Numbers 35 (BOGWICC)

1 Ku zigwa za Mowabu pafupi ndi Yorodani ku Yeriko, Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Lamula Aisraeli kuti apereke kwa Alevi midzi yoti azikhalamo kuchokera pa cholowa chomwe adzalandira. Muwapatsenso malo oweteramo ziweto kuzungulira midziyo. 3 Midziyo idzakhala yawo ndipo azidzakhala mʼmenemo. Malo a msipu adzakhala a ngʼombe, nkhosa ndi zoweta zawo zina zonse. 4 “Malo a msipu a mudziwo amene mudzawapatse Aleviwo, adzayambire ku khoma la mudzi ndipo adzatuluke kunja mamita 450, kuzungulira mudziwo. 5 Kunja kwa mudzi yezani mamita 900 kummawa, mamita 900 kumpoto ndipo mudziwo ukhale pakati. Adzakhala ndi dera limeneli ngati malo a midziyo, owetera ziweto zawo. 6 “Isanu ndi umodzi mwa midzi imene mudzapereke kwa Alevi idzakhala mizinda yopulumukirako, kumene munthu wopha mnzake adzathawireko. Ndipo mudzawapatsenso midzi ina 42. 7 Midzi yonse imene mudzapereke kwa Alevi idzakhale 48, pamodzi ndi malo oweterako ziweto. 8 Pamene mukupatula midzi imeneyi pa cholowa cha Aisraeli, muchotsepo midzi yambiri pa mafuko aakulu, ndipo midzi pangʼono pa mafuko aangʼono. Fuko lililonse lidzapereka kwa Alevi molingana ndi kukula kwa cholowa chimene lalandira.” 9 Ndipo Yehova anawuza Mose kuti, 10 “Yankhula ndi Aisraeli kuti, ‘Pamene muwoloka Yorodani kulowa mu Kanaani, 11 sankhani midzi ina kuti ikhale mizinda yanu yopulumukirako, kumene munthu wopha munthu wina mwangozi angathawireko. 12 Adzakhala malo obisalako pothawa munthu wofuna kulipsira, kuti munthu wopha mnzake mwangozi asaphedwe mpaka akayime pamaso pa gulu la anthu kuti akaweruzidwe. 13 Midzi isanu ndi umodzi imene muyiperekeyi idzakhala mizinda yopulumukirako. 14 Mupereke itatu mbali ino ya Yorodani ndi itatu ina mu Kanaani kuti ikhale mizinda yopulumukirako. 15 Midzi isanu ndi umodzi idzakhala malo opulumukirako Aisraeli, alendo ndi anthu ena onse okhala pakati pawo kuti wina aliyense wopha mnzake mwangozi adzathawireko. 16 “ ‘Ngati munthu amenya mnzake ndi chitsulo, munthuyo nʼkufa, ndiye kuti iyeyo ndi wakupha ndipo wakuphayo aphedwe. 17 Kapenanso ngati wina wake ali ndi mwala mʼdzanja mwake womwe ungaphe munthu, ndipo agenda nawo wina, munthu winayo nʼkufa, ndiye kuti iyeyo ndi wakupha ndipo wakuphayo adzayenera kuphedwa. 18 Kapenanso ngati wina ali ndi chibonga mʼdzanja mwake choti nʼkupha nacho munthu, namenya nacho munthu, munthuyo nʼkufa, ndiye kuti iyeyo ndi wakupha, wakuphayo ayenera kuphedwa. 19 Wolipsira adzamuphanso wakuphayo. Pamene akumana naye adzayenera kumupha ndithu. 20 Ndipo ngati wina wake, chifukwa cha udani, aganiza zokankha munthu wina kapena kumuponyera chinthu china mwadala munthuyo nʼkufa, 21 kapena ngati, chifukwa cha udani, amenya mnzake ndi nkhonya, mnzakeyo ndi kufa, munthuyo ayenera kuphedwa. Iyeyo ndi wakupha. Wolipsira adzamuphe wakuphayo pamene akumana naye. 22 “ ‘Koma ngati popanda udani wina uliwonse, mwadzidzidzi akankha wina kapena kumuponyera chinthu osati mwadala, 23 kapena mosamuona nʼkumuponyera mwala womwe utha kumupha, munthuyo nʼkufa, tsono pakuti sanali mdani wake ndipo sanaganizire zomupweteka, 24 gulu liweruze pakati pa iye ndi wolipsira monga mwa malamulo ake. 25 Gulu lidzapulumutsa munthu wakuphayo mʼmanja mwa wolipsira uja ndi kumubwezera ku mzinda wopulumukirako kumene anathawira. Ayenera kukhala kumeneko kufikira imfa ya mkulu wa ansembe, amene anadzozedwa ndi mafuta oyera. 26 “ ‘Koma ngati wolakwayo atuluka kunja kwa malire a mzinda wopulumukirako kumene anathawira 27 ndipo wobwezera choyipa nʼkumupeza kunja kwa mzindawo, wolipsirayo atha kumupha wolakwayo popanda kugamula mlandu wakupha. 28 Wolakwayo ayenera kukhala mu mzinda wopulumukiramowo mpaka imfa ya mkulu wa ansembe ndipo pamenepo atha kubwerera kwawo. Pokhapokha atafa mkulu wa ansembe ndi pamene angathe kubwerera ku malo ake. 29 “ ‘Amenewa akhale malamulo ndi malangizo kwa inu nthawi zonse ndi ku mibado ya mʼtsogolo, kulikonse kumene mudzakhalako. 30 “ ‘Aliyense wopha munthu ayeneranso kuphedwa ngati pali umboni okwanira. Koma wina asaphedwe ngati pali mboni imodzi yokha. 31 “ ‘Osalola kulandira dipo lowombolera munthu wakupha yemwe ayenera kuphedwa. Wakupha ayenera kuphedwa. 32 “ ‘Simuyeneranso kulandira dipo kwa munthu amene wathawira ku mzinda wopulumikirako kuti wothawayo abwerere kwawo, pokhapokha ngati mkulu wa ansembe wamwalira. 33 “ ‘Musayipitse dziko limene mukukhalamolo. Magazi amayipitsa dziko ndipo nʼkosatheka kulipirira dziko chifukwa cha magazi amene akhetsedwa mʼmenemo, kupatula pokhetsa magazi a munthu amene anakhetsa magaziyo. 34 Choncho musadetse dziko limene mukukhalamo, dziko limene Inenso ndimakhalamo, pakuti Ine Yehova, ndimakhala pakati pa Aisraeli.’ ”

In Other Versions

Numbers 35 in the ANGEFD

Numbers 35 in the ANTPNG2D

Numbers 35 in the AS21

Numbers 35 in the BAGH

Numbers 35 in the BBPNG

Numbers 35 in the BBT1E

Numbers 35 in the BDS

Numbers 35 in the BEV

Numbers 35 in the BHAD

Numbers 35 in the BIB

Numbers 35 in the BLPT

Numbers 35 in the BNT

Numbers 35 in the BNTABOOT

Numbers 35 in the BNTLV

Numbers 35 in the BOATCB

Numbers 35 in the BOATCB2

Numbers 35 in the BOBCV

Numbers 35 in the BOCNT

Numbers 35 in the BOECS

Numbers 35 in the BOHCB

Numbers 35 in the BOHCV

Numbers 35 in the BOHLNT

Numbers 35 in the BOHNTLTAL

Numbers 35 in the BOICB

Numbers 35 in the BOILNTAP

Numbers 35 in the BOITCV

Numbers 35 in the BOKCV

Numbers 35 in the BOKCV2

Numbers 35 in the BOKHWOG

Numbers 35 in the BOKSSV

Numbers 35 in the BOLCB

Numbers 35 in the BOLCB2

Numbers 35 in the BOMCV

Numbers 35 in the BONAV

Numbers 35 in the BONCB

Numbers 35 in the BONLT

Numbers 35 in the BONUT2

Numbers 35 in the BOPLNT

Numbers 35 in the BOSCB

Numbers 35 in the BOSNC

Numbers 35 in the BOTLNT

Numbers 35 in the BOVCB

Numbers 35 in the BOYCB

Numbers 35 in the BPBB

Numbers 35 in the BPH

Numbers 35 in the BSB

Numbers 35 in the CCB

Numbers 35 in the CUV

Numbers 35 in the CUVS

Numbers 35 in the DBT

Numbers 35 in the DGDNT

Numbers 35 in the DHNT

Numbers 35 in the DNT

Numbers 35 in the ELBE

Numbers 35 in the EMTV

Numbers 35 in the ESV

Numbers 35 in the FBV

Numbers 35 in the FEB

Numbers 35 in the GGMNT

Numbers 35 in the GNT

Numbers 35 in the HARY

Numbers 35 in the HNT

Numbers 35 in the IRVA

Numbers 35 in the IRVB

Numbers 35 in the IRVG

Numbers 35 in the IRVH

Numbers 35 in the IRVK

Numbers 35 in the IRVM

Numbers 35 in the IRVM2

Numbers 35 in the IRVO

Numbers 35 in the IRVP

Numbers 35 in the IRVT

Numbers 35 in the IRVT2

Numbers 35 in the IRVU

Numbers 35 in the ISVN

Numbers 35 in the JSNT

Numbers 35 in the KAPI

Numbers 35 in the KBT1ETNIK

Numbers 35 in the KBV

Numbers 35 in the KJV

Numbers 35 in the KNFD

Numbers 35 in the LBA

Numbers 35 in the LBLA

Numbers 35 in the LNT

Numbers 35 in the LSV

Numbers 35 in the MAAL

Numbers 35 in the MBV

Numbers 35 in the MBV2

Numbers 35 in the MHNT

Numbers 35 in the MKNFD

Numbers 35 in the MNG

Numbers 35 in the MNT

Numbers 35 in the MNT2

Numbers 35 in the MRS1T

Numbers 35 in the NAA

Numbers 35 in the NASB

Numbers 35 in the NBLA

Numbers 35 in the NBS

Numbers 35 in the NBVTP

Numbers 35 in the NET2

Numbers 35 in the NIV11

Numbers 35 in the NNT

Numbers 35 in the NNT2

Numbers 35 in the NNT3

Numbers 35 in the PDDPT

Numbers 35 in the PFNT

Numbers 35 in the RMNT

Numbers 35 in the SBIAS

Numbers 35 in the SBIBS

Numbers 35 in the SBIBS2

Numbers 35 in the SBICS

Numbers 35 in the SBIDS

Numbers 35 in the SBIGS

Numbers 35 in the SBIHS

Numbers 35 in the SBIIS

Numbers 35 in the SBIIS2

Numbers 35 in the SBIIS3

Numbers 35 in the SBIKS

Numbers 35 in the SBIKS2

Numbers 35 in the SBIMS

Numbers 35 in the SBIOS

Numbers 35 in the SBIPS

Numbers 35 in the SBISS

Numbers 35 in the SBITS

Numbers 35 in the SBITS2

Numbers 35 in the SBITS3

Numbers 35 in the SBITS4

Numbers 35 in the SBIUS

Numbers 35 in the SBIVS

Numbers 35 in the SBT

Numbers 35 in the SBT1E

Numbers 35 in the SCHL

Numbers 35 in the SNT

Numbers 35 in the SUSU

Numbers 35 in the SUSU2

Numbers 35 in the SYNO

Numbers 35 in the TBIAOTANT

Numbers 35 in the TBT1E

Numbers 35 in the TBT1E2

Numbers 35 in the TFTIP

Numbers 35 in the TFTU

Numbers 35 in the TGNTATF3T

Numbers 35 in the THAI

Numbers 35 in the TNFD

Numbers 35 in the TNT

Numbers 35 in the TNTIK

Numbers 35 in the TNTIL

Numbers 35 in the TNTIN

Numbers 35 in the TNTIP

Numbers 35 in the TNTIZ

Numbers 35 in the TOMA

Numbers 35 in the TTENT

Numbers 35 in the UBG

Numbers 35 in the UGV

Numbers 35 in the UGV2

Numbers 35 in the UGV3

Numbers 35 in the VBL

Numbers 35 in the VDCC

Numbers 35 in the YALU

Numbers 35 in the YAPE

Numbers 35 in the YBVTP

Numbers 35 in the ZBP