Ruth 2 (BOGWICC)

1 Naomi anali ndi mʼbale wake wolemera kwambiri wochokera ku banja la mwamuna wake Elimeleki, dzina lake Bowazi. 2 Tsiku lina Rute, Mmowabu uja anati kwa Naomi, “Mundilole kuti ndikakunkhe barele ku munda wa munthu aliyense amene akandikomere mtima.” Naomi anati kwa iye, “Pita mwana wanga.” 3 Choncho Rute ananyamuka kupita kukakunkha ku minda yokololedwa kale. Tsono zinangochitika kuti Rute anafika mʼmunda wa Bowazi, yemwe anali wochokera ku banja la Elimeleki. 4 Posakhalitsa Bowazi anafika kuchokera ku Betelehemu ndipo analonjera okolola aja kuti, “Yehova akhale nanu!”Iwo anayankha kuti, “Yehova akudalitseni.” 5 Bowazi anafunsa kapitawo wake amene ankayangʼanira okolola aja kuti, “Mayi uyo ndi ndani?” 6 Kapitawo uja anayankha kuti, “Mayiyu ndi Mmowabu amene anabwera ndi Naomi kuchokera ku dziko la Mowabu. 7 Iye anandipempha kuti, ‘Chonde mundilole kuti ndikunkhe barele mʼminda moti akololamo kale.’ Iye wakhala akukunkha kuyambira mmawa mpaka tsopano lino osapuma nʼpangʼono pomwe.” 8 Choncho Bowazi anati kwa Rute, “Tamvera mwana wanga, usapite kukakunkha mʼmunda wina, ndipo usachoke mʼmunda uno. Koma uzitsata adzakazi angawa. 9 Uziyangʼana munda akukolola anyamatawo akamakolola mʼmundamu, ndipo iwe uzitsata pambuyo pawo. Ndawawuza anyamatawo kuti asakuvutitse. Ndipo ukamva ludzu, uzipita ku mitsuko ndi kukamwa madzi amene anyamatawa atunga.” 10 Atamva zimenezi Rute anawerama nazolikitsa nkhope yake pansi. Kenaka anafunsa kuti, “Mwandikomera mtima chotere mlendo ngati ine chifukwa chiyani?” 11 Bowazi anayankha kuti, “Ine ndawuzidwa zonse zimene wakhala ukuchitira apongozi ako chimwalirire mwamuna wako. Ndamvanso kuti unasiya abambo ndi amayi ako komanso dziko la kwanu ndi kubwera kudzakhala ndi anthu amene sumawadziwa ndi kale lonse. 12 Yehova akubwezere pa zimene wachitazi. Yehova Mulungu wa Israeli, amene wabwera pansi pa mapiko ake kuti akuteteze, akupatse mphotho yayikulu.” 13 Rute anati, “Mwandikomera mtima, mbuye wanga. Ndipo mwandisangalatsa ndi kundiyankhula mwa chifundo ngakhale sindili mmodzi mwa adzakazi anu.” 14 Nthawi ya chakudya cha masana Bowazi anati kwa iye, “Bwera kuno, utenge buledi ndi kusunsa nthongo mu vinyo.” Choncho anakhala pansi pafupi ndi okololawo, ndipo Bowazi anamupatsa chakudya ndi nyama yowotcha. Anadya chilichonse amafuna ndipo chakudya china chinatsalako. 15 Atanyamuka kuti azikakunkha, Bowazi analangiza anyamata ake kuti, “Ngakhale mayiyu azikunkha pakati pa mitolo musamuletse ndi kumuchititsa manyazi. 16 Koma muzimusololerako ngala zina za mʼmitolo ndi kumusiyira kuti azikunkha ndipo musamukalipire.” 17 Choncho Rute anakunkha mʼmundamo mpaka madzulo. Kenaka anapuntha barele anakunkhayo, ndipo anakwanira pafupifupi makilogalamu khumi. 18 Anasenza barele uja kupita naye ku mudzi, nakaonetsa apongozi ake. Kenaka anatulutsa chakudya chimene chinatsalira atakhuta chija ndi kupatsa apongozi ake. 19 Apongozi akewo anamufunsa kuti, “Kodi lero unakakunkha kuti? Unakagwira kuti ntchitoyi? Adalitsike munthu amene anakukomera mtimayo.” Ndipo Rute anawuza mpongozi wake za munthu amene ku malo ake anakagwirako ntchito. Iye anati, “Munthuyo dzina lake ndi Bowazi.” 20 Naomi anati kwa mpongozi wakeyo, “Munthu ameneyu amudalitse Yehova, amene sanasiye kuchitira chifundo anthu amoyo ndi akufa omwe. Anatinso munthu ameneyu ndi mnansi wapaphata. Ndiye ali ndi udindo wotisamalira.” 21 Choncho Rute Mmowabuyo anati, “Iye anandiwuzanso kuti, ‘Uzitsata antchito angawa mpaka atamaliza kukolola munda wonse.’ ” 22 Naomi anati kwa Rute mpongozi wake, “Kuli bwino mwana wanga kuti uzipita ndi adzakazi ake kuopa kuti mʼmunda wa munthu wina angakuvute.” 23 Choncho Rute ankatsatira adzakazi a Bowazi namakunkha mpaka anthu atamaliza kudula barele ndi tirigu. Ndipo amakhalabe ndi mpongozi wakeyo.

In Other Versions

Ruth 2 in the ANGEFD

Ruth 2 in the ANTPNG2D

Ruth 2 in the AS21

Ruth 2 in the BAGH

Ruth 2 in the BBPNG

Ruth 2 in the BBT1E

Ruth 2 in the BDS

Ruth 2 in the BEV

Ruth 2 in the BHAD

Ruth 2 in the BIB

Ruth 2 in the BLPT

Ruth 2 in the BNT

Ruth 2 in the BNTABOOT

Ruth 2 in the BNTLV

Ruth 2 in the BOATCB

Ruth 2 in the BOATCB2

Ruth 2 in the BOBCV

Ruth 2 in the BOCNT

Ruth 2 in the BOECS

Ruth 2 in the BOHCB

Ruth 2 in the BOHCV

Ruth 2 in the BOHLNT

Ruth 2 in the BOHNTLTAL

Ruth 2 in the BOICB

Ruth 2 in the BOILNTAP

Ruth 2 in the BOITCV

Ruth 2 in the BOKCV

Ruth 2 in the BOKCV2

Ruth 2 in the BOKHWOG

Ruth 2 in the BOKSSV

Ruth 2 in the BOLCB

Ruth 2 in the BOLCB2

Ruth 2 in the BOMCV

Ruth 2 in the BONAV

Ruth 2 in the BONCB

Ruth 2 in the BONLT

Ruth 2 in the BONUT2

Ruth 2 in the BOPLNT

Ruth 2 in the BOSCB

Ruth 2 in the BOSNC

Ruth 2 in the BOTLNT

Ruth 2 in the BOVCB

Ruth 2 in the BOYCB

Ruth 2 in the BPBB

Ruth 2 in the BPH

Ruth 2 in the BSB

Ruth 2 in the CCB

Ruth 2 in the CUV

Ruth 2 in the CUVS

Ruth 2 in the DBT

Ruth 2 in the DGDNT

Ruth 2 in the DHNT

Ruth 2 in the DNT

Ruth 2 in the ELBE

Ruth 2 in the EMTV

Ruth 2 in the ESV

Ruth 2 in the FBV

Ruth 2 in the FEB

Ruth 2 in the GGMNT

Ruth 2 in the GNT

Ruth 2 in the HARY

Ruth 2 in the HNT

Ruth 2 in the IRVA

Ruth 2 in the IRVB

Ruth 2 in the IRVG

Ruth 2 in the IRVH

Ruth 2 in the IRVK

Ruth 2 in the IRVM

Ruth 2 in the IRVM2

Ruth 2 in the IRVO

Ruth 2 in the IRVP

Ruth 2 in the IRVT

Ruth 2 in the IRVT2

Ruth 2 in the IRVU

Ruth 2 in the ISVN

Ruth 2 in the JSNT

Ruth 2 in the KAPI

Ruth 2 in the KBT1ETNIK

Ruth 2 in the KBV

Ruth 2 in the KJV

Ruth 2 in the KNFD

Ruth 2 in the LBA

Ruth 2 in the LBLA

Ruth 2 in the LNT

Ruth 2 in the LSV

Ruth 2 in the MAAL

Ruth 2 in the MBV

Ruth 2 in the MBV2

Ruth 2 in the MHNT

Ruth 2 in the MKNFD

Ruth 2 in the MNG

Ruth 2 in the MNT

Ruth 2 in the MNT2

Ruth 2 in the MRS1T

Ruth 2 in the NAA

Ruth 2 in the NASB

Ruth 2 in the NBLA

Ruth 2 in the NBS

Ruth 2 in the NBVTP

Ruth 2 in the NET2

Ruth 2 in the NIV11

Ruth 2 in the NNT

Ruth 2 in the NNT2

Ruth 2 in the NNT3

Ruth 2 in the PDDPT

Ruth 2 in the PFNT

Ruth 2 in the RMNT

Ruth 2 in the SBIAS

Ruth 2 in the SBIBS

Ruth 2 in the SBIBS2

Ruth 2 in the SBICS

Ruth 2 in the SBIDS

Ruth 2 in the SBIGS

Ruth 2 in the SBIHS

Ruth 2 in the SBIIS

Ruth 2 in the SBIIS2

Ruth 2 in the SBIIS3

Ruth 2 in the SBIKS

Ruth 2 in the SBIKS2

Ruth 2 in the SBIMS

Ruth 2 in the SBIOS

Ruth 2 in the SBIPS

Ruth 2 in the SBISS

Ruth 2 in the SBITS

Ruth 2 in the SBITS2

Ruth 2 in the SBITS3

Ruth 2 in the SBITS4

Ruth 2 in the SBIUS

Ruth 2 in the SBIVS

Ruth 2 in the SBT

Ruth 2 in the SBT1E

Ruth 2 in the SCHL

Ruth 2 in the SNT

Ruth 2 in the SUSU

Ruth 2 in the SUSU2

Ruth 2 in the SYNO

Ruth 2 in the TBIAOTANT

Ruth 2 in the TBT1E

Ruth 2 in the TBT1E2

Ruth 2 in the TFTIP

Ruth 2 in the TFTU

Ruth 2 in the TGNTATF3T

Ruth 2 in the THAI

Ruth 2 in the TNFD

Ruth 2 in the TNT

Ruth 2 in the TNTIK

Ruth 2 in the TNTIL

Ruth 2 in the TNTIN

Ruth 2 in the TNTIP

Ruth 2 in the TNTIZ

Ruth 2 in the TOMA

Ruth 2 in the TTENT

Ruth 2 in the UBG

Ruth 2 in the UGV

Ruth 2 in the UGV2

Ruth 2 in the UGV3

Ruth 2 in the VBL

Ruth 2 in the VDCC

Ruth 2 in the YALU

Ruth 2 in the YAPE

Ruth 2 in the YBVTP

Ruth 2 in the ZBP