Psalms 113 (BOGWICC)
1 Tamandani Yehova. Mutamandeni, inu atumiki a Yehova,tamandani dzina la Yehova. 2 Yehova atamandidwe,kuyambira tsopano mpaka muyaya. 3 Kuyambira ku matulukiro a dzuwa mpaka ku malowero ake,dzina la Yehova liyenera kutamandidwa. 4 Yehova wakwezeka pa anthu a mitundu yonse,ulemerero wake ndi woposa mayiko akumwamba. 5 Ndani wofanana ndi Yehova Mulungu wathu,Iye amene amakhala mwaufumu mmwamba? 6 amene amawerama pansi kuyangʼanamiyamba ndi dziko lapansi? 7 Iye amakweza munthu wosauka kuchoka pa fumbindi kutukula munthu wosowa kuchoka pa dzala; 8 amawakhazika pamodzi ndi mafumu,pamodzi ndi mafumu a anthu ake. 9 Amakhazikitsa mayi wosabereka mʼnyumba yakemonga mayi wa ana wosangalala. Tamandani Yehova.