Numbers 22 (BOGWICC)

1 Aisraeli anayenda kupita ku zigwa za Mowabu nakamanga misasa yawo tsidya lina la Yorodani moyangʼanana ndi Yeriko. 2 Tsono Balaki mwana wa Zipori anaona zonse zimene Aisraeli anachitira Aamori, 3 ndipo Amowabu anaopa anthuwo chifukwa analipo ambiri. Amowabuwo anachita mantha kwambiri mpaka ananjenjemera chifukwa cha Aisraeli. 4 Iwo anati kwa akuluakulu a ku Midiyani, “Gulu ili lidzabudula zonse zimene zatizungulira monga momwe ngʼombe yothena imathera udzu wa ku tchire.”Tsono Balaki mwana wa Zipori, yemwe anali mfumu ya Mowabu pa nthawi imeneyo, 5 anatumiza amithenga kwa Balaamu mwana wa Beori, yemwe anali ku Petori, pafupi ndi mtsinje, mʼdziko la kwawo kuti akamuyitane. Balaki anati:“Taonani, anthu ochokera ku Igupto abwera, adzaza dziko lonse ndipo akufuna kuchita nane nkhondo. 6 Tsopano bwera, utemberere anthu amenewa chifukwa ndi amphamvu kwambiri kuposa ine. Mwina ndingadzawagonjetse ndi kuwatulutsira kunja kwa dzikoli chifukwa ndikudziwa kuti amene umawadalitsa amadalitsika, ndipo amene umawatemberera amatembereredwa.” 7 Akuluakulu a Mowabu ndi akuluakulu a Midiyani ananyamuka atatenga ndalama zokalipirira mawula. Atafika kwa Balaamu, anamuwuza zomwe Balaki ananena. 8 Balaamu anawawuza kuti, “Mugone konkuno usiku uno, ndipo ndikuyankhani zomwe Yehova andiwuze.” Choncho akuluakulu a Amowabu anagona kwa Balaamu. 9 Mulungu anabwera kwa Balaamu namufunsa kuti, “Kodi anthu ali ndi iwewa ndani?” 10 Balaamu anayankha Mulungu kuti, “Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu, ananditumizira uthenga uwu: 11 ‘Taonani, anthu amene achokera ku dziko la Igupto adzaza dziko lonse. Tsopano bwera udzawatemberere mʼmalo mwanga. Mwina ndidzatha kumenyana nawo ndi kuwatulutsa.’ ” 12 Koma Mulungu anawuza Balaamu kuti, “Usapite nawo. Usawatemberere anthu amenewo chifukwa ndi odalitsika.” 13 Mmawa mwake Balaamu anadzuka ndi kuwuza akuluakulu a Balaki aja kuti, “Bwererani ku dziko la kwanu chifukwa Yehova sanandilole kuti ndipite nanu.” 14 Kotero akuluakulu a Mowabu anabwerera kwa Balaki ndi kukanena kuti, “Balaamu wakana kubwera nafe.” 15 Kenaka Balaki anatumanso akuluakulu ena ambiri ndi olemekezeka kwambiri kuposa oyamba aja ndipo 16 anafika kwa Balaamu nati;“Zomwe Balaki mwana wa Zipori akunena ndi izi: ‘Usalole kuti china chilichonse chikulepheretse kubwera kwa ine, 17 chifukwa ndidzakulipira bwino kwambiri ndipo ndidzakuchitira chilichonse chimene unganene. Bwera ndipo uwatemberere anthu amenewa mʼmalo mwanga.’ ” 18 Koma Balaamu anayankha atumiki a Balaki kuti, “Ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingachite chilichonse chachikulu kapena chachingʼono kuposa kuchita lamulo la Yehova Mulungu wanga. 19 Tsopano mukhale kuno usiku uno monga ena anachitira, ndidzaona chimene Yehova adzandiwuza.” 20 Usiku umenewo Mulungu anabwera kwa Balaamu ndipo anati, “Popeza anthu awa abwera kudzakuyitana, nyamuka, pita nawo koma ukachite zokhazo zimene ndikuwuze.” 21 Balaamu anadzuka mmawa, namanga bulu wake wamkazi ndipo anapita ndi akuluakulu a Mowabu. 22 Koma Mulungu anakwiya kwambiri pamene ankapita ndipo mngelo wa Yehova anayima pa njira kutsutsana naye. Balaamu anakwera bulu wake wamkazi ndipo antchito ake awiri anali naye. 23 Pamene buluyo anaona mngelo wa Yehova atayima pa njira ndi lupanga mʼmanja mwake, anapatukira kumbali kwa msewu napita kutchire. Balaamu anamumenya kuti abwerere mu msewu. 24 Kenaka mngelo wa Yehova anayima mʼkanjira kakangʼono pakati pa minda iwiri ya mpesa yokhala ndi makoma mbali zonse 25 Bulu uja ataona mngelo wa Yehova anadzipanikiza ku khoma, kukhukhuza phazi la Balaamu kukhomako. Ndipo pomwepo Balaamu anamenya buluyo kachiwiri. 26 Kenaka mngelo wa Yehova anapita patsogolo ndi kuyima pamalo opanikizika pomwe panalibe poti nʼkutembenukira ku dzanja lamanja kapena lamanzere. 27 Buluyo ataonanso mngelo wa Yehova uja, anagona pansi Balaamu ali pa msana, ndipo iye anakwiya ndi kumumenya ndi ndodo yake. 28 Pamenepo Yehova anayankhulitsa bulu uja, ndipo buluyo anati kwa Balaamu, “Ndakuchitirani chiyani kuti mundimenye katatuka?” 29 Balaamu anati kwa buluyo, “Wandipusitsa, ndikanakhala ndi lupanga mʼmanja mwanga, ndikanakupha pomwe pano.” 30 Buluyo anati kwa Balaamu, “Kodi sindine bulu wanu, amene mumakwera nthawi zonse kufikira lero? Kodi ndinakuchitiranipo zoterezi?”Iye anati “Ayi.” 31 Pomwepo Yehova anatsekula maso Balaamu ndipo anaona mngelo wa Yehovayo ali chiyimire pa njira ndi lupanga losolola. Tsono iye anawerama nalambira pamaso pake. 32 Mngelo wa Yehova anamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani wamenya bulu wako katatu? Taona, Ine ndabwera kudzakutsutsa chifukwa ulendo wakowu ndi woyipa pamaso panga. 33 Buluyu anandiona ndi kupatuka katatu aka. Akanakhala kuti sanapatuke, ndikanakupha tsopano, koma buluyu nʼkanamusiya ndi moyo.” 34 Balaamu anati kwa mngelo wa Yehova uja, “Ndachimwa. Sindinadziwe kuti munayima pa njira kunditsutsa. Tsopano ngati Inu simunakondwe, ineyo ndibwerera.” 35 Mngelo wa Yehova anati kwa Balaamu, “Pita ndi anthuwa koma ukayankhule zokhazo zimene ndikakuwuze.” Choncho Balaamu anapita ndi akuluakulu a Balaki. 36 Balaki atamva kuti Balaamu akubwera, anapita kukakumana naye ku mzinda wa Mowabu umene unali mʼmalire a Arinoni, mʼmphepete mwa dziko lake. 37 Balaki anati kwa Balaamu, “Kodi sindinakutumizire uthenga woti ubwere msanga? Chifukwa chiyani sunabwere kwa ine? Kodi sindingathe kukulipira mokwanira?” 38 Balaamu anayankha Balaki kuti, “Taonani, ndabwera kwa inu lero, kodi ine ndili ndi mphamvu zoti nʼkuyankhula chilichonse? Inetu ndiyenera kuyankhula zokhazo zimene Mulungu wandiwuza.” 39 Pamenepo Balaamu anapita pamodzi ndi Balaki ku Kiriati-Huzoti. 40 Balaki anapereka nsembe ngʼombe ndi nkhosa, ndipo anapereka zina kwa Balaamu ndi kwa akuluakulu omwe anali naye. 41 Mmawa mwake Balaki anatenga Balaamu napita limodzi ku Bamoti Baala, ndipo kumeneko anakaonako gulu lina la Aisraeliwo.

In Other Versions

Numbers 22 in the ANGEFD

Numbers 22 in the ANTPNG2D

Numbers 22 in the AS21

Numbers 22 in the BAGH

Numbers 22 in the BBPNG

Numbers 22 in the BBT1E

Numbers 22 in the BDS

Numbers 22 in the BEV

Numbers 22 in the BHAD

Numbers 22 in the BIB

Numbers 22 in the BLPT

Numbers 22 in the BNT

Numbers 22 in the BNTABOOT

Numbers 22 in the BNTLV

Numbers 22 in the BOATCB

Numbers 22 in the BOATCB2

Numbers 22 in the BOBCV

Numbers 22 in the BOCNT

Numbers 22 in the BOECS

Numbers 22 in the BOHCB

Numbers 22 in the BOHCV

Numbers 22 in the BOHLNT

Numbers 22 in the BOHNTLTAL

Numbers 22 in the BOICB

Numbers 22 in the BOILNTAP

Numbers 22 in the BOITCV

Numbers 22 in the BOKCV

Numbers 22 in the BOKCV2

Numbers 22 in the BOKHWOG

Numbers 22 in the BOKSSV

Numbers 22 in the BOLCB

Numbers 22 in the BOLCB2

Numbers 22 in the BOMCV

Numbers 22 in the BONAV

Numbers 22 in the BONCB

Numbers 22 in the BONLT

Numbers 22 in the BONUT2

Numbers 22 in the BOPLNT

Numbers 22 in the BOSCB

Numbers 22 in the BOSNC

Numbers 22 in the BOTLNT

Numbers 22 in the BOVCB

Numbers 22 in the BOYCB

Numbers 22 in the BPBB

Numbers 22 in the BPH

Numbers 22 in the BSB

Numbers 22 in the CCB

Numbers 22 in the CUV

Numbers 22 in the CUVS

Numbers 22 in the DBT

Numbers 22 in the DGDNT

Numbers 22 in the DHNT

Numbers 22 in the DNT

Numbers 22 in the ELBE

Numbers 22 in the EMTV

Numbers 22 in the ESV

Numbers 22 in the FBV

Numbers 22 in the FEB

Numbers 22 in the GGMNT

Numbers 22 in the GNT

Numbers 22 in the HARY

Numbers 22 in the HNT

Numbers 22 in the IRVA

Numbers 22 in the IRVB

Numbers 22 in the IRVG

Numbers 22 in the IRVH

Numbers 22 in the IRVK

Numbers 22 in the IRVM

Numbers 22 in the IRVM2

Numbers 22 in the IRVO

Numbers 22 in the IRVP

Numbers 22 in the IRVT

Numbers 22 in the IRVT2

Numbers 22 in the IRVU

Numbers 22 in the ISVN

Numbers 22 in the JSNT

Numbers 22 in the KAPI

Numbers 22 in the KBT1ETNIK

Numbers 22 in the KBV

Numbers 22 in the KJV

Numbers 22 in the KNFD

Numbers 22 in the LBA

Numbers 22 in the LBLA

Numbers 22 in the LNT

Numbers 22 in the LSV

Numbers 22 in the MAAL

Numbers 22 in the MBV

Numbers 22 in the MBV2

Numbers 22 in the MHNT

Numbers 22 in the MKNFD

Numbers 22 in the MNG

Numbers 22 in the MNT

Numbers 22 in the MNT2

Numbers 22 in the MRS1T

Numbers 22 in the NAA

Numbers 22 in the NASB

Numbers 22 in the NBLA

Numbers 22 in the NBS

Numbers 22 in the NBVTP

Numbers 22 in the NET2

Numbers 22 in the NIV11

Numbers 22 in the NNT

Numbers 22 in the NNT2

Numbers 22 in the NNT3

Numbers 22 in the PDDPT

Numbers 22 in the PFNT

Numbers 22 in the RMNT

Numbers 22 in the SBIAS

Numbers 22 in the SBIBS

Numbers 22 in the SBIBS2

Numbers 22 in the SBICS

Numbers 22 in the SBIDS

Numbers 22 in the SBIGS

Numbers 22 in the SBIHS

Numbers 22 in the SBIIS

Numbers 22 in the SBIIS2

Numbers 22 in the SBIIS3

Numbers 22 in the SBIKS

Numbers 22 in the SBIKS2

Numbers 22 in the SBIMS

Numbers 22 in the SBIOS

Numbers 22 in the SBIPS

Numbers 22 in the SBISS

Numbers 22 in the SBITS

Numbers 22 in the SBITS2

Numbers 22 in the SBITS3

Numbers 22 in the SBITS4

Numbers 22 in the SBIUS

Numbers 22 in the SBIVS

Numbers 22 in the SBT

Numbers 22 in the SBT1E

Numbers 22 in the SCHL

Numbers 22 in the SNT

Numbers 22 in the SUSU

Numbers 22 in the SUSU2

Numbers 22 in the SYNO

Numbers 22 in the TBIAOTANT

Numbers 22 in the TBT1E

Numbers 22 in the TBT1E2

Numbers 22 in the TFTIP

Numbers 22 in the TFTU

Numbers 22 in the TGNTATF3T

Numbers 22 in the THAI

Numbers 22 in the TNFD

Numbers 22 in the TNT

Numbers 22 in the TNTIK

Numbers 22 in the TNTIL

Numbers 22 in the TNTIN

Numbers 22 in the TNTIP

Numbers 22 in the TNTIZ

Numbers 22 in the TOMA

Numbers 22 in the TTENT

Numbers 22 in the UBG

Numbers 22 in the UGV

Numbers 22 in the UGV2

Numbers 22 in the UGV3

Numbers 22 in the VBL

Numbers 22 in the VDCC

Numbers 22 in the YALU

Numbers 22 in the YAPE

Numbers 22 in the YBVTP

Numbers 22 in the ZBP