1 Kings 11 (BOGWICC)

1 Komatu Mfumu Solomoni anakonda akazi ambiri achilendo ndipo kuwonjezera pa mwana wamkazi wa Farao, analinso ndi akazi a mitundu iyi: Amowabu, Aamoni, Aedomu, Asidoni, ndi Ahiti. 2 Akazi amenewa anali ochokera ku mitundu ija imene Yehova anawuza Aisraeli kuti, “Simuyenera kudzakwatirana nawo amenewa, chifukwa ndithu, amenewa adzatembenuza mitima yanu kuti mutsatire milungu yawo.” Komabe Solomoni anawakonda kwambiri akazi amenewa. 3 Iye anali ndi akazi 700 ochokera ku mabanja achifumu ndi azikazi 300 ndipo akaziwo anamusocheretsa. 4 Solomoni atakalamba, akazi akewo anakopa mtima wake kuti atsatire milungu ina, ndipo sanatsatire Yehova Mulungu wake ndi mtima wodzipereka, monga unalili mtima wa Davide abambo ake. 5 Pakuti iye ankapembedza Asitoreti, mulungu wamkazi wa Asidoni, ndiponso Moleki mulungu wonyansa wa Aamoni. 6 Kotero Solomoni anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Sanatsatire Yehova kwathunthu monga anachitira Davide abambo ake. 7 Pa phiri la kummawa kwa Yerusalemu, anamanga malo opembedzerapo Kemosi, mulungu wonyansa wa Mowabu, ndiponso malo a Moleki, mulungu wonyansa wa Aamoni. 8 Iye anamangiranso malo oterewa akazi ake onse achilendo, amene amafukiza lubani ndi kumapereka nsembe kwa milungu yawo. 9 Choncho Yehova anakwiyira Solomoni chifukwa mtima wake unatembenuka kuchoka kwa Yehova Mulungu wa Israeli, amene anamuonekera kawiri konse. 10 Ngakhale kuti Yehova anamuletsa Solomoni kutsatira milungu ina, iyeyo sanamvere lamulo la Yehova. 11 Pamenepo Yehova anati kwa Solomoni, “Popeza mtima wako ndi wotere ndipo sunasunge pangano langa ndi malamulo anga amene ndinakuwuza, ndithudi, Ine ndidzawugawa ufumuwu kuwuchotsa kwa iwe ndi kuwupereka kwa mmodzi mwa atumiki ako. 12 Koma chifukwa cha Davide abambo ako, sindidzachita zimenezi iwe uli moyo. Ndidzawugawa mʼdzanja la mwana wako. 13 Komabe sindidzamulanda ufumu wonse, koma ndidzamusiyira fuko limodzi chifukwa cha mtumiki wanga Davide ndiponso chifukwa cha Yerusalemu, mzinda umene ndinawusankha.” 14 Ndipo Yehova anamuutsira Solomoni mdani, Hadadi Mwedomu, wochokera ku banja laufumu ku Edomu. 15 Kale pamene Davide ankachita nkhondo ndi Aedomu, Yowabu mkulu wa ankhondo, amene anapita kukakwirira Aisraeli akufa, anakantha amuna onse ku Edomu. 16 Yowabu ndi Aisraeli onse anakhala kumeneko miyezi isanu ndi umodzi mpaka anawononga amuna onse a ku Edomu. 17 Koma Hadadi akanali mwana anathawira ku Igupto pamodzi ndi akuluakulu ena a ku Edomu amene ankatumikira abambo ake. 18 Iwo ananyamuka ku Midiya ndi kupita ku Parani. Ndipo anatenga amuna ena ku Paraniko, napita nawo ku Igupto, kwa Farao mfumu ya Igupto, amene anamupatsa nyumba, malo ndiponso chakudya. 19 Farao anamukomera mtima Hadadi ndipo anamupatsa mkazi amene anali mngʼono wake wa Mfumukazi Tahipenesi. 20 Mngʼono wake wa Tahipenesi anabereka mwana wamwamuna ndipo anamutcha Genubati, amene analeredwa mʼnyumba yaufumu ndi Tahipenesi. Genubatiyo ankakhala limodzi ndi ana a Farao. 21 Ali ku Iguptoko, Hadadi anamva kuti Davide ndi Yowabu anamwalira. Pamenepo Hadadi anati kwa Farao, “Loleni ndichoke kuti ndibwerere ku dziko la kwathu.” 22 Farao anafunsa kuti, “Kodi ukusowa chiyani kuno kuti ufune kubwerera ku dziko la kwanu?”Hadadi anayankha kuti, “Palibe chimene ndikusowa, koma loleni kuti ndichoke!” 23 Ndipo Mulungu anawutsira Solomoni mdani wina, Rezoni mwana wa Eliada, amene anali atathawa mbuye wake, Hadadezeri mfumu ya ku Zoba. 24 Iye anasonkhanitsa anthu ndipo anali mtsogoleri wa anthu owukira pamene Davide anapha ankhondo a ku Zoba. Anthu owukirawa anapita ku Damasiko, nakakhala kumeneko ndi kuyamba kulamulira. 25 Rezoni anali mdani wa Israeli pa masiku onse a Solomoni, kuwonjezera pa mavuto amene ankabweretsa Hadadi. Kotero Rezoni ankalamulira ku Aramu ndipo ankadana ndi Israeli. 26 Yeroboamu, mwana wa Nebati anawukiranso mfumu. Iye anali mmodzi mwa akuluakulu a Solomoni wa fuko la Efereimu, wa ku Zeredi, ndipo amayi ake anali Zeruya, mkazi wamasiye. 27 Nkhani ya kuwukira kwa Yeroboamu inali yotere: Solomoni anamanga malo a chitetezo a Milo ndipo anakonza khoma logumuka la mzinda wa Davide, abambo ake. 28 Tsono Yeroboamu anali munthu wamphamvu kwambiri ndipo Solomoni ataona kuti mnyamatayo amadziwa kugwira ntchito bwino, anamuyika kukhala woyangʼanira anthu a ntchito onse a nyumba ya Yosefe. 29 Tsiku lina Yeroboamu ali pa ulendo kuchokera ku Yerusalemu, anakumana ndi mneneri Ahiya pa msewu, ndipo Ahiyayo anali atavala mwinjiro watsopano. Awiriwo anali okha kuthengoko, 30 ndipo Ahiya anagwira mwinjiro watsopano umene anavala ndi kuwungʼamba zidutswa 12. 31 Tsono iye anati kwa Yeroboamu, “Tenga zidutswa khumi, pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Taona, Ine ndidzachotsa ufumu mʼdzanja la Solomoni ndipo ndidzakupatsa iwe mafuko khumi. 32 Koma chifukwa cha mtumiki wanga Davide ndiponso mzinda wa Yerusalemu, umene ndinawusankha pakati pa mafuko a Israeli, iye adzakhala ndi fuko limodzi lokha. 33 Ndidzachita zimenezi chifukwa wandisiya Ine ndi kupembedza Asitoreti mulungu wamkazi wa Asidoni, Kemosi mulungu wa Amowabu ndiponso Moleki mulungu wa Aamoni, ndipo sanayende mʼnjira yanga, kapena kusunga mawu anga ndi malamulo anga monga anachitira Davide abambo ake. 34 “ ‘Koma sindidzalanda ufumu wonse mʼdzanja la Solomoni. Ine ndamuyika kukhala wolamulira masiku onse a moyo wake chifukwa cha mtumiki wanga Davide, amene ndinamusankha ndiponso amene anamvera malamulo anga ndi mawu anga. 35 Ndidzalanda ufumu mʼdzanja la mwana wake ndipo ndidzakupatsa iwe mafuko khumi. 36 Ndidzapereka fuko limodzi kwa mwana wake ndi cholinga choti Davide mtumiki wanga adzakhale nyale nthawi zonse pamaso panga mu Yerusalemu, mzinda umene ndinawusankha kuyikamo Dzina langa. 37 Koma kunena za iwe, ndidzakutenga ndipo udzalamulira chilichonse chimene mtima wako ukukhumba; udzakhala mfumu ya Israeli. 38 Ngati udzamvera zonse zimene ndidzakulamula ndi kuyenda mʼnjira yanga ndi kuchita zabwino pamaso panga, posunga malamulo anga ndi mawu anga monga anachitira Davide mtumiki wanga, Ine ndidzakhala nawe. Ndidzakupatsa ufumu umene udzakhala wokhazikika monga ndinamupatsira Davide, ndipo Ine ndidzakupatsa Israeli. 39 Ine ndidzalanga zidzukulu za Davide chifukwa cha zimenezi, koma osati kwamuyaya.’ ” 40 Solomoni anafunitsitsa kupha Yeroboamu, koma Yeroboamu anathawira ku Igupto, kwa Sisaki mfumu ya Igupto ndipo anakhala kumeneko mpaka Solomoni atamwalira. 41 Ntchito zina za Solomoni, zonse zomwe anachita komanso za nzeru zake, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya Solomoni? 42 Solomoni analamulira Aisraeli onse mu Yerusalemu kwa zaka makumi anayi. 43 Ndipo anagona ndi makolo ake nayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide abambo ake. Ndipo Rehobowamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo ake.

In Other Versions

1 Kings 11 in the ANGEFD

1 Kings 11 in the ANTPNG2D

1 Kings 11 in the AS21

1 Kings 11 in the BAGH

1 Kings 11 in the BBPNG

1 Kings 11 in the BBT1E

1 Kings 11 in the BDS

1 Kings 11 in the BEV

1 Kings 11 in the BHAD

1 Kings 11 in the BIB

1 Kings 11 in the BLPT

1 Kings 11 in the BNT

1 Kings 11 in the BNTABOOT

1 Kings 11 in the BNTLV

1 Kings 11 in the BOATCB

1 Kings 11 in the BOATCB2

1 Kings 11 in the BOBCV

1 Kings 11 in the BOCNT

1 Kings 11 in the BOECS

1 Kings 11 in the BOHCB

1 Kings 11 in the BOHCV

1 Kings 11 in the BOHLNT

1 Kings 11 in the BOHNTLTAL

1 Kings 11 in the BOICB

1 Kings 11 in the BOILNTAP

1 Kings 11 in the BOITCV

1 Kings 11 in the BOKCV

1 Kings 11 in the BOKCV2

1 Kings 11 in the BOKHWOG

1 Kings 11 in the BOKSSV

1 Kings 11 in the BOLCB

1 Kings 11 in the BOLCB2

1 Kings 11 in the BOMCV

1 Kings 11 in the BONAV

1 Kings 11 in the BONCB

1 Kings 11 in the BONLT

1 Kings 11 in the BONUT2

1 Kings 11 in the BOPLNT

1 Kings 11 in the BOSCB

1 Kings 11 in the BOSNC

1 Kings 11 in the BOTLNT

1 Kings 11 in the BOVCB

1 Kings 11 in the BOYCB

1 Kings 11 in the BPBB

1 Kings 11 in the BPH

1 Kings 11 in the BSB

1 Kings 11 in the CCB

1 Kings 11 in the CUV

1 Kings 11 in the CUVS

1 Kings 11 in the DBT

1 Kings 11 in the DGDNT

1 Kings 11 in the DHNT

1 Kings 11 in the DNT

1 Kings 11 in the ELBE

1 Kings 11 in the EMTV

1 Kings 11 in the ESV

1 Kings 11 in the FBV

1 Kings 11 in the FEB

1 Kings 11 in the GGMNT

1 Kings 11 in the GNT

1 Kings 11 in the HARY

1 Kings 11 in the HNT

1 Kings 11 in the IRVA

1 Kings 11 in the IRVB

1 Kings 11 in the IRVG

1 Kings 11 in the IRVH

1 Kings 11 in the IRVK

1 Kings 11 in the IRVM

1 Kings 11 in the IRVM2

1 Kings 11 in the IRVO

1 Kings 11 in the IRVP

1 Kings 11 in the IRVT

1 Kings 11 in the IRVT2

1 Kings 11 in the IRVU

1 Kings 11 in the ISVN

1 Kings 11 in the JSNT

1 Kings 11 in the KAPI

1 Kings 11 in the KBT1ETNIK

1 Kings 11 in the KBV

1 Kings 11 in the KJV

1 Kings 11 in the KNFD

1 Kings 11 in the LBA

1 Kings 11 in the LBLA

1 Kings 11 in the LNT

1 Kings 11 in the LSV

1 Kings 11 in the MAAL

1 Kings 11 in the MBV

1 Kings 11 in the MBV2

1 Kings 11 in the MHNT

1 Kings 11 in the MKNFD

1 Kings 11 in the MNG

1 Kings 11 in the MNT

1 Kings 11 in the MNT2

1 Kings 11 in the MRS1T

1 Kings 11 in the NAA

1 Kings 11 in the NASB

1 Kings 11 in the NBLA

1 Kings 11 in the NBS

1 Kings 11 in the NBVTP

1 Kings 11 in the NET2

1 Kings 11 in the NIV11

1 Kings 11 in the NNT

1 Kings 11 in the NNT2

1 Kings 11 in the NNT3

1 Kings 11 in the PDDPT

1 Kings 11 in the PFNT

1 Kings 11 in the RMNT

1 Kings 11 in the SBIAS

1 Kings 11 in the SBIBS

1 Kings 11 in the SBIBS2

1 Kings 11 in the SBICS

1 Kings 11 in the SBIDS

1 Kings 11 in the SBIGS

1 Kings 11 in the SBIHS

1 Kings 11 in the SBIIS

1 Kings 11 in the SBIIS2

1 Kings 11 in the SBIIS3

1 Kings 11 in the SBIKS

1 Kings 11 in the SBIKS2

1 Kings 11 in the SBIMS

1 Kings 11 in the SBIOS

1 Kings 11 in the SBIPS

1 Kings 11 in the SBISS

1 Kings 11 in the SBITS

1 Kings 11 in the SBITS2

1 Kings 11 in the SBITS3

1 Kings 11 in the SBITS4

1 Kings 11 in the SBIUS

1 Kings 11 in the SBIVS

1 Kings 11 in the SBT

1 Kings 11 in the SBT1E

1 Kings 11 in the SCHL

1 Kings 11 in the SNT

1 Kings 11 in the SUSU

1 Kings 11 in the SUSU2

1 Kings 11 in the SYNO

1 Kings 11 in the TBIAOTANT

1 Kings 11 in the TBT1E

1 Kings 11 in the TBT1E2

1 Kings 11 in the TFTIP

1 Kings 11 in the TFTU

1 Kings 11 in the TGNTATF3T

1 Kings 11 in the THAI

1 Kings 11 in the TNFD

1 Kings 11 in the TNT

1 Kings 11 in the TNTIK

1 Kings 11 in the TNTIL

1 Kings 11 in the TNTIN

1 Kings 11 in the TNTIP

1 Kings 11 in the TNTIZ

1 Kings 11 in the TOMA

1 Kings 11 in the TTENT

1 Kings 11 in the UBG

1 Kings 11 in the UGV

1 Kings 11 in the UGV2

1 Kings 11 in the UGV3

1 Kings 11 in the VBL

1 Kings 11 in the VDCC

1 Kings 11 in the YALU

1 Kings 11 in the YAPE

1 Kings 11 in the YBVTP

1 Kings 11 in the ZBP