1 Kings 16 (BOGWICC)

1 Ndipo Yehova anayankhula kudzera mwa Yehu mwana wa Hanani, mawu odzudzula Baasa kuti, 2 “Ine ndinakukuza kuchokera pa fumbi ndipo ndinakupanga kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisraeli, koma iwe wakhala ukuyenda mʼnjira za Yeroboamu ndi kuchimwitsa anthu anga Aisraeli naputa mkwiyo wanga chifukwa cha machimo awo. 3 Taonani, Ine ndatsala pangʼono kuwononga Baasa pamodzi ndi nyumba yake, ndipo ndidzachitira nyumba yake zimene ndinachita pa nyumba ya Yeroboamu mwana wa Nebati. 4 Agalu adzadya aliyense wa banja la Baasa amene adzafere mu mzinda, ndipo mbalame za mu mlengalenga zidzadya iwo amene adzafere kuthengo.” 5 Tsono ntchito zina za Baasa ndi zamphamvu zake zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? 6 Baasa anamwalira nayikidwa mʼmanda amene anayikidwa makolo ake ku Tiriza. Ndipo Ela mwana wake anakhala mfumu mʼmalo mwake. 7 Komatu Yehova anayankhula kwa Baasa pamodzi ndi banja lake lonse kudzera mwa mneneri Yehu mwana wa Hanani, chifukwa cha zoyipa zonse zimene iye anachita pamaso pa Yehova, kukwiyitsa Yehovayo nakhala ngati nyumba ya Yeroboamu ndiponso chifukwa anawonongeratu banja la Yeroboamu. 8 Mʼchaka cha 26 cha ufumu wa Asa mfumu ya Yuda, Ela mwana wa Baasa anakhala mfumu ya Israeli, ndipo analamulira ku Tiriza zaka ziwiri. 9 Zimuri, mmodzi mwa akuluakulu ake, amene ankalamulira theka la magaleta ake, anamuchitira chiwembu. Nthawi imeneyi Ela anali ku Tiriza, akumwa koledzera nako mʼnyumba ya Ariza, munthu amene ankayangʼanira nyumba yaufumu ku Tiriza. 10 Zimuri anadzalowa, namukantha ndi kumupha mʼchaka cha 27 cha Asa mfumu ya Yuda. Ndipo Zimuriyo anakhala mfumu mʼmalo mwake. 11 Zimuri atangoyamba kulamulira, anapha banja lonse la Baasa. Sanasiyepo munthu wamwamuna ndi mmodzi yemwe, wachibale kapena bwenzi lake. 12 Choncho Zimuri anawononga banja lonse la Baasa, molingana ndi mawu amene Yehova anayankhula motsutsa Baasa kudzera mwa mneneri Yehu, 13 chifukwa cha machimo onse amene Baasa ndi mwana wake Ela anachita nachimwitsa Israeli, anakwiyitsa Yehova, Mulungu wa Israeli ndi mafano awo osapindulitsa. 14 Tsono ntchito zina za Ela ndi zina zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? 15 Mʼchaka cha 27 cha Asa mfumu ya Yuda, Zimuri analamulira ku Tiriza masiku asanu ndi awiri. Gulu la ankhondo linali litamanga misasa pafupi ndi Gibetoni, mzinda wa Afilisti. 16 Ankhondo amene anali ku misasa atamva kuti Zimuri wachita chiwembu ndi kupha mfumu, tsiku lomwelo ku misasako anasankha Omuri, mkulu wa ankhondo kukhala mfumu ya Israeli. 17 Tsono Omuri ndi Aisraeli onse amene anali naye anachoka ku Gibetoni ndi kukazinga Mzinda wa Tiriza. 18 Zimuri ataona kuti mzinda walandidwa, anathawira ku nsanja ya nyumba ya mfumu ndipo anatentha nyumbayo iye ali momwemo. Kotero iyeyo anafa, 19 chifukwa cha machimo amene iye anachita, kuchita zoyipa pamaso pa Yehova ndi kuyenda mʼnjira za Yeroboamu, nachimwitsa nazo Aisraeli. 20 Tsono ntchito zina za Zimuri ndi chiwembu chake chimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? 21 Pambuyo pake Aisraeli anagawikana pakati: theka linatsatira Tibini mwana wa Ginati kuti limulonge ufumu, ndipo theka lina linatsatira Omuri. 22 Koma anthu otsatira Omuri anali amphamvu kupambana amene ankatsatira Tibini mwana wa Ginati. Choncho Tibini anafa ndipo Omuri anakhala mfumu. 23 Mʼchaka cha 31 cha Asa mfumu ya Yuda, Omuri anakhala mfumu ya Israeli, ndipo analamulira zaka 12 ndi miyezi isanu ndi umodzi ku Tiriza. 24 Iye anagula phiri la Samariya kwa Semeri pa mtengo wa ndalama 6,000 za siliva ndipo pa phiripo anamangapo mzinda, nawutcha Samariya, potsata dzina la Semeri, dzina la mwini wakale wa phirilo. 25 Koma Omuri anachita zoyipa pamaso pa Yehova ndipo anachimwa kuposa mafumu ena onse amene analipo iye asanakhale mfumu. 26 Pakuti iye anayenda mʼnjira zonse za Yeroboamu mwana wa Nebati, ndipo tchimo lake anachimwitsa nalo Aisraeli, nakwiyitsa Yehova Mulungu wa Israeli ndi mafano awo opandapake. 27 Tsono ntchito zina za Omuri ndi zamphamvu zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? 28 Choncho Omuri anamwalira nayikidwa mʼmanda amene anayikidwa makolo ake ku Samariya. Ndipo Ahabu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. 29 Mʼchaka cha 38 cha ufumu wa Asa, mfumu ya Yuda, Ahabu mwana wa Omuri anakhala mfumu ya Israeli nalamulira Israeli ku Samariya zaka 22. 30 Ahabu mwana wa Omuri anachita zoyipa zambiri pamaso pa Yehova kupambana mafumu onse akale. 31 Iye sanachiyese ngati chinthu chochepa chabe kuchita machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, koma anakwatiranso Yezebeli, mwana wa Etibaala mfumu ya Asidoni, nayamba kutumikira Baala ndi kumupembedza. 32 Iye anapangira Baala guwa lansembe mʼnyumba ya Baala imene anamanga ku Samariya. 33 Ahabu anapanganso fano la Asera ndi kukwiyitsa kwambiri Yehova Mulungu wa Israeli, kupambana mafumu onse a Israeli amene analipo iye asanakhale mfumu. 34 Pa nthawi ya Ahabu, Hiyeli wa ku Beteli anamanganso mzinda wa Yeriko. Pa nthawi yomanga maziko ake, mwana wake woyamba wa mwamuna, Abiramu anamwalira, ndipo pa nthawi yomanga zipata zake, mwana wa mngʼono wa mwamuna Segubu, anamwaliranso. Izi zinachitika monga momwe Yehova ananenera kudzera mwa Yoswa mwana wa Nuni.

In Other Versions

1 Kings 16 in the ANGEFD

1 Kings 16 in the ANTPNG2D

1 Kings 16 in the AS21

1 Kings 16 in the BAGH

1 Kings 16 in the BBPNG

1 Kings 16 in the BBT1E

1 Kings 16 in the BDS

1 Kings 16 in the BEV

1 Kings 16 in the BHAD

1 Kings 16 in the BIB

1 Kings 16 in the BLPT

1 Kings 16 in the BNT

1 Kings 16 in the BNTABOOT

1 Kings 16 in the BNTLV

1 Kings 16 in the BOATCB

1 Kings 16 in the BOATCB2

1 Kings 16 in the BOBCV

1 Kings 16 in the BOCNT

1 Kings 16 in the BOECS

1 Kings 16 in the BOHCB

1 Kings 16 in the BOHCV

1 Kings 16 in the BOHLNT

1 Kings 16 in the BOHNTLTAL

1 Kings 16 in the BOICB

1 Kings 16 in the BOILNTAP

1 Kings 16 in the BOITCV

1 Kings 16 in the BOKCV

1 Kings 16 in the BOKCV2

1 Kings 16 in the BOKHWOG

1 Kings 16 in the BOKSSV

1 Kings 16 in the BOLCB

1 Kings 16 in the BOLCB2

1 Kings 16 in the BOMCV

1 Kings 16 in the BONAV

1 Kings 16 in the BONCB

1 Kings 16 in the BONLT

1 Kings 16 in the BONUT2

1 Kings 16 in the BOPLNT

1 Kings 16 in the BOSCB

1 Kings 16 in the BOSNC

1 Kings 16 in the BOTLNT

1 Kings 16 in the BOVCB

1 Kings 16 in the BOYCB

1 Kings 16 in the BPBB

1 Kings 16 in the BPH

1 Kings 16 in the BSB

1 Kings 16 in the CCB

1 Kings 16 in the CUV

1 Kings 16 in the CUVS

1 Kings 16 in the DBT

1 Kings 16 in the DGDNT

1 Kings 16 in the DHNT

1 Kings 16 in the DNT

1 Kings 16 in the ELBE

1 Kings 16 in the EMTV

1 Kings 16 in the ESV

1 Kings 16 in the FBV

1 Kings 16 in the FEB

1 Kings 16 in the GGMNT

1 Kings 16 in the GNT

1 Kings 16 in the HARY

1 Kings 16 in the HNT

1 Kings 16 in the IRVA

1 Kings 16 in the IRVB

1 Kings 16 in the IRVG

1 Kings 16 in the IRVH

1 Kings 16 in the IRVK

1 Kings 16 in the IRVM

1 Kings 16 in the IRVM2

1 Kings 16 in the IRVO

1 Kings 16 in the IRVP

1 Kings 16 in the IRVT

1 Kings 16 in the IRVT2

1 Kings 16 in the IRVU

1 Kings 16 in the ISVN

1 Kings 16 in the JSNT

1 Kings 16 in the KAPI

1 Kings 16 in the KBT1ETNIK

1 Kings 16 in the KBV

1 Kings 16 in the KJV

1 Kings 16 in the KNFD

1 Kings 16 in the LBA

1 Kings 16 in the LBLA

1 Kings 16 in the LNT

1 Kings 16 in the LSV

1 Kings 16 in the MAAL

1 Kings 16 in the MBV

1 Kings 16 in the MBV2

1 Kings 16 in the MHNT

1 Kings 16 in the MKNFD

1 Kings 16 in the MNG

1 Kings 16 in the MNT

1 Kings 16 in the MNT2

1 Kings 16 in the MRS1T

1 Kings 16 in the NAA

1 Kings 16 in the NASB

1 Kings 16 in the NBLA

1 Kings 16 in the NBS

1 Kings 16 in the NBVTP

1 Kings 16 in the NET2

1 Kings 16 in the NIV11

1 Kings 16 in the NNT

1 Kings 16 in the NNT2

1 Kings 16 in the NNT3

1 Kings 16 in the PDDPT

1 Kings 16 in the PFNT

1 Kings 16 in the RMNT

1 Kings 16 in the SBIAS

1 Kings 16 in the SBIBS

1 Kings 16 in the SBIBS2

1 Kings 16 in the SBICS

1 Kings 16 in the SBIDS

1 Kings 16 in the SBIGS

1 Kings 16 in the SBIHS

1 Kings 16 in the SBIIS

1 Kings 16 in the SBIIS2

1 Kings 16 in the SBIIS3

1 Kings 16 in the SBIKS

1 Kings 16 in the SBIKS2

1 Kings 16 in the SBIMS

1 Kings 16 in the SBIOS

1 Kings 16 in the SBIPS

1 Kings 16 in the SBISS

1 Kings 16 in the SBITS

1 Kings 16 in the SBITS2

1 Kings 16 in the SBITS3

1 Kings 16 in the SBITS4

1 Kings 16 in the SBIUS

1 Kings 16 in the SBIVS

1 Kings 16 in the SBT

1 Kings 16 in the SBT1E

1 Kings 16 in the SCHL

1 Kings 16 in the SNT

1 Kings 16 in the SUSU

1 Kings 16 in the SUSU2

1 Kings 16 in the SYNO

1 Kings 16 in the TBIAOTANT

1 Kings 16 in the TBT1E

1 Kings 16 in the TBT1E2

1 Kings 16 in the TFTIP

1 Kings 16 in the TFTU

1 Kings 16 in the TGNTATF3T

1 Kings 16 in the THAI

1 Kings 16 in the TNFD

1 Kings 16 in the TNT

1 Kings 16 in the TNTIK

1 Kings 16 in the TNTIL

1 Kings 16 in the TNTIN

1 Kings 16 in the TNTIP

1 Kings 16 in the TNTIZ

1 Kings 16 in the TOMA

1 Kings 16 in the TTENT

1 Kings 16 in the UBG

1 Kings 16 in the UGV

1 Kings 16 in the UGV2

1 Kings 16 in the UGV3

1 Kings 16 in the VBL

1 Kings 16 in the VDCC

1 Kings 16 in the YALU

1 Kings 16 in the YAPE

1 Kings 16 in the YBVTP

1 Kings 16 in the ZBP