Psalms 43 (BOGWICC)
1 Onetsani kusalakwa kwanga Inu Mulungu;ndipo mundinenere mlandu wanga kutsutsana ndi mtundu wosapembedza;mundilanditse mʼmanja mwa achinyengo ndi anthu oyipa. 2 Pajatu Inu Mulungu ndinu mphamvu zanga.Nʼchifukwa chiyani mwandikana ine?Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira,woponderezedwa ndi mdani? 3 Tumizani kuwunika kwanu ndi choonadi chanukuti zinditsogolere;mulole kuti zindifikitse ku phiri lanu loyera,kumalo kumene inu mumakhala. 4 Ndipo ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu,kwa Mulungu, chimwemwe changa ndi chikondwerero changa.Ndidzakutamandani ndi zeze,Inu Mulungu wanga. 5 Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni iwe moyo wanga?Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga?Khulupirira Mulungu,pakuti ndidzamutamandabe Iye,Mpulumutsi wanga ndi Mulungu wanga.