1 Kings 15 (BOGWICC)

1 Mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yeroboamu mwana wa Nebati, Abiya anakhala mfumu ya Yuda, 2 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka zitatu. Amayi ake anali Maaka, mwana wa Abisalomu. 3 Abiya anachita zoyipa zonse zimene abambo ake anazichita. Sanali wangwiro pamaso pa Yehova Mulungu wake, monga linachitira kholo lake Davide. 4 Komabe chifukwa cha Davide, Yehova Mulungu wake anamupatsa nyale mu Yerusalemu pomupatsa mwana wolowa mʼmalo mwake ndi kumukhazikitsa kukhala wamphamvu mu Yerusalemu; 5 pakuti Davide anachita zolungama pamaso pa Yehova ndipo sanalephere kusunga chilichonse chimene Yehova anamulamula masiku onse a moyo wake kupatula nkhani ija ya Uriya Mhiti. 6 Panali nkhondo pakati pa Rehobowamu ndi Yeroboamu masiku onse a moyo wa Abiya. 7 Tsono ntchito zina za Abiya, ndi zina zonse anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yeroboamu. 8 Ndipo Abiya anamwalira nayikidwa mʼmanda momwe anayikidwa makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Asa, mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. 9 Mʼchaka cha makumi awiri cha Yeroboamu mfumu ya Israeli, Asa anakhala mfumu ya Yuda, 10 ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 41. Agogo ake akazi anali Maaka mwana wa Abisalomu. 11 Asa anachita zolungama pamaso pa Yehova monga anachitira Davide kholo lake. 12 Iye anachotsa mʼdzikomo amuna onse ochita zadama pochita chipembedzo chawo ndiponso anachotsa mafano onse amene makolo ake anawapanga. 13 Iye anachotsanso gogo wake Maaka pa udindo wake wa amayi a mfumu, chifukwa choti anapanga fano lonyansa la Asera. Asa anagwetsa fanolo nakalitentha ku Chigwa cha Kidroni. 14 Ngakhale sanachotse malo opembedzerapo mafano, mtima wa Asa unali wodzipereka kwathunthu kwa Yehova masiku onse a moyo wake. 15 Asa anabweretsa ku Nyumba ya Yehova zinthu zimene abambo ake anazipereka, ndiponso zinthu zimene iye mwini anazipereka: zagolide, siliva ndi ziwiya zotengera. 16 Panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israeli nthawi yonse ya ulamuliro wawo. 17 Baasa mfumu ya Israeli anapita kukathira nkhondo dziko la Yuda, ndipo anamangira linga mzinda wa Rama kuletsa kuti wina aliyense asatuluke kapena kulowa mʼdziko la Asa, mfumu ya Yuda. 18 Tsono Asa anatenga siliva yense pamodzi ndi golide zimene zinatsala ku malo osungira chuma cha ku Nyumba ya Yehova ndiponso ku nyumba yake yaufumu. Anazipereka kwa atumiki ake, nawatuma kupita nazo kwa Beni-Hadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Heziyoni, mfumu ya Aramu, amene ankakhala ku Damasiko ndipo anakamuwuza kuti, 19 “Tiyeni tigwirizane inu ndi ine, monga panali mgwirizano pakati pa abambo anu ndi abambo anga. Onani, ndikukutumizirani mphatso za siliva ndi golide. Tsopano kathetseni mgwirizano wanu ndi Baasa mfumu ya Israeli kuti andisiye.” 20 Choncho Beni-Hadadi anamvera zimene ananena mfumu Asa ndipo anatumiza olamulira magulu ake ankhondo ku mizinda ya Israeli. Ndipo iye anagonjetsa Iyoni, Dani, Abeli-Beti-Maaka ndi dera lonse la Kinereti kuphatikiza dziko lonse la Nafutali. 21 Baasa atamva zimenezi, anasiya kumangira linga Rama ndipo anakakhala ku Tiriza. 22 Pamenepo Mfumu Asa analamula anthu onse a ku Yuda osasiya ndi mmodzi yemwe, ndipo anachotsa ku Rama miyala ndi matabwa amene Baasa ankamangira kumeneko. Zipangizo zimenezi Mfumu Asa inamangira linga la Geba ku Benjamini ndi la ku Mizipa. 23 Tsono ntchito zina za Asa, za mphamvu zake ndi mizinda imene anayimanga ndi zina zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Koma pa nthawi ya ukalamba wake anadwala nthenda ya mapazi. 24 Ndipo Asa anamwalira nayikidwa mʼmanda momwe anayikidwa makolo ake mu mzinda wa Davide kholo lake. Ndipo Yehosafati mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. 25 Nadabu, mwana wa Yeroboamu anakhala mfumu ya Israeli mʼchaka chachiwiri cha Asa mfumu ya Yuda, ndipo analamulira Israeli zaka ziwiri. 26 Nadabu anachita zoyipa pamaso pa Yehova, anayenda mʼnjira za abambo ake ndi mu uchimo womwe anachimwitsa nawo Israeli. 27 Baasa mwana wa Ahiya, wa banja la Isakara anakonzera Nadabuyo chiwembu, ndipo anamukantha ku Gibetoni, mzinda wa Afilisti, pamene Nadabu ndi anthu onse a ku Israeli anali atawuzungulira. 28 Baasa anapha Nadabu mʼchaka chachitatu cha Asa, mfumu ya ku Yuda ndipo analowa ufumu mʼmalo mwake. 29 Iye atangoyamba kulamulira, anapha anthu onse a banja la Yeroboamu. Sanasiye ndi mmodzi yemwe wamoyo pa banjapo, koma anawononga anthu onse, molingana ndi mawu a Yehova amene anayankhula mwa mtumiki wake Ahiya wa ku Silo 30 chifukwa cha machimo amene Yeroboamu anachita, ndiponso kuchimwitsa anthu a ku Israeli, naputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israeli. 31 Tsono ntchito za Nadabu ndi zina zonse zimene anazichita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? 32 Panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israeli pa nthawi yonse ya ulamuliro wawo. 33 Chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, Baasa mwana wa Ahiya anakhala mfumu ya Aisraeli onse ku Tiriza, ndipo analamulira zaka 24. 34 Anachita zoyipa pamaso pa Yehova, nayenda mʼnjira za Yeroboamu ndi kuchita tchimo lake limene linachimwitsa anthu a ku Israeli.

In Other Versions

1 Kings 15 in the ANGEFD

1 Kings 15 in the ANTPNG2D

1 Kings 15 in the AS21

1 Kings 15 in the BAGH

1 Kings 15 in the BBPNG

1 Kings 15 in the BBT1E

1 Kings 15 in the BDS

1 Kings 15 in the BEV

1 Kings 15 in the BHAD

1 Kings 15 in the BIB

1 Kings 15 in the BLPT

1 Kings 15 in the BNT

1 Kings 15 in the BNTABOOT

1 Kings 15 in the BNTLV

1 Kings 15 in the BOATCB

1 Kings 15 in the BOATCB2

1 Kings 15 in the BOBCV

1 Kings 15 in the BOCNT

1 Kings 15 in the BOECS

1 Kings 15 in the BOHCB

1 Kings 15 in the BOHCV

1 Kings 15 in the BOHLNT

1 Kings 15 in the BOHNTLTAL

1 Kings 15 in the BOICB

1 Kings 15 in the BOILNTAP

1 Kings 15 in the BOITCV

1 Kings 15 in the BOKCV

1 Kings 15 in the BOKCV2

1 Kings 15 in the BOKHWOG

1 Kings 15 in the BOKSSV

1 Kings 15 in the BOLCB

1 Kings 15 in the BOLCB2

1 Kings 15 in the BOMCV

1 Kings 15 in the BONAV

1 Kings 15 in the BONCB

1 Kings 15 in the BONLT

1 Kings 15 in the BONUT2

1 Kings 15 in the BOPLNT

1 Kings 15 in the BOSCB

1 Kings 15 in the BOSNC

1 Kings 15 in the BOTLNT

1 Kings 15 in the BOVCB

1 Kings 15 in the BOYCB

1 Kings 15 in the BPBB

1 Kings 15 in the BPH

1 Kings 15 in the BSB

1 Kings 15 in the CCB

1 Kings 15 in the CUV

1 Kings 15 in the CUVS

1 Kings 15 in the DBT

1 Kings 15 in the DGDNT

1 Kings 15 in the DHNT

1 Kings 15 in the DNT

1 Kings 15 in the ELBE

1 Kings 15 in the EMTV

1 Kings 15 in the ESV

1 Kings 15 in the FBV

1 Kings 15 in the FEB

1 Kings 15 in the GGMNT

1 Kings 15 in the GNT

1 Kings 15 in the HARY

1 Kings 15 in the HNT

1 Kings 15 in the IRVA

1 Kings 15 in the IRVB

1 Kings 15 in the IRVG

1 Kings 15 in the IRVH

1 Kings 15 in the IRVK

1 Kings 15 in the IRVM

1 Kings 15 in the IRVM2

1 Kings 15 in the IRVO

1 Kings 15 in the IRVP

1 Kings 15 in the IRVT

1 Kings 15 in the IRVT2

1 Kings 15 in the IRVU

1 Kings 15 in the ISVN

1 Kings 15 in the JSNT

1 Kings 15 in the KAPI

1 Kings 15 in the KBT1ETNIK

1 Kings 15 in the KBV

1 Kings 15 in the KJV

1 Kings 15 in the KNFD

1 Kings 15 in the LBA

1 Kings 15 in the LBLA

1 Kings 15 in the LNT

1 Kings 15 in the LSV

1 Kings 15 in the MAAL

1 Kings 15 in the MBV

1 Kings 15 in the MBV2

1 Kings 15 in the MHNT

1 Kings 15 in the MKNFD

1 Kings 15 in the MNG

1 Kings 15 in the MNT

1 Kings 15 in the MNT2

1 Kings 15 in the MRS1T

1 Kings 15 in the NAA

1 Kings 15 in the NASB

1 Kings 15 in the NBLA

1 Kings 15 in the NBS

1 Kings 15 in the NBVTP

1 Kings 15 in the NET2

1 Kings 15 in the NIV11

1 Kings 15 in the NNT

1 Kings 15 in the NNT2

1 Kings 15 in the NNT3

1 Kings 15 in the PDDPT

1 Kings 15 in the PFNT

1 Kings 15 in the RMNT

1 Kings 15 in the SBIAS

1 Kings 15 in the SBIBS

1 Kings 15 in the SBIBS2

1 Kings 15 in the SBICS

1 Kings 15 in the SBIDS

1 Kings 15 in the SBIGS

1 Kings 15 in the SBIHS

1 Kings 15 in the SBIIS

1 Kings 15 in the SBIIS2

1 Kings 15 in the SBIIS3

1 Kings 15 in the SBIKS

1 Kings 15 in the SBIKS2

1 Kings 15 in the SBIMS

1 Kings 15 in the SBIOS

1 Kings 15 in the SBIPS

1 Kings 15 in the SBISS

1 Kings 15 in the SBITS

1 Kings 15 in the SBITS2

1 Kings 15 in the SBITS3

1 Kings 15 in the SBITS4

1 Kings 15 in the SBIUS

1 Kings 15 in the SBIVS

1 Kings 15 in the SBT

1 Kings 15 in the SBT1E

1 Kings 15 in the SCHL

1 Kings 15 in the SNT

1 Kings 15 in the SUSU

1 Kings 15 in the SUSU2

1 Kings 15 in the SYNO

1 Kings 15 in the TBIAOTANT

1 Kings 15 in the TBT1E

1 Kings 15 in the TBT1E2

1 Kings 15 in the TFTIP

1 Kings 15 in the TFTU

1 Kings 15 in the TGNTATF3T

1 Kings 15 in the THAI

1 Kings 15 in the TNFD

1 Kings 15 in the TNT

1 Kings 15 in the TNTIK

1 Kings 15 in the TNTIL

1 Kings 15 in the TNTIN

1 Kings 15 in the TNTIP

1 Kings 15 in the TNTIZ

1 Kings 15 in the TOMA

1 Kings 15 in the TTENT

1 Kings 15 in the UBG

1 Kings 15 in the UGV

1 Kings 15 in the UGV2

1 Kings 15 in the UGV3

1 Kings 15 in the VBL

1 Kings 15 in the VDCC

1 Kings 15 in the YALU

1 Kings 15 in the YAPE

1 Kings 15 in the YBVTP

1 Kings 15 in the ZBP