1 Samuel 19 (BOGWICC)

1 Sauli anawuza mwana wake Yonatani ndi nduna zake zonse kuti aphe Davide. Koma Yonatani amamukonda kwambiri Davide. 2 Choncho anawuza Davide kuti, “Abambo anga Sauli akufuna kukupha. Tsono uchenjere. Mmawa upite ukabisale ndipo ukakhale komweko. 3 Ine ndidzapita ndi kukayima pafupi ndi abambo anga ku munda kumene iwe ukabisale. Ndipo ndidzayankhula ndi abambo anga za iwe ndipo chilichonse chimene ndikamve ndidzakuwuza.” 4 Tsono Yonatani anakanena zabwino za Davide kwa abambo ake Sauli ndipo anati, “Mfumu musachimwire mtumiki wanu Davide, sanakuchimwireni, koma amakuchitirani zabwino kwambiri. 5 Iye anayika moyo wake pa chiswe pamene anapha Mfilisiti uja. Choncho Yehova anachita zazikulu popambanitsa Aisraeli pa nkhondo. Inu munaona zonsezo ndipo munakondwera. Nanga nʼchifukwa chiyani mukufuna kuchimwira munthu wosalakwa pofuna kupha Davide?” 6 Sauli anamvera mawu a Yonatani ndipo analumbira kuti, “Pali Yehova, Davide sadzaphedwa.” 7 Pambuyo pake Yonatani anayitana Davide namuwuza zonsezi. Choncho Yonatani anabwera naye Davide kwa Sauli ndipo ankamutumikira Sauliyo monga kale. 8 Panabukanso nkhondo ina ndipo Davide anapita ndi kukamenyana ndi Afilisti. Iye anawakantha mwamphamvu kotero kuti Afilisti anathawa. 9 Tsiku lina mzimu woyipa uja unafikanso pa Sauli. Nthawi imeneyi nʼkuti Sauli uja ali mʼnyumba mwake, mkondo uli mʼdzanja lake ndi Davide akuyimba zeze, 10 Sauli anafuna kumubaya Davide ndi kumukhomera kukhoma, koma Davide anapewa mkondowo kotero Sauli anakabaya pa khoma. Usiku womwewo Davide anathawa. 11 Usiku womwewo Sauli anatumiza anthu ku nyumba ya Davide kuti akamubisalire ndi kumupha mmamawa. Koma Mikala mkazi wake anamuchenjeza nati, “Ngati usiku uno supulumutsa moyo wako, mawa udzaphedwa.” 12 Choncho Mikala anamutulutsira Davide pa zenera, ndipo anathawa ndi kupulumuka. 13 Kenaka Mikala anatenga fano naligoneka pa bedi nayika pilo wa ubweya wa mbuzi ku mutu kwa fanolo ndipo analifunditsa nsalu. 14 Pamene amithenga a Sauli aja anafika kuti akamugwire Davide, Mikala anati, “Davide akudwala.” 15 Koma Sauli anatumanso anthuwo kuti akamuone Davide, nati, “Mubwere naye kuno ali pa bedi pomwepo kuti ndidzamuphe.” 16 Koma pamene anthuwo analowa, anangoona fano pa bedipo ndi pilo wa ubweya wa mbuzi ku mutu kwake. 17 Tsono Sauli anafunsa Mikala kuti, “Nʼchifukwa chiyani wandinamiza chotere polola kuti mdani wanga athawe?”Mikala anayankha kuti, “Davide anandiwuza kuti, ‘Ukapanda kutero ndikupha.’ ” 18 Choncho Davide anathawa napulumuka. Pambuyo pake anapita kwa Samueli ku Rama nakamuwuza zonse zimene Sauli anamuchita. Kenaka iye ndi Samueli anapita kukakhala ku Nayoti. 19 Sauli anamva kuti, “Davide ali ku Nayoti ku Rama.” 20 Choncho iye anatumiza anthu kuti akamugwire Davide. Koma anaona gulu la aneneri likulosera ndi Samueli akuwatsogolera. Pomwepo Mzimu wa Mulungu unawafikira ndipo nawonso anayamba kulosera. 21 Sauli atamva zimenezi anatumizanso anthu ena, koma nawonso anayamba kulosa. Anatumanso anthu ena kachitatu, koma nawonso anayamba kulosa. 22 Pomaliza Sauli mwini wake ananyamuka kupita ku Rama ndipo anafika ku chitsime chachikulu cha ku Seku. Ndipo anafunsa, “Samueli ndi Davide ali kuti?”Munthu wina anamuyankha kuti, “Ali ku Nayoti ku Rama.” 23 Choncho Sauli anapita ku Nayoti ku Rama. Koma Mzimu wa Mulungu unafikanso pa iye ndipo ankalosa akuyenda mpaka anafika ku Nayoti. 24 Nayenso anavula zovala zake nayamba kulosa pamaso pa Samueli. Kenaka anagona wamaliseche tsiku lonse ndi usiku wonse. Nʼchifukwa chake anthu amati, “Kodi Sauli alinso mmodzi wa aneneri?”

In Other Versions

1 Samuel 19 in the ANGEFD

1 Samuel 19 in the ANTPNG2D

1 Samuel 19 in the AS21

1 Samuel 19 in the BAGH

1 Samuel 19 in the BBPNG

1 Samuel 19 in the BBT1E

1 Samuel 19 in the BDS

1 Samuel 19 in the BEV

1 Samuel 19 in the BHAD

1 Samuel 19 in the BIB

1 Samuel 19 in the BLPT

1 Samuel 19 in the BNT

1 Samuel 19 in the BNTABOOT

1 Samuel 19 in the BNTLV

1 Samuel 19 in the BOATCB

1 Samuel 19 in the BOATCB2

1 Samuel 19 in the BOBCV

1 Samuel 19 in the BOCNT

1 Samuel 19 in the BOECS

1 Samuel 19 in the BOHCB

1 Samuel 19 in the BOHCV

1 Samuel 19 in the BOHLNT

1 Samuel 19 in the BOHNTLTAL

1 Samuel 19 in the BOICB

1 Samuel 19 in the BOILNTAP

1 Samuel 19 in the BOITCV

1 Samuel 19 in the BOKCV

1 Samuel 19 in the BOKCV2

1 Samuel 19 in the BOKHWOG

1 Samuel 19 in the BOKSSV

1 Samuel 19 in the BOLCB

1 Samuel 19 in the BOLCB2

1 Samuel 19 in the BOMCV

1 Samuel 19 in the BONAV

1 Samuel 19 in the BONCB

1 Samuel 19 in the BONLT

1 Samuel 19 in the BONUT2

1 Samuel 19 in the BOPLNT

1 Samuel 19 in the BOSCB

1 Samuel 19 in the BOSNC

1 Samuel 19 in the BOTLNT

1 Samuel 19 in the BOVCB

1 Samuel 19 in the BOYCB

1 Samuel 19 in the BPBB

1 Samuel 19 in the BPH

1 Samuel 19 in the BSB

1 Samuel 19 in the CCB

1 Samuel 19 in the CUV

1 Samuel 19 in the CUVS

1 Samuel 19 in the DBT

1 Samuel 19 in the DGDNT

1 Samuel 19 in the DHNT

1 Samuel 19 in the DNT

1 Samuel 19 in the ELBE

1 Samuel 19 in the EMTV

1 Samuel 19 in the ESV

1 Samuel 19 in the FBV

1 Samuel 19 in the FEB

1 Samuel 19 in the GGMNT

1 Samuel 19 in the GNT

1 Samuel 19 in the HARY

1 Samuel 19 in the HNT

1 Samuel 19 in the IRVA

1 Samuel 19 in the IRVB

1 Samuel 19 in the IRVG

1 Samuel 19 in the IRVH

1 Samuel 19 in the IRVK

1 Samuel 19 in the IRVM

1 Samuel 19 in the IRVM2

1 Samuel 19 in the IRVO

1 Samuel 19 in the IRVP

1 Samuel 19 in the IRVT

1 Samuel 19 in the IRVT2

1 Samuel 19 in the IRVU

1 Samuel 19 in the ISVN

1 Samuel 19 in the JSNT

1 Samuel 19 in the KAPI

1 Samuel 19 in the KBT1ETNIK

1 Samuel 19 in the KBV

1 Samuel 19 in the KJV

1 Samuel 19 in the KNFD

1 Samuel 19 in the LBA

1 Samuel 19 in the LBLA

1 Samuel 19 in the LNT

1 Samuel 19 in the LSV

1 Samuel 19 in the MAAL

1 Samuel 19 in the MBV

1 Samuel 19 in the MBV2

1 Samuel 19 in the MHNT

1 Samuel 19 in the MKNFD

1 Samuel 19 in the MNG

1 Samuel 19 in the MNT

1 Samuel 19 in the MNT2

1 Samuel 19 in the MRS1T

1 Samuel 19 in the NAA

1 Samuel 19 in the NASB

1 Samuel 19 in the NBLA

1 Samuel 19 in the NBS

1 Samuel 19 in the NBVTP

1 Samuel 19 in the NET2

1 Samuel 19 in the NIV11

1 Samuel 19 in the NNT

1 Samuel 19 in the NNT2

1 Samuel 19 in the NNT3

1 Samuel 19 in the PDDPT

1 Samuel 19 in the PFNT

1 Samuel 19 in the RMNT

1 Samuel 19 in the SBIAS

1 Samuel 19 in the SBIBS

1 Samuel 19 in the SBIBS2

1 Samuel 19 in the SBICS

1 Samuel 19 in the SBIDS

1 Samuel 19 in the SBIGS

1 Samuel 19 in the SBIHS

1 Samuel 19 in the SBIIS

1 Samuel 19 in the SBIIS2

1 Samuel 19 in the SBIIS3

1 Samuel 19 in the SBIKS

1 Samuel 19 in the SBIKS2

1 Samuel 19 in the SBIMS

1 Samuel 19 in the SBIOS

1 Samuel 19 in the SBIPS

1 Samuel 19 in the SBISS

1 Samuel 19 in the SBITS

1 Samuel 19 in the SBITS2

1 Samuel 19 in the SBITS3

1 Samuel 19 in the SBITS4

1 Samuel 19 in the SBIUS

1 Samuel 19 in the SBIVS

1 Samuel 19 in the SBT

1 Samuel 19 in the SBT1E

1 Samuel 19 in the SCHL

1 Samuel 19 in the SNT

1 Samuel 19 in the SUSU

1 Samuel 19 in the SUSU2

1 Samuel 19 in the SYNO

1 Samuel 19 in the TBIAOTANT

1 Samuel 19 in the TBT1E

1 Samuel 19 in the TBT1E2

1 Samuel 19 in the TFTIP

1 Samuel 19 in the TFTU

1 Samuel 19 in the TGNTATF3T

1 Samuel 19 in the THAI

1 Samuel 19 in the TNFD

1 Samuel 19 in the TNT

1 Samuel 19 in the TNTIK

1 Samuel 19 in the TNTIL

1 Samuel 19 in the TNTIN

1 Samuel 19 in the TNTIP

1 Samuel 19 in the TNTIZ

1 Samuel 19 in the TOMA

1 Samuel 19 in the TTENT

1 Samuel 19 in the UBG

1 Samuel 19 in the UGV

1 Samuel 19 in the UGV2

1 Samuel 19 in the UGV3

1 Samuel 19 in the VBL

1 Samuel 19 in the VDCC

1 Samuel 19 in the YALU

1 Samuel 19 in the YAPE

1 Samuel 19 in the YBVTP

1 Samuel 19 in the ZBP