Leviticus 18 (BOGWICC)
1 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 3 Musamachite zomwe amachita anthu a ku Igupto kumene munkakhala kuja, ndiponso musamachite zomwe amachita anthu a ku Kanaani kumene ndikukupititsani. Musatsatire miyambo yawo. 4 Inu muzimvera malamulo anga ndipo muzisamalitsa kutsatira malangizo anga. Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 5 Choncho sungani malangizo ndi malamulo anga, popeza munthu amene amvera zimenezi adzakhala ndi moyo. Ine ndine Yehova. 6 “ ‘Munthu aliyense asagonane ndi wachibale wake. Ine ndine Yehova. 7 “ ‘Usachititse manyazi abambo ako pogonana ndi amayi ako. Iwo ndi amayi ako. Usagonane nawo. 8 “ ‘Usagonane ndi mkazi wa abambo ako (osakhala amayi okubala). Ukatero ukuchititsa manyazi abambo ako. 9 “ ‘Usagonane ndi mlongo wako, mwana wamkazi wa abambo ako, kapena mwana wamkazi wa amayi ako, kaya anabadwira mʼnyumba mwanu kapena kwina. 10 “ ‘Usagonane ndi mdzukulu wako: mwana wa mwana wako wamwamuna kapena mwana wa mwana wako wamkazi. Kutero nʼkudzichotsa ulemu. 11 “ ‘Usagonane ndi mwana wamkazi wa mkazi wa abambo ako, amene abambo akowo anabereka; popeza ameneyo ndi mlongo wako. 12 “ ‘Usagonane ndi mlongo wa abambo ako; popeza ameneyo ndi thupi limodzi ndi abambo ako. 13 “ ‘Usagonane ndi mchemwali wa amayi ako chifukwa ameneyo ndi thupi limodzi ndi amayi ako. 14 “ ‘Usachititse manyazi mchimwene wa abambo ako pogonana ndi mkazi wake popeza amenewo ndi azakhali ako. 15 “ ‘Usagonane ndi mpongozi wako popeza ameneyo ndi mkazi wa mwana wako. Choncho usamuchititse manyazi. 16 “ ‘Usagonane ndi mkazi wa mchimwene wako popeza potero ukuchititsa manyazi mʼbale wakoyo. 17 “ ‘Usagonane ndi mkazi ndiponso mwana wake wamkazi. Usagonane ndi mwana wamkazi wa mwana wake wamwamuna, kapena mwana wamkazi wa mwana wake wamkazi. Amenewo ndi thupi limodzi ndi mkaziyo. Kutero ndikuchita chinthu choyipa kwambiri. 18 “ ‘Usakwatire mchemwali wa mkazi wako ndi kumagonana naye mkazi wakoyo ali moyo ngati wopikisana naye. 19 “ ‘Usamuyandikire mkazi kuti ugonane naye pa nthawi yake yosamba. 20 “ ‘Usagonane ndi mkazi wa mnzako ndi kudziyipitsa naye. 21 “ ‘Usapereke mwana wako aliyense kuti akhale nsembe yamoto kwa Moleki ndi kuyipitsa dzina la Yehova. Ine ndine Yehova. 22 “ ‘Usagonane ndi mwamuna ngati mkazi; chimenecho ndi chinthu chonyansa. 23 “ ‘Usagonane ndi nyama ndi kudziyipitsa nayo. Mkazi asadzipereke kwa nyama kuti agonane nayo. Chimenecho ndi chisokonezo. 24 “ ‘Musadzidetse ndi zinthu zimenezi chifukwa umo ndi mmene mitundu ina imene ndikuyithamangitsa pamaso panu inadzidetsera. 25 Choncho dziko linayipa ndipo ndinalilanga chifukwa cha tchimo lake. Motero dzikolo linasanza anthu ake okhalamo. 26 Koma inu mukasunge malangizo ndi malamulo anga. Mbadwa ndiponso alendo amene akukhala pakati panu asakachite china chilichonse cha zinthu zonyansazi, 27 pakuti zinthu zonsezi ndi zomwe ankachita anthu amene ankakhala mʼdzikomo inu musanafike, ndipo dziko linayipitsidwa. 28 Koma inu musachite zimenezi kuti dziko lingakusanzeni mutaliyipitsa monga linasanzira mitundu imene imakhalamo inu musanafike. 29 “ ‘Aliyense wochita zinthu zonyansa zimenezi achotsedwe pakati pa anthu anzake. 30 Choncho mverani malangizo anga oletsa kuchita miyambo yonyansayi imene ankatsatira anthu amene analipo inu musanafike ndi kudziyipitsa nayo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”
In Other Versions
Leviticus 18 in the ANGEFD
Leviticus 18 in the ANTPNG2D
Leviticus 18 in the AS21
Leviticus 18 in the BAGH
Leviticus 18 in the BBPNG
Leviticus 18 in the BBT1E
Leviticus 18 in the BDS
Leviticus 18 in the BEV
Leviticus 18 in the BHAD
Leviticus 18 in the BIB
Leviticus 18 in the BLPT
Leviticus 18 in the BNT
Leviticus 18 in the BNTABOOT
Leviticus 18 in the BNTLV
Leviticus 18 in the BOATCB
Leviticus 18 in the BOATCB2
Leviticus 18 in the BOBCV
Leviticus 18 in the BOCNT
Leviticus 18 in the BOECS
Leviticus 18 in the BOHCB
Leviticus 18 in the BOHCV
Leviticus 18 in the BOHLNT
Leviticus 18 in the BOHNTLTAL
Leviticus 18 in the BOICB
Leviticus 18 in the BOILNTAP
Leviticus 18 in the BOITCV
Leviticus 18 in the BOKCV
Leviticus 18 in the BOKCV2
Leviticus 18 in the BOKHWOG
Leviticus 18 in the BOKSSV
Leviticus 18 in the BOLCB
Leviticus 18 in the BOLCB2
Leviticus 18 in the BOMCV
Leviticus 18 in the BONAV
Leviticus 18 in the BONCB
Leviticus 18 in the BONLT
Leviticus 18 in the BONUT2
Leviticus 18 in the BOPLNT
Leviticus 18 in the BOSCB
Leviticus 18 in the BOSNC
Leviticus 18 in the BOTLNT
Leviticus 18 in the BOVCB
Leviticus 18 in the BOYCB
Leviticus 18 in the BPBB
Leviticus 18 in the BPH
Leviticus 18 in the BSB
Leviticus 18 in the CCB
Leviticus 18 in the CUV
Leviticus 18 in the CUVS
Leviticus 18 in the DBT
Leviticus 18 in the DGDNT
Leviticus 18 in the DHNT
Leviticus 18 in the DNT
Leviticus 18 in the ELBE
Leviticus 18 in the EMTV
Leviticus 18 in the ESV
Leviticus 18 in the FBV
Leviticus 18 in the FEB
Leviticus 18 in the GGMNT
Leviticus 18 in the GNT
Leviticus 18 in the HARY
Leviticus 18 in the HNT
Leviticus 18 in the IRVA
Leviticus 18 in the IRVB
Leviticus 18 in the IRVG
Leviticus 18 in the IRVH
Leviticus 18 in the IRVK
Leviticus 18 in the IRVM
Leviticus 18 in the IRVM2
Leviticus 18 in the IRVO
Leviticus 18 in the IRVP
Leviticus 18 in the IRVT
Leviticus 18 in the IRVT2
Leviticus 18 in the IRVU
Leviticus 18 in the ISVN
Leviticus 18 in the JSNT
Leviticus 18 in the KAPI
Leviticus 18 in the KBT1ETNIK
Leviticus 18 in the KBV
Leviticus 18 in the KJV
Leviticus 18 in the KNFD
Leviticus 18 in the LBA
Leviticus 18 in the LBLA
Leviticus 18 in the LNT
Leviticus 18 in the LSV
Leviticus 18 in the MAAL
Leviticus 18 in the MBV
Leviticus 18 in the MBV2
Leviticus 18 in the MHNT
Leviticus 18 in the MKNFD
Leviticus 18 in the MNG
Leviticus 18 in the MNT
Leviticus 18 in the MNT2
Leviticus 18 in the MRS1T
Leviticus 18 in the NAA
Leviticus 18 in the NASB
Leviticus 18 in the NBLA
Leviticus 18 in the NBS
Leviticus 18 in the NBVTP
Leviticus 18 in the NET2
Leviticus 18 in the NIV11
Leviticus 18 in the NNT
Leviticus 18 in the NNT2
Leviticus 18 in the NNT3
Leviticus 18 in the PDDPT
Leviticus 18 in the PFNT
Leviticus 18 in the RMNT
Leviticus 18 in the SBIAS
Leviticus 18 in the SBIBS
Leviticus 18 in the SBIBS2
Leviticus 18 in the SBICS
Leviticus 18 in the SBIDS
Leviticus 18 in the SBIGS
Leviticus 18 in the SBIHS
Leviticus 18 in the SBIIS
Leviticus 18 in the SBIIS2
Leviticus 18 in the SBIIS3
Leviticus 18 in the SBIKS
Leviticus 18 in the SBIKS2
Leviticus 18 in the SBIMS
Leviticus 18 in the SBIOS
Leviticus 18 in the SBIPS
Leviticus 18 in the SBISS
Leviticus 18 in the SBITS
Leviticus 18 in the SBITS2
Leviticus 18 in the SBITS3
Leviticus 18 in the SBITS4
Leviticus 18 in the SBIUS
Leviticus 18 in the SBIVS
Leviticus 18 in the SBT
Leviticus 18 in the SBT1E
Leviticus 18 in the SCHL
Leviticus 18 in the SNT
Leviticus 18 in the SUSU
Leviticus 18 in the SUSU2
Leviticus 18 in the SYNO
Leviticus 18 in the TBIAOTANT
Leviticus 18 in the TBT1E
Leviticus 18 in the TBT1E2
Leviticus 18 in the TFTIP
Leviticus 18 in the TFTU
Leviticus 18 in the TGNTATF3T
Leviticus 18 in the THAI
Leviticus 18 in the TNFD
Leviticus 18 in the TNT
Leviticus 18 in the TNTIK
Leviticus 18 in the TNTIL
Leviticus 18 in the TNTIN
Leviticus 18 in the TNTIP
Leviticus 18 in the TNTIZ
Leviticus 18 in the TOMA
Leviticus 18 in the TTENT
Leviticus 18 in the UBG
Leviticus 18 in the UGV
Leviticus 18 in the UGV2
Leviticus 18 in the UGV3
Leviticus 18 in the VBL
Leviticus 18 in the VDCC
Leviticus 18 in the YALU
Leviticus 18 in the YAPE
Leviticus 18 in the YBVTP
Leviticus 18 in the ZBP