Joshua 21 (BOGWICC)

1 Tsono atsogoleri a mabanja a fuko la Levi anabwera kwa wansembe Eliezara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa atsogoleri a mabanja a mafuko onse a Aisraeli, 2 ku Silo mʼdziko la Kanaani ndipo anati, “Yehova analamula kudzera mwa Mose kuti atipatse mizinda kuti tikhalemo, pamodzi ndi malo odyetseramo ziweto zathu.” 3 Choncho, Aisraeli anapereka kwa fuko la Levi mizinda iyi pamodzi ndi malo owetera ziweto zawo kuchokera ku madera awo, monga Yehova analamulira: 4 Maere oyamba anagwera mabanja a Kohati, Alevi amene anali zidzukulu za wansembe Aaroni anapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini. 5 Ndipo mabanja otsala a Kohati anapatsidwa mizinda khumi kuchokera ku mafuko a Efereimu, Dani ndi theka la fuko la Manase. 6 Zidzukulu za Geresoni zinapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mabanja a mafuko a Isakara, Aseri, Nafutali ndi theka la fuko la Manase ku Basani. 7 Mabanja a Merari anapatsidwa mizinda khumi ndi iwiri kuchokera ku mafuko a Rubeni, Gadi ndi Zebuloni. 8 Choncho Aisraeli anapereka kwa fuko la Levi mizindayi pamodzi ndi malo odyetserako ziweto pogwiritsa ntchito maere, monga Yehova analamula kudzera mwa Mose. 9 Awa ndi mayina a mizinda ya mafuko a Yuda ndi Simeoni imene inaperekedwa kwa zidzukulu za Aaroni, 10 ku banja la Kohati amene anali Alevi. Paja maere oyamba anagwera mabanja a Kohati kuti alandira mizinda. 11 Anapatsidwa mzinda wa Kiriati Ariba. (Paja Ariba ndiye kholo la Anaaki). Dzina lina la mzindawu ndi Hebroni, ndipo unali mʼdziko la mapiri la Yuda. Pamodzi ndi mzindawu anapatsidwanso mabusa ake onse ozungulira. 12 Komabe minda ndi midzi yozungulira mizindayi inali itaperekedwa kale kwa Kalebe, mwana wa Yefune kuti ikhale cholowa chake. 13 Choncho zidzukulu za Aaroni wansembe, zinapatsidwa Hebroni (mzinda wopulumukirako amene wapha munthu), Libina, 14 Yatiri, Esitemowa, 15 Holoni, Debri, 16 Aini, Yuta, ndi Beti-Semesi pamodzi ndi mabusa odyetseramo ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda isanu ndi inayi yochokera ku mafuko awiriwa. 17 Fuko la Benjamini linapereka Gibiyoni, Geba, 18 Anatoti ndi Alimoni, pamodzi ndi mabusa odyetsera ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi. 19 Choncho mizinda 13 pamodzi ndi malo odyetsera ziweto anapatsidwa kwa ansembe, zidzukulu za Aaroni. 20 Mabanja ena otsalira a Kohati a fuko la Levi anapatsidwa mizinda iyi kuchokera ku fuko la Efereimu: 21 Mizinda ya Sekemu ndi Gezeri ndiye inali mizinda wopulumukirako munthu aliyense wopha mnzake mwangozi. Mizindayi inali ku mapiri a Efereimu. 22 Analandiranso mizinda ya Gezeri, Kibuzaimu, Beti-Horoni pamodzi ndi malo odyetsera ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi. 23 Fuko la Dani linapereka mizinda ya Eliteke, Gibetoni, 24 Ayaloni, Gati-Rimoni pamodzi ndi mabusa odyetsera ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi. 25 Kuchokera ku theka la fuko la Manase analandira Taanaki ndi Gati-Rimoni pamodzi ndi malo awo owetera ziweto, mizinda iwiri. 26 Mizinda khumi yonseyi pamodzi ndi malo odyetsera ziweto, zinapatsidwa ku mabanja ena onse a Akohati. 27 Mabanja a Ageresoni a fuko la Levi anapatsidwa mizinda iwirikuchokera ku theka la Manase wa kummawa,Golani ku Basani (mzinda wopulumukirako amene wapha munthu mwangozi) ndi Beesitera, pamodzi ndi malo awo odyetserako ziweto. 28 Fuko la Isakara linapereka mizinda yaKisoni, Daberati, 29 Yarimuti ndi Eni Ganimu, pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi. 30 Fuko la Aseri linapereka mizinda yaMisali, Abidoni, 31 Helikati ndi Rehobu pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi. 32 Fuko la Nafutali linapereka mizinda yaKedesi wa ku Galileya, mzinda umene unali wopulumukiramo munthu wopha mnzake mwangozi. Analandiranso mizinda ya Hamoti-Dori ndi Karitani. Kuphatikizira apa, analandira malo odyetsera ziweto a mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi. 33 Mabanja onse a Ageresoni analandira mizinda 13 pamodzi ndi malo awo odyetsera a ziweto. 34 Mabanja a Merari amene anali otsala a fuko la Levi, anapatsidwamizinda iyi kuchokera ku fuko la Zebuloni:Yokineamu, Karita, 35 Dimuna ndi Nahalali, pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi. 36 Kuchokera ku fuko la Rubeni analandiraBezeri, Yahaza, 37 Kedemoti ndi Mefaati, pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi. 38 Kuchokera ku fuko la Gadianalandira mzinda wa Ramoti ku Giliyadi. Mzinda umene unali wopulumukiramo munthu wopha mnzake mwangozi. 39 Analandiranso mizinda ya Mahanaimu, Hesiboni, Yazeri pamodzi ndi malo odyetserako ziweto ozungulira mizinda yonseyi. Yonse pamodzi inali mizindayi anayi. 40 Choncho mabanja onse a Merari, amene anali otsala a fuko la Levi analandira mizinda khumi ndi iwiri pogwiritsa ntchito maere. 41 Motero mizinda 48 ya mʼdziko limene Aisraeli analanda inapatsidwa kwa Alevi, kuphatikizapo malo ake odyetsera ziweto. 42 Iliyonse mwa mizindayi inali ndi malo owetera ziweto oyizungulira. 43 Motero Yehova anapereka kwa Israeli dziko limene analumbira kulipereka kwa makolo awo. Atalilandira anadzakhalamo. 44 Yehova anawapatsa mtendere mʼdziko lonse monga momwe analonjezera makolo awo. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa adani awo amene anatha kuwagonjetsa chifukwa Yehova anapereka adani awo onse mʼmanja mwawo. 45 Yehova anakwaniritsa zonse zimene analonjeza kwa Aisraeli.

In Other Versions

Joshua 21 in the ANGEFD

Joshua 21 in the ANTPNG2D

Joshua 21 in the AS21

Joshua 21 in the BAGH

Joshua 21 in the BBPNG

Joshua 21 in the BBT1E

Joshua 21 in the BDS

Joshua 21 in the BEV

Joshua 21 in the BHAD

Joshua 21 in the BIB

Joshua 21 in the BLPT

Joshua 21 in the BNT

Joshua 21 in the BNTABOOT

Joshua 21 in the BNTLV

Joshua 21 in the BOATCB

Joshua 21 in the BOATCB2

Joshua 21 in the BOBCV

Joshua 21 in the BOCNT

Joshua 21 in the BOECS

Joshua 21 in the BOHCB

Joshua 21 in the BOHCV

Joshua 21 in the BOHLNT

Joshua 21 in the BOHNTLTAL

Joshua 21 in the BOICB

Joshua 21 in the BOILNTAP

Joshua 21 in the BOITCV

Joshua 21 in the BOKCV

Joshua 21 in the BOKCV2

Joshua 21 in the BOKHWOG

Joshua 21 in the BOKSSV

Joshua 21 in the BOLCB

Joshua 21 in the BOLCB2

Joshua 21 in the BOMCV

Joshua 21 in the BONAV

Joshua 21 in the BONCB

Joshua 21 in the BONLT

Joshua 21 in the BONUT2

Joshua 21 in the BOPLNT

Joshua 21 in the BOSCB

Joshua 21 in the BOSNC

Joshua 21 in the BOTLNT

Joshua 21 in the BOVCB

Joshua 21 in the BOYCB

Joshua 21 in the BPBB

Joshua 21 in the BPH

Joshua 21 in the BSB

Joshua 21 in the CCB

Joshua 21 in the CUV

Joshua 21 in the CUVS

Joshua 21 in the DBT

Joshua 21 in the DGDNT

Joshua 21 in the DHNT

Joshua 21 in the DNT

Joshua 21 in the ELBE

Joshua 21 in the EMTV

Joshua 21 in the ESV

Joshua 21 in the FBV

Joshua 21 in the FEB

Joshua 21 in the GGMNT

Joshua 21 in the GNT

Joshua 21 in the HARY

Joshua 21 in the HNT

Joshua 21 in the IRVA

Joshua 21 in the IRVB

Joshua 21 in the IRVG

Joshua 21 in the IRVH

Joshua 21 in the IRVK

Joshua 21 in the IRVM

Joshua 21 in the IRVM2

Joshua 21 in the IRVO

Joshua 21 in the IRVP

Joshua 21 in the IRVT

Joshua 21 in the IRVT2

Joshua 21 in the IRVU

Joshua 21 in the ISVN

Joshua 21 in the JSNT

Joshua 21 in the KAPI

Joshua 21 in the KBT1ETNIK

Joshua 21 in the KBV

Joshua 21 in the KJV

Joshua 21 in the KNFD

Joshua 21 in the LBA

Joshua 21 in the LBLA

Joshua 21 in the LNT

Joshua 21 in the LSV

Joshua 21 in the MAAL

Joshua 21 in the MBV

Joshua 21 in the MBV2

Joshua 21 in the MHNT

Joshua 21 in the MKNFD

Joshua 21 in the MNG

Joshua 21 in the MNT

Joshua 21 in the MNT2

Joshua 21 in the MRS1T

Joshua 21 in the NAA

Joshua 21 in the NASB

Joshua 21 in the NBLA

Joshua 21 in the NBS

Joshua 21 in the NBVTP

Joshua 21 in the NET2

Joshua 21 in the NIV11

Joshua 21 in the NNT

Joshua 21 in the NNT2

Joshua 21 in the NNT3

Joshua 21 in the PDDPT

Joshua 21 in the PFNT

Joshua 21 in the RMNT

Joshua 21 in the SBIAS

Joshua 21 in the SBIBS

Joshua 21 in the SBIBS2

Joshua 21 in the SBICS

Joshua 21 in the SBIDS

Joshua 21 in the SBIGS

Joshua 21 in the SBIHS

Joshua 21 in the SBIIS

Joshua 21 in the SBIIS2

Joshua 21 in the SBIIS3

Joshua 21 in the SBIKS

Joshua 21 in the SBIKS2

Joshua 21 in the SBIMS

Joshua 21 in the SBIOS

Joshua 21 in the SBIPS

Joshua 21 in the SBISS

Joshua 21 in the SBITS

Joshua 21 in the SBITS2

Joshua 21 in the SBITS3

Joshua 21 in the SBITS4

Joshua 21 in the SBIUS

Joshua 21 in the SBIVS

Joshua 21 in the SBT

Joshua 21 in the SBT1E

Joshua 21 in the SCHL

Joshua 21 in the SNT

Joshua 21 in the SUSU

Joshua 21 in the SUSU2

Joshua 21 in the SYNO

Joshua 21 in the TBIAOTANT

Joshua 21 in the TBT1E

Joshua 21 in the TBT1E2

Joshua 21 in the TFTIP

Joshua 21 in the TFTU

Joshua 21 in the TGNTATF3T

Joshua 21 in the THAI

Joshua 21 in the TNFD

Joshua 21 in the TNT

Joshua 21 in the TNTIK

Joshua 21 in the TNTIL

Joshua 21 in the TNTIN

Joshua 21 in the TNTIP

Joshua 21 in the TNTIZ

Joshua 21 in the TOMA

Joshua 21 in the TTENT

Joshua 21 in the UBG

Joshua 21 in the UGV

Joshua 21 in the UGV2

Joshua 21 in the UGV3

Joshua 21 in the VBL

Joshua 21 in the VDCC

Joshua 21 in the YALU

Joshua 21 in the YAPE

Joshua 21 in the YBVTP

Joshua 21 in the ZBP