Psalms 99 (BOGWICC)
1 Yehova akulamulira,mitundu ya anthu injenjemere;Iye wakhala pa mpando wake waufumu, pakati pa akerubi,dziko lapansi ligwedezeke. 2 Mʼziyoni wamkulu ndi Yehova;Iye ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu. 3 Anthu atamande dzina lanu lalikulu ndi loopsa kwambiri,Iye ndi woyera. 4 Mfumu yamphamvu, iyo imakonda chilungamoInu mwakhazikitsa khalidwe losakondera;mwachita zolungama ndi zoyenera mwa Yakobo. 5 Kwezani Yehova Mulungu wathundipo mulambireni pa mapazi ake;Iye ndi woyera. 6 Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake,Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake;iwo anayitana Yehovandipo Iyeyo anawayankha. 7 Iye anayankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo;iwo anasunga malamulo ake ndi zophunzitsa zomwe anawapatsa. 8 Inu Yehova Mulungu wathu,munawayankha iwo;Inu kwa Israeli munali Mulungu wokhululuka,ngakhale munawalanga pa zochita zawo zoyipa. 9 Kwezani Yehova Mulungu wathundipo mumulambire pa phiri lake loyera,pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera.