Leviticus 7 (BOGWICC)

1 “ ‘Malamulo a nsembe yopepesera kupalamula imene ndi nsembe yopatulika kwambiri ndi awa: 2 Nsembe yopepesera machimo iziphedwa pamalo pomwe amaphera nsembe yopsereza ndipo awaze magazi ake mbali zonse za guwa. 3 Tsono apereke mafuta ake onse: mchira wamafuta ndi mafuta amene amakuta matumbo. 4 Aperekenso impsyo ziwiri, mafuta ake pamodzi ndi mafuta onse amene ali chamʼchiwuno, ndiponso mafuta onse amene aphimba chiwindi. 5 Wansembe azitenthe pa guwa kuti zikhale nsembe yotentha pa moto, yoperekedwa kwa Yehova. Imeneyi ndi nsembe yopepesera tchimo lopalamula. 6 Munthu wamwamuna aliyense wa mʼbanja la wansembe angathe kudyako nsembeyo koma adyere ku malo opatulika. Imeneyi ndi nsembe yopatulika kwambiri. 7 “ ‘Nsembe yopepesera tchimo lopalamula ndi yofanana ndi nsembe yoperekedwa chifukwa cha tchimo. Ndipo nsembe ziwiri zonsezi zili ndi lamulo limodzi lokha. Wansembe amene wachita mwambo wa nsembe yopepesera machimo a kupalamula atenge nyamayo ngati yake. 8 Wansembe wopereka nsembe yopsereza ya munthu wina aliyense, atenge chikopa cha nsembe yopserezayo kuti chikhale chake. 9 Chopereka chilichonse cha chakudya chophika mu uvuni kapena chokazinga mu mʼphika kapena mu chiwaya ndi cha wansembe amene wapereka nsembezo. 10 Ndipo chopereka china chilichonse cha chakudya chosakaniza ndi mafuta kapena chowuma, chikhale cha ana onse a Aaroni ndipo anawo achigawane mofanana. 11 “ ‘Malamulo a nsembe ya chiyanjano imene munthu angathe kupereka kwa Yehova ndi awa: 12 “ ‘Ngati munthuyo apereka chifukwa cha kuthokoza, apereke nsembeyo pamodzi ndi makeke wopanda yisiti, osakaniza ndi mafuta; timitanda ta buledi wopanda yisiti, topyapyala, topaka mafuta, ndiponso makeke a ufa wosalala wophikidwa bwino, wosakaniza ndi mafuta. 13 Pamodzi ndi nsembe yachiyanjano yothokozerayo abwerenso ndi makeke opangidwa ndi yisiti ngati chopereka chake. 14 Munthuyo atenge mtanda umodzi pa mtanda wa buledi wa mtundu uliwonse kuti ukhale nsembe yopereka kwa Yehova. Tsono mtanda umenewo ndi wake wa wansembe amene awaze magazi a nsembe yachiyanjano. 15 Nyama ya nsembe yachiyanjano yothokozera idyedwe pa tsiku lomwe nsembeyo yaperekedwa ndipo isatsaleko mpaka mmawa. 16 “ ‘Koma ngati nsembe yakeyo apereka chifukwa cha lumbiro kapena mwaufulu, nsembeyo adye tsiku lomwe yaperekedwalo. Koma yotsala angathe kuyidya mmawa mwake. 17 Ngati nyama ina ya nsembe yatsalabe mpaka tsiku lachitatu, imeneyo itenthedwe pa moto. 18 Ngati munthu adya nyama yachiyanjano pa tsiku lachitatu, nsembeyo sidzalandiridwa. Amene wayipereka nsembeyo Mulungu sadzamulandira ndipo nsembeyo idzakhala yonyansa pamaso pa Mulungu, yosamupindulira kanthu woperekayo. 19 “ ‘Nyama imene yakhudza chilichonse chodetsedwa, munthu asayidye, koma itenthedwe pa moto. Aliyense amene ali woyeretsedwa angathe kudya nyama inayo. 20 Koma ngati munthu wina amene ndi wosayeretsedwa adya nyama ya nsembe yachiyanjano imene ndi ya Yehova, ameneyo achotsedwe pakati pa anthu a mtundu wake. 21 Ndipo ngati munthu wina akhudza chinthu chodetsedwa, kaya chonyansa cha munthu kapena cha nyama, kapenanso chonyansa china chilichonse, ndipo kenaka nʼkudya nyama ya nsembe yachiyanjano imene ndi ya Yehova, munthu ameneyo achotsedwe pakati anthu a mtundu wake.’ ” 22 Yehova anayankhula ndi Mose kuti, 23 “Awuze Aisraeli kuti, ‘Musadye mafuta a ngʼombe, nkhosa kapenanso mbuzi. 24 Mafuta a nyama yofa yokha, kapena mafuta a nyama yophedwa ndi zirombo akhoza kuwagwiritsa ntchito iliyonse, koma inu musadye mafuta amenewo. 25 Pakuti munthu wakudya mafuta a nyama yoperekedwa kwa Yehova ngati nsembe yotentha pa moto, ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu a mtundu wake. 26 Ndipo kulikonse kumene mukakhale musakadye magazi a mbalame iliyonse kapena magazi a nyama iliyonse. 27 Ngati munthu aliyense adya magazi achotsedwe pakati pa anthu a mtundu wake.’ ” 28 Yehova anayankhula ndi Mose kuti, 29 “Awuze Aisraeli kuti, Aliyense amene apereka nsembe yachiyanjano kwa Yehova, abwere ndi gawo la nsembeyo kwa Yehova. 30 Atenge ndi manja ake zigawo za chopereka zoyenera kuzitentha pa moto ngati chopereka kwa Yehova. Abweretse mafuta, pamodzi ndi chidale chomwe, ndipo chidalecho achiweyule kuti chikhale chopereka choweyula kwa Yehova. 31 Wansembe atenthe mafutawo pa guwa koma chidalecho chikhale cha Aaroni ndi ana ake. 32 Mumupatse wansembe ntchafu ya kumanja ya nsembe yanu yachiyanjano kuti ikhale chopereka chanu kwa iye. 33 Mwana wa Aaroni amene amapereka magazi ndi mafuta a nsembe yachiyanjano, adzitenga ntchafu ya kumanja kukhala gawo lake. 34 Choncho pa zopereka zachiyanjano za Aisraeli, Ine ndatengapo chidale chomwe amaweyula ndi ntchafu zimene amapereka nsembe ndipo ndazipereka kwa wansembe Aaroni ndi ana ake. Izi ndizo gawo lawo nthawi zonse pa zopereka za Aisraeli.” 35 Zimenezi ndi chigawo cha Aaroni ndi ana ake chotapidwa pa zopereka kwa Yehova zoti zitenthedwe pa moto zimene zinaperekedwa pa tsiku limene anapatulidwa kuti akhale ansembe otumikira Yehova. 36 Yehova ndiye analamulira kuti pa zopereka za Aisraeli azitapapo zimenezi ndi kuwapatsa ansembe ngati gawo lawo. Yehovayo analamula zimenezi pa tsiku limene ansembewo anapatulidwa ndipo anachikhazikitsa ngati lamulo la nthawi zonse. 37 Awa ndi malamulo a nsembe izi: nsembe yopsereza, nsembe yachakudya, nsembe yopepesera machimo, nsembe yopepesera kupalamula, nsembe ya mwambo wodzoza ndi nsembe yachiyanjano. 38 Malamulo amenewa Yehova anapereka kwa Mose pa Phiri la Sinai pa tsiku limene Yehova analamulira Aisraeli kuti abwere ndi zopereka za kwa Yehova, ku chipululu cha Sinai kuja.

In Other Versions

Leviticus 7 in the ANGEFD

Leviticus 7 in the ANTPNG2D

Leviticus 7 in the AS21

Leviticus 7 in the BAGH

Leviticus 7 in the BBPNG

Leviticus 7 in the BBT1E

Leviticus 7 in the BDS

Leviticus 7 in the BEV

Leviticus 7 in the BHAD

Leviticus 7 in the BIB

Leviticus 7 in the BLPT

Leviticus 7 in the BNT

Leviticus 7 in the BNTABOOT

Leviticus 7 in the BNTLV

Leviticus 7 in the BOATCB

Leviticus 7 in the BOATCB2

Leviticus 7 in the BOBCV

Leviticus 7 in the BOCNT

Leviticus 7 in the BOECS

Leviticus 7 in the BOHCB

Leviticus 7 in the BOHCV

Leviticus 7 in the BOHLNT

Leviticus 7 in the BOHNTLTAL

Leviticus 7 in the BOICB

Leviticus 7 in the BOILNTAP

Leviticus 7 in the BOITCV

Leviticus 7 in the BOKCV

Leviticus 7 in the BOKCV2

Leviticus 7 in the BOKHWOG

Leviticus 7 in the BOKSSV

Leviticus 7 in the BOLCB

Leviticus 7 in the BOLCB2

Leviticus 7 in the BOMCV

Leviticus 7 in the BONAV

Leviticus 7 in the BONCB

Leviticus 7 in the BONLT

Leviticus 7 in the BONUT2

Leviticus 7 in the BOPLNT

Leviticus 7 in the BOSCB

Leviticus 7 in the BOSNC

Leviticus 7 in the BOTLNT

Leviticus 7 in the BOVCB

Leviticus 7 in the BOYCB

Leviticus 7 in the BPBB

Leviticus 7 in the BPH

Leviticus 7 in the BSB

Leviticus 7 in the CCB

Leviticus 7 in the CUV

Leviticus 7 in the CUVS

Leviticus 7 in the DBT

Leviticus 7 in the DGDNT

Leviticus 7 in the DHNT

Leviticus 7 in the DNT

Leviticus 7 in the ELBE

Leviticus 7 in the EMTV

Leviticus 7 in the ESV

Leviticus 7 in the FBV

Leviticus 7 in the FEB

Leviticus 7 in the GGMNT

Leviticus 7 in the GNT

Leviticus 7 in the HARY

Leviticus 7 in the HNT

Leviticus 7 in the IRVA

Leviticus 7 in the IRVB

Leviticus 7 in the IRVG

Leviticus 7 in the IRVH

Leviticus 7 in the IRVK

Leviticus 7 in the IRVM

Leviticus 7 in the IRVM2

Leviticus 7 in the IRVO

Leviticus 7 in the IRVP

Leviticus 7 in the IRVT

Leviticus 7 in the IRVT2

Leviticus 7 in the IRVU

Leviticus 7 in the ISVN

Leviticus 7 in the JSNT

Leviticus 7 in the KAPI

Leviticus 7 in the KBT1ETNIK

Leviticus 7 in the KBV

Leviticus 7 in the KJV

Leviticus 7 in the KNFD

Leviticus 7 in the LBA

Leviticus 7 in the LBLA

Leviticus 7 in the LNT

Leviticus 7 in the LSV

Leviticus 7 in the MAAL

Leviticus 7 in the MBV

Leviticus 7 in the MBV2

Leviticus 7 in the MHNT

Leviticus 7 in the MKNFD

Leviticus 7 in the MNG

Leviticus 7 in the MNT

Leviticus 7 in the MNT2

Leviticus 7 in the MRS1T

Leviticus 7 in the NAA

Leviticus 7 in the NASB

Leviticus 7 in the NBLA

Leviticus 7 in the NBS

Leviticus 7 in the NBVTP

Leviticus 7 in the NET2

Leviticus 7 in the NIV11

Leviticus 7 in the NNT

Leviticus 7 in the NNT2

Leviticus 7 in the NNT3

Leviticus 7 in the PDDPT

Leviticus 7 in the PFNT

Leviticus 7 in the RMNT

Leviticus 7 in the SBIAS

Leviticus 7 in the SBIBS

Leviticus 7 in the SBIBS2

Leviticus 7 in the SBICS

Leviticus 7 in the SBIDS

Leviticus 7 in the SBIGS

Leviticus 7 in the SBIHS

Leviticus 7 in the SBIIS

Leviticus 7 in the SBIIS2

Leviticus 7 in the SBIIS3

Leviticus 7 in the SBIKS

Leviticus 7 in the SBIKS2

Leviticus 7 in the SBIMS

Leviticus 7 in the SBIOS

Leviticus 7 in the SBIPS

Leviticus 7 in the SBISS

Leviticus 7 in the SBITS

Leviticus 7 in the SBITS2

Leviticus 7 in the SBITS3

Leviticus 7 in the SBITS4

Leviticus 7 in the SBIUS

Leviticus 7 in the SBIVS

Leviticus 7 in the SBT

Leviticus 7 in the SBT1E

Leviticus 7 in the SCHL

Leviticus 7 in the SNT

Leviticus 7 in the SUSU

Leviticus 7 in the SUSU2

Leviticus 7 in the SYNO

Leviticus 7 in the TBIAOTANT

Leviticus 7 in the TBT1E

Leviticus 7 in the TBT1E2

Leviticus 7 in the TFTIP

Leviticus 7 in the TFTU

Leviticus 7 in the TGNTATF3T

Leviticus 7 in the THAI

Leviticus 7 in the TNFD

Leviticus 7 in the TNT

Leviticus 7 in the TNTIK

Leviticus 7 in the TNTIL

Leviticus 7 in the TNTIN

Leviticus 7 in the TNTIP

Leviticus 7 in the TNTIZ

Leviticus 7 in the TOMA

Leviticus 7 in the TTENT

Leviticus 7 in the UBG

Leviticus 7 in the UGV

Leviticus 7 in the UGV2

Leviticus 7 in the UGV3

Leviticus 7 in the VBL

Leviticus 7 in the VDCC

Leviticus 7 in the YALU

Leviticus 7 in the YAPE

Leviticus 7 in the YBVTP

Leviticus 7 in the ZBP