Psalms 49 (BOGWICC)

undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora. 1 Imvani izi anthu a mitundu yonse;mvetserani, nonse amene mumakhala pa dziko lonse, 2 anthu wamba pamodzi ndi anthu odziwika,olemera pamodzinso ndi osauka: 3 Pakamwa panga padzayankhula mawu anzeru;mawu ochokera mu mtima mwanga adzapereka nzeru. 4 Ndidzatchera khutu langa ku mwambo,ndi pangwe ndidzafotokoza momveka mwambi wanga. 5 Ine ndichitirenji mantha pamene masiku oyipa afika,pamene achinyengo oyipa andizungulira. 6 Iwo amene adalira kulemera kwawondi kutamandira kuchuluka kwa chuma chawo? 7 Palibe munthu amene angawombole moyo wa mnzakekapena kuperekera mnzake dipo kwa Mulungu. 8 Dipo la moyo ndi la mtengowapatali,palibe malipiro amene angakwanire, 9 kuti iye akhale ndi moyo mpaka muyayandi kusapita ku manda. 10 Pakuti onse amaona kuti anthu anzeru amamwalira;opusa ndi opanda nzeru chimodzimodzinso amawonongekandipo amasiyira chuma chawo anthu ena. 11 Manda awo adzakhala nyumba zawo mpaka muyaya,malo awo okhalako kwa nthawi yonse ya mibado yawo,ngakhale anatchula malo mayina awo. 12 Ngakhale munthu akhale wachuma chotani,adzafa ngati nyama. 13 Izi ndi zimene zimachitikira iwo amene amadzidalira okha,ndi owatsatira awo amene amavomereza zimene amayankhula. Sela 14 Monga nkhosa iwo ayenera kupita ku manda,ndipo imfa idzawadya.Olungama adzawalamulira mmawa;matupi awo adzavunda mʼmanda,kutali ndi nyumba zawo zaufumu. 15 Koma Mulungu adzawombola moyo wanga kuchoka ku manda;ndithu Iye adzanditengera kwa Iye mwini. 16 Usavutike mu mtima pamene munthu akulemera,pamene ulemerero wa nyumba yake ukuchulukirachulukira; 17 Pakuti sadzatenga kanthu pamodzi naye pamene wamwalira,ulemerero wake sudzapita pamodzi naye. 18 Ngakhale pamene munthuyo ali moyo amadziyesa wodala,ndipo ngakhale atamandidwe pamene zinthu zikumuyendera bwino, 19 iyeyo adzakakhala pamodzi ndi mʼbado wa makolo ake,amene sadzaonanso kuwala. 20 Munthu amene ali ndi chuma koma wopanda nzeruadzafa ngati nyama yakuthengo.

In Other Versions

Psalms 49 in the ANGEFD

Psalms 49 in the ANTPNG2D

Psalms 49 in the AS21

Psalms 49 in the BAGH

Psalms 49 in the BBPNG

Psalms 49 in the BBT1E

Psalms 49 in the BDS

Psalms 49 in the BEV

Psalms 49 in the BHAD

Psalms 49 in the BIB

Psalms 49 in the BLPT

Psalms 49 in the BNT

Psalms 49 in the BNTABOOT

Psalms 49 in the BNTLV

Psalms 49 in the BOATCB

Psalms 49 in the BOATCB2

Psalms 49 in the BOBCV

Psalms 49 in the BOCNT

Psalms 49 in the BOECS

Psalms 49 in the BOHCB

Psalms 49 in the BOHCV

Psalms 49 in the BOHLNT

Psalms 49 in the BOHNTLTAL

Psalms 49 in the BOICB

Psalms 49 in the BOILNTAP

Psalms 49 in the BOITCV

Psalms 49 in the BOKCV

Psalms 49 in the BOKCV2

Psalms 49 in the BOKHWOG

Psalms 49 in the BOKSSV

Psalms 49 in the BOLCB

Psalms 49 in the BOLCB2

Psalms 49 in the BOMCV

Psalms 49 in the BONAV

Psalms 49 in the BONCB

Psalms 49 in the BONLT

Psalms 49 in the BONUT2

Psalms 49 in the BOPLNT

Psalms 49 in the BOSCB

Psalms 49 in the BOSNC

Psalms 49 in the BOTLNT

Psalms 49 in the BOVCB

Psalms 49 in the BOYCB

Psalms 49 in the BPBB

Psalms 49 in the BPH

Psalms 49 in the BSB

Psalms 49 in the CCB

Psalms 49 in the CUV

Psalms 49 in the CUVS

Psalms 49 in the DBT

Psalms 49 in the DGDNT

Psalms 49 in the DHNT

Psalms 49 in the DNT

Psalms 49 in the ELBE

Psalms 49 in the EMTV

Psalms 49 in the ESV

Psalms 49 in the FBV

Psalms 49 in the FEB

Psalms 49 in the GGMNT

Psalms 49 in the GNT

Psalms 49 in the HARY

Psalms 49 in the HNT

Psalms 49 in the IRVA

Psalms 49 in the IRVB

Psalms 49 in the IRVG

Psalms 49 in the IRVH

Psalms 49 in the IRVK

Psalms 49 in the IRVM

Psalms 49 in the IRVM2

Psalms 49 in the IRVO

Psalms 49 in the IRVP

Psalms 49 in the IRVT

Psalms 49 in the IRVT2

Psalms 49 in the IRVU

Psalms 49 in the ISVN

Psalms 49 in the JSNT

Psalms 49 in the KAPI

Psalms 49 in the KBT1ETNIK

Psalms 49 in the KBV

Psalms 49 in the KJV

Psalms 49 in the KNFD

Psalms 49 in the LBA

Psalms 49 in the LBLA

Psalms 49 in the LNT

Psalms 49 in the LSV

Psalms 49 in the MAAL

Psalms 49 in the MBV

Psalms 49 in the MBV2

Psalms 49 in the MHNT

Psalms 49 in the MKNFD

Psalms 49 in the MNG

Psalms 49 in the MNT

Psalms 49 in the MNT2

Psalms 49 in the MRS1T

Psalms 49 in the NAA

Psalms 49 in the NASB

Psalms 49 in the NBLA

Psalms 49 in the NBS

Psalms 49 in the NBVTP

Psalms 49 in the NET2

Psalms 49 in the NIV11

Psalms 49 in the NNT

Psalms 49 in the NNT2

Psalms 49 in the NNT3

Psalms 49 in the PDDPT

Psalms 49 in the PFNT

Psalms 49 in the RMNT

Psalms 49 in the SBIAS

Psalms 49 in the SBIBS

Psalms 49 in the SBIBS2

Psalms 49 in the SBICS

Psalms 49 in the SBIDS

Psalms 49 in the SBIGS

Psalms 49 in the SBIHS

Psalms 49 in the SBIIS

Psalms 49 in the SBIIS2

Psalms 49 in the SBIIS3

Psalms 49 in the SBIKS

Psalms 49 in the SBIKS2

Psalms 49 in the SBIMS

Psalms 49 in the SBIOS

Psalms 49 in the SBIPS

Psalms 49 in the SBISS

Psalms 49 in the SBITS

Psalms 49 in the SBITS2

Psalms 49 in the SBITS3

Psalms 49 in the SBITS4

Psalms 49 in the SBIUS

Psalms 49 in the SBIVS

Psalms 49 in the SBT

Psalms 49 in the SBT1E

Psalms 49 in the SCHL

Psalms 49 in the SNT

Psalms 49 in the SUSU

Psalms 49 in the SUSU2

Psalms 49 in the SYNO

Psalms 49 in the TBIAOTANT

Psalms 49 in the TBT1E

Psalms 49 in the TBT1E2

Psalms 49 in the TFTIP

Psalms 49 in the TFTU

Psalms 49 in the TGNTATF3T

Psalms 49 in the THAI

Psalms 49 in the TNFD

Psalms 49 in the TNT

Psalms 49 in the TNTIK

Psalms 49 in the TNTIL

Psalms 49 in the TNTIN

Psalms 49 in the TNTIP

Psalms 49 in the TNTIZ

Psalms 49 in the TOMA

Psalms 49 in the TTENT

Psalms 49 in the UBG

Psalms 49 in the UGV

Psalms 49 in the UGV2

Psalms 49 in the UGV3

Psalms 49 in the VBL

Psalms 49 in the VDCC

Psalms 49 in the YALU

Psalms 49 in the YAPE

Psalms 49 in the YBVTP

Psalms 49 in the ZBP