Proverbs 7 (BOGWICC)

1 Mwana wanga, mvera mawu anga;usunge bwino malamulo angawa. 2 Utsate malamulo anga ndipo udzakhala ndi moyo;samala malangizo angawa monga uchitira ndi maso ako. 3 Uchite ngati wawamangirira pa zala zako,ndiponso ngati kuti wawalemba pa mtima pako. 4 Nzeru uyiwuze kuti, “Iwe ndiwe mlongo wanga,”ndipo khalidwe lomvetsa bwino zinthu ulitchule kuti, “Bwenzi langa lapamtima.” 5 Zidzakuteteza kwa mkazi wachigololondiponso zidzakuthandiza kusamvera mawu oshashalika a mkazi wachilendo. 6 Tsiku lina pa zenera la nyumba yangandinasuzumira pa zenera. 7 Ndinaona pakati pa anthu opusa,pakati pa anyamata,mnyamata wina wopanda nzeru. 8 Iye ankayenda njira yodutsa pafupi ndi nyumba ya mkaziyo,kuyenda molunjika nyumba ya mkaziyo. 9 Inali nthawi yachisisira madzulo,nthawi ya usiku, kuli mdima. 10 Ndipo mkaziyo anadzakumana naye,atavala ngati munthu wachiwerewere wa mtima wonyenga. 11 (Mkaziyo ndi wolongolola ndiponso nkhutukumve,iye ndi wosakhazikika pa khomo. 12 Mwina umupeza pa msewu, mwina umupeza pa msika,ndipo amadikirira munthu pa mphambano iliyonse). 13 Tsono amagwira mnyamatayo ndi kupsompsonandi nkhope yake yopanda manyazi amamuwuza kuti, 14 “Ndinayenera kupereka nsembe zachiyanjano.Lero ndakwaniritsa malumbiro anga. 15 Choncho ndinabwera kudzakumana nawe;ndinkakufunafuna ndipo ndakupeza! 16 Pa bedi panga ndayalaponsalu zosalala zokongola zochokera ku Igupto. 17 Pa bedi panga ndawazapo zonunkhiraza mure, mafuta onunkhira a aloe ndi sinamoni. 18 Bwera, tiye tikhale malo amodzi kukondwerera chikondi mpaka mmawa;tiye tisangalatsane mwachikondi! 19 Mwamuna wanga kulibe ku nyumbako;wapita ulendo wautali: 20 Anatenga thumba la ndalamandipo adzabwera ku nyumba mwezi ukakhwima.” 21 Ndi mawu ake onyengerera amamukakamiza mnyamatayo;amukopa ndi mawu ake oshashalika. 22 Nthawi yomweyo chitsiru chimamutsatira mkaziyongati ngʼombe yopita kukaphedwa,monga momwe mbawala ikodwera mu msampha, 23 mpaka muvi utalasa chiwindi chake,chimakhala ngati mbalame yothamangira mʼkhwekhwe,osadziwa kuti moyo wake uwonongeka. 24 Tsono ana inu, ndimvereni;mvetsetsani zimene ndikunena. 25 Musatengeke mtima ndi njira za mkazi ameneyu;musasochere potsata njira zake. 26 Paja iye anagwetsa anthu ambiri;wapha gulu lalikulu la anthu. 27 Nyumba yake ndi njira yopita ku manda,yotsikira ku malo a anthu akufa.

In Other Versions

Proverbs 7 in the ANGEFD

Proverbs 7 in the ANTPNG2D

Proverbs 7 in the AS21

Proverbs 7 in the BAGH

Proverbs 7 in the BBPNG

Proverbs 7 in the BBT1E

Proverbs 7 in the BDS

Proverbs 7 in the BEV

Proverbs 7 in the BHAD

Proverbs 7 in the BIB

Proverbs 7 in the BLPT

Proverbs 7 in the BNT

Proverbs 7 in the BNTABOOT

Proverbs 7 in the BNTLV

Proverbs 7 in the BOATCB

Proverbs 7 in the BOATCB2

Proverbs 7 in the BOBCV

Proverbs 7 in the BOCNT

Proverbs 7 in the BOECS

Proverbs 7 in the BOHCB

Proverbs 7 in the BOHCV

Proverbs 7 in the BOHLNT

Proverbs 7 in the BOHNTLTAL

Proverbs 7 in the BOICB

Proverbs 7 in the BOILNTAP

Proverbs 7 in the BOITCV

Proverbs 7 in the BOKCV

Proverbs 7 in the BOKCV2

Proverbs 7 in the BOKHWOG

Proverbs 7 in the BOKSSV

Proverbs 7 in the BOLCB

Proverbs 7 in the BOLCB2

Proverbs 7 in the BOMCV

Proverbs 7 in the BONAV

Proverbs 7 in the BONCB

Proverbs 7 in the BONLT

Proverbs 7 in the BONUT2

Proverbs 7 in the BOPLNT

Proverbs 7 in the BOSCB

Proverbs 7 in the BOSNC

Proverbs 7 in the BOTLNT

Proverbs 7 in the BOVCB

Proverbs 7 in the BOYCB

Proverbs 7 in the BPBB

Proverbs 7 in the BPH

Proverbs 7 in the BSB

Proverbs 7 in the CCB

Proverbs 7 in the CUV

Proverbs 7 in the CUVS

Proverbs 7 in the DBT

Proverbs 7 in the DGDNT

Proverbs 7 in the DHNT

Proverbs 7 in the DNT

Proverbs 7 in the ELBE

Proverbs 7 in the EMTV

Proverbs 7 in the ESV

Proverbs 7 in the FBV

Proverbs 7 in the FEB

Proverbs 7 in the GGMNT

Proverbs 7 in the GNT

Proverbs 7 in the HARY

Proverbs 7 in the HNT

Proverbs 7 in the IRVA

Proverbs 7 in the IRVB

Proverbs 7 in the IRVG

Proverbs 7 in the IRVH

Proverbs 7 in the IRVK

Proverbs 7 in the IRVM

Proverbs 7 in the IRVM2

Proverbs 7 in the IRVO

Proverbs 7 in the IRVP

Proverbs 7 in the IRVT

Proverbs 7 in the IRVT2

Proverbs 7 in the IRVU

Proverbs 7 in the ISVN

Proverbs 7 in the JSNT

Proverbs 7 in the KAPI

Proverbs 7 in the KBT1ETNIK

Proverbs 7 in the KBV

Proverbs 7 in the KJV

Proverbs 7 in the KNFD

Proverbs 7 in the LBA

Proverbs 7 in the LBLA

Proverbs 7 in the LNT

Proverbs 7 in the LSV

Proverbs 7 in the MAAL

Proverbs 7 in the MBV

Proverbs 7 in the MBV2

Proverbs 7 in the MHNT

Proverbs 7 in the MKNFD

Proverbs 7 in the MNG

Proverbs 7 in the MNT

Proverbs 7 in the MNT2

Proverbs 7 in the MRS1T

Proverbs 7 in the NAA

Proverbs 7 in the NASB

Proverbs 7 in the NBLA

Proverbs 7 in the NBS

Proverbs 7 in the NBVTP

Proverbs 7 in the NET2

Proverbs 7 in the NIV11

Proverbs 7 in the NNT

Proverbs 7 in the NNT2

Proverbs 7 in the NNT3

Proverbs 7 in the PDDPT

Proverbs 7 in the PFNT

Proverbs 7 in the RMNT

Proverbs 7 in the SBIAS

Proverbs 7 in the SBIBS

Proverbs 7 in the SBIBS2

Proverbs 7 in the SBICS

Proverbs 7 in the SBIDS

Proverbs 7 in the SBIGS

Proverbs 7 in the SBIHS

Proverbs 7 in the SBIIS

Proverbs 7 in the SBIIS2

Proverbs 7 in the SBIIS3

Proverbs 7 in the SBIKS

Proverbs 7 in the SBIKS2

Proverbs 7 in the SBIMS

Proverbs 7 in the SBIOS

Proverbs 7 in the SBIPS

Proverbs 7 in the SBISS

Proverbs 7 in the SBITS

Proverbs 7 in the SBITS2

Proverbs 7 in the SBITS3

Proverbs 7 in the SBITS4

Proverbs 7 in the SBIUS

Proverbs 7 in the SBIVS

Proverbs 7 in the SBT

Proverbs 7 in the SBT1E

Proverbs 7 in the SCHL

Proverbs 7 in the SNT

Proverbs 7 in the SUSU

Proverbs 7 in the SUSU2

Proverbs 7 in the SYNO

Proverbs 7 in the TBIAOTANT

Proverbs 7 in the TBT1E

Proverbs 7 in the TBT1E2

Proverbs 7 in the TFTIP

Proverbs 7 in the TFTU

Proverbs 7 in the TGNTATF3T

Proverbs 7 in the THAI

Proverbs 7 in the TNFD

Proverbs 7 in the TNT

Proverbs 7 in the TNTIK

Proverbs 7 in the TNTIL

Proverbs 7 in the TNTIN

Proverbs 7 in the TNTIP

Proverbs 7 in the TNTIZ

Proverbs 7 in the TOMA

Proverbs 7 in the TTENT

Proverbs 7 in the UBG

Proverbs 7 in the UGV

Proverbs 7 in the UGV2

Proverbs 7 in the UGV3

Proverbs 7 in the VBL

Proverbs 7 in the VDCC

Proverbs 7 in the YALU

Proverbs 7 in the YAPE

Proverbs 7 in the YBVTP

Proverbs 7 in the ZBP