Leviticus 25 (BOGWICC)

1 Yehova anawuza Mose pa phiri la Sinai kuti, 2 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Mukadzalowa mʼdziko limene ndikukupatsani, nthakayo iyenera kumakasunga Sabata la Yehova. 3 Pa zaka zisanu ndi chimodzi muzikalima minda yanu, ndipo kwa zaka zisanu ndi chimodzi muzikasadza mitengo yanu ya mpesa ndi kuthyola zipatso zake. 4 Koma chaka chachisanu ndi chiwiri ndi chaka choti nthaka ipume, chaka cha Sabata la Yehova. Musalime mʼminda yanu kapena kusadza mitengo yanu ya mpesa. 5 Musakolole zimene zinamera zokha mʼmunda mwanu. Musakakolole kapena kuthyola mphesa za mʼmitengo imene simunasadze. Chaka chimenechi nʼchoti nthaka ipumule. 6 Chaka chimene nthakayo ipumula mudzakhala ndi chakudya chokwanira inuyo, akapolo anu aamuna ndi aakazi, antchito ndi alendo okhala nanu. 7 Ziweto zanu pamodzi ndi nyama za mʼdziko lanu zizidzadya zipatso za mʼnthaka. 8 “ ‘Muzichotsera Masabata asanu ndi awiri a zaka, ndi kuchulukitsa zaka zisanu ndi ziwiri kasanu ndi kawirinso kuti Masabata asanu ndi awiri a zakawo akwane zaka 49. 9 Ndipo pa tsiku la khumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri mulize lipenga mofuwula. Tsiku lochita mwambo wopepesera machimo muziliza lipenga mʼdziko lanu lonse. 10 Mupatule chaka cha makumi asanu, ndipo mulengeze kuti pakhale ufulu mʼdziko lonse kwa onse amene ali mʼmenemo. Kwa inu chakachi chidzakhala choyimba lipenga la chikondwerero. Aliyense wa inu adzayenera kubwerera pa munda wake, ndipo aliyense wa inu adzabwerera ku fuko lake. 11 Kwa inu chakachi chidzakhaladi chaka choyimba lipenga kukondwerera zaka makumi asanu. Pa chaka chimenechi musadzale kanthu ndipo musakolole mbewu zomera zokha kapenanso kuthyola mphesa pa mitengo yosasadzira. 12 Chimenechi ndi chaka chokondwerera zaka makumi asanu. Choncho chikhale chaka chopatulika kwa inu. Muzidya zokhazo zimene zakololedwa mʼminda. 13 “ ‘Chaka chimenechi ndi choliza lipenga, kukondwerera zaka makumi asanu, ndipo aliyense abwerere pa malo ake. 14 “ ‘Ngati unagulitsa kapena kugula malo ako kwa mnzako wa mʼdzikomo, pasakhale kuchenjeretsana. 15 Ugule kwa mnzako potsata chiwerengero cha zaka zimene zatha kuyambira pa chikondwerero cha chaka cha makumi asanu chapita. Ndipo mnzakoyo akugulitse potsata chiwerengero cha zaka zokolola zomwe zatsala. 16 Zaka zikakhala zochuluka, uwonjezere mtengo, ndipo zaka zikakhala zochepa, uchepetse mtengo, pakuti chimene iye akukugulitsa ndi zaka zokolola. 17 Musachenjeretsane koma muope Mulungu wanu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 18 “ ‘Tsatirani malangizo anga ndipo mverani mosamala malamulo anga ndipo mudzakhala mʼdzikomo mwamtendere. 19 Ndipo nthaka idzakupatsani zipatso zake. Mudzadya mpaka kukhuta ndiponso mudzakhala mʼdzikomo mwamtendere. 20 Mwina nʼkafunsa kuti, ‘Kodi chaka chachisanu ndi chiwiri tidzadya chiyani ngati sitidzala kapena kukolola mbewu zathu?’ 21 Ine ndidzatumiza madalitso ambiri chaka chachisanu ndi chimodzi moti nthaka yanu idzabala zinthu zokwanira kudya zaka zitatu. 22 Pamene mukudzala chaka chachisanu ndi chitatu, muzidzadya chakudya chogonera ndipo mudzapitirira kudya mpaka nthawi yokolola mʼchaka chachisanu ndi chinayi. 23 “ ‘Malo asagulitsidwe mpaka muyaya chifukwa dzikolo ndi langa. Inu ndinu alendo okhala ndi Ine. 24 Malo onse amene ali mʼmanja mwanu mudzalole kuti amene anakugulitsani awawombole. 25 “ ‘Ngati Mwisraeli mnzanu wasauka nagulitsako gawo lina la malo ake, mʼbale wake wapaphata abwere kudzawombola malo amene mʼbale wakeyo wagulitsa. 26 Koma ngati munthuyo alibe wachibale woti nʼkuwombola malowo koma pambuyo pake iye mwini nʼkulemera ndi kupeza zokwanira kuwombolera, awombole malowo. 27 Awerengerane zaka kuyambira pamene anagulitsa mundawo ndipo amubwezere amene anagulayo ndalama zimene akanayenera kuzipereka mpaka chaka chokondwerera zaka makumi asanu. Atatero angathe kubwerera pa malo ake. 28 Koma ngati sakhala nazo zokwanira kuti amubwezere amene anagula malowo, gawo limene anagulitsalo lidzakhala mʼmanja mwa munthu amene anagulayo mpaka chaka chokondwerera zaka makumi asanu. Malowo adzabwezedwa chaka chimenechi, ndipo iye adzatha kubwerera pa malo ake. 29 “ ‘Ngati munthu agulitsa nyumba ya mu mzinda umene uli mu linga, angathe kuyiwombola nyumbayo chisanathe chaka chathunthu chigulitsire. Mu nthawi imeneyi wogulitsayo atha kuyiwombola. 30 Ngati nyumbayo siwomboledwa chisanathe chaka chimodzicho, nyumbayo idzakhala ya amene anagulayo ndi zidzukulu zake mpaka muyaya. Sidzabwezedwanso kwa mwini wake mʼchaka chokondwerera zaka makumi asanu. 31 Koma nyumba za mʼmizinda yosazingidwa ndi linga ziwomboledwe monga mmene achitira ndi minda ya mʼdzikomo. 32 “ ‘Alevi ali ndi ufulu owombola nyumba zawo za mʼmidzi yawo nthawi ina iliyonse. 33 Koma ngati Mlevi sawombola nyumba imene inagulitsidwa mʼmudzi mwake, ndiye kuti idzabwezedwe mʼchaka choliza lipenga pokondwerera zaka makumi asanu, popeza nyumba zimenezi zili mʼmidzi ya Alevi ndi yawo pakati pa Aisraeli. 34 Koma malo owetera ziweto a mʼmidzi yawoyo sayenera kugulitsidwa. Awa ndi malo awo mpaka muyaya. 35 “ ‘Ngati mʼbale wako akhala wosauka kuti sangathe kudzisamalira yekha, umuthandize. Ukhale naye ngati mlendo kapena ngati munthu amene ukhala naye kwa kanthawi. 36 Usalandire chiwongoladzanja chilichonse kuchokera kwa iye kapena kuwonjezerapo kanthu kena, koma uziopa Mulungu kuti mʼbale wakoyo akhale nawe. 37 Musakongoze mnzanu ndalama kuti mulandire chiwongoladzanja, kapena kumugulitsa chakudya kuti mupeze phindu. 38 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti ndikupatseni dziko la Kanaani ndi kuti ndikhale Mulungu wanu. 39 “ ‘Ngati mʼbale wanu asauka ndipo adzigulitsa yekha kwa inu, musamugwiritse ntchito ngati kapolo. 40 Akhale ngati wantchito kapena ngati mlendo. Akugwirireni ntchito mpaka chaka chokondwerera zaka makumi asanu. 41 Kenaka iye ndi ana ake achoke, ndipo apite ku fuko lake ndi kubwerera ku malo a makolo ake. 42 Chifukwa Aisraeli ndi atumiki anga amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto, asagulitsidwe ngati akapolo. 43 Musawalamulire mwankhanza koma wopani Mulungu wanu. 44 “ ‘Kunena za akapolo aamuna ndi aakazi, amenewa mungathe kuwagula kuchokera kwa mitundu ya anthu imene yakuzungulirani. 45 Mungathenso kugula akapolo kuchokera kwa alendo amene akukhala nanu kapena kuchokera ku mabanja amene mukukhala nawo amene ndi mbadwa za mʼdziko lanu. Iwowa akhoza kukhala akapolo anu. 46 Akapolowo mungathe kuwasiya mʼmanja mwa ana anu inu mutafa kuti akhale cholowa chawo moyo wawo wonse. Koma musawalamulire mwankhanza Aisraeli anzanu. 47 “ ‘Ngati mlendo kapena munthu amene akukhala nanu kwa kanthawi kochepa alemera ndipo mmodzi wa abale anu amene akukhala naye pafupi nʼkusauka, nadzigulitsa yekha kwa mlendo amene akukhala pakati panuyo kapena kwa mmodzi wa fuko la munthu wongokhala pafupi nayeyo, 48 wodzigulitsayo ali ndi ufulu wowomboledwa. Mmodzi mwa abale ake angathe kumuwombola: 49 amalume ake kapena mwana wa amalume ake, kapena wachibale wa mu fuko lake. Kapena ngati iye mwini alemera, atha kudziwombola yekha. 50 Iye pamodzi ndi munthu amene anamugulayo awerengerane kuyambira chaka chimene anadzigulitsa kwa iyeyo mpaka chaka chokondwerera zaka makumi asanu. Mtengo wodziwombolera ukhale wofanana ndi zakazo. Ndipo nthawi imene anali ndi mbuye wakeyo iwerengedwe ngati nthawi ya munthu wantchito. 51 Ngati patsala zaka zambiri, iye ayenera kulipira mtengo woposera umene anamugulira. 52 Ngati kwatsala zaka zochepa kuti ifike nthawi ya chaka chokondwerera zaka makumi asanu, iye awerengerane ndi mbuye wake, ndipo apereke ndalama za zowomboledwera molingana ndi zaka zotsalazo. 53 Azikhala naye ngati wantchito wolembedwa chaka ndi chaka. Ndipo muonetsetse kuti mbuye wakeyo sakumulamulira mwankhanza. 54 “ ‘Ngakhale munthuyo atapanda kuwomboledwa mwa njira zimenezi, iye ndi ana ake ayenera kumasulidwa mʼchaka chokondwerera zaka makumi asanu, 55 pakuti Aisraeli ndi atumiki anga. Iwo ndi atumiki anga amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

In Other Versions

Leviticus 25 in the ANGEFD

Leviticus 25 in the ANTPNG2D

Leviticus 25 in the AS21

Leviticus 25 in the BAGH

Leviticus 25 in the BBPNG

Leviticus 25 in the BBT1E

Leviticus 25 in the BDS

Leviticus 25 in the BEV

Leviticus 25 in the BHAD

Leviticus 25 in the BIB

Leviticus 25 in the BLPT

Leviticus 25 in the BNT

Leviticus 25 in the BNTABOOT

Leviticus 25 in the BNTLV

Leviticus 25 in the BOATCB

Leviticus 25 in the BOATCB2

Leviticus 25 in the BOBCV

Leviticus 25 in the BOCNT

Leviticus 25 in the BOECS

Leviticus 25 in the BOHCB

Leviticus 25 in the BOHCV

Leviticus 25 in the BOHLNT

Leviticus 25 in the BOHNTLTAL

Leviticus 25 in the BOICB

Leviticus 25 in the BOILNTAP

Leviticus 25 in the BOITCV

Leviticus 25 in the BOKCV

Leviticus 25 in the BOKCV2

Leviticus 25 in the BOKHWOG

Leviticus 25 in the BOKSSV

Leviticus 25 in the BOLCB

Leviticus 25 in the BOLCB2

Leviticus 25 in the BOMCV

Leviticus 25 in the BONAV

Leviticus 25 in the BONCB

Leviticus 25 in the BONLT

Leviticus 25 in the BONUT2

Leviticus 25 in the BOPLNT

Leviticus 25 in the BOSCB

Leviticus 25 in the BOSNC

Leviticus 25 in the BOTLNT

Leviticus 25 in the BOVCB

Leviticus 25 in the BOYCB

Leviticus 25 in the BPBB

Leviticus 25 in the BPH

Leviticus 25 in the BSB

Leviticus 25 in the CCB

Leviticus 25 in the CUV

Leviticus 25 in the CUVS

Leviticus 25 in the DBT

Leviticus 25 in the DGDNT

Leviticus 25 in the DHNT

Leviticus 25 in the DNT

Leviticus 25 in the ELBE

Leviticus 25 in the EMTV

Leviticus 25 in the ESV

Leviticus 25 in the FBV

Leviticus 25 in the FEB

Leviticus 25 in the GGMNT

Leviticus 25 in the GNT

Leviticus 25 in the HARY

Leviticus 25 in the HNT

Leviticus 25 in the IRVA

Leviticus 25 in the IRVB

Leviticus 25 in the IRVG

Leviticus 25 in the IRVH

Leviticus 25 in the IRVK

Leviticus 25 in the IRVM

Leviticus 25 in the IRVM2

Leviticus 25 in the IRVO

Leviticus 25 in the IRVP

Leviticus 25 in the IRVT

Leviticus 25 in the IRVT2

Leviticus 25 in the IRVU

Leviticus 25 in the ISVN

Leviticus 25 in the JSNT

Leviticus 25 in the KAPI

Leviticus 25 in the KBT1ETNIK

Leviticus 25 in the KBV

Leviticus 25 in the KJV

Leviticus 25 in the KNFD

Leviticus 25 in the LBA

Leviticus 25 in the LBLA

Leviticus 25 in the LNT

Leviticus 25 in the LSV

Leviticus 25 in the MAAL

Leviticus 25 in the MBV

Leviticus 25 in the MBV2

Leviticus 25 in the MHNT

Leviticus 25 in the MKNFD

Leviticus 25 in the MNG

Leviticus 25 in the MNT

Leviticus 25 in the MNT2

Leviticus 25 in the MRS1T

Leviticus 25 in the NAA

Leviticus 25 in the NASB

Leviticus 25 in the NBLA

Leviticus 25 in the NBS

Leviticus 25 in the NBVTP

Leviticus 25 in the NET2

Leviticus 25 in the NIV11

Leviticus 25 in the NNT

Leviticus 25 in the NNT2

Leviticus 25 in the NNT3

Leviticus 25 in the PDDPT

Leviticus 25 in the PFNT

Leviticus 25 in the RMNT

Leviticus 25 in the SBIAS

Leviticus 25 in the SBIBS

Leviticus 25 in the SBIBS2

Leviticus 25 in the SBICS

Leviticus 25 in the SBIDS

Leviticus 25 in the SBIGS

Leviticus 25 in the SBIHS

Leviticus 25 in the SBIIS

Leviticus 25 in the SBIIS2

Leviticus 25 in the SBIIS3

Leviticus 25 in the SBIKS

Leviticus 25 in the SBIKS2

Leviticus 25 in the SBIMS

Leviticus 25 in the SBIOS

Leviticus 25 in the SBIPS

Leviticus 25 in the SBISS

Leviticus 25 in the SBITS

Leviticus 25 in the SBITS2

Leviticus 25 in the SBITS3

Leviticus 25 in the SBITS4

Leviticus 25 in the SBIUS

Leviticus 25 in the SBIVS

Leviticus 25 in the SBT

Leviticus 25 in the SBT1E

Leviticus 25 in the SCHL

Leviticus 25 in the SNT

Leviticus 25 in the SUSU

Leviticus 25 in the SUSU2

Leviticus 25 in the SYNO

Leviticus 25 in the TBIAOTANT

Leviticus 25 in the TBT1E

Leviticus 25 in the TBT1E2

Leviticus 25 in the TFTIP

Leviticus 25 in the TFTU

Leviticus 25 in the TGNTATF3T

Leviticus 25 in the THAI

Leviticus 25 in the TNFD

Leviticus 25 in the TNT

Leviticus 25 in the TNTIK

Leviticus 25 in the TNTIL

Leviticus 25 in the TNTIN

Leviticus 25 in the TNTIP

Leviticus 25 in the TNTIZ

Leviticus 25 in the TOMA

Leviticus 25 in the TTENT

Leviticus 25 in the UBG

Leviticus 25 in the UGV

Leviticus 25 in the UGV2

Leviticus 25 in the UGV3

Leviticus 25 in the VBL

Leviticus 25 in the VDCC

Leviticus 25 in the YALU

Leviticus 25 in the YAPE

Leviticus 25 in the YBVTP

Leviticus 25 in the ZBP