Numbers 16 (BOGWICC)

1 Kora mwana wa Izihari, mwana wa Kohati, mwana wa Levi ndi Datani ndi Abiramu ana a Eliabu, pamodzi ndi Oni mwana wa Perezi, ana a Rubeni, anayamba kudzikuza, 2 ndipo anawukira Mose. Mʼgulu mwawo munali atsogoleri a Aisraeli 250, anthu otchuka amene anasankhidwa ndi anthu pa msonkhano. 3 Iwo anasonkhana kudzatsutsana ndi Mose ndi Aaroni nawawuza kuti, “Mwawonjeza! Anthu onsewa ndi oyera, aliyense wa iwo, ndipo Yehova ali pakati pawo. Chifukwa chiyani mukudzikuza pakati pa gulu lonse la Yehova?” 4 Mose atamva izi, anagwa chafufumimba. 5 Ndipo iye anawuza Kora ndi anthu onse amene ankamutsatira kuti, “Yehova mawa mmawa adzasonyeza yemwe ndi wake ndiponso amene ndi woyera mtima. Munthuyo adzabwera pafupi ndi Iye. Munthu amene adzamusankheyo adzamusendeza pafupi. 6 Iwe Kora pamodzi ndi onse amene akukutsatira chitani izi: Tengani zofukizira 7 ndipo mawa muyikemo moto ndi lubani pamaso pa Yehova. Munthu amene Yehova amusankhe ndiye amene ali woyera. Alevi inu mwawonjeza kwambiri!” 8 Mose anawuzanso Kora kuti, “Inu Alevi, tsopano tamverani! 9 Kodi sizinakukwanireni kuti Mulungu wa Israeli anakupatulani pakati pa gulu lonse la Aisraeli ndi kukubweretsani pafupi ndi Iye, kuti muzigwira ntchito ku nyumba ya Yehova ndi kumayima pamaso pa gulu, kumatumikira? 10 Wakubweretsa iwe pamodzi ndi Alevi anzako kufupi ndi Iye mwini. Koma tsopano ukufuna kutenganso unsembe. 11 Nʼkulakwira Yehova kuti iwe ndi gulu lako lonseli mwasonkhana kuti mutsutsane ndi Yehova. Kodi Aaroni ndani kuti muzikangana naye?” 12 Kenaka Mose anayitana Datani ndi Abiramu, ana aamuna a Eliabu koma iwo anati, “Sitibwera! 13 Kodi sikukwanira kuti unatitulutsa, kutichotsa mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi kuti udzatiphe mʼchipululu muno? Kodi tsopano ukufunanso kutilemetsa? 14 Kuwonjezera apo, sunatilowetse mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi kapena kutipatsa malo wolima ndi minda ya mpesa. Kodi ukufuna kuchotsa maso a anthuwa? Ayi, sitibwera!” 15 Pamenepo Mose anakwiya kwambiri ndipo anati kwa Yehova, “Musalandire chopereka chawo. Sindinatenge kalikonse kwa iwo ngakhale bulu, ndiponso sindinalakwire wina aliyense wa iwo.” 16 Mose anati kwa Kora, “Iwe ndi okutsatira onse mudzaonekere pamaso pa Yehova mawa, iweyo ndi iwowo pamodzi ndi Aaroni. 17 Munthu aliyense akatenge chofukizira ndi kuyikamo lubani, zofukizira 250 zonse pamodzi ndi kuzibweretsa pamaso pa Yehova. Iwe ndi Aaroni mudzabweretsenso zofukizira zanu.” 18 Choncho munthu aliyense anatenga chofukizira chake nayikamo moto ndi lubani, ndipo anayima pamodzi ndi Mose ndi Aaroni pa khomo la tenti ya msonkhano. 19 Kora atasonkhanitsa omutsatira ake onse amene amatsutsa nawo pa khomo la tenti ya msonkhano, ulemerero wa Yehova unaonekera kwa gulu lonselo. 20 Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti, 21 “Chokani pakati pa gulu ili kuti ndithetse mkanganowu kamodzinʼkamodzi.” 22 Koma Mose ndi Aaroni anadzigwetsa chafufumimba ndipo analira mokweza, “Chonde Mulungu, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, kodi mudzakwiyira gulu lonse pamene munthu mmodzi yekha ndiye amene wachimwa?” 23 Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, 24 “Uza gulu lonse kuti, ‘Khalani kutali ndi matenti a Kora, Datani ndi Abiramu.’ ” 25 Mose anayimirira napita kwa Datani, Abiramu ndi kwa akuluakulu a Israeli amene ankamutsatira. 26 Anachenjeza gulu lonse kuti, “Khalani kutali ndi matenti a anthu oyipawa! Musakhudze kanthu kawo kalikonse, mukatero mudzawonongedwa limodzi nawo chifukwa cha machimo awo.” 27 Choncho anthuwo anachokadi ku matenti a Kora, Datani ndi Abiramu. Datani ndi Abiramu anali atatuluka nayima pamodzi ndi akazi awo, ana awo ndi makanda awo pa makomo a matenti awo. 28 Tsono Mose anati, “Umu ndi mmene mudzadziwire kuti Yehova ndiye amene anandituma kuti ndichite zinthu zonsezi ndipo kuti si maganizo anga. 29 Ngati anthu awa afa ndi imfa ya chilengedwe ndi kuwachitikira zomwe zimachitikira munthu aliyense, ndiye kuti Yehova sananditume. 30 Koma Yehova akachita china chake chachilendo, nthaka nitsekula pakamwa pake ndi kuwameza iwo pamodzi ndi zonse zimene ali nazo, iwowa nʼkulowa mʼmanda ali moyo, pamenepo mudzazindikira kuti anthu amenewa ananyoza Yehova.” 31 Atangotsiriza kuyankhula zimenezi, nthaka ya pamene anayimapo inagawikana 32 ndipo dziko linatsekula pakamwa pake ndi kuwameza pamodzi ndi nyumba zawo ndi anthu onse a Kora ndi katundu wawo yense. 33 Analowa mʼmanda amoyo pamodzi ndi zonse zimene anali nazo. Nthaka inawatsekera ndi kuwawononga ndipo sanaonekenso. 34 Atamva kulira kwawo, Aisraeli onse amene anali pafupi ndi anthuwo anathawa akufuwula kuti, “Nthaka imezanso ife!” 35 Ndipo moto wochokera kwa Yehova unabwera nʼkunyeketsa anthu 250 amene ankapereka nsembe yofukiza aja. 36 Yehova anawuza Mose kuti, 37 “Uza Eliezara mwana wa Aaroni, wansembe kuti atenge zofukizirazo pakati pa mitembo yopsererayo ndipo amwazire makalawo kutali chifukwa zofukizirazo nʼzopatulika. 38 Izi ndi zofukizira za anthu omwe anafa chifukwa cha uchimo wawo. Musule zofukizirazo kuti zikhale zophimbira pa guwa lansembe, chifukwa zinaperekedwa kwa Yehova ndipo ndi zopatulika. Zimenezi zikhale chizindikiro kwa Aisraeli.” 39 Choncho Eliezara, wansembe, anasonkhanitsa zofukizira zamkuwa zija zomwe anthu opsererawo anabwera nazo ndipo anazisula kuti zikhale zophimbira pa guwa lansembe, 40 monga momwe Yehova anamulangizira kudzera mwa Mose. Chimenechi chinali chikumbutso kwa Aisraeli kuti munthu wina aliyense, kupatula zidzukulu za Aaroni, sayenera kupsereza lubani pamaso pa Yehova, kuopa kuti munthu woteroyo angakhale ngati Kora ndi omutsatira ake. 41 Tsiku lotsatira, gulu lonse la Aisraeli linatsutsana ndi Mose ndi Aaroni. Iwo anati, “Inu mwapha anthu a Yehova.” 42 Koma pamene anthuwo anasonkhana kuti atsutsane ndi Mose ndi Aaroni, atatembenuka kuyangʼana ku tenti ya msonkhano, mwadzidzidzi mtambo unaphimba tentiyo ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera. 43 Pamenepo Mose ndi Aaroni anapita patsogolo pa tenti ya msonkhano ija 44 ndipo Yehova anawuza Mose kuti, 45 “Chokani pakati pa gulu la anthuwa kuti ndiwawononge kamodzinʼkamodzi.” Ndipo iwo anagwa pansi chafufumimba. 46 Kenaka Mose anawuza Aaroni kuti, “Tenga chofukizira chako ndipo ikamo lubani pamodzi ndi moto wochokera pa guwa lansembe, fulumira, pita pa gulu la anthuwo ndipo ukachite nsembe yopepesera machimo awo popeza mkwiyo wa Yehova wafika, mliri wayamba.” 47 Ndipo Aaroni anachita monga ananenera Mose, nathamangira mʼkatikati mwa gulu la anthuwo. Pamenepo nʼkuti mliri utayamba kale pakati pa anthu aja ndipo Aaroni anafukiza lubani ndi kupereka nsembe yopepesera machimo awo. 48 Iye anayimirira pakati pa anthu amoyo ndi akufa ndipo mliri unaleka. 49 Komabe anthu 14, 700 anafa ndi mliriwo, kuwonjezera pa aja amene anafa chifukwa cha Kora. 50 Ndipo Aaroni anabwerera kwa Mose ku khomo la tenti ya msonkhano, chifukwa mliriwo unali utatha.

In Other Versions

Numbers 16 in the ANGEFD

Numbers 16 in the ANTPNG2D

Numbers 16 in the AS21

Numbers 16 in the BAGH

Numbers 16 in the BBPNG

Numbers 16 in the BBT1E

Numbers 16 in the BDS

Numbers 16 in the BEV

Numbers 16 in the BHAD

Numbers 16 in the BIB

Numbers 16 in the BLPT

Numbers 16 in the BNT

Numbers 16 in the BNTABOOT

Numbers 16 in the BNTLV

Numbers 16 in the BOATCB

Numbers 16 in the BOATCB2

Numbers 16 in the BOBCV

Numbers 16 in the BOCNT

Numbers 16 in the BOECS

Numbers 16 in the BOHCB

Numbers 16 in the BOHCV

Numbers 16 in the BOHLNT

Numbers 16 in the BOHNTLTAL

Numbers 16 in the BOICB

Numbers 16 in the BOILNTAP

Numbers 16 in the BOITCV

Numbers 16 in the BOKCV

Numbers 16 in the BOKCV2

Numbers 16 in the BOKHWOG

Numbers 16 in the BOKSSV

Numbers 16 in the BOLCB

Numbers 16 in the BOLCB2

Numbers 16 in the BOMCV

Numbers 16 in the BONAV

Numbers 16 in the BONCB

Numbers 16 in the BONLT

Numbers 16 in the BONUT2

Numbers 16 in the BOPLNT

Numbers 16 in the BOSCB

Numbers 16 in the BOSNC

Numbers 16 in the BOTLNT

Numbers 16 in the BOVCB

Numbers 16 in the BOYCB

Numbers 16 in the BPBB

Numbers 16 in the BPH

Numbers 16 in the BSB

Numbers 16 in the CCB

Numbers 16 in the CUV

Numbers 16 in the CUVS

Numbers 16 in the DBT

Numbers 16 in the DGDNT

Numbers 16 in the DHNT

Numbers 16 in the DNT

Numbers 16 in the ELBE

Numbers 16 in the EMTV

Numbers 16 in the ESV

Numbers 16 in the FBV

Numbers 16 in the FEB

Numbers 16 in the GGMNT

Numbers 16 in the GNT

Numbers 16 in the HARY

Numbers 16 in the HNT

Numbers 16 in the IRVA

Numbers 16 in the IRVB

Numbers 16 in the IRVG

Numbers 16 in the IRVH

Numbers 16 in the IRVK

Numbers 16 in the IRVM

Numbers 16 in the IRVM2

Numbers 16 in the IRVO

Numbers 16 in the IRVP

Numbers 16 in the IRVT

Numbers 16 in the IRVT2

Numbers 16 in the IRVU

Numbers 16 in the ISVN

Numbers 16 in the JSNT

Numbers 16 in the KAPI

Numbers 16 in the KBT1ETNIK

Numbers 16 in the KBV

Numbers 16 in the KJV

Numbers 16 in the KNFD

Numbers 16 in the LBA

Numbers 16 in the LBLA

Numbers 16 in the LNT

Numbers 16 in the LSV

Numbers 16 in the MAAL

Numbers 16 in the MBV

Numbers 16 in the MBV2

Numbers 16 in the MHNT

Numbers 16 in the MKNFD

Numbers 16 in the MNG

Numbers 16 in the MNT

Numbers 16 in the MNT2

Numbers 16 in the MRS1T

Numbers 16 in the NAA

Numbers 16 in the NASB

Numbers 16 in the NBLA

Numbers 16 in the NBS

Numbers 16 in the NBVTP

Numbers 16 in the NET2

Numbers 16 in the NIV11

Numbers 16 in the NNT

Numbers 16 in the NNT2

Numbers 16 in the NNT3

Numbers 16 in the PDDPT

Numbers 16 in the PFNT

Numbers 16 in the RMNT

Numbers 16 in the SBIAS

Numbers 16 in the SBIBS

Numbers 16 in the SBIBS2

Numbers 16 in the SBICS

Numbers 16 in the SBIDS

Numbers 16 in the SBIGS

Numbers 16 in the SBIHS

Numbers 16 in the SBIIS

Numbers 16 in the SBIIS2

Numbers 16 in the SBIIS3

Numbers 16 in the SBIKS

Numbers 16 in the SBIKS2

Numbers 16 in the SBIMS

Numbers 16 in the SBIOS

Numbers 16 in the SBIPS

Numbers 16 in the SBISS

Numbers 16 in the SBITS

Numbers 16 in the SBITS2

Numbers 16 in the SBITS3

Numbers 16 in the SBITS4

Numbers 16 in the SBIUS

Numbers 16 in the SBIVS

Numbers 16 in the SBT

Numbers 16 in the SBT1E

Numbers 16 in the SCHL

Numbers 16 in the SNT

Numbers 16 in the SUSU

Numbers 16 in the SUSU2

Numbers 16 in the SYNO

Numbers 16 in the TBIAOTANT

Numbers 16 in the TBT1E

Numbers 16 in the TBT1E2

Numbers 16 in the TFTIP

Numbers 16 in the TFTU

Numbers 16 in the TGNTATF3T

Numbers 16 in the THAI

Numbers 16 in the TNFD

Numbers 16 in the TNT

Numbers 16 in the TNTIK

Numbers 16 in the TNTIL

Numbers 16 in the TNTIN

Numbers 16 in the TNTIP

Numbers 16 in the TNTIZ

Numbers 16 in the TOMA

Numbers 16 in the TTENT

Numbers 16 in the UBG

Numbers 16 in the UGV

Numbers 16 in the UGV2

Numbers 16 in the UGV3

Numbers 16 in the VBL

Numbers 16 in the VDCC

Numbers 16 in the YALU

Numbers 16 in the YAPE

Numbers 16 in the YBVTP

Numbers 16 in the ZBP