Jeremiah 29 (BOGWICC)

1 Yeremiya anatumiza kalata kuchokera ku Yerusalemu kupita kwa akuluakulu amene anali ku ukapolo, ndiponso kwa ansembe, aneneri pamodzi ndi anthu onse amene Nebukadinezara anawatenga ku Yerusalemu kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni. 2 Zimenezi zinachitika mfumu Yekoniya, amayi a mfumu, nduna za mfumu ndiponso atsogoleri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu, anthu aluso ndi amisiri atatengedwa ku Yerusalemu kupita ku ukapolo. 3 Yeremiya anapatsira kalatayo Eleasa mwana wa Safani ndi Gemariya mwana wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya Yuda anawatumiza kwa Mfumu Nebukadinezara ku Babuloni. Mʼkalatamo analembamo kuti: 4 Anthu onse amene anatengedwa ukapolo kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Babuloni, Yehova akuwawuza kuti, 5 “Mangani nyumba ndipo muzikhalamo. Limani minda ndipo mudye zipatso zake. 6 Kwatirani ndipo mubereke ana aamuna ndi aakazi. Ana anu aamuna muwasankhire akazi ndipo muwasankhire amuna ana anu aakaziwo, kuti nawonso abale ana aamuna ndi aakazi. Muchulukane kumeneko. Chiwerengero chanu chisachepe. 7 Ndiponso muzifunafuna mtendere ndi ubwino wa mzinda umene ndinakupirikitsirani ku ukapoloko. Muzipempherera mzindawo kwa Yehova, kuti zikuyendereni bwino.” 8 Inde, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akunena kuti, “Musalole kuti aneneri ndi owombeza amene ali pakati panu akunyengeni. Musamvere maloto awo. 9 Iwo akunenera zabodza kwa inu mʼdzina langa ngakhale Ine sindinawatume,” akutero Yehova. 10 Yehova akuti, “Zaka 70 za ku Babuloni zikadzatha, ndidzabwera kudzakuchitirani zabwino zonse zimene ndinakulonjezani zija, ndipo ndidzakubwezerani ku malo ano. 11 Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani,” akutero Yehova, “ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo. 12 Nthawi imeneyo mudzandiyitana, ndi kunditama mopemba ndipo ndidzakumverani. 13 Mudzandifunafuna ndipo mudzandipeza. Mukadzandifuna ndi mtima wanu wonse 14 mudzandipezadi,” akutero Yehova, “ndipo ndidzakubwezerani zabwino zanu. Ndidzakusonkhanitsani kuchokera ku mayiko onse ndi kumalo konse kumene munali,” akutero Yehova, “ndipo ndidzakubweretsani kumalo kumene munali ndisanakuchotseni kukupititsani ku ukapolo.” 15 Inu mumati, “Yehova watiwutsira aneneri athu ku Babuloni,” 16 koma zimene Yehova akunena za mfumu imene ikukhala pa mpando waufumu wa Davide pamodzi ndi anthu onse amene anatsala mu mzinda muno, abale anu amene sanapite nanu ku ukapolo ndi izi, 17 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ndidzawapha ndi nkhondo, njala ndi mliri ndipo ndidzawasandutsa ngati nkhuyu zowola kwambiri, zosati nʼkudya. 18 Ndidzawalondola ndi lupanga, njala ndi mliri ndipo ndidzawasandutsa chinthu chonyansa kwa anthu amayiko onse a pa dziko lapansi. Adzakhala otembereredwa, ochititsa mantha, onyozeka ndiponso ochitidwa chipongwe pakati pa anthu a mitundu yonse kumene ndawapirikitsirako. 19 Zidzatero chifukwa sanamvere mawu anga amene ndinkawatumizira kudzera mwa atumiki anga, aneneri. Ngakhale inu amene muli ku ukapolo simunamverenso,” akutero Yehova. 20 Choncho, imvani mawu a Yehova, inu akapolo nonse amene ndinakuchotsani mu Yerusalemu ndi kukupititsani ku Babuloni. 21 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti zokhudza Ahabu mwana wa Kolaya ndi Zedekiya mwana wa Maseya, amene akulosera zabodza kwa inu mʼdzina langa: “Taonani ndidzawapereka kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, ndipo adzawapha inu mukupenya. 22 Chifukwa cha anthu awiriwo, akapolo onse ochokera ku Yuda amene ali ku Babuloni adzagwiritsa ntchito mawu awa potemberera: ‘Yehova achite nawe monga mmene anachitira ndi Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babuloni inawatentha.’ 23 Pakuti anthu amenewa achita zoyipa kwambiri mu Israeli; achita chigololo ndi akazi a eni ake ndipo mʼdzina langa ankayankhula zabodza zimene sindinawawuze kuti atero. Ine ndikuzidziwa ndipo ndine mboni ya zimenezi,” akutero Yehova. 24 Ukamuwuze Semaya wa ku Nehelamu kuti, 25 “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Iwe unatumiza kalata mʼdzina lako kwa anthu onse a mu Yerusalemu, kwa Zefaniya mwana wa wansembe Maseya, ndi kwa ansembe onse. Unalemba mu kalatayo kuti, 26 ‘Yehova wakusankha kukhala wansembe mʼmalo mwa Yehoyada kuti ukhale wamkulu woyangʼanira Nyumba ya Yehova. Munthu aliyense wamisala amene akudziyesa kuti ndi mneneri uzimuponya mʼndende ndi kumuveka goli lachitsulo. 27 Nanga tsono chifukwa chiyani simunamuchitire zimenezi Yeremiya wa ku Anatoti, amene amakhala ngati mneneri pakati panu? 28 Yeremiyayo watitumizira uthenga uwu kuno ku Babuloni: Ukapolo wanu ukhala wa nthawi yayitali. Choncho mangani nyumba ndipo muzikhalamo; limani minda ndipo mudye zipatso zake.’ ” 29 Koma wansembe Zefaniya anayiwerenga kalatayo pamaso pa mneneri Yeremiya. 30 Ndipo Yehova anawuza Yeremiya kuti, 31 “Tumiza uthenga uwu kwa akapolo onse: ‘Yehova akuti zokhudza Semaya wa ku Nehelamu: Semaya wakuloserani, ngakhale kuti Ine sindinamutume, ndipo wakunyengani kuti muzikhulupirira bodza. 32 Nʼchifukwa chake Ine Yehova ndikuti: Mʼbanja lakelo sipadzakhala munthu pakati pa mtundu uno wa anthu amene adzaone zinthu zabwino zimene ndidzachitira anthu anga chifukwa analalika zondiwukira,’ ” akutero Yehova.

In Other Versions

Jeremiah 29 in the ANGEFD

Jeremiah 29 in the ANTPNG2D

Jeremiah 29 in the AS21

Jeremiah 29 in the BAGH

Jeremiah 29 in the BBPNG

Jeremiah 29 in the BBT1E

Jeremiah 29 in the BDS

Jeremiah 29 in the BEV

Jeremiah 29 in the BHAD

Jeremiah 29 in the BIB

Jeremiah 29 in the BLPT

Jeremiah 29 in the BNT

Jeremiah 29 in the BNTABOOT

Jeremiah 29 in the BNTLV

Jeremiah 29 in the BOATCB

Jeremiah 29 in the BOATCB2

Jeremiah 29 in the BOBCV

Jeremiah 29 in the BOCNT

Jeremiah 29 in the BOECS

Jeremiah 29 in the BOHCB

Jeremiah 29 in the BOHCV

Jeremiah 29 in the BOHLNT

Jeremiah 29 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 29 in the BOICB

Jeremiah 29 in the BOILNTAP

Jeremiah 29 in the BOITCV

Jeremiah 29 in the BOKCV

Jeremiah 29 in the BOKCV2

Jeremiah 29 in the BOKHWOG

Jeremiah 29 in the BOKSSV

Jeremiah 29 in the BOLCB

Jeremiah 29 in the BOLCB2

Jeremiah 29 in the BOMCV

Jeremiah 29 in the BONAV

Jeremiah 29 in the BONCB

Jeremiah 29 in the BONLT

Jeremiah 29 in the BONUT2

Jeremiah 29 in the BOPLNT

Jeremiah 29 in the BOSCB

Jeremiah 29 in the BOSNC

Jeremiah 29 in the BOTLNT

Jeremiah 29 in the BOVCB

Jeremiah 29 in the BOYCB

Jeremiah 29 in the BPBB

Jeremiah 29 in the BPH

Jeremiah 29 in the BSB

Jeremiah 29 in the CCB

Jeremiah 29 in the CUV

Jeremiah 29 in the CUVS

Jeremiah 29 in the DBT

Jeremiah 29 in the DGDNT

Jeremiah 29 in the DHNT

Jeremiah 29 in the DNT

Jeremiah 29 in the ELBE

Jeremiah 29 in the EMTV

Jeremiah 29 in the ESV

Jeremiah 29 in the FBV

Jeremiah 29 in the FEB

Jeremiah 29 in the GGMNT

Jeremiah 29 in the GNT

Jeremiah 29 in the HARY

Jeremiah 29 in the HNT

Jeremiah 29 in the IRVA

Jeremiah 29 in the IRVB

Jeremiah 29 in the IRVG

Jeremiah 29 in the IRVH

Jeremiah 29 in the IRVK

Jeremiah 29 in the IRVM

Jeremiah 29 in the IRVM2

Jeremiah 29 in the IRVO

Jeremiah 29 in the IRVP

Jeremiah 29 in the IRVT

Jeremiah 29 in the IRVT2

Jeremiah 29 in the IRVU

Jeremiah 29 in the ISVN

Jeremiah 29 in the JSNT

Jeremiah 29 in the KAPI

Jeremiah 29 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 29 in the KBV

Jeremiah 29 in the KJV

Jeremiah 29 in the KNFD

Jeremiah 29 in the LBA

Jeremiah 29 in the LBLA

Jeremiah 29 in the LNT

Jeremiah 29 in the LSV

Jeremiah 29 in the MAAL

Jeremiah 29 in the MBV

Jeremiah 29 in the MBV2

Jeremiah 29 in the MHNT

Jeremiah 29 in the MKNFD

Jeremiah 29 in the MNG

Jeremiah 29 in the MNT

Jeremiah 29 in the MNT2

Jeremiah 29 in the MRS1T

Jeremiah 29 in the NAA

Jeremiah 29 in the NASB

Jeremiah 29 in the NBLA

Jeremiah 29 in the NBS

Jeremiah 29 in the NBVTP

Jeremiah 29 in the NET2

Jeremiah 29 in the NIV11

Jeremiah 29 in the NNT

Jeremiah 29 in the NNT2

Jeremiah 29 in the NNT3

Jeremiah 29 in the PDDPT

Jeremiah 29 in the PFNT

Jeremiah 29 in the RMNT

Jeremiah 29 in the SBIAS

Jeremiah 29 in the SBIBS

Jeremiah 29 in the SBIBS2

Jeremiah 29 in the SBICS

Jeremiah 29 in the SBIDS

Jeremiah 29 in the SBIGS

Jeremiah 29 in the SBIHS

Jeremiah 29 in the SBIIS

Jeremiah 29 in the SBIIS2

Jeremiah 29 in the SBIIS3

Jeremiah 29 in the SBIKS

Jeremiah 29 in the SBIKS2

Jeremiah 29 in the SBIMS

Jeremiah 29 in the SBIOS

Jeremiah 29 in the SBIPS

Jeremiah 29 in the SBISS

Jeremiah 29 in the SBITS

Jeremiah 29 in the SBITS2

Jeremiah 29 in the SBITS3

Jeremiah 29 in the SBITS4

Jeremiah 29 in the SBIUS

Jeremiah 29 in the SBIVS

Jeremiah 29 in the SBT

Jeremiah 29 in the SBT1E

Jeremiah 29 in the SCHL

Jeremiah 29 in the SNT

Jeremiah 29 in the SUSU

Jeremiah 29 in the SUSU2

Jeremiah 29 in the SYNO

Jeremiah 29 in the TBIAOTANT

Jeremiah 29 in the TBT1E

Jeremiah 29 in the TBT1E2

Jeremiah 29 in the TFTIP

Jeremiah 29 in the TFTU

Jeremiah 29 in the TGNTATF3T

Jeremiah 29 in the THAI

Jeremiah 29 in the TNFD

Jeremiah 29 in the TNT

Jeremiah 29 in the TNTIK

Jeremiah 29 in the TNTIL

Jeremiah 29 in the TNTIN

Jeremiah 29 in the TNTIP

Jeremiah 29 in the TNTIZ

Jeremiah 29 in the TOMA

Jeremiah 29 in the TTENT

Jeremiah 29 in the UBG

Jeremiah 29 in the UGV

Jeremiah 29 in the UGV2

Jeremiah 29 in the UGV3

Jeremiah 29 in the VBL

Jeremiah 29 in the VDCC

Jeremiah 29 in the YALU

Jeremiah 29 in the YAPE

Jeremiah 29 in the YBVTP

Jeremiah 29 in the ZBP