG
Jeremiah 11 in the IRVH
Jeremiah 11 in the IRVK
Jeremiah 11 in the IRVM
Jeremiah 11 in the IRVM2
Jeremiah 11 in the IRVO
Jeremiah 11 in the IRVP
Jeremiah 11 in the IRVT
Jeremiah 11 in the IRVT2
Jeremiah 11 in the IRVU
Jeremiah 11 in the ISVN
Jeremiah 11 in the JSNT
Jeremiah 11 in the KAPI
Jeremiah 11 in the KBT1ETNIK
Jeremiah 11 in the KBV
Jeremiah 11 in the KJV
Jeremiah 11 in the KNFD
Jeremiah 11 in the LBA
Jeremiah 11 in the LBLA
Jeremiah 11 in the LNT
Jeremiah 11 in the LSV
Jeremiah 11 in the MAAL
Jeremiah 11 in the MBV
Jeremiah 11 in the MBV2
Jeremiah 11 in the MHNT
Jeremiah 11 in the MKNFD
Jeremiah 11 in the MNG
Jeremiah 11 in the MNT
Jeremiah 11 in the MNT2
Jeremiah 11 in the MRS1T
Jeremiah 11 in the NAA
Jeremiah 11 in the NASB
Jeremiah 11 in the NBLA
Jeremiah 11 in the NBS
Jeremiah 11 in the NBVTP
Jeremiah 11 in the NET2
Jeremiah 11 in the NIV11
Jeremiah 11 in the NNT
Jeremiah 11 in the NNT2
Jeremiah 11 in the NNT3
Jeremiah 11 in the PDDPT
Jeremiah 11 in the PFNT
Jeremiah 11 in the RMNT
Jeremiah 11 in the SBIAS
Jeremiah 11 in the SBIBS
Jeremiah 11 in the SBIBS2
Jeremiah 11 in the SBICS
Jeremiah 11 in the SBIDS
Jeremiah 11 in the SBIGS
Jeremiah 11 in the SBIHS
Jeremiah 11 in the SBIIS
Jeremiah 11 in the SBIIS2
Jeremiah 11 in the SBIIS3
Jeremiah 11 in the SBIKS
Jeremiah 11 in the SBIKS2
Jeremiah 11 in the SBIMS
Jeremiah 11 in the SBIOS
Jeremiah 11 in the SBIPS
Jeremiah 11 in the SBISS
Jeremiah 11 in the SBITS
Jeremiah 11 in the SBITS2
Jeremiah 11 in the SBITS3
Jeremiah 11 in the SBITS4
Jeremiah 11 in the SBIUS
Jeremiah 11 in the SBIVS
Jeremiah 11 in the SBT
Jeremiah 11 in the SBT1E
Jeremiah 11 in the SCHL
Jeremiah 11 in the SNT
Jeremiah 11 in the SUSU
Jeremiah 11 in the SUSU2
Jeremiah 11 in the SYNO
Jeremiah 11 in the TBIAOTANT
Jeremiah 11 in the TBT1E
Jeremiah 11 in the TBT1E2
Jeremiah 11 in the TFTIP
Jeremiah 11 in the TFTU
Jeremiah 11 in the TGNTATF3T
Jeremiah 11 in the THAI
Jeremiah 11 in the TNFD
Jeremiah 11 in the TNT
Jeremiah 11 in the TNTIK
Jeremiah 11 in the TNTIL
Jeremiah 11 in the TNTIN
Jeremiah 11 in the TNTIP
Jeremiah 11 in the TNTIZ
Jeremiah 11 in the TOMA
Jeremiah 11 in the TTENT
Jeremiah 11 in the UBG
Jeremiah 11 in the UGV
Jeremiah 11 in the UGV2
Jeremiah 11 in the UGV3
Jeremiah 11 in the VBL
Jeremiah 11 in the VDCC
Jeremiah 11 in the YALU
Jeremiah 11 in the YAPE
Jeremiah 11 in the YBVTP
Jeremiah 11 in the ZBP