Numbers 26 (BOGWICC)
1 Utatha mliri Yehova anati kwa Mose ndi Eliezara mwana wa Aaroni, 2 “Werengani Aisraeli onse mwa mabanja awo, onse a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali mʼgulu lankhondo la Israeli.” 3 Kotero mu zigwa za Mowabu pafupi ndi mtsinje wa Yorodani ku Yeriko, Mose ndi wansembe Eliezara anayankhula nawo kuti, 4 “Werengani amuna a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo, monga momwe Yehova walamulira Mose.” Aisraeli omwe anachokera ku Igupto ndi awa: 5 Zidzukulu za Rubeni, mwana woyamba wamwamuna wa Israeli, zinali izi:kuchokera mwa Hanoki, fuko la Ahanoki;kuchokera mwa Palu, fuko la Apalu; 6 kuchokera mwa Hezironi, fuko la Ahezironi;kuchokera mwa Karimi, fuko la Akarimi. 7 Awa anali mafuko a Rubeni: onse amene anawerengedwa analipo 43,730. 8 Mwana wa Palu anali Eliabu, 9 ndipo ana a Eliabu anali Nemueli, Datani ndi Abiramu. Datani ndi Abiramu anali gulu la akuluakulu aja amene anawukira Mose ndi Aaroni ndipo analinso mʼgulu la otsatira Kora pamene anawukira Yehova. 10 Nthaka inangʼambika ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, kotero kuti gulu lawo linafa pamene moto unapsereza anthu 250 aja, nasanduka chenjezo. 11 Koma ana a Kora sanafe nawo. 12 Zidzukulu za Simeoni mwa mafuko awo zinali izi:kuchokera mwa Nemueli, fuko la Anemuele;kuchokera mwa Yamini, fuko la Ayamini;kuchokera mwa Yakini fuko la Ayakini; 13 kuchokera mwa Zera, mbumba ya Zera;kuchokera mwa Sauli, fuko la Asauli. 14 Awa anali mafuko a Simeoni. Iwowa analipo amuna 22,200. 15 Zidzukulu za Gadi mwa mafuko awo ndi izi:kuchokera mwa Zefoni, fuko la Azefoni;kuchokera mwa Hagi, fuko la Ahagi;kuchokera mwa Suni, fuko la Asuni; 16 kuchokera mwa Ozini, fuko la Aozini;kuchokera mwa Eri, fuko la Aeri; 17 kuchokera mwa Arodi, fuko la Aarodi;kuchokera mwa Arieli, fuko la a Areli. 18 Awa ndiwo anali mafuko a Gadi. Onse amene anawerengedwa analipo 40,500. 19 Eri ndi Onani anali ana aamuna a Yuda, koma anafera mu Kanaani. 20 Zidzukulu za Yuda monga mwa mafuko awo zinali izi:kuchokera mwa Sela, fuko la Asera;kuchokera mwa Perezi, fuko la Aperezi;kuchokera mwa Zera, mbumba ya Zera. 21 Zidzukulu za Perezi zinali izi:kuchokera mwa Hezironi, fuko la Ahezironi;kuchokera mwa Hamuli, fuko la Ahamuli. 22 Awa ndiwo anali mafuko a Yuda. Amene anawerenga analipo 76,500. 23 Zidzukulu za Isakara monga mwa mafuko awo zinali izi:kuchokera mwa Tola, fuko la Atola;kuchokera mwa Puwa, fuko la Apuwa; 24 kuchokera mwa Yasubu, fuko la Ayasubu.Kuchokera mwa Simironi, fuko la Asimironi. 25 Awa ndi amene anali a fuko la Isakara. Amene anawerengedwa analipo 64,300. 26 Zidzukulu za Zebuloni mwa mafuko awo zinali izi:kuchokera mwa Seredi, fuko la Aseredi;kuchokera mwa Eloni, fuko la Aeloni;kuchokera mwa Yahaleeli, fuko la Ayahaleeli. 27 Awa ndiwo anali mafuko a Zebuloni. Amene anawerengedwa analipo 60,500. 28 Zidzukulu za Yosefe mwa mafuko awo kupyolera mwa Manase ndi Efereimu zinali izi: 29 Zidzukulu za Manase:kuchokera mwa Makiri, fuko la Amakiri (Makiri anali abambo ake a Giliyadi);kuchokera mwa Giliyadi, fuko la Agiliyadi. 30 Izi ndizo zinali zidzukulu za Giliyadi;kuchokera mwa Iyezeri, fuko la Aiyezeri;kuchokera mwa Heleki, fuko la Aheleki; 31 kuchokera mwa Asirieli, fuko la Aasirieli;kuchokera mwa Sekemu, fuko la Asekemu; 32 kuchokera mwa Semida, fuko la Asemida;kuchokera mwa Heferi, fuko la Aheferi. 33 (Zelofehadi mwana wa Heferi analibe ana aamuna koma ana aakazi okha, amene mayina awo anali: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.) 34 Awa ndiwo anali mafuko a Manase. Amene anawerengedwa analipo 52,700. 35 Zidzukulu za Efereimu monga mwa mafuko awo zinali izi;kuchokera mwa Sutela, fuko la Asutela;kuchokera mwa Bekeri, fuko la Abekeri;kuchokera mwa Tahani, fuko la Atahani. 36 Zidzukulu za Sutela zinali izi:kuchokera mwa Erani, fuko la Aerani. 37 Awa ndiwo anali mafuko a Efereimu. Amene anawerengedwa analipo 32,500.Zimenezi zinali zidzukulu za Yosefe monga mwa mafuko awo. 38 Zidzukulu za Benjamini monga mwa mabanja awo zinali izi:kuchokera mwa Bela, fuko la Abela;kuchokera mwa Asibeli, fuko la Aasibeli;kuchokera mwa Ahiramu, fuko la Ahiramu; 39 kuchokera mwa Sufamu, fuko la Asufamu;kuchokera mwa Hufamu, fuko la Ahufamu; 40 Zidzukulu za Bela kupyolera mwa Aridi ndi Naamani zinali izi:kuchokera mwa Aridi, fuko la Aaridi;kuchokera mwa Naamani, fuko la Anaamani; 41 Awa ndiwo anali mabanja a Benjamini. Amene nawerengedwa analipo 45,600. 42 Zidzukulu za Dani mwa mabanja awo zinali izi:kuchokera mwa Suhamu fuko la Asuhamu.Izi zinali zidzukulu za Dani. 43 Onse a fuko la Asuhamu amene anawerengedwa analipo 64,400. 44 Zidzukulu za Aseri monga mwa mafuko awo zinali izi:kuchokera mwa Imina, fuko la Aimuna;kuchokera mwa Isivi, fuko la Ayisivi;kuchokera mwa Beriya, fuko la Aberiya; 45 ndipo kupyolera mwa zidzukulu za Beriya:kuchokera mwa Heberi, fuko la Aheberi;kuchokera mwa Malikieli, fuko la Amalikieli; 46 (Aseri anali ndi mwana wamkazi dzina lake Sera) 47 Awa ndiwo anali mafuko a Aseri. Onse amene anawerengedwa analipo 53,400. 48 Zidzukulu za Nafutali mwa mafuko awo zinali izi:kuchokera mwa Yahazeeli, fuko la Ayahazeeli;kuchokera mwa Guni, fuko la Aguni; 49 kuchokera mwa Yezeri, fuko la Ayezeri;kuchokera mwa Silemu, fuko la Asilemu. 50 Awa ndiwo anali mafuko a Nafutali. Onse amene anawerengedwa analipo 45,400. 51 Chiwerengero chonse cha amuna mu Israeli chinalipo 601,730. 52 Yehova anawuza Mose kuti, 53 “Uwagawire dziko anthu awa kuti likhale cholowa chawo molingana ndi chiwerengero cha mayina awo. 54 Gulu lalikulu ulipatse cholowa chachikulu, ndipo lochepa cholowa chocheperapo. Gulu lililonse lilandire cholowa chake molingana ndi chiwerengero cha amene anawerengedwa. 55 Dzikolo uligawe pochita maere. Alandire cholowa chawocho potsata mayina a mafuko a makolo awo. 56 Cholowa chawo uchigawe pakati pa fuko lalikulu ndi lalingʼono mwa maere.” 57 Alevi omwe anawerengedwa monga mwa mafuko awo ndi awa:kuchokera mwa Geresoni, fuko la Ageresoni;kuchokera mwa Kohati, fuko la Akohati;kuchokera mwa Merari, fuko la Amerari. 58 Awanso anali mabanja a Alevi:banja la Alibini,banja la Ahebroni,banja la Amali,banja la Amusi, fuko la Korabanja la Akohati,(Kohati anali abambo a Amramu. 59 Dzina la mkazi wa Amramu linali Yokobedi, mdzukulu wa Levi, yemwe anabadwa mwa Alevi mu Igupto. Yokobedi anaberekera Amramu Aaroni, Mose ndi Miriamu mlongo wawo. 60 Aaroni anali abambo a Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara. 61 Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamene anapereka nsembe pamaso pa Yehova ndi moto wachilendo). 62 Alevi onse aamuna a mwezi umodzi kapena kuposera pamenepa analipo 23,000. Iwowo sanawerengedwe pamodzi ndi Aisraeli ena chifukwa sanalandire cholowa pakati pawo. 63 Awa ndi amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eliezara wansembe pamene ankawerenga Aisraeli pa zigwa za ku Mowabu mʼmbali mwa Yorodani ku Yeriko. 64 Mwa anthu amenewa panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali mʼgulu la Aisraeli omwe Mose ndi wansembe Aaroni anawawerenga mʼchipululu cha Sinai; 65 Chifukwa Yehova anali atawuza Aisraeliwo kuti adzafera ndithu mʼchipululu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.