Psalms 6 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Molingana ndi seminiti. Salimo la Davide. 1 Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu,kapena kundilanga mu ukali wanu. 2 Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka;Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu. 3 Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu.Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti? 4 Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse;pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. 5 Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira;Amakutamandani ndani ali ku manda? 6 Ine ndatopa ndi kubuwula;usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga;ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi. 7 Maso anga atupa chifukwa cha chisoni;akulephera kuona chifukwa cha adani anga. 8 Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa,pakuti Yehova wamva kulira kwanga. 9 Yehova wamva kupempha kwanga kofuna chifundo;Yehova walandira pemphero langa. 10 Adani anga onse adzachita manyazi ndipo adzakhala ndi mantha;adzabwerera msangamsanga mwa manyazi.