1 Kings 14 (BOGWICC)

1 Pa nthawi imeneyo Abiya mwana wa Yeroboamu anayamba kudwala, 2 ndipo Yeroboamu anati kwa mkazi wake, “Nyamuka ndipo udzibise kuti usadziwike kuti ndiwe mkazi wa Yeroboamu, ndipo upite ku Silo. Kumeneko kuli mneneri Ahiya amene anandiwuza kuti ndidzakhala mfumu ya anthu awa. 3 Utenge buledi khumi, makeke ndiponso botolo la uchi ndipo upite kwa mneneriyo. Iye adzakuwuza zimene zidzamuchitikire mwanayu.” 4 Choncho mkazi wa Yeroboamu anadzibisa ndipo anapita ku nyumba ya Ahiya ku Silo.Tsono Ahiya sankatha kupenya bwino. Ankangoona kuti mbuu chifukwa cha ukalamba. 5 Koma Yehova nʼkuti atamuwuza Ahiya kuti, “Taona, mkazi wa Yeroboamu akubwera kudzafunsa iwe za mwana wake pakuti akudwala, ndiye udzamuyankhe zakutizakuti mkaziyo. Iye akafika, adzadzibisa.” 6 Tsono Ahiya atamva mgugu wa mapazi ake pa khomo, anati, “Lowa, iwe mkazi wa Yeroboamu. Bwanji ukudzibisa? Ine ndatumidwa kuti ndikuwuze nkhani yoyipa. 7 Pita, kamuwuze Yeroboamu kuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndinakukweza pakati pa anthu ndipo ndinakuyika kukhala mtsogoleri wa anthu anga Aisraeli. 8 Ndinachotsa ufumu ku nyumba ya Davide ndi kuwupereka kwa iwe, koma iwe sunafanane ndi mtumiki wanga Davide, amene ankasunga malamulo anga ndi kunditsata Ine ndi mtima wake wonse, kuchita zolungama zokhazokha pamaso panga. 9 Ndipo iwe wachita zoyipa kupambana onse amene analipo kale. Wadzipangira milungu ina, mafano a zitsulo. Iweyo wandikwiyitsa ndipo wandiwukira. 10 “ ‘Choncho taona, ndidzabweretsa masautso pa nyumba ya Yeroboamu. Ndipo ndidzawononga munthu wamwamuna aliyense wa pa banja lako, kapolo pamodzi ndi mfulu yemwe mʼdziko la Israeli. Ndidzatentha nyumba ya Yeroboamu monga mmene munthu amatenthera ndowe mpaka yonse kutheratu. 11 Agalu adzadya aliyense wa banja la Yeroboamu amene adzafere mu mzinda, ndipo mbalame zamlengalenga zidzadya iwo amene adzafere ku thengo, pakuti Yehova watero!’ 12 “Ndipo iwe nyamuka, bwerera ku nyumba kwako. Phazi lako likadzangoponda mu mzindamo, mwanayo adzamwalira. 13 Aisraeli onse adzalira maliro ake ndi kumuyika mʼmanda. Ndi yekhayo wa banja la Yeroboamu amene adzayikidwe mʼmanda, pakuti ndi mwa iye yekha mmene Yehova Mulungu wa Israeli wapezamo kanthu kabwino. 14 “Koma Yehova adzadzisankhira yekha mfumu yolamulira Israeli imene idzawononga banja la Yeroboamu. Tsiku lake ndi lero! Ndati chiyani? Inde, ndi lero lomwe lino. 15 Ndipo Yehova adzakantha Israeli, kotero kuti adzakhala ngati bango logwedera pa madzi. Iye adzazula Israeli mʼdziko labwino limene analipereka kwa makolo ake ndi kuwamwazira kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate, chifukwa anakwiyitsa Yehova pamene anapanga mafano a Asera. 16 Ndipo Iye sadzasamalanso Israeli chifukwa cha machimo amene anachita Yeroboamu ndi kuchimwitsa nawo Israeli.” 17 Tsono mkazi wa Yeroboamu anayimirira nachoka kupita ku Tiriza. Atangoponda pa khonde la nyumba yake, mwana uja anamwalira. 18 Aisraeli anamuyika mʼmanda, ndipo onse analira maliro ake, monga momwe Yehova ananenera kudzera mwa mtumiki wake, mneneri Ahiya. 19 Ntchito zina pa nthawi ya ulamuliro wa Yeroboamu, nkhondo zake ndi mmene ankalamulirira zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli. 20 Iye analamulira zaka 22 ndipo anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Nadabu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. 21 Rehobowamu mwana wa Solomoni anali mfumu ya ku Yuda. Iye analowa ufumu ali ndi zaka 41, ndipo analamulira zaka 17 ku Yerusalemu, mzinda umene Yehova anawusankha pakati pa mafuko a Israeli kuti ayikemo Dzina lake. Amayi ake anali Naama, wa ku Amoni. 22 Anthu a ku Yuda anachita zoyipa pamaso pa Yehova kupambana mmene anachitira makolo awo ndipo Yehova anawakwiyira. 23 Iwonso anadzipangira malo opembedzerapo mafano pa chitunda chilichonse ndi kuyimika miyala ya chipembedzo ndi mitengo ya Asera pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri. 24 Mʼdzikomo munalinso amuna ochita zachiwerewere mwa chipembedzo. Anthu ankachita zonyansa zonse za anthu a mitundu ina imene Yehova anayipirikitsa asanafike Aisraeli. 25 Chaka chachisanu cha ufumu wa Rehobowamu, Sisaki, mfumu ya Igupto, anadzathira nkhondo Yerusalemu. 26 Ananyamula chuma cha ku Nyumba ya Yehova ndiponso chuma cha ku nyumba ya mfumu. Anatenga chilichonse, ngakhalenso zishango zonse zagolide zimene Solomoni anapanga. 27 Ndipo Mfumu Rehobowamu anapanga zishango zamkuwa mʼmalo mwake, nazipereka mʼmanja mwa olamulira alonda a pa khomo pa nyumba ya mfumu. 28 Nthawi zonse mfumu ikamapita ku Nyumba ya Yehova, alonda ankanyamula zishangozo, kenaka ankazisunga mʼchipinda cha alonda. 29 Tsono ntchito zina za Rehobowamu ndi zina zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 30 Panali nkhondo zosalekeza pakati pa Rehobowamu ndi Yeroboamu. 31 Ndipo Rehobowamu anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. Amayi ake anali Naama wa ku Amoni. Ndipo Abiya analowa ufumu mʼmalo mwa abambo ake.

In Other Versions

1 Kings 14 in the ANGEFD

1 Kings 14 in the ANTPNG2D

1 Kings 14 in the AS21

1 Kings 14 in the BAGH

1 Kings 14 in the BBPNG

1 Kings 14 in the BBT1E

1 Kings 14 in the BDS

1 Kings 14 in the BEV

1 Kings 14 in the BHAD

1 Kings 14 in the BIB

1 Kings 14 in the BLPT

1 Kings 14 in the BNT

1 Kings 14 in the BNTABOOT

1 Kings 14 in the BNTLV

1 Kings 14 in the BOATCB

1 Kings 14 in the BOATCB2

1 Kings 14 in the BOBCV

1 Kings 14 in the BOCNT

1 Kings 14 in the BOECS

1 Kings 14 in the BOHCB

1 Kings 14 in the BOHCV

1 Kings 14 in the BOHLNT

1 Kings 14 in the BOHNTLTAL

1 Kings 14 in the BOICB

1 Kings 14 in the BOILNTAP

1 Kings 14 in the BOITCV

1 Kings 14 in the BOKCV

1 Kings 14 in the BOKCV2

1 Kings 14 in the BOKHWOG

1 Kings 14 in the BOKSSV

1 Kings 14 in the BOLCB

1 Kings 14 in the BOLCB2

1 Kings 14 in the BOMCV

1 Kings 14 in the BONAV

1 Kings 14 in the BONCB

1 Kings 14 in the BONLT

1 Kings 14 in the BONUT2

1 Kings 14 in the BOPLNT

1 Kings 14 in the BOSCB

1 Kings 14 in the BOSNC

1 Kings 14 in the BOTLNT

1 Kings 14 in the BOVCB

1 Kings 14 in the BOYCB

1 Kings 14 in the BPBB

1 Kings 14 in the BPH

1 Kings 14 in the BSB

1 Kings 14 in the CCB

1 Kings 14 in the CUV

1 Kings 14 in the CUVS

1 Kings 14 in the DBT

1 Kings 14 in the DGDNT

1 Kings 14 in the DHNT

1 Kings 14 in the DNT

1 Kings 14 in the ELBE

1 Kings 14 in the EMTV

1 Kings 14 in the ESV

1 Kings 14 in the FBV

1 Kings 14 in the FEB

1 Kings 14 in the GGMNT

1 Kings 14 in the GNT

1 Kings 14 in the HARY

1 Kings 14 in the HNT

1 Kings 14 in the IRVA

1 Kings 14 in the IRVB

1 Kings 14 in the IRVG

1 Kings 14 in the IRVH

1 Kings 14 in the IRVK

1 Kings 14 in the IRVM

1 Kings 14 in the IRVM2

1 Kings 14 in the IRVO

1 Kings 14 in the IRVP

1 Kings 14 in the IRVT

1 Kings 14 in the IRVT2

1 Kings 14 in the IRVU

1 Kings 14 in the ISVN

1 Kings 14 in the JSNT

1 Kings 14 in the KAPI

1 Kings 14 in the KBT1ETNIK

1 Kings 14 in the KBV

1 Kings 14 in the KJV

1 Kings 14 in the KNFD

1 Kings 14 in the LBA

1 Kings 14 in the LBLA

1 Kings 14 in the LNT

1 Kings 14 in the LSV

1 Kings 14 in the MAAL

1 Kings 14 in the MBV

1 Kings 14 in the MBV2

1 Kings 14 in the MHNT

1 Kings 14 in the MKNFD

1 Kings 14 in the MNG

1 Kings 14 in the MNT

1 Kings 14 in the MNT2

1 Kings 14 in the MRS1T

1 Kings 14 in the NAA

1 Kings 14 in the NASB

1 Kings 14 in the NBLA

1 Kings 14 in the NBS

1 Kings 14 in the NBVTP

1 Kings 14 in the NET2

1 Kings 14 in the NIV11

1 Kings 14 in the NNT

1 Kings 14 in the NNT2

1 Kings 14 in the NNT3

1 Kings 14 in the PDDPT

1 Kings 14 in the PFNT

1 Kings 14 in the RMNT

1 Kings 14 in the SBIAS

1 Kings 14 in the SBIBS

1 Kings 14 in the SBIBS2

1 Kings 14 in the SBICS

1 Kings 14 in the SBIDS

1 Kings 14 in the SBIGS

1 Kings 14 in the SBIHS

1 Kings 14 in the SBIIS

1 Kings 14 in the SBIIS2

1 Kings 14 in the SBIIS3

1 Kings 14 in the SBIKS

1 Kings 14 in the SBIKS2

1 Kings 14 in the SBIMS

1 Kings 14 in the SBIOS

1 Kings 14 in the SBIPS

1 Kings 14 in the SBISS

1 Kings 14 in the SBITS

1 Kings 14 in the SBITS2

1 Kings 14 in the SBITS3

1 Kings 14 in the SBITS4

1 Kings 14 in the SBIUS

1 Kings 14 in the SBIVS

1 Kings 14 in the SBT

1 Kings 14 in the SBT1E

1 Kings 14 in the SCHL

1 Kings 14 in the SNT

1 Kings 14 in the SUSU

1 Kings 14 in the SUSU2

1 Kings 14 in the SYNO

1 Kings 14 in the TBIAOTANT

1 Kings 14 in the TBT1E

1 Kings 14 in the TBT1E2

1 Kings 14 in the TFTIP

1 Kings 14 in the TFTU

1 Kings 14 in the TGNTATF3T

1 Kings 14 in the THAI

1 Kings 14 in the TNFD

1 Kings 14 in the TNT

1 Kings 14 in the TNTIK

1 Kings 14 in the TNTIL

1 Kings 14 in the TNTIN

1 Kings 14 in the TNTIP

1 Kings 14 in the TNTIZ

1 Kings 14 in the TOMA

1 Kings 14 in the TTENT

1 Kings 14 in the UBG

1 Kings 14 in the UGV

1 Kings 14 in the UGV2

1 Kings 14 in the UGV3

1 Kings 14 in the VBL

1 Kings 14 in the VDCC

1 Kings 14 in the YALU

1 Kings 14 in the YAPE

1 Kings 14 in the YBVTP

1 Kings 14 in the ZBP